Quran with Chichewa translation - Surah Ar-Ra‘d ayat 33 - الرَّعد - Page - Juz 13
﴿أَفَمَنۡ هُوَ قَآئِمٌ عَلَىٰ كُلِّ نَفۡسِۭ بِمَا كَسَبَتۡۗ وَجَعَلُواْ لِلَّهِ شُرَكَآءَ قُلۡ سَمُّوهُمۡۚ أَمۡ تُنَبِّـُٔونَهُۥ بِمَا لَا يَعۡلَمُ فِي ٱلۡأَرۡضِ أَم بِظَٰهِرٖ مِّنَ ٱلۡقَوۡلِۗ بَلۡ زُيِّنَ لِلَّذِينَ كَفَرُواْ مَكۡرُهُمۡ وَصُدُّواْ عَنِ ٱلسَّبِيلِۗ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِنۡ هَادٖ ﴾
[الرَّعد: 33]
﴿أفمن هو قائم على كل نفس بما كسبت وجعلوا لله شركاء قل﴾ [الرَّعد: 33]
Khaled Ibrahim Betala “Kodi amene akuimilira mzimu uliwonse pa zimene udapeza (kuti adzaulipire, sindiye woyenera kupembedzedwa)? Ndipo ampangira Allah anzake. Nena: “Atchuleni (anzakewo).” Kodi kapena mukumuuza zomwe sakuzidziwa pa dziko, kapena (zomwe mukunenazo) ndimawu chabe (opanda cholinga chilichonse)? Koma amene sadakhulupirire akometsedwa ndi bodza lawoli lamkunkhuniza, ndipo atsekerezedwa kunjira (ya choonadi). Ndipo amene Allah wamulekelera kusokera alibe muongoli (wina womuongolera) |