Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 93 - البَقَرَة - Page - Juz 1
﴿وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِيثَٰقَكُمۡ وَرَفَعۡنَا فَوۡقَكُمُ ٱلطُّورَ خُذُواْ مَآ ءَاتَيۡنَٰكُم بِقُوَّةٖ وَٱسۡمَعُواْۖ قَالُواْ سَمِعۡنَا وَعَصَيۡنَا وَأُشۡرِبُواْ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلۡعِجۡلَ بِكُفۡرِهِمۡۚ قُلۡ بِئۡسَمَا يَأۡمُرُكُم بِهِۦٓ إِيمَٰنُكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ ﴾
[البَقَرَة: 93]
﴿وإذ أخذنا ميثاقكم ورفعنا فوقكم الطور خذوا ما آتيناكم بقوة واسمعوا قالوا﴾ [البَقَرَة: 93]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo (kumbukirani nkhani iyi, inu ana a Israyeli) pamene tidalandira kwa inu pangano lamphamvu, ndipo tidakukwezerani phiri pamwamba panu (uku tikuti): “Gwiritsani mwamphamvu (malamulo) amene takupatsani, ndipo mverani.” (Iwo) adati: “Tamva (mawu anu), koma tanyozera.” Ndipo adamwetsedwa m’mitima mwawo kukonda kupembedza thole (mwana wang’ombe) chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Nena: “N’choipa zedi chimene chikhulupiliro chanu chikukulamulirani ngati inu mulidi okhulupirira.” |