Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 61 - التوبَة - Page - Juz 10
﴿وَمِنۡهُمُ ٱلَّذِينَ يُؤۡذُونَ ٱلنَّبِيَّ وَيَقُولُونَ هُوَ أُذُنٞۚ قُلۡ أُذُنُ خَيۡرٖ لَّكُمۡ يُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ وَيُؤۡمِنُ لِلۡمُؤۡمِنِينَ وَرَحۡمَةٞ لِّلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنكُمۡۚ وَٱلَّذِينَ يُؤۡذُونَ رَسُولَ ٱللَّهِ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ ﴾
[التوبَة: 61]
﴿ومنهم الذين يؤذون النبي ويقولون هو أذن قل أذن خير لكم يؤمن﴾ [التوبَة: 61]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo alipo ena mwa iwo amene akuzunza Mneneri ponena kuti: “Uyu ndi khutu (lomvetsera nkhani iliyonse popanda kuiganizira).” Nena: “Ndi khutu labwino kwa inu.” (Mwini khutulo) amakhulupirira Allah, amakhulupirira (zonena) za okhulupirira, ndipo (iye) ndichifundo kwa amene akhulupirira mwa inu. Ndipo amene akuvutitsa Mtumiki wa Allah adzakhala ndi chilango chopweteka |