×

Surah Al-Furqan in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Furqan

Translation of the Meanings of Surah Furqan in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Furqan translated into Chichewa, Surah Al-Furqan in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Furqan in Chichewa - نيانجا, Verses 77 - Surah Number 25 - Page 359.

بسم الله الرحمن الرحيم

تَبَارَكَ الَّذِي نَزَّلَ الْفُرْقَانَ عَلَىٰ عَبْدِهِ لِيَكُونَ لِلْعَالَمِينَ نَذِيرًا (1)
Alemekezeke Iye amene adavumbulutsa Korani kwa Mtumwi wake kuti akhoza kuchenjeza mitundu ya anthu
الَّذِي لَهُ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَلَمْ يَتَّخِذْ وَلَدًا وَلَمْ يَكُن لَّهُ شَرِيكٌ فِي الْمُلْكِ وَخَلَقَ كُلَّ شَيْءٍ فَقَدَّرَهُ تَقْدِيرًا (2)
Iye ndiye Mfumu ya kumwamba ndi dziko lapansi. Iye ndiye amene sadabereke mwana ndipo alibe wothandizana naye mu Ufumu wake. Iye ndiye amene adalenga zinthu zonse ndipo adakhazikitsa mmene zili ndi mapeto ake
وَاتَّخَذُوا مِن دُونِهِ آلِهَةً لَّا يَخْلُقُونَ شَيْئًا وَهُمْ يُخْلَقُونَ وَلَا يَمْلِكُونَ لِأَنفُسِهِمْ ضَرًّا وَلَا نَفْعًا وَلَا يَمْلِكُونَ مَوْتًا وَلَا حَيَاةً وَلَا نُشُورًا (3)
Komabe anthu osakhulupirira amapembedza milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni imene siingathe kulenga china chilichonse chifukwa chakuti nayonso idachita kulengedwa. Ndi imene singathe kuwathandiza kapena kuwaononga ndiponso imene ilibe mphamvu pa nkhani zokhudza imfa kapena moyo kapena kuukitsa anthu akufa
وَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا إِنْ هَٰذَا إِلَّا إِفْكٌ افْتَرَاهُ وَأَعَانَهُ عَلَيْهِ قَوْمٌ آخَرُونَ ۖ فَقَدْ جَاءُوا ظُلْمًا وَزُورًا (4)
Anthu osakhulupirira amanena kuti, “Zonsezi ndi zinthu zabodza zimene wapeka yekha, ndiponso anthu ena amamuthandiza. Zonse zimene watulutsa ndi zopanda pake ndipo zabodza
وَقَالُوا أَسَاطِيرُ الْأَوَّلِينَ اكْتَتَبَهَا فَهِيَ تُمْلَىٰ عَلَيْهِ بُكْرَةً وَأَصِيلًا (5)
Ndipo iwo amati, “Izi ndi nkhani zopanda pake za anthu amakedzana zimene iye walemba. Izo zimalembetsedwa kwa Iye m’mawa ndi masana aliwonse.”
قُلْ أَنزَلَهُ الَّذِي يَعْلَمُ السِّرَّ فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ إِنَّهُ كَانَ غَفُورًا رَّحِيمًا (6)
Nena, “Wavumbulutsa ndiye amene amadziwa zinsinsi za kumwamba ndi za padziko lapansi. Iye amakhululukira ndipo ndi Mwini chisoni chosatha.”
وَقَالُوا مَالِ هَٰذَا الرَّسُولِ يَأْكُلُ الطَّعَامَ وَيَمْشِي فِي الْأَسْوَاقِ ۙ لَوْلَا أُنزِلَ إِلَيْهِ مَلَكٌ فَيَكُونَ مَعَهُ نَذِيرًا (7)
Iwo amanena kuti, “Uyu, ndi Mtumwi wotani amene amadya ndipo amayendayenda ku msika? Kodi bwanji mngelo sanathe kutumizidwa pansi pamodzi ndi iye kudzatichenjeza ife?”
أَوْ يُلْقَىٰ إِلَيْهِ كَنزٌ أَوْ تَكُونُ لَهُ جَنَّةٌ يَأْكُلُ مِنْهَا ۚ وَقَالَ الظَّالِمُونَ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا رَجُلًا مَّسْحُورًا (8)
“Nanga ndi chifukwa chiyani sadapatsidwe chuma ndipo alibe munda woti azipezako chakudya?” Ndipo anthu ochita zoipa amati, “Ndithudi munthu amene muli kumutsatira ndi wolodzedwa.”
انظُرْ كَيْفَ ضَرَبُوا لَكَ الْأَمْثَالَ فَضَلُّوا فَلَا يَسْتَطِيعُونَ سَبِيلًا (9)
Taona mafanizo amene amakupatsa iwe! Iwo asochera ndipo sangathe kubwerera kunjira yoyenera
تَبَارَكَ الَّذِي إِن شَاءَ جَعَلَ لَكَ خَيْرًا مِّن ذَٰلِكَ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ وَيَجْعَل لَّكَ قُصُورًا (10)
Alemekezeke Iye amene, ngati afuna akhoza kukupatsa iwe zinthu zabwino kuposa zimenezi monga minda yothiriridwa ndi madzi a m’mitsinje ndi nyumba zachifumu
بَلْ كَذَّبُوا بِالسَّاعَةِ ۖ وَأَعْتَدْنَا لِمَن كَذَّبَ بِالسَّاعَةِ سَعِيرًا (11)
Iyayi. Iwo amakana ola lachiweruzo, ndipo iwo amene amakana olali, Ife tawakonzera moto woyaka
إِذَا رَأَتْهُم مِّن مَّكَانٍ بَعِيدٍ سَمِعُوا لَهَا تَغَيُّظًا وَزَفِيرًا (12)
Pamene idzawaona iwo kuchokera kutali, iwo adzamva mkokomo wake
وَإِذَا أُلْقُوا مِنْهَا مَكَانًا ضَيِّقًا مُّقَرَّنِينَ دَعَوْا هُنَالِكَ ثُبُورًا (13)
Ndipo onse akadzamangidwa limodzi, adzaponyedwa kumalo opanikizika. Ndithudi iwo adzafuna imfa itadza pa iwo
لَّا تَدْعُوا الْيَوْمَ ثُبُورًا وَاحِدًا وَادْعُوا ثُبُورًا كَثِيرًا (14)
Lero musaitane imfa imodzi yokha ayi koma itanani imfa zambiri
قُلْ أَذَٰلِكَ خَيْرٌ أَمْ جَنَّةُ الْخُلْدِ الَّتِي وُعِدَ الْمُتَّقُونَ ۚ كَانَتْ لَهُمْ جَزَاءً وَمَصِيرًا (15)
Nena, “Kodi chimenecho ndi chabwino kapena Paradiso yosatha imene anthu angwiro adalonjezedwa?” Imeneyo ndiyo mphotho yawo ndi kobwerera kwawo
لَّهُمْ فِيهَا مَا يَشَاءُونَ خَالِدِينَ ۚ كَانَ عَلَىٰ رَبِّكَ وَعْدًا مَّسْئُولًا (16)
Iwo adzapeza m’menemo zonse zimene anali kufuna ndi kukhala momwemo. Limenelo ndilo lonjezo limene ndi lofunika kumapempha pafupipafupi kuchokera kwa Ambuye wako
وَيَوْمَ يَحْشُرُهُمْ وَمَا يَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ فَيَقُولُ أَأَنتُمْ أَضْلَلْتُمْ عِبَادِي هَٰؤُلَاءِ أَمْ هُمْ ضَلُّوا السَّبِيلَ (17)
Patsiku limene Iye adzawasonkhanitsa onse ndi zomwe amapembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo Iye adzati, “Kodi ndinu amene munasocheza akapolo anga kapena ndi iwo okha anasochera ku njira yoyenera?”
قَالُوا سُبْحَانَكَ مَا كَانَ يَنبَغِي لَنَا أَن نَّتَّخِذَ مِن دُونِكَ مِنْ أَوْلِيَاءَ وَلَٰكِن مَّتَّعْتَهُمْ وَآبَاءَهُمْ حَتَّىٰ نَسُوا الذِّكْرَ وَكَانُوا قَوْمًا بُورًا (18)
Iwo adzati, “Ulemerero ukhale kwa Inu! Si koyenera kwa ife kuti tisankhe otisamalira ena oonjezera pa Inu. Koma Inu mudawapatsa iwo ndi makolo awo zinthu zokoma za dziko, kotero kuti iwo adaiwala chenjezo lanu ndipo adali anthu oonongeka.”
فَقَدْ كَذَّبُوكُم بِمَا تَقُولُونَ فَمَا تَسْتَطِيعُونَ صَرْفًا وَلَا نَصْرًا ۚ وَمَن يَظْلِم مِّنكُمْ نُذِقْهُ عَذَابًا كَبِيرًا (19)
Kotero iwo adatsutsa mawu anu ndipo inu simungathe kuthawa kapena kupeza chithandizo ndipo aliyense amene ndi wosalungama pakati panu, Ife tidzamupatsa chilango chachikulu
وَمَا أَرْسَلْنَا قَبْلَكَ مِنَ الْمُرْسَلِينَ إِلَّا إِنَّهُمْ لَيَأْكُلُونَ الطَّعَامَ وَيَمْشُونَ فِي الْأَسْوَاقِ ۗ وَجَعَلْنَا بَعْضَكُمْ لِبَعْضٍ فِتْنَةً أَتَصْبِرُونَ ۗ وَكَانَ رَبُّكَ بَصِيرًا (20)
Ife sitidatumizepo Atumwi kale amene sanali kudya ndi kuyenda m’misika. Ife tidakupangani ena a inu kukhala mayesero a ena. Kodi simungapirire? Ambuye wanu amaona chilichonse
۞ وَقَالَ الَّذِينَ لَا يَرْجُونَ لِقَاءَنَا لَوْلَا أُنزِلَ عَلَيْنَا الْمَلَائِكَةُ أَوْ نَرَىٰ رَبَّنَا ۗ لَقَدِ اسْتَكْبَرُوا فِي أَنفُسِهِمْ وَعَتَوْا عُتُوًّا كَبِيرًا (21)
Iwo amene alibe chikhulupiriro choti adzakumana ndi Ife amati, “Kodi ndi chifukwa chiyani angelo sadatumizidwe kwa ife? Kapena ndi chifukwa chiyani kuti ife sitingaone Ambuye wathu?” Ndithudi iwo adadzikweza kwambiri
يَوْمَ يَرَوْنَ الْمَلَائِكَةَ لَا بُشْرَىٰ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُجْرِمِينَ وَيَقُولُونَ حِجْرًا مَّحْجُورًا (22)
Patsiku limene iwo adzaona angelo, anthu ochita zoipa sadzasangalala ayi ndipo iwo adzati, “Ambuye wathu! Ikani malire pakati pa ife ndi iwo.”
وَقَدِمْنَا إِلَىٰ مَا عَمِلُوا مِنْ عَمَلٍ فَجَعَلْنَاهُ هَبَاءً مَّنثُورًا (23)
Ndipo Ife tidzabweretsa zonse zimene adachita ndikuzionetsa kuti ndi zinthu zopanda ntchito ngati fumbi louluka
أَصْحَابُ الْجَنَّةِ يَوْمَئِذٍ خَيْرٌ مُّسْتَقَرًّا وَأَحْسَنُ مَقِيلًا (24)
Anthu okhala ku Paradiso, adzakhala kumalo abwino patsiku limeneli ndiponso malo abwino opumulako
وَيَوْمَ تَشَقَّقُ السَّمَاءُ بِالْغَمَامِ وَنُزِّلَ الْمَلَائِكَةُ تَنزِيلًا (25)
Patsiku limeneli kumwamba pamodzi ndi mitambo yake idzagawanika pakati ndipo angelo adzatumizidwa pansi pano m’maudindo awo
الْمُلْكُ يَوْمَئِذٍ الْحَقُّ لِلرَّحْمَٰنِ ۚ وَكَانَ يَوْمًا عَلَى الْكَافِرِينَ عَسِيرًا (26)
Patsiku limeneli ufumu wonse udzakhala wa Mwini chisoni chosatha. Limeneli lidzakhala tsiku lovuta kwambiri kwa anthu osakhulupirira
وَيَوْمَ يَعَضُّ الظَّالِمُ عَلَىٰ يَدَيْهِ يَقُولُ يَا لَيْتَنِي اتَّخَذْتُ مَعَ الرَّسُولِ سَبِيلًا (27)
Patsiku limeneli munthu ochita zoipa adzanong’oneza bombono nati, “Oh zikadakhala bwino ndikadakhala kuti ndidatsatira zimene Mtumwi anali kunena!”
يَا وَيْلَتَىٰ لَيْتَنِي لَمْ أَتَّخِذْ فُلَانًا خَلِيلًا (28)
“oh kalanga ine! Ndikadakhala kuti sindidasankhe a uje ndi a uje kuti akhale anzanga!”
لَّقَدْ أَضَلَّنِي عَنِ الذِّكْرِ بَعْدَ إِذْ جَاءَنِي ۗ وَكَانَ الشَّيْطَانُ لِلْإِنسَانِ خَذُولًا (29)
“Mosakayika ndiwo amene adandisokoneza ine kuti ndisakhulupirire machenjezo a Mulungu pamene machenjezowo atandifika. Ndithudi Satana ndi wachinyengo nthawi zonse kwa munthu.”
وَقَالَ الرَّسُولُ يَا رَبِّ إِنَّ قَوْمِي اتَّخَذُوا هَٰذَا الْقُرْآنَ مَهْجُورًا (30)
Mtumwi adati, “Ambuye wanga! Ndithudi anthu anga alikana Buku la Korani.”
وَكَذَٰلِكَ جَعَلْنَا لِكُلِّ نَبِيٍّ عَدُوًّا مِّنَ الْمُجْرِمِينَ ۗ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ هَادِيًا وَنَصِيرًا (31)
Motero Ife tapanga kwa Mtumwi aliyense mdani kuchokera kwa anthu ochimwa, anthu otsutsana naye, ndipo Ambuye wako ali wokwana kukhala wokutsogolera mu zabwino ndiponso ngati wokuthandiza wako
وَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا لَوْلَا نُزِّلَ عَلَيْهِ الْقُرْآنُ جُمْلَةً وَاحِدَةً ۚ كَذَٰلِكَ لِنُثَبِّتَ بِهِ فُؤَادَكَ ۖ وَرَتَّلْنَاهُ تَرْتِيلًا (32)
Anthu osakhulupirira anati, “Kodi ndi chifukwa chiyani Korani yonse siidavumbulutsidwe kwa iye nthawi imodzi?” Ife talivumbulutsa kotero kuti tikhoza kulimbikitsa mtima wako ndipo takupatsa ilo kwa iwe mu chivumbulutso chapang’onopang’ono
وَلَا يَأْتُونَكَ بِمَثَلٍ إِلَّا جِئْنَاكَ بِالْحَقِّ وَأَحْسَنَ تَفْسِيرًا (33)
Iwo sadzatha kubwera ndi mtsutso umene Ife sitidakonze yankho loona ndi kafotokozedwe kake
الَّذِينَ يُحْشَرُونَ عَلَىٰ وُجُوهِهِمْ إِلَىٰ جَهَنَّمَ أُولَٰئِكَ شَرٌّ مَّكَانًا وَأَضَلُّ سَبِيلًا (34)
Iwo adzaduduluzidwa cha mphumi kupita ku Gahena ndipo iwo adzakhala ndi malo oipa okhalamo ndipo njira yawo ndi yosochera
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ وَجَعَلْنَا مَعَهُ أَخَاهُ هَارُونَ وَزِيرًا (35)
Ndithudi Ife tidavumbulutsa mawu a Mulungu kwa Mose ndipo tidamupatsa m’bale wake Aroni kuti akhale nduna yomuthandiza
فَقُلْنَا اذْهَبَا إِلَى الْقَوْمِ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا فَدَمَّرْنَاهُمْ تَدْمِيرًا (36)
Tidawauza iwo kuti, “Pitani nonse kwa anthu amene adakana zizindikiro zathu” ndipo pambuyo pake tidawaononga kotheratu
وَقَوْمَ نُوحٍ لَّمَّا كَذَّبُوا الرُّسُلَ أَغْرَقْنَاهُمْ وَجَعَلْنَاهُمْ لِلنَّاسِ آيَةً ۖ وَأَعْتَدْنَا لِلظَّالِمِينَ عَذَابًا أَلِيمًا (37)
Akakhala anthu a Nowa, tidawamiza pamene iwo adakana Atumwi awo ndipo tidawapanga iwo kukhala phunziro kwa anthu a mitundu yonse. Ndipo anthu ochimwa tawakonzera chilango chowawa
وَعَادًا وَثَمُودَ وَأَصْحَابَ الرَّسِّ وَقُرُونًا بَيْنَ ذَٰلِكَ كَثِيرًا (38)
Mitundu ya anthu a ku Thamoud ndi Aad nawonso tidawaononga ndiponso iwo amene anali kukhala ku Raas ndi mibadwo yochuluka imene idadza pakati pawo
وَكُلًّا ضَرَبْنَا لَهُ الْأَمْثَالَ ۖ وَكُلًّا تَبَّرْنَا تَتْبِيرًا (39)
Ndipo onsewa, tidawapatsa zitsanzo ndipo onse tidawaononga kotheratu
وَلَقَدْ أَتَوْا عَلَى الْقَرْيَةِ الَّتِي أُمْطِرَتْ مَطَرَ السَّوْءِ ۚ أَفَلَمْ يَكُونُوا يَرَوْنَهَا ۚ بَلْ كَانُوا لَا يَرْجُونَ نُشُورًا (40)
Ndithudi anthu osakhulupirira adadutsa pa mzinda umene udaonongeka ndi madzi a mvula. Kodi iwo sadauone mzindawu? Komabe iwo adalibe chikhulupiriro mu kuukanso kwa akufa
وَإِذَا رَأَوْكَ إِن يَتَّخِذُونَكَ إِلَّا هُزُوًا أَهَٰذَا الَّذِي بَعَثَ اللَّهُ رَسُولًا (41)
Nthawi zonse akakuona iwe amakunyoza ndipo amati, “Kodi uyu ndiye munthu amene akuti Mulungu wamutumiza ngati Mtumwi wake?”
إِن كَادَ لَيُضِلُّنَا عَنْ آلِهَتِنَا لَوْلَا أَن صَبَرْنَا عَلَيْهَا ۚ وَسَوْفَ يَعْلَمُونَ حِينَ يَرَوْنَ الْعَذَابَ مَنْ أَضَلُّ سَبِيلًا (42)
Ngati ife tikadapanda kulimba popembedza milungu yathu ndithudi iye akadatitembenuza ife kuti tisiye milungu yathu. Koma posakhalitsa iwo adzaona chilango ndipo adzadziwa kuti ndani amene adasochera kwambiri
أَرَأَيْتَ مَنِ اتَّخَذَ إِلَٰهَهُ هَوَاهُ أَفَأَنتَ تَكُونُ عَلَيْهِ وَكِيلًا (43)
Kodi wamuona iye amene amayesa zilakolako zake ngati milungu? Kodi iwe ungakhale munthu wosamalira munthu wotere
أَمْ تَحْسَبُ أَنَّ أَكْثَرَهُمْ يَسْمَعُونَ أَوْ يَعْقِلُونَ ۚ إِنْ هُمْ إِلَّا كَالْأَنْعَامِ ۖ بَلْ هُمْ أَضَلُّ سَبِيلًا (44)
Kodi iwe umaganiza kuti ambiri a iwo angathe kumva kapena kuzindikira? Iwo si chinthu china chilichonse koma ali ngati nyama yosochera kwambiri
أَلَمْ تَرَ إِلَىٰ رَبِّكَ كَيْفَ مَدَّ الظِّلَّ وَلَوْ شَاءَ لَجَعَلَهُ سَاكِنًا ثُمَّ جَعَلْنَا الشَّمْسَ عَلَيْهِ دَلِيلًا (45)
Kodi iwe siuona mmeneAmbuye wako amatambasulira mthunzi? Mulungu akadafuna, akadaupanga kuti ukhale wokhazikika. Ndipo Ife tapanga dzuwa kukhala chizindikiro chake
ثُمَّ قَبَضْنَاهُ إِلَيْنَا قَبْضًا يَسِيرًا (46)
Ndipo timaubweretsa kwa Ife mwapang’onopang’onomosavuta
وَهُوَ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ اللَّيْلَ لِبَاسًا وَالنَّوْمَ سُبَاتًا وَجَعَلَ النَّهَارَ نُشُورًا (47)
Ndiyeamenewapanga usiku kukhala chofunda ndi tulo kuti tikhale mpumulo, ndipo wapanga usana kuti uzikhala nthawi yodzuka ndi kumagwira ntchito
وَهُوَ الَّذِي أَرْسَلَ الرِّيَاحَ بُشْرًا بَيْنَ يَدَيْ رَحْمَتِهِ ۚ وَأَنزَلْنَا مِنَ السَّمَاءِ مَاءً طَهُورًا (48)
Ndiye amene amatumiza mphepo ngati mthenga wobweretsa chisomo chake ndipo timatumiza madzi abwino kuchokera kumwamba
لِّنُحْيِيَ بِهِ بَلْدَةً مَّيْتًا وَنُسْقِيَهُ مِمَّا خَلَقْنَا أَنْعَامًا وَأَنَاسِيَّ كَثِيرًا (49)
Ndi cholinga choti tipereke moyo ku nthaka imene inali yakufa ndi kuti timwetse zinthu zimene talenga, nyama ndi anthu ambiri
وَلَقَدْ صَرَّفْنَاهُ بَيْنَهُمْ لِيَذَّكَّرُوا فَأَبَىٰ أَكْثَرُ النَّاسِ إِلَّا كُفُورًا (50)
Ndithudi tawatumizira pakati pawo, kuti akhoza kukumbukira, chisomo cha Mulungu koma anthu ambiri amakana. Ndipo iwo amasankha kusakhulupirira
وَلَوْ شِئْنَا لَبَعَثْنَا فِي كُلِّ قَرْيَةٍ نَّذِيرًا (51)
Chikadakhala chifuniro chathu, tikadautsa wowachenjeza ku mzinda uliwonse
فَلَا تُطِعِ الْكَافِرِينَ وَجَاهِدْهُم بِهِ جِهَادًا كَبِيرًا (52)
Iwe usawamvere anthu osakhulupirira koma limbana nawo kwambiri pogwiritsa ntchito Korani ino
۞ وَهُوَ الَّذِي مَرَجَ الْبَحْرَيْنِ هَٰذَا عَذْبٌ فُرَاتٌ وَهَٰذَا مِلْحٌ أُجَاجٌ وَجَعَلَ بَيْنَهُمَا بَرْزَخًا وَحِجْرًا مَّحْجُورًا (53)
Ndiye amene adatumiza nyanja ziwiri, ina yamadzi ozuna ndi abwino pamene ina ndi yamadzi a mchere ndi owawa ndipo adakhazikitsa malire olimba kwambiri pakati pa nyanjazi
وَهُوَ الَّذِي خَلَقَ مِنَ الْمَاءِ بَشَرًا فَجَعَلَهُ نَسَبًا وَصِهْرًا ۗ وَكَانَ رَبُّكَ قَدِيرًا (54)
Ndiye amene adamulenga munthu kuchokera ku madzi ndipo adamupatsa abale chifukwa cha magazi amodzi ndiponso chifukwa cha ukwati. Ndipo Ambuye wako ndiye mwini mphamvu zonse ndipo amachita zimene afuna
وَيَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ مَا لَا يَنفَعُهُمْ وَلَا يَضُرُّهُمْ ۗ وَكَانَ الْكَافِرُ عَلَىٰ رَبِّهِ ظَهِيرًا (55)
Komabe anthu osakhulupirira amapembedza mafano moonjezerapa Mulungu Mafanowosangathekuwathandiza kapena kuwaononga. Munthu wosakhulupirira amathandiza Satana kuchita zoipa zosakomera Ambuye wake
وَمَا أَرْسَلْنَاكَ إِلَّا مُبَشِّرًا وَنَذِيرًا (56)
Ndipo takutumiza iwe ngati wobweretsa nkhani yabwino ndiponso munthu wopereka chenjezo
قُلْ مَا أَسْأَلُكُمْ عَلَيْهِ مِنْ أَجْرٍ إِلَّا مَن شَاءَ أَن يَتَّخِذَ إِلَىٰ رَبِّهِ سَبِيلًا (57)
Nena, “Ine sindili kukupemphani malipiro pa ntchito iyi ayi kupatula kuti iye amene afuna atsatire njira yoyenera yopita kwa Ambuye wake.”
وَتَوَكَّلْ عَلَى الْحَيِّ الَّذِي لَا يَمُوتُ وَسَبِّحْ بِحَمْدِهِ ۚ وَكَفَىٰ بِهِ بِذُنُوبِ عِبَادِهِ خَبِيرًا (58)
Ndipo ika chikhulupiriro chako mwa Iye wa moyo amene sakufa ayi. Ndipo mulemekeze nthawi zonse. Iye ndi okwana chifukwa Iye amadziwa bwinobwino za machimo a akapolo ake
الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ وَمَا بَيْنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ ثُمَّ اسْتَوَىٰ عَلَى الْعَرْشِ ۚ الرَّحْمَٰنُ فَاسْأَلْ بِهِ خَبِيرًا (59)
Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo masiku asanu ndi limodzi. Ndipo atatero adabuka pa chimpando chaufumu, Mwini Chisononi chosatha. Motero mufunse Iye chifukwa amadziwa china chili chonse
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ اسْجُدُوا لِلرَّحْمَٰنِ قَالُوا وَمَا الرَّحْمَٰنُ أَنَسْجُدُ لِمَا تَأْمُرُنَا وَزَادَهُمْ نُفُورًا ۩ (60)
Pamene zimanenedwa kwa iwo kuti, “Lambirani Mwini chisoni chosatha,” Iwo amati; “Kodi Mwini chisoni chosatha ndani? Kodi iwe ufuna kuti ife tizipembedza chilichonse chimene iwe utilamula?” Mawu amenewa amaonjezera kukana kwawo
تَبَارَكَ الَّذِي جَعَلَ فِي السَّمَاءِ بُرُوجًا وَجَعَلَ فِيهَا سِرَاجًا وَقَمَرًا مُّنِيرًا (61)
Alemekezeke Iye amene adalenga gulu la nyenyezi kumtambo ndipo adalenga dzuwa ndi mwezi wowala
وَهُوَ الَّذِي جَعَلَ اللَّيْلَ وَالنَّهَارَ خِلْفَةً لِّمَنْ أَرَادَ أَن يَذَّكَّرَ أَوْ أَرَادَ شُكُورًا (62)
Ndipo ndiye amene amasinthanitsa usiku ndi usana chifukwa cha iye amene afuna kukumbukira kapena afuna kuonetsa kuyamika kwake
وَعِبَادُ الرَّحْمَٰنِ الَّذِينَ يَمْشُونَ عَلَى الْأَرْضِ هَوْنًا وَإِذَا خَاطَبَهُمُ الْجَاهِلُونَ قَالُوا سَلَامًا (63)
Ndipo akapolo a Mwini Chisoni Chosatha ndi iwo amene amayenda modzichepetsa padziko lapansi ndipo ngati mbuli zikawayankhula mwachipongwe iwo amayankha mwaulemu
وَالَّذِينَ يَبِيتُونَ لِرَبِّهِمْ سُجَّدًا وَقِيَامًا (64)
Ndipo iwo amene amachezera pamaso pa Ambuye wawo, amagwada ndi kuima
وَالَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا اصْرِفْ عَنَّا عَذَابَ جَهَنَّمَ ۖ إِنَّ عَذَابَهَا كَانَ غَرَامًا (65)
Amene amanena kuti, “Ambuye wathu! Tichotsereni chilango cha ku Gahena.” Ndithudi chilango chake ndi chosatha
إِنَّهَا سَاءَتْ مُسْتَقَرًّا وَمُقَامًا (66)
Ndithudi kumeneko ndi malo wonyansa kupumirako ndiponso malo wonyansa kukhalako
وَالَّذِينَ إِذَا أَنفَقُوا لَمْ يُسْرِفُوا وَلَمْ يَقْتُرُوا وَكَانَ بَيْنَ ذَٰلِكَ قَوَامًا (67)
Iwo akamapereka saononga chuma chawo moposa muyeso ndipo saumira koma amakhala pakatikati
وَالَّذِينَ لَا يَدْعُونَ مَعَ اللَّهِ إِلَٰهًا آخَرَ وَلَا يَقْتُلُونَ النَّفْسَ الَّتِي حَرَّمَ اللَّهُ إِلَّا بِالْحَقِّ وَلَا يَزْنُونَ ۚ وَمَن يَفْعَلْ ذَٰلِكَ يَلْقَ أَثَامًا (68)
Ndipo anthu amene sapembedza mulungu wina kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo sakupha mzimu umene Mulungu waletsa kupatula mu njira yachilungamo ndipo sachita chigololo. Ndipo aliyense amene achita izi adzalandira chilango
يُضَاعَفْ لَهُ الْعَذَابُ يَوْمَ الْقِيَامَةِ وَيَخْلُدْ فِيهِ مُهَانًا (69)
Chilango chake chidzaonjezedwa kawiri patsiku la kuuka kwa akufa ndipo adzakhala ndi manyazi nthawi zonse
إِلَّا مَن تَابَ وَآمَنَ وَعَمِلَ عَمَلًا صَالِحًا فَأُولَٰئِكَ يُبَدِّلُ اللَّهُ سَيِّئَاتِهِمْ حَسَنَاتٍ ۗ وَكَانَ اللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا (70)
Kupatula okhawo amene alapa ndi kukhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, chifukwa potero Mulungu adzasintha zoipa zawo kukhala ntchito zabwino. Ndipo Mulungu amakhululukira ndi wachisoni chosatha
وَمَن تَابَ وَعَمِلَ صَالِحًا فَإِنَّهُ يَتُوبُ إِلَى اللَّهِ مَتَابًا (71)
Iye amene alapa ndi kuchita ntchito zabwino, ndithudi, ndiye kuti wabwerera kwa Mulungu
وَالَّذِينَ لَا يَشْهَدُونَ الزُّورَ وَإِذَا مَرُّوا بِاللَّغْوِ مَرُّوا كِرَامًا (72)
Iwo amene sapereka umboni ku zinthu zabodza ndipo akamadutsa pamalo pamene pakuchitika zinthu zoipa kapena zoletsedwa, iwo amadutsa modzilemekeza
وَالَّذِينَ إِذَا ذُكِّرُوا بِآيَاتِ رَبِّهِمْ لَمْ يَخِرُّوا عَلَيْهَا صُمًّا وَعُمْيَانًا (73)
Amene sanyozera chivumbulutso cha Ambuye wawo ndipo pamene akumbutsidwa za icho sachita ngati kuti iwo ndi a gonthi kapena a khungu
وَالَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا هَبْ لَنَا مِنْ أَزْوَاجِنَا وَذُرِّيَّاتِنَا قُرَّةَ أَعْيُنٍ وَاجْعَلْنَا لِلْمُتَّقِينَ إِمَامًا (74)
Ndipo anthu amene amanena kuti, “Ambuye wathu! Tipatseni chisangalalo mu akazi ndi ana athu ndipo tipangeni ife kukhala atsogoleri a iwo amene amakuopani Inu!”
أُولَٰئِكَ يُجْزَوْنَ الْغُرْفَةَ بِمَا صَبَرُوا وَيُلَقَّوْنَ فِيهَا تَحِيَّةً وَسَلَامًا (75)
Amenewa adzalipidwa Paradiso wa pamwamba chifukwa cha kupirira kwawo. Kumeneko adzalandiridwa ndi malonje abwino mawu amtendere ndi aulemu
خَالِدِينَ فِيهَا ۚ حَسُنَتْ مُسْتَقَرًّا وَمُقَامًا (76)
Adzakhala kumeneko nthawi zonse ndipo ndi malo abwino kukhalako ndiponso ndi malo abwino opumirako
قُلْ مَا يَعْبَأُ بِكُمْ رَبِّي لَوْلَا دُعَاؤُكُمْ ۖ فَقَدْ كَذَّبْتُمْ فَسَوْفَ يَكُونُ لِزَامًا (77)
Nena “Ambuye wanga amakusamalani inu chifukwa cha mapempheroanuakwa Iyeyekha. Komatsopano, ndithudi, inu mwamukana Iye. Motero chilango chidzakhala chanu mpaka kalekale.”
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas