Quran with Chichewa translation - Surah al-‘Imran ayat 195 - آل عِمران - Page - Juz 4
﴿فَٱسۡتَجَابَ لَهُمۡ رَبُّهُمۡ أَنِّي لَآ أُضِيعُ عَمَلَ عَٰمِلٖ مِّنكُم مِّن ذَكَرٍ أَوۡ أُنثَىٰۖ بَعۡضُكُم مِّنۢ بَعۡضٖۖ فَٱلَّذِينَ هَاجَرُواْ وَأُخۡرِجُواْ مِن دِيَٰرِهِمۡ وَأُوذُواْ فِي سَبِيلِي وَقَٰتَلُواْ وَقُتِلُواْ لَأُكَفِّرَنَّ عَنۡهُمۡ سَيِّـَٔاتِهِمۡ وَلَأُدۡخِلَنَّهُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ ثَوَابٗا مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِۚ وَٱللَّهُ عِندَهُۥ حُسۡنُ ٱلثَّوَابِ ﴾
[آل عِمران: 195]
﴿فاستجاب لهم ربهم أني لا أضيع عمل عامل منكم من ذكر أو﴾ [آل عِمران: 195]
Khaled Ibrahim Betala “Choncho Mbuye wawo adawavomereza (zopempha zawo ponena kuti): “Ndithudi, ine sindidzasokoneza (khama la) ntchito yabwino kwa ochita ntchito mwa inu, kaya atakhala mwamuna kapena mkazi, (pakuti) inu ndinu amodzi. Choncho amene asamuka (kumidzi yawo mwachifuniro chawo), naapirikitsidwa m’midzi yawo navutitsidwa pa njira Yanga, namenya nkhondo ndikuphedwa, ndithudi, ndiwafafanizira zolakwa zawo. Ndipo ndidzawalowetsa m’Minda yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda. Amenewo ndimalipiro ochokera kwa Allah, ndipo kwa Allah kuli malipiro abwino.” |