×

Surah Ash_shuraa in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah shura

Translation of the Meanings of Surah shura in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah shura translated into Chichewa, Surah Ash_shuraa in Chichewa. We provide accurate translation of Surah shura in Chichewa - نيانجا, Verses 53 - Surah Number 42 - Page 483.

بسم الله الرحمن الرحيم

حم (1)
Ha Mim
عسق (2)
Ain Sin Qaf
كَذَٰلِكَ يُوحِي إِلَيْكَ وَإِلَى الَّذِينَ مِن قَبْلِكَ اللَّهُ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (3)
Motero Mulungu, Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru amatumiza chivumbulutso kwa iwe monga anali kuvumbulutsira kwa iwo amene adalipo iwe usanabadwe
لَهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۖ وَهُوَ الْعَلِيُّ الْعَظِيمُ (4)
Iye ndiye Mwini wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndipo Iye ndi wapamwamba, ndiponso wamkulu
تَكَادُ السَّمَاوَاتُ يَتَفَطَّرْنَ مِن فَوْقِهِنَّ ۚ وَالْمَلَائِكَةُ يُسَبِّحُونَ بِحَمْدِ رَبِّهِمْ وَيَسْتَغْفِرُونَ لِمَن فِي الْأَرْضِ ۗ أَلَا إِنَّ اللَّهَ هُوَ الْغَفُورُ الرَّحِيمُ (5)
Kumwamba kumafuna kuphulika chifukwa cha ulemerero wake ndipo angelo amaimba mayamiko a Ambuye wawo ndipo amapempha chikhululukiro cha zolengedwa zonse za padziko lapansi. Ndithudi, Mulungu, ndiye amene amakhululukira ndipo ndi Mwini chisoni chosatha
وَالَّذِينَ اتَّخَذُوا مِن دُونِهِ أَوْلِيَاءَ اللَّهُ حَفِيظٌ عَلَيْهِمْ وَمَا أَنتَ عَلَيْهِم بِوَكِيلٍ (6)
Ndipo iwo amene amasankha ena ake kukhala atetezi awo m’malo mwake, Mulungu amawayang’anira ndipo iwe ulibe ulamuliro pa iwo
وَكَذَٰلِكَ أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ قُرْآنًا عَرَبِيًّا لِّتُنذِرَ أُمَّ الْقُرَىٰ وَمَنْ حَوْلَهَا وَتُنذِرَ يَوْمَ الْجَمْعِ لَا رَيْبَ فِيهِ ۚ فَرِيقٌ فِي الْجَنَّةِ وَفَرِيقٌ فِي السَّعِيرِ (7)
Kotero tavumbulutsa kwa iwe Buku la Korani m’Chiarabu, kuti ukhoza kuchenjeza make wa Mizinda ndi iyo youzungulira. Ndipo kuti uchenjeze za tsiku la chiweruzo limene mosakayika lidzadza pamene gulu lina lidzakhala ku Paradiso ndi gulu linzake lidzakhala kumoto
وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ لَجَعَلَهُمْ أُمَّةً وَاحِدَةً وَلَٰكِن يُدْخِلُ مَن يَشَاءُ فِي رَحْمَتِهِ ۚ وَالظَّالِمُونَ مَا لَهُم مِّن وَلِيٍّ وَلَا نَصِيرٍ (8)
Ndipo ngati Mulungu akadafuna, akadawapanga onse kukhala mtundu umodzi koma Iye amasankha amene wamufuna kulandira chisomo chake ndipo onse osalungama sadzapeza mtetezi kapena wowathandiza
أَمِ اتَّخَذُوا مِن دُونِهِ أَوْلِيَاءَ ۖ فَاللَّهُ هُوَ الْوَلِيُّ وَهُوَ يُحْيِي الْمَوْتَىٰ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (9)
Kodi kapena iwo asankha kuti aziwapembedza atetezi ena m’malo mwake? Koma Mulungu ndiye Mtetezi. Ndipo ndiye amene amapereka moyo kwa akufa ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
وَمَا اخْتَلَفْتُمْ فِيهِ مِن شَيْءٍ فَحُكْمُهُ إِلَى اللَّهِ ۚ ذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبِّي عَلَيْهِ تَوَكَّلْتُ وَإِلَيْهِ أُنِيبُ (10)
Ndipo pa chilichonse chimene mumatsutsana, chiweruzo chake chili ndiMulunguMwiniwake.AmeneyondiMulunguweniweni, Ambuye wanga ndipo mwa Iye ine ndimakhulupirira ndipo kwa Iye ndiko ndimalapa machimo anga
فَاطِرُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ جَعَلَ لَكُم مِّنْ أَنفُسِكُمْ أَزْوَاجًا وَمِنَ الْأَنْعَامِ أَزْوَاجًا ۖ يَذْرَؤُكُمْ فِيهِ ۚ لَيْسَ كَمِثْلِهِ شَيْءٌ ۖ وَهُوَ السَّمِيعُ الْبَصِيرُ (11)
Namalenga wakumwamba ndi dziko lapansi. Iye adalenga anzanu kuchokera pakati panu ndi anzawo kuchokera ku nyama. Mwanjira imeneyi Iye amakulengani inu. Palibe chilichonse chofanana naye ndipo Iye ndi wakumva ndi woona
لَهُ مَقَالِيدُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ يَبْسُطُ الرِّزْقَ لِمَن يَشَاءُ وَيَقْدِرُ ۚ إِنَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (12)
Iye ndiye amene ali ndi makiyi a kumwamba ndi a pa dziko lapansi. Iye amachulukitsa kapena kuchepetsa chakudya cha aliyense amene wamufuna. Ndithudi Iye amadziwa bwino za chinthu china chilichonse
۞ شَرَعَ لَكُم مِّنَ الدِّينِ مَا وَصَّىٰ بِهِ نُوحًا وَالَّذِي أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ وَمَا وَصَّيْنَا بِهِ إِبْرَاهِيمَ وَمُوسَىٰ وَعِيسَىٰ ۖ أَنْ أَقِيمُوا الدِّينَ وَلَا تَتَفَرَّقُوا فِيهِ ۚ كَبُرَ عَلَى الْمُشْرِكِينَ مَا تَدْعُوهُمْ إِلَيْهِ ۚ اللَّهُ يَجْتَبِي إِلَيْهِ مَن يَشَاءُ وَيَهْدِي إِلَيْهِ مَن يُنِيبُ (13)
Iye wakukhazikitsirani chipembedzo chimene adakhazikitsira Nowa kuti atsatire, ndi chimene tavumbulutsa kwa iwe, ndi chimene tidakhazikitsira Abrahamu ndi Mose ndi Yesu powauza kuti inu mukhazikitse chipembedzo ndipo musapatukane. Ndi kovuta kuti anthu osakhulupirira atsatire zimene iwe uwaitanira. Mulungu amasankha yekha onse amene wawafuna ndipo amatsogolera onse amene amagonja kwa Iye
وَمَا تَفَرَّقُوا إِلَّا مِن بَعْدِ مَا جَاءَهُمُ الْعِلْمُ بَغْيًا بَيْنَهُمْ ۚ وَلَوْلَا كَلِمَةٌ سَبَقَتْ مِن رَّبِّكَ إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى لَّقُضِيَ بَيْنَهُمْ ۚ وَإِنَّ الَّذِينَ أُورِثُوا الْكِتَابَ مِن بَعْدِهِمْ لَفِي شَكٍّ مِّنْهُ مُرِيبٍ (14)
Koma iwo adapatukana pamene nzeru zidadza kwa iwo ndipo anali kuchitirana mwano. Koma kukadakhala kuti padalibe mawu amene adanenedwa kale kuchokera kwa Ambuye wako wokhudza chimaliziro, chiweruzo chikadadza kale pa iwo. Ndipo, ndithudi, iwo amene adalandira Buku pambuyo pawo, ndithudi, ali ndi chikayiko chachikulu pa icho
فَلِذَٰلِكَ فَادْعُ ۖ وَاسْتَقِمْ كَمَا أُمِرْتَ ۖ وَلَا تَتَّبِعْ أَهْوَاءَهُمْ ۖ وَقُلْ آمَنتُ بِمَا أَنزَلَ اللَّهُ مِن كِتَابٍ ۖ وَأُمِرْتُ لِأَعْدِلَ بَيْنَكُمُ ۖ اللَّهُ رَبُّنَا وَرَبُّكُمْ ۖ لَنَا أَعْمَالُنَا وَلَكُمْ أَعْمَالُكُمْ ۖ لَا حُجَّةَ بَيْنَنَا وَبَيْنَكُمُ ۖ اللَّهُ يَجْمَعُ بَيْنَنَا ۖ وَإِلَيْهِ الْمَصِيرُ (15)
Kotero pitiriza kuwaitana ndipo limbikira potsatira njira yoyenera monga momwe walamulidwira. Iwe usatsatire zilakolako zawo zachabe, ndipo nena, “Ine ndimakhulupirira mawu onse a Mulungu amene wavumbulutsa mu Buku lake, ndipo ine ndalamulidwa kuonetsa chilungamo pakati panu. Mulungu ndi Ambuye wathu ndiponso Ambuye wanu. Kwa ife ntchito zathu ndipo kwa inu ntchito. Ndipo palibe mkangano pakati pa ife ndi inu. Mulungu adzatisonkhanitsa tonse ndipo ndi kwa Iye kumene tonse tidzabwerera.”
وَالَّذِينَ يُحَاجُّونَ فِي اللَّهِ مِن بَعْدِ مَا اسْتُجِيبَ لَهُ حُجَّتُهُمْ دَاحِضَةٌ عِندَ رَبِّهِمْ وَعَلَيْهِمْ غَضَبٌ وَلَهُمْ عَذَابٌ شَدِيدٌ (16)
Ndipo iwo amene amatsutsa za Mulungu atavomereza kale kuti adzamumvera, mitsutso yawo siidzakhala yomveka kwa Ambuye wawo ndipo mkwiyo wake udzadza pa iwo ndipo iwo adzalangidwa kwambiri
اللَّهُ الَّذِي أَنزَلَ الْكِتَابَ بِالْحَقِّ وَالْمِيزَانَ ۗ وَمَا يُدْرِيكَ لَعَلَّ السَّاعَةَ قَرِيبٌ (17)
Ndi Mulungu amene watumiza Buku mwachoonadi ndi muyeso. Kodi ndi chiyani chimene chingakudziwitseni inu kuti mwina ola lachiweruzo lili pafupi
يَسْتَعْجِلُ بِهَا الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِهَا ۖ وَالَّذِينَ آمَنُوا مُشْفِقُونَ مِنْهَا وَيَعْلَمُونَ أَنَّهَا الْحَقُّ ۗ أَلَا إِنَّ الَّذِينَ يُمَارُونَ فِي السَّاعَةِ لَفِي ضَلَالٍ بَعِيدٍ (18)
okhawo amene sakhulupilira amafuna kuti ola lidze msanga pamene onse amene amakhulupirira amaliopa ilo chifukwa amadziwa kuti ndi loonadi. Ndithudi onse amene amakana za olali ndi otayika kwambiri
اللَّهُ لَطِيفٌ بِعِبَادِهِ يَرْزُقُ مَن يَشَاءُ ۖ وَهُوَ الْقَوِيُّ الْعَزِيزُ (19)
Mulungu ndi wachifundo ndi wachisoni kwa akapolo ake. Iye amapereka chakudya kwa aliyense amene wamufuna. Ndipo Iye ndi wamphamvu ndi Mwini mphamvu zonse
مَن كَانَ يُرِيدُ حَرْثَ الْآخِرَةِ نَزِدْ لَهُ فِي حَرْثِهِ ۖ وَمَن كَانَ يُرِيدُ حَرْثَ الدُّنْيَا نُؤْتِهِ مِنْهَا وَمَا لَهُ فِي الْآخِرَةِ مِن نَّصِيبٍ (20)
Aliyense amene afuna zabwino za m’moyo umene uli nkudza, Ife tidzamupatsa zambiri ndipo wina aliyense amene afuna zabwino za m’moyo uno tidzamupatsa koma iye sadzakhala ndi gawo lina m’moyo umene uli nkudza
أَمْ لَهُمْ شُرَكَاءُ شَرَعُوا لَهُم مِّنَ الدِّينِ مَا لَمْ يَأْذَن بِهِ اللَّهُ ۚ وَلَوْلَا كَلِمَةُ الْفَصْلِ لَقُضِيَ بَيْنَهُمْ ۗ وَإِنَّ الظَّالِمِينَ لَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (21)
Kodi kapena iwo ali ndi anzawo amene akhazikitsa chipembedzo china popanda chilolezo cha Mulungu? Ndipo pakadapanda kuti mawu adanenedwa kale, chiweruzo chikadafika kale pakati pawo. Ndithudi anthu ochita zoipa adzalandira chilango chowawa kwambiri
تَرَى الظَّالِمِينَ مُشْفِقِينَ مِمَّا كَسَبُوا وَهُوَ وَاقِعٌ بِهِمْ ۗ وَالَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ فِي رَوْضَاتِ الْجَنَّاتِ ۖ لَهُم مَّا يَشَاءُونَ عِندَ رَبِّهِمْ ۚ ذَٰلِكَ هُوَ الْفَضْلُ الْكَبِيرُ (22)
Iwe udzawaona anthu ochimwa ali ndi mantha chifukwa cha ntchito zawo ndipo ndithudi mazunzo adzadza pa iwo pamene iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzakhala ku Paradiso. Iwo adzalandira, kuchokera kwa Ambuye wawo zonse zimene adzafuna. Chimenechi ndicho chisomo chachikulu
ذَٰلِكَ الَّذِي يُبَشِّرُ اللَّهُ عِبَادَهُ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ ۗ قُل لَّا أَسْأَلُكُمْ عَلَيْهِ أَجْرًا إِلَّا الْمَوَدَّةَ فِي الْقُرْبَىٰ ۗ وَمَن يَقْتَرِفْ حَسَنَةً نَّزِدْ لَهُ فِيهَا حُسْنًا ۚ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ شَكُورٌ (23)
Imeneyi ndi nkhani yabwino imene Mulungu ali kuwauza akapolo ake amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino. Nena, “Ine sindili kukupemphani malipiro ayi kupatula kuti muzionetsa chikondi kwa ine chifukwa cha ubale wanga ndi inu.” Ndipo aliyense amene alandira chabwino, tidzamuonjezera zabwino zambiri mofanana ndi izo. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wokonzeka kulipira
أَمْ يَقُولُونَ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا ۖ فَإِن يَشَإِ اللَّهُ يَخْتِمْ عَلَىٰ قَلْبِكَ ۗ وَيَمْحُ اللَّهُ الْبَاطِلَ وَيُحِقُّ الْحَقَّ بِكَلِمَاتِهِ ۚ إِنَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (24)
Kapena iwo akuti, “Iye wapeka yekha bodza lokhudza Mulungu?” Ngati Mulungu akadafuna akadatseka mtima wako. Ndipo Mulungu amafafaniza bodza ndi kukhazikitsa choonadi ndi mawu ake. Ndithudi Iye amadziwa zinsinsi zonse zimene zili m’mtima
وَهُوَ الَّذِي يَقْبَلُ التَّوْبَةَ عَنْ عِبَادِهِ وَيَعْفُو عَنِ السَّيِّئَاتِ وَيَعْلَمُ مَا تَفْعَلُونَ (25)
Ndiye amene amavomera kulapa kwa akapolo ake ndipo Iye amawakhululukira machimo awo ndipo Iye amadziwa zonse zimene mumachita
وَيَسْتَجِيبُ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ وَيَزِيدُهُم مِّن فَضْلِهِ ۚ وَالْكَافِرُونَ لَهُمْ عَذَابٌ شَدِيدٌ (26)
Ndipo Iye amayankha onse amene amakukhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino ndipo amawapatsa zambiri kuchokera ku chisomo chake. Akakhala anthu osakhulupirira iwo adzalandira chilango chowawa
۞ وَلَوْ بَسَطَ اللَّهُ الرِّزْقَ لِعِبَادِهِ لَبَغَوْا فِي الْأَرْضِ وَلَٰكِن يُنَزِّلُ بِقَدَرٍ مَّا يَشَاءُ ۚ إِنَّهُ بِعِبَادِهِ خَبِيرٌ بَصِيرٌ (27)
Ndipo ngati Mulungu akadaonjezera zabwino kwa akapolo ake, ndithudi, iwo akadaswa malamulo mopyola muyeso pa dziko lonse. Koma Iye amatumiza atayesa mwachifuniro chake. Ndithudi Iye amalemekeza akapolo ake, amadziwa zonse ndipo amayang’anitsitsa akapolo ake
وَهُوَ الَّذِي يُنَزِّلُ الْغَيْثَ مِن بَعْدِ مَا قَنَطُوا وَيَنشُرُ رَحْمَتَهُ ۚ وَهُوَ الْوَلِيُّ الْحَمِيدُ (28)
Ndipo ndiye amene amagwetsa mvula pa nthawi imene iwo ataya chikhulupiriro ndipo amaonetsa chifundo chake ponseponse. Ndipo Iye ndiye Mtetezi wamphamvu ndi Woyenera kulemekezeka
وَمِنْ آيَاتِهِ خَلْقُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا بَثَّ فِيهِمَا مِن دَابَّةٍ ۚ وَهُوَ عَلَىٰ جَمْعِهِمْ إِذَا يَشَاءُ قَدِيرٌ (29)
Ndipo pakati pa zizindikiro zake, pali kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi ndi zolengedwa zamoyo zimene adazimwaza monsemu. Ndipo Iye ali ndi mphamvu yozisonkhanitsa zonse pamodzi pamene Iye wafuna
وَمَا أَصَابَكُم مِّن مُّصِيبَةٍ فَبِمَا كَسَبَتْ أَيْدِيكُمْ وَيَعْفُو عَن كَثِيرٍ (30)
Ndipo mavuto onse amene amagwa pa inu amadza chifukwa cha ntchito zanu. Komabe Iye amakukhululukirani zolakwa zanu zambiri
وَمَا أَنتُم بِمُعْجِزِينَ فِي الْأَرْضِ ۖ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ اللَّهِ مِن وَلِيٍّ وَلَا نَصِيرٍ (31)
Ndipo inu simungathe kuthawa padziko lapansi ndipo inu mulibe wina aliyense kupatula Mulungu amene angakutetezeni kapena kukuthandizani
وَمِنْ آيَاتِهِ الْجَوَارِ فِي الْبَحْرِ كَالْأَعْلَامِ (32)
Ndipo pakati pa zizindikiro zake pali zombo zonga mapiri zimene zimayenda pa nyanja
إِن يَشَأْ يُسْكِنِ الرِّيحَ فَيَظْلَلْنَ رَوَاكِدَ عَلَىٰ ظَهْرِهِ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّكُلِّ صَبَّارٍ شَكُورٍ (33)
Ngati Iye afuna, Iye amaimitsamphepondipoiwoamaimaosayendapamwamba pa nyanja. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa aliyense amene amapirira ndipo amayamika
أَوْ يُوبِقْهُنَّ بِمَا كَسَبُوا وَيَعْفُ عَن كَثِيرٍ (34)
Kapena akhoza kuwaononga chifukwa cha zolakwa zimene iwo adachita. Koma Iye amawakhululukira zolakwa zambiri
وَيَعْلَمَ الَّذِينَ يُجَادِلُونَ فِي آيَاتِنَا مَا لَهُم مِّن مَّحِيصٍ (35)
Onse amene amakana chivumbulutso chathu ayenera kudziwa kuti alibe malo othawirako
فَمَا أُوتِيتُم مِّن شَيْءٍ فَمَتَاعُ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۖ وَمَا عِندَ اللَّهِ خَيْرٌ وَأَبْقَىٰ لِلَّذِينَ آمَنُوا وَعَلَىٰ رَبِّهِمْ يَتَوَكَّلُونَ (36)
Motero chilichonse chimene mwapatsidwa padziko lapansindichongosangalatsacham’moyounokomachimene chilindi Mulungundichabwinondiponsochosathakwaiwo amene amakhulupirira ndipo amaika chikhulupiriro chawo mwa Ambuye wawo
وَالَّذِينَ يَجْتَنِبُونَ كَبَائِرَ الْإِثْمِ وَالْفَوَاحِشَ وَإِذَا مَا غَضِبُوا هُمْ يَغْفِرُونَ (37)
Ndi iwo amene amapewa kuchita machimo aakuluakulu ndi zinthu zochititsa manyazi ndipo pamene akwiya amakhululuka
وَالَّذِينَ اسْتَجَابُوا لِرَبِّهِمْ وَأَقَامُوا الصَّلَاةَ وَأَمْرُهُمْ شُورَىٰ بَيْنَهُمْ وَمِمَّا رَزَقْنَاهُمْ يُنفِقُونَ (38)
Iwo amene amamvera kuitana kwa Ambuye wawo ndipo amapemphera panthawi yake amachita zinthu zawo atakambirana ndiponso amapereka kuchokera ku zinthu zimene tawapatsa iwo
وَالَّذِينَ إِذَا أَصَابَهُمُ الْبَغْيُ هُمْ يَنتَصِرُونَ (39)
Ndiiwoameneakaponderezedwa,amabwezera
وَجَزَاءُ سَيِّئَةٍ سَيِّئَةٌ مِّثْلُهَا ۖ فَمَنْ عَفَا وَأَصْلَحَ فَأَجْرُهُ عَلَى اللَّهِ ۚ إِنَّهُ لَا يُحِبُّ الظَّالِمِينَ (40)
Ndipo kubwezera kwa ntchito zoipa ndi choipa cholingana ndi ntchitozo ngati munthu akhululukira mnzake ndi kusintha maganizo ake, iye adzalandira mphotho yake kuchokera kwa Mulungu. Ndithudi Iye sakonda anthu osalungama
وَلَمَنِ انتَصَرَ بَعْدَ ظُلْمِهِ فَأُولَٰئِكَ مَا عَلَيْهِم مِّن سَبِيلٍ (41)
Ndipo aliyense amene amabwezera ataponderezedwa, iye sadzakhala ndi mlandu wina uliwonse
إِنَّمَا السَّبِيلُ عَلَى الَّذِينَ يَظْلِمُونَ النَّاسَ وَيَبْغُونَ فِي الْأَرْضِ بِغَيْرِ الْحَقِّ ۚ أُولَٰئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (42)
Mlandu uli pa iwo amene amapondereza anthu pochita zoipa ndipo mwamwano amaswa malamulo mopyola muyeso padziko. Ndipo kwa otere kudzakhala chilango chowawa kwambiri
وَلَمَن صَبَرَ وَغَفَرَ إِنَّ ذَٰلِكَ لَمِنْ عَزْمِ الْأُمُورِ (43)
Ndipo, ndithudi, aliyense amene aonetsa kupirira ndi chikhululukiro, chimenechi ndi chimodzi cha zinthu zimene zimayamikidwa ndi Mulungu
وَمَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَمَا لَهُ مِن وَلِيٍّ مِّن بَعْدِهِ ۗ وَتَرَى الظَّالِمِينَ لَمَّا رَأَوُا الْعَذَابَ يَقُولُونَ هَلْ إِلَىٰ مَرَدٍّ مِّن سَبِيلٍ (44)
Kwa aliyense amene Mulungu amusocheretsa, kulibe wina amene angamuteteze. Ndipo iwe udzawaona anthu ochita zoipa pamene iwo adzaona chilango ali kunena kuti, “Kodi pali njira yoti tingathe kubwerera?”
وَتَرَاهُمْ يُعْرَضُونَ عَلَيْهَا خَاشِعِينَ مِنَ الذُّلِّ يَنظُرُونَ مِن طَرْفٍ خَفِيٍّ ۗ وَقَالَ الَّذِينَ آمَنُوا إِنَّ الْخَاسِرِينَ الَّذِينَ خَسِرُوا أَنفُسَهُمْ وَأَهْلِيهِمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۗ أَلَا إِنَّ الظَّالِمِينَ فِي عَذَابٍ مُّقِيمٍ (45)
Ndipo iwe udzawaona ali kubweretsedwa kuchilango monyozedwa ndipo ali ndi nkhope zachisoni. Ndipo iwo amene amakhulupirira adzati, “Ndithudi otayika ndi anthu amene adzitaya ndi owatsatira awo patsiku lachiweruzo. Ndithudi anthu ochita zoipa adzakhala ku chilango chosatha.”
وَمَا كَانَ لَهُم مِّنْ أَوْلِيَاءَ يَنصُرُونَهُم مِّن دُونِ اللَّهِ ۗ وَمَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَمَا لَهُ مِن سَبِيلٍ (46)
Ndipo iwo sadzakhala ndi abwenzi oti awathandize kupatula Mulungu. Ndipo aliyense amene Mulungu wamusocheza alibe wina womutsogolera
اسْتَجِيبُوا لِرَبِّكُم مِّن قَبْلِ أَن يَأْتِيَ يَوْمٌ لَّا مَرَدَّ لَهُ مِنَ اللَّهِ ۚ مَا لَكُم مِّن مَّلْجَإٍ يَوْمَئِذٍ وَمَا لَكُم مِّن نَّكِيرٍ (47)
Kotero bwererani kwa Ambuye wanu mwamsanga tsiku limene simungathe kubwerera lisanadze. Inu simudzakhala ndi kothawira pa tsiku limeneli ndipo inu simudzakhala ndi mwayi wokana
فَإِنْ أَعْرَضُوا فَمَا أَرْسَلْنَاكَ عَلَيْهِمْ حَفِيظًا ۖ إِنْ عَلَيْكَ إِلَّا الْبَلَاغُ ۗ وَإِنَّا إِذَا أَذَقْنَا الْإِنسَانَ مِنَّا رَحْمَةً فَرِحَ بِهَا ۖ وَإِن تُصِبْهُمْ سَيِّئَةٌ بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيهِمْ فَإِنَّ الْإِنسَانَ كَفُورٌ (48)
Koma ngati iwo akana, Ife sitidakutumize iwe ngati owayang’anira iwo. Udindo wako ndi kungopereka uthenga. Ndipo, ndithudi, ngati Ife timupanga munthu kulawa chisomo chathu, iye amasangalala kwambiri chifukwa cha chisomocho koma ngati vuto lidza pa iwo chifukwa cha zolakwa zawo zimene adachita, ndithudi munthu amakhala osayamika
لِّلَّهِ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ يَخْلُقُ مَا يَشَاءُ ۚ يَهَبُ لِمَن يَشَاءُ إِنَاثًا وَيَهَبُ لِمَن يَشَاءُ الذُّكُورَ (49)
Ufumu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi Mwini wake ndi Mulungu. Ndipo Iye amalenga chimene wafuna. Iye amapereka ana aakazi kwa amene Iye wamufuna ndipo amapereka ana aamuna kwa amene wamufuna
أَوْ يُزَوِّجُهُمْ ذُكْرَانًا وَإِنَاثًا ۖ وَيَجْعَلُ مَن يَشَاءُ عَقِيمًا ۚ إِنَّهُ عَلِيمٌ قَدِيرٌ (50)
Kapena amawapatsa, ana aamuna ndi ana aakazi, ndipo amapanga amene wamufuna kuti akhale chumba. Ndithudi iye amadziwa zonse ndipo amatha kuchita chilichonse
۞ وَمَا كَانَ لِبَشَرٍ أَن يُكَلِّمَهُ اللَّهُ إِلَّا وَحْيًا أَوْ مِن وَرَاءِ حِجَابٍ أَوْ يُرْسِلَ رَسُولًا فَيُوحِيَ بِإِذْنِهِ مَا يَشَاءُ ۚ إِنَّهُ عَلِيٌّ حَكِيمٌ (51)
Si koyenera kuti Mulungu ayankhule ndi munthu kupatula kudzera m’chivumbulutso kapena kuchokera kumalo obisika kapena potumiza Mtumwi kudzawauza, chimene Mulungu afuna ndi chilolezo chake. Ndithudi Iye ndi wapamwamba ndi wanzeru zosatha
وَكَذَٰلِكَ أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ رُوحًا مِّنْ أَمْرِنَا ۚ مَا كُنتَ تَدْرِي مَا الْكِتَابُ وَلَا الْإِيمَانُ وَلَٰكِن جَعَلْنَاهُ نُورًا نَّهْدِي بِهِ مَن نَّشَاءُ مِنْ عِبَادِنَا ۚ وَإِنَّكَ لَتَهْدِي إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (52)
Kotero, mwaulamuliro wathu, tatumiza chivumbulutso chathu kwa iwe. Iwe siumadziwa kuti chivumbulutso chidali chiyani kapena kuti chikhulupiriro chidali chiyani. Koma Ife tachipanga icho kukhala muuni umene timatsogolera nawo akapolo athu mwachifuniro chathu. Ndithudi iwe umalangiza anthu ku njira yoyenera
صِرَاطِ اللَّهِ الَّذِي لَهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۗ أَلَا إِلَى اللَّهِ تَصِيرُ الْأُمُورُ (53)
Njira ya Mulungu amene ali Mwini wake wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndi chilichonse chimene chili pa dziko lapansi. Ndithudi kwa Mulungu zinthu zonse zimabwerera
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas