Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ahqaf ayat 8 - الأحقَاف - Page - Juz 26
﴿أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۖ قُلۡ إِنِ ٱفۡتَرَيۡتُهُۥ فَلَا تَمۡلِكُونَ لِي مِنَ ٱللَّهِ شَيۡـًٔاۖ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَا تُفِيضُونَ فِيهِۚ كَفَىٰ بِهِۦ شَهِيدَۢا بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡۖ وَهُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ ﴾
[الأحقَاف: 8]
﴿أم يقولون افتراه قل إن افتريته فلا تملكون لي من الله شيئا﴾ [الأحقَاف: 8]
Khaled Ibrahim Betala “Kapena akunena kuti: “Waipeka (Qur’an)?” Nena: “Ngati ine ndaipeka, tero simungapeze chondithandizira nacho kwa Allah (ku chilango Chake). Iye ndiwodziwa kwambiri zimene mukuzijijirikira. Iye akukwana kukhala mboni pakati pa ine ndi inu ndipo Iye Ngokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha.” |