Quran with Chichewa translation - Surah Al-A‘raf ayat 43 - الأعرَاف - Page - Juz 8
﴿وَنَزَعۡنَا مَا فِي صُدُورِهِم مِّنۡ غِلّٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهِمُ ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ وَقَالُواْ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي هَدَىٰنَا لِهَٰذَا وَمَا كُنَّا لِنَهۡتَدِيَ لَوۡلَآ أَنۡ هَدَىٰنَا ٱللَّهُۖ لَقَدۡ جَآءَتۡ رُسُلُ رَبِّنَا بِٱلۡحَقِّۖ وَنُودُوٓاْ أَن تِلۡكُمُ ٱلۡجَنَّةُ أُورِثۡتُمُوهَا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ ﴾
[الأعرَاف: 43]
﴿ونـزعنا ما في صدورهم من غل تجري من تحتهم الأنهار وقالوا الحمد﴾ [الأعرَاف: 43]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo tidzachotsa kusakondana (komwe kudali) m’mitima mwawo; (adzakhala okondana ngakhale pa dziko lapansi adali odana), uku pansi ndi patsogolo pawo mitsinje ikuyenda; ndipo adzanena (m’kuthokoza kwawo): “Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Yemwe adatitsogolera ku ichi (chomwe chatidzetsera mtendere). Sitikadaongoka pakadapanda Allah kutiongola. Atumiki a Mbuye wathu adadza ndi choonadi.” Ndipo adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): “Uwu ndi Munda wamtendere umene mwapatsidwa chifukwa cha zomwe mudali kuchita.” |