×

Surah Ya-Sin in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Yasin

Translation of the Meanings of Surah Yasin in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Yasin translated into Chichewa, Surah Ya-Sin in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Yasin in Chichewa - نيانجا, Verses 83 - Surah Number 36 - Page 440.

بسم الله الرحمن الرحيم

يس (1)
Ya seen
وَالْقُرْآنِ الْحَكِيمِ (2)
Ndili kulumbira pali Buku la nzeru la Korani
إِنَّكَ لَمِنَ الْمُرْسَلِينَ (3)
Ndithudi iwe ndiwe mmodzi mwa amene adatumizidwa
عَلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (4)
Pa njira yoyenera
تَنزِيلَ الْعَزِيزِ الرَّحِيمِ (5)
Ichi ndi chivumbulutso cha Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni
لِتُنذِرَ قَوْمًا مَّا أُنذِرَ آبَاؤُهُمْ فَهُمْ غَافِلُونَ (6)
Kuti uwachenjeze anthu amene makolo awo sadachenjezedwe, kotero iwo ndi osamvera
لَقَدْ حَقَّ الْقَوْلُ عَلَىٰ أَكْثَرِهِمْ فَهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (7)
Ndithudi liwu la chilango latsimikizidwa kwa ambiri a iwo koma iwo sali okhulupirira
إِنَّا جَعَلْنَا فِي أَعْنَاقِهِمْ أَغْلَالًا فَهِيَ إِلَى الْأَذْقَانِ فَهُم مُّقْمَحُونَ (8)
Ife taika magoli m’makosi mwawo, amene afika m’zigama ndipo mitu yawo yanyamulidwa
وَجَعَلْنَا مِن بَيْنِ أَيْدِيهِمْ سَدًّا وَمِنْ خَلْفِهِمْ سَدًّا فَأَغْشَيْنَاهُمْ فَهُمْ لَا يُبْصِرُونَ (9)
Ife taika chotchinga kutsogolo kwawo ndiponso kumbuyo kwawo ndipo tawakuta maso awo kuti asaone
وَسَوَاءٌ عَلَيْهِمْ أَأَنذَرْتَهُمْ أَمْ لَمْ تُنذِرْهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (10)
Ndi chimodzimodzi kaya uwachenjeza kapena ayi ndipo iwo sadzakhulupirira
إِنَّمَا تُنذِرُ مَنِ اتَّبَعَ الذِّكْرَ وَخَشِيَ الرَّحْمَٰنَ بِالْغَيْبِ ۖ فَبَشِّرْهُ بِمَغْفِرَةٍ وَأَجْرٍ كَرِيمٍ (11)
Ukhoza kumuchenjeza yekhayo amene watsatira chikumbutso ndi kuopa Mwini Chisoni ngakhale kuti iye sangamuone. Kwa iye umuuze nkhani yabwino ya chikhululukiro ndi mphotho yopambana
إِنَّا نَحْنُ نُحْيِي الْمَوْتَىٰ وَنَكْتُبُ مَا قَدَّمُوا وَآثَارَهُمْ ۚ وَكُلَّ شَيْءٍ أَحْصَيْنَاهُ فِي إِمَامٍ مُّبِينٍ (12)
Ndife amene tidzadzutsa anthu akufa ndi kulemba ntchito zonse za anthu ndi zizindikiro zimene asiya m’mbuyo: Talemba zonse mooneka bwino kwambiri m’buku
وَاضْرِبْ لَهُم مَّثَلًا أَصْحَابَ الْقَرْيَةِ إِذْ جَاءَهَا الْمُرْسَلُونَ (13)
Apatse chitsanzo cha anthu a mu mzinda umene mudadza Atumwi
إِذْ أَرْسَلْنَا إِلَيْهِمُ اثْنَيْنِ فَكَذَّبُوهُمَا فَعَزَّزْنَا بِثَالِثٍ فَقَالُوا إِنَّا إِلَيْكُم مُّرْسَلُونَ (14)
Pamene Ife tidawatumizira iwo awiri, iwo adawakana. Motero Ife tidatumizanso wina wachitatu, ndipo iwo adati, “Ndithudi ife tatumizidwa kwa inu.”
قَالُوا مَا أَنتُمْ إِلَّا بَشَرٌ مِّثْلُنَا وَمَا أَنزَلَ الرَّحْمَٰنُ مِن شَيْءٍ إِنْ أَنتُمْ إِلَّا تَكْذِبُونَ (15)
Iwo adati, “Inu ndinu anthu ngati ife tomwe. Mwini chisoni sadavumbulutse china chilichonse! Inu muli kunama basi.”
قَالُوا رَبُّنَا يَعْلَمُ إِنَّا إِلَيْكُمْ لَمُرْسَلُونَ (16)
Iwo adati, “Ambuye wathu akudziwa kuti ife tatumidwa.”
وَمَا عَلَيْنَا إِلَّا الْبَلَاغُ الْمُبِينُ (17)
“Udindo wathu ndi wongokuchenjezani basi.”
قَالُوا إِنَّا تَطَيَّرْنَا بِكُمْ ۖ لَئِن لَّمْ تَنتَهُوا لَنَرْجُمَنَّكُمْ وَلَيَمَسَّنَّكُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٌ (18)
Anthu adati, “Tili kuona malodza. Ngati mupitiriza tikuponyani miyala ndipo chilango chowawa chizadza pa inu.”
قَالُوا طَائِرُكُم مَّعَكُمْ ۚ أَئِن ذُكِّرْتُم ۚ بَلْ أَنتُمْ قَوْمٌ مُّسْرِفُونَ (19)
Iwo adati, “Malodza anu akhale ndi inu! Kodi chifukwa chakuti mwachenjezedwa? Iyayi koma inu ndinu anthu ochimwa kwambiri
وَجَاءَ مِنْ أَقْصَى الْمَدِينَةِ رَجُلٌ يَسْعَىٰ قَالَ يَا قَوْمِ اتَّبِعُوا الْمُرْسَلِينَ (20)
Nthawi yomweyo munthu wina adadza ali kuthamanga kuchokera kumbali ina ya mzinda. Iye adati, “Anthu anga! Tsatirani iwo amene atumidwa ndi Mulungu.”
اتَّبِعُوا مَن لَّا يَسْأَلُكُمْ أَجْرًا وَهُم مُّهْتَدُونَ (21)
“Atsatireni iwo amene safuna malipiro kuchokera kwa inu pokukumbutsani mawu a Mulungu ndipo ndi otsogozedwa bwino.”
وَمَا لِيَ لَا أَعْبُدُ الَّذِي فَطَرَنِي وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (22)
“Kodi pali chifukwa chotani chimene chingandilepheretse ine kuti ndim’pembedze Iye amene adandilenga popeza ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera?”
أَأَتَّخِذُ مِن دُونِهِ آلِهَةً إِن يُرِدْنِ الرَّحْمَٰنُ بِضُرٍّ لَّا تُغْنِ عَنِّي شَفَاعَتُهُمْ شَيْئًا وَلَا يُنقِذُونِ (23)
“Kodi ine ndizipembedza milungu ina osati Iyeyo? Ngati ndi chifuniro cha Mwini chisoni kundizunza, kukhala pakati kwawo sikudzandithandiza ndipo iwo sadzandipulumutsa ayi.”
إِنِّي إِذًا لَّفِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (24)
“Ndithudi ine ndikadatero, ndikadakhala mu chisokonezo choonekeratu.”
إِنِّي آمَنتُ بِرَبِّكُمْ فَاسْمَعُونِ (25)
Ndithudi ine ndakhulupirira mwa Ambuye wanu choncho ndimvereni.”
قِيلَ ادْخُلِ الْجَنَّةَ ۖ قَالَ يَا لَيْتَ قَوْمِي يَعْلَمُونَ (26)
Kudanenedwa kwa iye kuti, “Lowa mu Paradiso.” Iye adafuula kuti, “Akadakhala kuti anthu anga adadziwa.”
بِمَا غَفَرَ لِي رَبِّي وَجَعَلَنِي مِنَ الْمُكْرَمِينَ (27)
“Mmene Ambuye wanga wandionetsera chifundo chake kundiika mugulu la olemekezeka.”
۞ وَمَا أَنزَلْنَا عَلَىٰ قَوْمِهِ مِن بَعْدِهِ مِن جُندٍ مِّنَ السَّمَاءِ وَمَا كُنَّا مُنزِلِينَ (28)
Ndipo Ife sitidatumize padziko lapansi, kwa anthu ake, gulu lochokera kumwamba kuti lilimbane nawo ndipo sikudali koyenera kuti Ife tichite choncho
إِن كَانَتْ إِلَّا صَيْحَةً وَاحِدَةً فَإِذَا هُمْ خَامِدُونَ (29)
Udali mkuwo umodzi ndipo Oh! Onse adaonongedwa
يَا حَسْرَةً عَلَى الْعِبَادِ ۚ مَا يَأْتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (30)
Kalanga akapolo anga! Iwo amaseka pofuna kunyoza Mtumwi aliyense amene adadza kwa iwo
أَلَمْ يَرَوْا كَمْ أَهْلَكْنَا قَبْلَهُم مِّنَ الْقُرُونِ أَنَّهُمْ إِلَيْهِمْ لَا يَرْجِعُونَ (31)
Kodi iwo sadaone mibadwo yakale imene tidaiononga zaka zikwizikwi iwo asanabadwe? Ndipo iwo sadzabwereranso
وَإِن كُلٌّ لَّمَّا جَمِيعٌ لَّدَيْنَا مُحْضَرُونَ (32)
onse, popanda opatuka, adzadza kwa Ife
وَآيَةٌ لَّهُمُ الْأَرْضُ الْمَيْتَةُ أَحْيَيْنَاهَا وَأَخْرَجْنَا مِنْهَا حَبًّا فَمِنْهُ يَأْكُلُونَ (33)
Chizindikiro kwa iwo ndi nthaka yakufa imene tidaidzutsa ndipo timatulutsa m’nthakamo nthangala zomwe iwo amadya
وَجَعَلْنَا فِيهَا جَنَّاتٍ مِّن نَّخِيلٍ وَأَعْنَابٍ وَفَجَّرْنَا فِيهَا مِنَ الْعُيُونِ (34)
Taika m’nthakamo minda ya mitengo ya tende ndi ya mphesa ndipo timathirira ndi madzi a m’kasupe
لِيَأْكُلُوا مِن ثَمَرِهِ وَمَا عَمِلَتْهُ أَيْدِيهِمْ ۖ أَفَلَا يَشْكُرُونَ (35)
Moti akhoza kumadya zipatso zake. Si manja awo amene adapanga zimenezi ayi. Kodi sangathokoze
سُبْحَانَ الَّذِي خَلَقَ الْأَزْوَاجَ كُلَّهَا مِمَّا تُنبِتُ الْأَرْضُ وَمِنْ أَنفُسِهِمْ وَمِمَّا لَا يَعْلَمُونَ (36)
Ulemerero ukhale kwa Iye amene adalenga zinthu ziwiriziwiri, (chachimuna ndi chachikazi) zimene zimamera m’nthaka ndi zina za mtundu wawo ndi zinanso zimene sazidziwa
وَآيَةٌ لَّهُمُ اللَّيْلُ نَسْلَخُ مِنْهُ النَّهَارَ فَإِذَا هُم مُّظْلِمُونَ (37)
Chizindikiro cha kwa iwo ndi usiku. Kuchokera ku iwo timachotsa usana ndipo iwo amakhala mu mdima
وَالشَّمْسُ تَجْرِي لِمُسْتَقَرٍّ لَّهَا ۚ ذَٰلِكَ تَقْدِيرُ الْعَزِيزِ الْعَلِيمِ (38)
Dzuwa limayenda mofulumira kupita kumalo ake okapuma. Umenewu ndiwo ulamuliro wa Mwini Mphamvu zonse ndiponso Wodziwa chilichonse
وَالْقَمَرَ قَدَّرْنَاهُ مَنَازِلَ حَتَّىٰ عَادَ كَالْعُرْجُونِ الْقَدِيمِ (39)
Ndipo mwezi tidaulamulira kuti uyende mumsewu wake mpaka pamene ukamabwerera ngati nthawi yoyamba m’maonekedwe
لَا الشَّمْسُ يَنبَغِي لَهَا أَن تُدْرِكَ الْقَمَرَ وَلَا اللَّيْلُ سَابِقُ النَّهَارِ ۚ وَكُلٌّ فِي فَلَكٍ يَسْبَحُونَ (40)
Dzuwa sililoledwa kupitirira mwezi ndipo usiku siupyola usana. Chilichonse chimayenda mumsewu wake
وَآيَةٌ لَّهُمْ أَنَّا حَمَلْنَا ذُرِّيَّتَهُمْ فِي الْفُلْكِ الْمَشْحُونِ (41)
Ndipo chizindikiro china kwa iwo ndi chakuti tidanyamula makolo awo mu chombo chonyamula katundu
وَخَلَقْنَا لَهُم مِّن مِّثْلِهِ مَا يَرْكَبُونَ (42)
Tidalenga zombo za mtundu umenewu kuti iwo azikweramo
وَإِن نَّشَأْ نُغْرِقْهُمْ فَلَا صَرِيخَ لَهُمْ وَلَا هُمْ يُنقَذُونَ (43)
Timawamiza tikafuna ndipo palibe amene angawathandize ndipo sangathe kupulumutsidwa
إِلَّا رَحْمَةً مِّنَّا وَمَتَاعًا إِلَىٰ حِينٍ (44)
Kupatula kudzera m’chifundo chathu ndi kuwapatsa chisangalalo cha kanthawi kochepa
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ اتَّقُوا مَا بَيْنَ أَيْدِيكُمْ وَمَا خَلْفَكُمْ لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (45)
Pamene zinenedwa kwa iwo kuti, “Opani chinthu chimene chili patsogolo panu ndi pambuyo panu kuti mwina Mulungu angakuonetsereni chifundo” ndipo iwo samvera ayi
وَمَا تَأْتِيهِم مِّنْ آيَةٍ مِّنْ آيَاتِ رَبِّهِمْ إِلَّا كَانُوا عَنْهَا مُعْرِضِينَ (46)
Ndithudi palibe chizindikiro chochokera kwa Ambuye wawo chimene iwo amachivomera. Ndipo iwo salabadira
وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ أَنفِقُوا مِمَّا رَزَقَكُمُ اللَّهُ قَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا لِلَّذِينَ آمَنُوا أَنُطْعِمُ مَن لَّوْ يَشَاءُ اللَّهُ أَطْعَمَهُ إِنْ أَنتُمْ إِلَّا فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (47)
Ndipo pamene auzidwa kuti, “Perekani gawo la chopereka chaulere pa zinthu zimene Mulungu wakupatsani.” Anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ife tizidyetsa iwo amene Mulungu atafuna akhoza kuwadyetsa? Ndithudi inu ndi osochera kwambiri.”
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْوَعْدُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (48)
Iwo amanenanso kuti, “Kodi lonjezo limeneli la tsiku lachiweruzo lidzatsimikizidwa liti, ngati zimene uli kunenazi ndi zoona?”
مَا يَنظُرُونَ إِلَّا صَيْحَةً وَاحِدَةً تَأْخُذُهُمْ وَهُمْ يَخِصِّمُونَ (49)
Angodikira mkokomo umodzi wokha basi umene udzadza pa nthawi imene iwo ali kutsutsana
فَلَا يَسْتَطِيعُونَ تَوْصِيَةً وَلَا إِلَىٰ أَهْلِهِمْ يَرْجِعُونَ (50)
Iwo sadzakhala ndi mwayi wosiya mawu kapena kubwerera kwa abale awo
وَنُفِخَ فِي الصُّورِ فَإِذَا هُم مِّنَ الْأَجْدَاثِ إِلَىٰ رَبِّهِمْ يَنسِلُونَ (51)
Pamene lipenga lidzamveka, taona, kuchokera ku manda, anthu adzathamanga kupita kwa Ambuye wawo
قَالُوا يَا وَيْلَنَا مَن بَعَثَنَا مِن مَّرْقَدِنَا ۜ ۗ هَٰذَا مَا وَعَدَ الرَّحْمَٰنُ وَصَدَقَ الْمُرْسَلُونَ (52)
“Tsoka kwa ife!” Iwo adzatero. “Ndani amene watidzutsa kuchokera kumalo athu a mpumulo?” Ichi ndi chimene Ambuye wachifundo adalonjeza. “Atumwi adanenadi zoona!”
إِن كَانَتْ إِلَّا صَيْحَةً وَاحِدَةً فَإِذَا هُمْ جَمِيعٌ لَّدَيْنَا مُحْضَرُونَ (53)
Ndithudi ndi mfuwu umodzi wokha, onse panthawiyo, adzasonkhanitsidwa kwa Ife
فَالْيَوْمَ لَا تُظْلَمُ نَفْسٌ شَيْئًا وَلَا تُجْزَوْنَ إِلَّا مَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (54)
Patsiku limeneli sipadzakhala mzimu umene siudzaweruzidwa ndipo inu mudzalandira mphotho molingana ndi ntchito zanu
إِنَّ أَصْحَابَ الْجَنَّةِ الْيَوْمَ فِي شُغُلٍ فَاكِهُونَ (55)
Pa tsiku limeneli anthu okhala ku Paradiso adzakhala osangalala kwambiri
هُمْ وَأَزْوَاجُهُمْ فِي ظِلَالٍ عَلَى الْأَرَائِكِ مُتَّكِئُونَ (56)
Iwo pamodzi ndi akazi awo, adzakhala m’mithunzi ya nkhalango, pa mipando yawofowofo
لَهُمْ فِيهَا فَاكِهَةٌ وَلَهُم مَّا يَدَّعُونَ (57)
Iwo adzapeza m’menemo zipatso ndi zina zonse zimene adzafuna
سَلَامٌ قَوْلًا مِّن رَّبٍّ رَّحِيمٍ (58)
“Mtendere” ndiwo mawu amene adzachokere kwa Mulungu, Mwini Chisoni
وَامْتَازُوا الْيَوْمَ أَيُّهَا الْمُجْرِمُونَ (59)
Ndipo Iye adzati, “Khalani kutali inu oipa tsiku lalero?”
۞ أَلَمْ أَعْهَدْ إِلَيْكُمْ يَا بَنِي آدَمَ أَن لَّا تَعْبُدُوا الشَّيْطَانَ ۖ إِنَّهُ لَكُمْ عَدُوٌّ مُّبِينٌ (60)
“Kodi Ine sindidakuchenjezeni, inu ana a Adamu, kuti musamagwadire Satana, chifukwa iyeyu ndi mdani wanu woonekeratu?”
وَأَنِ اعْبُدُونِي ۚ هَٰذَا صِرَاطٌ مُّسْتَقِيمٌ (61)
“Ndi kuti muzindipembedza Ine? Ndithudi imeneyo ndiyo njira yoyenera.”
وَلَقَدْ أَضَلَّ مِنكُمْ جِبِلًّا كَثِيرًا ۖ أَفَلَمْ تَكُونُوا تَعْقِلُونَ (62)
Koma iye adasocheretsa anthu ambiri. Kodi mudalibe nzeru
هَٰذِهِ جَهَنَّمُ الَّتِي كُنتُمْ تُوعَدُونَ (63)
Imeneyi ndiyo Gahena imene munali kulonjezedwa
اصْلَوْهَا الْيَوْمَ بِمَا كُنتُمْ تَكْفُرُونَ (64)
Lowani m’menemo tsiku lalero ngati chilango, chifukwa chakusakhulupirira kwanu
الْيَوْمَ نَخْتِمُ عَلَىٰ أَفْوَاهِهِمْ وَتُكَلِّمُنَا أَيْدِيهِمْ وَتَشْهَدُ أَرْجُلُهُم بِمَا كَانُوا يَكْسِبُونَ (65)
Lero, Ife titseka pakamwa pawo, ndipo manja awo ndi amene ayankhule ndi Ife ndiponso miyendo yawo ichitira umboni pa ntchito zoipa zimene anali kuchita
وَلَوْ نَشَاءُ لَطَمَسْنَا عَلَىٰ أَعْيُنِهِمْ فَاسْتَبَقُوا الصِّرَاطَ فَأَنَّىٰ يُبْصِرُونَ (66)
Chikadakhala cholinga chathu, tikadawachititsa khungu kuti azivutika poyenda. Nanga akadaona bwanji machimo awo
وَلَوْ نَشَاءُ لَمَسَخْنَاهُمْ عَلَىٰ مَكَانَتِهِمْ فَمَا اسْتَطَاعُوا مُضِيًّا وَلَا يَرْجِعُونَ (67)
Chikadakhala cholinga chathu, tikadawasintha kuti asanduke china chake pamalo pamene adaimirira, kuti asapite patsogolo kapena kubwerera m’mbuyo
وَمَن نُّعَمِّرْهُ نُنَكِّسْهُ فِي الْخَلْقِ ۖ أَفَلَا يَعْقِلُونَ (68)
Aliyense amene timamukalambitsa, timam’bwezera ku ubwana. Kodi iwo sangazindikire chimenechi
وَمَا عَلَّمْنَاهُ الشِّعْرَ وَمَا يَنبَغِي لَهُ ۚ إِنْ هُوَ إِلَّا ذِكْرٌ وَقُرْآنٌ مُّبِينٌ (69)
Ife sitidamuphunzitse iye ndakatulo ayi ndiponso si koyenera kuti akhale mlakatuli. Ichi si china koma chikumbutso ndi dongosolo la Korani
لِّيُنذِرَ مَن كَانَ حَيًّا وَيَحِقَّ الْقَوْلُ عَلَى الْكَافِرِينَ (70)
Limene lichenjeza anthu a moyo ndi kupereka chiweruzo kwa anthu osakhulupirira
أَوَلَمْ يَرَوْا أَنَّا خَلَقْنَا لَهُم مِّمَّا عَمِلَتْ أَيْدِينَا أَنْعَامًا فَهُمْ لَهَا مَالِكُونَ (71)
Kodi iwo saona kuti pakati pa zinthu zimene tidalenga ndi manja athu tidawalengera nyama zimene iwo amazilamulira
وَذَلَّلْنَاهَا لَهُمْ فَمِنْهَا رَكُوبُهُمْ وَمِنْهَا يَأْكُلُونَ (72)
Tidalamula zimenezi kuti zizimvera malamulo awo kuti akhoza kumakwera ndi zina zoti azidya
وَلَهُمْ فِيهَا مَنَافِعُ وَمَشَارِبُ ۖ أَفَلَا يَشْكُرُونَ (73)
Ndipo amapezanso phindu lina lolekana. Iwo amamwa mkaka kuchokera ku izo. Kodi iwo sangathokoze
وَاتَّخَذُوا مِن دُونِ اللَّهِ آلِهَةً لَّعَلَّهُمْ يُنصَرُونَ (74)
Iwo akhazikitsa milungu ina powonjezera pa Mulungu weniweni, poganiza kuti mwina akhoza kuthandizidwa
لَا يَسْتَطِيعُونَ نَصْرَهُمْ وَهُمْ لَهُمْ جُندٌ مُّحْضَرُونَ (75)
Milunguyo siingawathandize. Iwo adzatengedwa mwankhondo kunka ku chilango
فَلَا يَحْزُنكَ قَوْلُهُمْ ۘ إِنَّا نَعْلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعْلِنُونَ (76)
Usalole kuti mawu awo akumvetse chisoni. Ife tikudziwa zonse zimene azibisa ndi zonse zimene akuzionetsa
أَوَلَمْ يَرَ الْإِنسَانُ أَنَّا خَلَقْنَاهُ مِن نُّطْفَةٍ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٌ مُّبِينٌ (77)
Kodi munthu, sadziwa kuti tidamulenga kuchokera ku dontho la umuna? Koma iye ndi otsutsana ndi Ife poyera
وَضَرَبَ لَنَا مَثَلًا وَنَسِيَ خَلْقَهُ ۖ قَالَ مَن يُحْيِي الْعِظَامَ وَهِيَ رَمِيمٌ (78)
Iye amatifanizira Ife ndi zina zake ndipo amaiwala za chilengedwe chake. Iye amafunsa kuti, “Kodi ndani amene adzapereka moyo ku mafupa oola?”
قُلْ يُحْيِيهَا الَّذِي أَنشَأَهَا أَوَّلَ مَرَّةٍ ۖ وَهُوَ بِكُلِّ خَلْقٍ عَلِيمٌ (79)
Nena “Iye amene adawalenga poyamba adzawapatsa moyo. Iye amadziwa chilichonse cha zolengedwa zake.”
الَّذِي جَعَلَ لَكُم مِّنَ الشَّجَرِ الْأَخْضَرِ نَارًا فَإِذَا أَنتُم مِّنْهُ تُوقِدُونَ (80)
Iye amene amakupatsani moto kuchokera ku mtengo wauwisi umene inu mumawunikira
أَوَلَيْسَ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ بِقَادِرٍ عَلَىٰ أَن يَخْلُقَ مِثْلَهُم ۚ بَلَىٰ وَهُوَ الْخَلَّاقُ الْعَلِيمُ (81)
Kodi Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, alibe mphamvu zolenga china chake chofanana nazo? Ndithudi ali nazo. Iye ndi Mlengi amene amadziwa chinthu china chilichonse
إِنَّمَا أَمْرُهُ إِذَا أَرَادَ شَيْئًا أَن يَقُولَ لَهُ كُن فَيَكُونُ (82)
Ndithudi pamene Iye afuna chinthu amangonena kuti, “Chikhale” ndipo chimakhaladi
فَسُبْحَانَ الَّذِي بِيَدِهِ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيْءٍ وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (83)
Ulemerero ukhale kwa Iye amene ali ndi ulamuliro pa chinthu china chilichonse; ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas