Quran with Chichewa translation - Surah Al-hadid ayat 20 - الحدِيد - Page - Juz 27
﴿ٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّمَا ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا لَعِبٞ وَلَهۡوٞ وَزِينَةٞ وَتَفَاخُرُۢ بَيۡنَكُمۡ وَتَكَاثُرٞ فِي ٱلۡأَمۡوَٰلِ وَٱلۡأَوۡلَٰدِۖ كَمَثَلِ غَيۡثٍ أَعۡجَبَ ٱلۡكُفَّارَ نَبَاتُهُۥ ثُمَّ يَهِيجُ فَتَرَىٰهُ مُصۡفَرّٗا ثُمَّ يَكُونُ حُطَٰمٗاۖ وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِ عَذَابٞ شَدِيدٞ وَمَغۡفِرَةٞ مِّنَ ٱللَّهِ وَرِضۡوَٰنٞۚ وَمَا ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَآ إِلَّا مَتَٰعُ ٱلۡغُرُورِ ﴾
[الحدِيد: 20]
﴿اعلموا أنما الحياة الدنيا لعب ولهو وزينة وتفاخر بينكم وتكاثر في الأموال﴾ [الحدِيد: 20]
Khaled Ibrahim Betala “Dziwani kuti ndithu moyo wa pa dziko lapansi ndimasewera, chibwana, chokometsera chabe, chonyadiritsana pakati panu (pa ulemelero) ndi kuchulukitsa chuma ndi ana (pomwe zonsezo sizikhala nthawi yayitali;) fanizo lake lili ngati mvula yomwe mmera wake umakondweretsa alimi; kenako umafota, ndipo uuona uli wachikasu; kenako nkukhala odukaduka (oonongeka). Koma tsiku lachimaliziro kuli chilango cha ukali; ndi chikhululuko komanso chikondi chochokera kwa Allah. Moyo wa pa dziko lapansi suli kanthu, koma ndichisangalalo chonyenga basi |