Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 97 - النِّسَاء - Page - Juz 5
﴿إِنَّ ٱلَّذِينَ تَوَفَّىٰهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ ظَالِمِيٓ أَنفُسِهِمۡ قَالُواْ فِيمَ كُنتُمۡۖ قَالُواْ كُنَّا مُسۡتَضۡعَفِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِۚ قَالُوٓاْ أَلَمۡ تَكُنۡ أَرۡضُ ٱللَّهِ وَٰسِعَةٗ فَتُهَاجِرُواْ فِيهَاۚ فَأُوْلَٰٓئِكَ مَأۡوَىٰهُمۡ جَهَنَّمُۖ وَسَآءَتۡ مَصِيرًا ﴾
[النِّسَاء: 97]
﴿إن الذين توفاهم الملائكة ظالمي أنفسهم قالوا فيم كنتم قالوا كنا مستضعفين﴾ [النِّسَاء: 97]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithudi amene angelo atenga miyoyo yawo, ali odzichitira okha zoipa (posasamuka ku Makka), adzawauza kuti: “Mudachitanji (pachipembedzo chanu?)” Iwo adzati: “Tidali ofooka ndi oponderezedwa padziko; (choncho sitidathe kuchita mapemphero athu).” (Angelo) adzati: “Kodi dziko la Allah silidali lotambasuka kotero kuti inu nkusamukira kwina m’menemo?” Iwowo malo awo ndi Jahannam. Taonani kuipa kwa malo obwerera |