Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 80 - التوبَة - Page - Juz 10
﴿ٱسۡتَغۡفِرۡ لَهُمۡ أَوۡ لَا تَسۡتَغۡفِرۡ لَهُمۡ إِن تَسۡتَغۡفِرۡ لَهُمۡ سَبۡعِينَ مَرَّةٗ فَلَن يَغۡفِرَ ٱللَّهُ لَهُمۡۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ كَفَرُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦۗ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡفَٰسِقِينَ ﴾
[التوبَة: 80]
﴿استغفر لهم أو لا تستغفر لهم إن تستغفر لهم سبعين مرة فلن﴾ [التوبَة: 80]
Khaled Ibrahim Betala “(E iwe Mtumiki!) Uwapemphere chikhululuko (achiphamaso) kapena usawapemphere, (zonsezo nchimodzimodzi). Ngakhale utawapemphera chikhululuko chochuluka kwabasi mokwanira makumi asanu ndi awiri Allah sangawakhululukire. Zimenezo nchifukwa chakuti iwo amkana Allah ndi Mtumiki Wake. Ndipo Allah satsogolera anthu ophwanya malamulo (Ake) |