Quran with Chichewa translation - Surah Al-hashr ayat 2 - الحَشر - Page - Juz 28
﴿هُوَ ٱلَّذِيٓ أَخۡرَجَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ مِن دِيَٰرِهِمۡ لِأَوَّلِ ٱلۡحَشۡرِۚ مَا ظَنَنتُمۡ أَن يَخۡرُجُواْۖ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُم مَّانِعَتُهُمۡ حُصُونُهُم مِّنَ ٱللَّهِ فَأَتَىٰهُمُ ٱللَّهُ مِنۡ حَيۡثُ لَمۡ يَحۡتَسِبُواْۖ وَقَذَفَ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلرُّعۡبَۚ يُخۡرِبُونَ بُيُوتَهُم بِأَيۡدِيهِمۡ وَأَيۡدِي ٱلۡمُؤۡمِنِينَ فَٱعۡتَبِرُواْ يَٰٓأُوْلِي ٱلۡأَبۡصَٰرِ ﴾
[الحَشر: 2]
﴿هو الذي أخرج الذين كفروا من أهل الكتاب من ديارهم لأول الحشر﴾ [الحَشر: 2]
Khaled Ibrahim Betala “Iye ndi Amene adatulutsa osakhulupirira ena mwa anthu a buku m’nyumba zawo mkusamusidwa koyamba (pa chilumba cha Arabu). Simunkaganizira kuti angatuluke (m’nyumba zawozo). Ndipo iwo amaganiza kuti malinga awo awateteza kwa Allah. Koma Allah adawalanga kupyolera mmene samayembekezera, ndipo adathira mantha oopsa m’mitima mwawo (potumiza Mtumiki Wake kwa iwo), adagumula nyumba zawo ndi manja awo ndi manja a okhulupirira. Choncho lingalirani (zimenezi) E inu eni nzeru |