×

Sikunali koyenera kwa anthu a ku Medina ndi Maarabu a mchipululu a 9:120 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah At-Taubah ⮕ (9:120) ayat 120 in Chichewa

9:120 Surah At-Taubah ayat 120 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 120 - التوبَة - Page - Juz 11

﴿مَا كَانَ لِأَهۡلِ ٱلۡمَدِينَةِ وَمَنۡ حَوۡلَهُم مِّنَ ٱلۡأَعۡرَابِ أَن يَتَخَلَّفُواْ عَن رَّسُولِ ٱللَّهِ وَلَا يَرۡغَبُواْ بِأَنفُسِهِمۡ عَن نَّفۡسِهِۦۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ لَا يُصِيبُهُمۡ ظَمَأٞ وَلَا نَصَبٞ وَلَا مَخۡمَصَةٞ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ وَلَا يَطَـُٔونَ مَوۡطِئٗا يَغِيظُ ٱلۡكُفَّارَ وَلَا يَنَالُونَ مِنۡ عَدُوّٖ نَّيۡلًا إِلَّا كُتِبَ لَهُم بِهِۦ عَمَلٞ صَٰلِحٌۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُضِيعُ أَجۡرَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ ﴾
[التوبَة: 120]

Sikunali koyenera kwa anthu a ku Medina ndi Maarabu a mchipululu a m’mbali mwawo kutsalira m’mbuyo mwa Mtumwi wa Mulungu kapena kukonda miyoyo yawo kuposa moyo wake. Icho ndi chifukwa chakuti iwo savutika ndi ludzu kapena kutopa kapena njala mu njira ya Mulungu kapena sachita chinthu chowanyasa anthu osakhulupirira kapena kubweretsa mavuto pa adani koma kudalembedwa kwa iwo kuti ndi ntchito yabwino. Ndithudi Mulungu saononga mphotho ya a anthu ochita zabwino

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ما كان لأهل المدينة ومن حولهم من الأعراب أن يتخلفوا عن رسول, باللغة نيانجا

﴿ما كان لأهل المدينة ومن حولهم من الأعراب أن يتخلفوا عن رسول﴾ [التوبَة: 120]

Khaled Ibrahim Betala
“Nkosayenera kwa anthu a mu mzinda wa Madina ndi amene ali m’mphepete mwawo, mwa Arabu a kuchimizi, kutsalira m’mbuyo mwa Mtumiki wa Allah (poleka kutsagana naye ku nkhondo), ndiponso nkosayenera kwa iwo kudzikonda okha kuposa iye (Mtumiki). Zimenezo nchifukwa chakuti iwo silingaapeze ludzu kapena mavuto kapena njala pa njira ya Allah, ndipo sangaponde malo owakwiitsa osakhulupirira, ndipo sangampatse mdani chompatsa chilichonse chopweteka koma kulembedwa kwa iwo pa zimenezo (kuti achita) ntchito yabwino. Ndithu Allah sawononga malipiro a ochita zabwino
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek