Quran with Chichewa translation - Surah al-‘Imran ayat 167 - آل عِمران - Page - Juz 4
﴿وَلِيَعۡلَمَ ٱلَّذِينَ نَافَقُواْۚ وَقِيلَ لَهُمۡ تَعَالَوۡاْ قَٰتِلُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ أَوِ ٱدۡفَعُواْۖ قَالُواْ لَوۡ نَعۡلَمُ قِتَالٗا لَّٱتَّبَعۡنَٰكُمۡۗ هُمۡ لِلۡكُفۡرِ يَوۡمَئِذٍ أَقۡرَبُ مِنۡهُمۡ لِلۡإِيمَٰنِۚ يَقُولُونَ بِأَفۡوَٰهِهِم مَّا لَيۡسَ فِي قُلُوبِهِمۡۚ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا يَكۡتُمُونَ ﴾
[آل عِمران: 167]
﴿وليعلم الذين نافقوا وقيل لهم تعالوا قاتلوا في سبيل الله أو ادفعوا﴾ [آل عِمران: 167]
Khaled Ibrahim Betala “Ndi kuwadziwitsa amene adachita uchiphamaso. Iwo adauzidwa: “Bwerani, menyani (nkhondo) pa njira ya Allah kapena mwatsekereze (adani kwa ife).” Adati: “Tikadadziwa kuti pali kumenyana, ndithudi, tikadakutsatani (koma kumeneko kuli kuphedwa kokhakokha basi).” Iwo tsiku limenelo adali pafupi ndikusakhulupirira kuposa chikhulupiliro (ngakhale kuti masiku onse amasonyeza Chisilamu mwa chiphamaso). Akunena ndi milomo yawo zomwe sizili m’mitima mwawo. Koma Allah akudziwa bwinobwino (zonse) zomwe akubisa |