Quran with Chichewa translation - Surah Al-An‘am ayat 148 - الأنعَام - Page - Juz 8
﴿سَيَقُولُ ٱلَّذِينَ أَشۡرَكُواْ لَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَآ أَشۡرَكۡنَا وَلَآ ءَابَآؤُنَا وَلَا حَرَّمۡنَا مِن شَيۡءٖۚ كَذَٰلِكَ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ حَتَّىٰ ذَاقُواْ بَأۡسَنَاۗ قُلۡ هَلۡ عِندَكُم مِّنۡ عِلۡمٖ فَتُخۡرِجُوهُ لَنَآۖ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَإِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا تَخۡرُصُونَ ﴾
[الأنعَام: 148]
﴿سيقول الذين أشركوا لو شاء الله ما أشركنا ولا آباؤنا ولا حرمنا﴾ [الأنعَام: 148]
Khaled Ibrahim Betala “Amene akuphatikiza (Allah ndi mafano) anena: “Ngati Allah akadafuna, sitikadam’phatikiza, ife ngakhale makolo athu. Ndipo sitikadaletsa chilichonse. (Choncho, izi zomwe tikuchita, Allah akuziyanja). Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo kufikira adalawa chilango chathu. Nena: “Kodi muli nako kudziwa (kokutsimikizirani zimenezi), koti mungatitulutsire (umboni wake wotsimikizira kuti Allah adakulamulani zimenezi)? Inu simutsatira china, koma zongoganizira basi. Ndipo Simukunena china koma zabodza basi.” |