تَبَارَكَ الَّذِي بِيَدِهِ الْمُلْكُ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (1) wodalitsika ndiye amene mmanja mwake muli Ufumu ndipo ali ndi mphamvu pa zinthu zonse |
الَّذِي خَلَقَ الْمَوْتَ وَالْحَيَاةَ لِيَبْلُوَكُمْ أَيُّكُمْ أَحْسَنُ عَمَلًا ۚ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْغَفُورُ (2) Iye amene adalenga imfa ndi moyo kuti akhoza kukuyesani inu kuti ndani wa inu amene wasunga malamulo onse mwaubwino. Ndipo Iye ndi Wamphamvu ndi Wokhululukira |
الَّذِي خَلَقَ سَبْعَ سَمَاوَاتٍ طِبَاقًا ۖ مَّا تَرَىٰ فِي خَلْقِ الرَّحْمَٰنِ مِن تَفَاوُتٍ ۖ فَارْجِعِ الْبَصَرَ هَلْ تَرَىٰ مِن فُطُورٍ (3) Iye ndi amene adalenga miyamba isanu ndi iwiri, wina pamwamba pa unzake. Inu simungaone cholakwa china chilichonse mu chilengedwe cha Mwini chisoni chosatha. Tapenyetsetsani! Kodi inu mungaone cholakwika china chilichonse |
ثُمَّ ارْجِعِ الْبَصَرَ كَرَّتَيْنِ يَنقَلِبْ إِلَيْكَ الْبَصَرُ خَاسِئًا وَهُوَ حَسِيرٌ (4) Tapenyetsetsaninso! Ndipo mawonekedwe anu adzakubwererani pamene ali osokonezeka ndi otopa |
وَلَقَدْ زَيَّنَّا السَّمَاءَ الدُّنْيَا بِمَصَابِيحَ وَجَعَلْنَاهَا رُجُومًا لِّلشَّيَاطِينِ ۖ وَأَعْتَدْنَا لَهُمْ عَذَابَ السَّعِيرِ (5) Ndithudi Ife takongoletsa thambo loyamba ndi nyali ndipo tazipanga nyalizo ngati mipaliro yothamangitsira Satana ndipo tawakonzera iwo chilango chamoto woyaka |
وَلِلَّذِينَ كَفَرُوا بِرَبِّهِمْ عَذَابُ جَهَنَّمَ ۖ وَبِئْسَ الْمَصِيرُ (6) Ndipo iwo amene sakhulupirira mwa Ambuye wawo, kuli chilango cha kumoto ndipo chimaliziro chawo chidzakhala choipa |
إِذَا أُلْقُوا فِيهَا سَمِعُوا لَهَا شَهِيقًا وَهِيَ تَفُورُ (7) Ndipo pamene iwo adzaponyedwa m’moto, iwo adzaumva uli kuyaka ndi kubwata |
تَكَادُ تَمَيَّزُ مِنَ الْغَيْظِ ۖ كُلَّمَا أُلْقِيَ فِيهَا فَوْجٌ سَأَلَهُمْ خَزَنَتُهَا أَلَمْ يَأْتِكُمْ نَذِيرٌ (8) Pafupifupi kuphulika chifukwa cha kukwiya. Ndipo nthawi zonse pamene gulu liponyedwamo, amene amayang’anira moto adzafunsa kuti: “Kodi panalibe wina aliyense amene adadza kwa inu kudzakuchenjezani?” |
قَالُوا بَلَىٰ قَدْ جَاءَنَا نَذِيرٌ فَكَذَّبْنَا وَقُلْنَا مَا نَزَّلَ اللَّهُ مِن شَيْءٍ إِنْ أَنتُمْ إِلَّا فِي ضَلَالٍ كَبِيرٍ (9) Ndipo iwo adzati: “Inde. Ndithudi Mchenjezi adadza kwa ife koma tidamukana ndipo tinkati: Mulungu sadavumbulutse china chilichonse ndipo iwe ndiwe wosokoneza kwambiri.” |
وَقَالُوا لَوْ كُنَّا نَسْمَعُ أَوْ نَعْقِلُ مَا كُنَّا فِي أَصْحَابِ السَّعِيرِ (10) Ndipo iwo adzati: “Tikadakhala kuti tidamvera kapena kuganiza bwino, ife sitikadakhala m’gulu la anthu opita ku moto.” |
فَاعْتَرَفُوا بِذَنبِهِمْ فَسُحْقًا لِّأَصْحَابِ السَّعِيرِ (11) Motero iwo adzabvomera machimo awo. Motero apite kutali anthu a ku moto |
إِنَّ الَّذِينَ يَخْشَوْنَ رَبَّهُم بِالْغَيْبِ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَأَجْرٌ كَبِيرٌ (12) Ndithudi! Iwo amene amaopa Ambuye wawo ngakhale samuona, ndithudi, iwo adzawakhululukira machimo awo ndipo adzalandira mphotho ya mtengo wapatali |
وَأَسِرُّوا قَوْلَكُمْ أَوِ اجْهَرُوا بِهِ ۖ إِنَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (13) Ndipo kaya mubisa mawu anu kapena muulula, Iye amadziwa zonse zimene zili m’mitima mwanu |
أَلَا يَعْلَمُ مَنْ خَلَقَ وَهُوَ اللَّطِيفُ الْخَبِيرُ (14) Kodi Iye amene adalenga zinthu zonse asadziwe? Ndithudi Iye ndi wa Chisoni chosatha ndi Mwini kudziwa chili chonse |
هُوَ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ الْأَرْضَ ذَلُولًا فَامْشُوا فِي مَنَاكِبِهَا وَكُلُوا مِن رِّزْقِهِ ۖ وَإِلَيْهِ النُّشُورُ (15) Iye ndiye amene anakukonzerani dziko, motero pitani paliponse mu ilo, ndipo idyani zokoma zake zimene wakupatsanindipondikwaIyekumenezonsezidzabwerera |
أَأَمِنتُم مَّن فِي السَّمَاءِ أَن يَخْسِفَ بِكُمُ الْأَرْضَ فَإِذَا هِيَ تَمُورُ (16) Kodi inu mumaganiza kuti ndinu wokhazikika moti Iye amene ali pamwamba pa kumwamba sangathe kung’amba nthaka imene ili pansi panu kuti ikumezeni? Taonani! Ili kugwedezeka |
أَمْ أَمِنتُم مَّن فِي السَّمَاءِ أَن يُرْسِلَ عَلَيْكُمْ حَاصِبًا ۖ فَسَتَعْلَمُونَ كَيْفَ نَذِيرِ (17) Kapena mumaganiza kuti inu ndinu okhazikika kuposa zimene zili kumwamba kuti Iye sangathe kukutumizirani mphepo ya mkuntho? Kotero inu mudzadziwa kuopsa kwa chenjezo langa |
وَلَقَدْ كَذَّبَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ فَكَيْفَ كَانَ نَكِيرِ (18) Ndithudi iwo amene adalipo kale anakana. Kodi chilango changa chinali bwanji |
أَوَلَمْ يَرَوْا إِلَى الطَّيْرِ فَوْقَهُمْ صَافَّاتٍ وَيَقْبِضْنَ ۚ مَا يُمْسِكُهُنَّ إِلَّا الرَّحْمَٰنُ ۚ إِنَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ بَصِيرٌ (19) Kodiiwosaonambalamezimenezimaulukapamwamba pawo, zikutambasula ndi kutseka mapiko awo? Palibe chimene chimazigwira kupatula Mwini chisoni chosatha. Ndithudi Iye amaona chilichonse |
أَمَّنْ هَٰذَا الَّذِي هُوَ جُندٌ لَّكُمْ يَنصُرُكُم مِّن دُونِ الرَّحْمَٰنِ ۚ إِنِ الْكَافِرُونَ إِلَّا فِي غُرُورٍ (20) Kodi ndani amene angakuthandizeni inu kupatula Mwini chisoni chosatha? Anthu onse osakhulupirira ndi olakwa |
أَمَّنْ هَٰذَا الَّذِي يَرْزُقُكُمْ إِنْ أَمْسَكَ رِزْقَهُ ۚ بَل لَّجُّوا فِي عُتُوٍّ وَنُفُورٍ (21) Kodi ndani amene angakupatseni chisamaliro ngati Iye atakaniza chisamaliro chake? Koma iwo amapitiriza kuchita mtudzu ndi kugalukira |
أَفَمَن يَمْشِي مُكِبًّا عَلَىٰ وَجْهِهِ أَهْدَىٰ أَمَّن يَمْشِي سَوِيًّا عَلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (22) Kodi iye amene amayenda osaona ndi ofanana ndi amene walangizidwa kapena amene amayenda mu njira yoyenera |
قُلْ هُوَ الَّذِي أَنشَأَكُمْ وَجَعَلَ لَكُمُ السَّمْعَ وَالْأَبْصَارَ وَالْأَفْئِدَةَ ۖ قَلِيلًا مَّا تَشْكُرُونَ (23) Nena: “Ndiye amene adakulengani inu ndipo adakupatsani makutu, maso ndi mitima. Inu simuthokoza kawirikawiri.” |
قُلْ هُوَ الَّذِي ذَرَأَكُمْ فِي الْأَرْضِ وَإِلَيْهِ تُحْشَرُونَ (24) Nena: “Ndiye amene anakulengani inu kuchokera ku doti ndipo kwa Iye nonse mudzasonkhanitsidwa.” |
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْوَعْدُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (25) Iwo amati: “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene ulikunena ndi zoona?” |
قُلْ إِنَّمَا الْعِلْمُ عِندَ اللَّهِ وَإِنَّمَا أَنَا نَذِيرٌ مُّبِينٌ (26) Nena: “Mulungu yekha ndiye amene adziwa nthawi yake. Ntchito yanga ndikungokuchenjezani basi.” |
فَلَمَّا رَأَوْهُ زُلْفَةً سِيئَتْ وُجُوهُ الَّذِينَ كَفَرُوا وَقِيلَ هَٰذَا الَّذِي كُنتُم بِهِ تَدَّعُونَ (27) Koma pamene iwo adzachiona chili nkudza pafupi, nkhope za anthu osakhulupirira zidzakhala za chisoni ndipo kudzanenedwa kuti: “Ichi ndi chimaliziro chimene munkafunsa kuti chidzafika liti?” |
قُلْ أَرَأَيْتُمْ إِنْ أَهْلَكَنِيَ اللَّهُ وَمَن مَّعِيَ أَوْ رَحِمَنَا فَمَن يُجِيرُ الْكَافِرِينَ مِنْ عَذَابٍ أَلِيمٍ (28) Nena: “Ndiuzeni! Kodi ngati Mulungu atandiononga ine pamodzi ndi iwo amene ali nane, ngakhale kuti Iye adzaonetsa chifundo pa ife, ndani amene angateteze anthu osakhulupirira ku chilango chowawa?” |
قُلْ هُوَ الرَّحْمَٰنُ آمَنَّا بِهِ وَعَلَيْهِ تَوَكَّلْنَا ۖ فَسَتَعْلَمُونَ مَنْ هُوَ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (29) Nena: “Iye ndi Mwini chifundo chosatha, mwa Iye ife timakhulupirira ndipo mwa Iye ife timaika chikhulupiriro chathu. Kotero inu mudzadziwa posachedwapa kuti ndani amene ali wochimwa.” |
قُلْ أَرَأَيْتُمْ إِنْ أَصْبَحَ مَاؤُكُمْ غَوْرًا فَمَن يَأْتِيكُم بِمَاءٍ مَّعِينٍ (30) Nena: “Ndiuzeni! Kodi ngati madzi anu ataphwa, ndani amene angakupatseni inu madzi oyenda?” |