يس (1) Ya seen |
وَالْقُرْآنِ الْحَكِيمِ (2) Ndili kulumbira pali Buku la nzeru la Korani |
إِنَّكَ لَمِنَ الْمُرْسَلِينَ (3) Ndithudi iwe ndiwe mmodzi mwa amene adatumizidwa |
عَلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (4) Pa njira yoyenera |
تَنزِيلَ الْعَزِيزِ الرَّحِيمِ (5) Ichi ndi chivumbulutso cha Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni |
لِتُنذِرَ قَوْمًا مَّا أُنذِرَ آبَاؤُهُمْ فَهُمْ غَافِلُونَ (6) Kuti uwachenjeze anthu amene makolo awo sadachenjezedwe, kotero iwo ndi osamvera |
لَقَدْ حَقَّ الْقَوْلُ عَلَىٰ أَكْثَرِهِمْ فَهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (7) Ndithudi liwu la chilango latsimikizidwa kwa ambiri a iwo koma iwo sali okhulupirira |
إِنَّا جَعَلْنَا فِي أَعْنَاقِهِمْ أَغْلَالًا فَهِيَ إِلَى الْأَذْقَانِ فَهُم مُّقْمَحُونَ (8) Ife taika magoli m’makosi mwawo, amene afika m’zigama ndipo mitu yawo yanyamulidwa |
وَجَعَلْنَا مِن بَيْنِ أَيْدِيهِمْ سَدًّا وَمِنْ خَلْفِهِمْ سَدًّا فَأَغْشَيْنَاهُمْ فَهُمْ لَا يُبْصِرُونَ (9) Ife taika chotchinga kutsogolo kwawo ndiponso kumbuyo kwawo ndipo tawakuta maso awo kuti asaone |
وَسَوَاءٌ عَلَيْهِمْ أَأَنذَرْتَهُمْ أَمْ لَمْ تُنذِرْهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (10) Ndi chimodzimodzi kaya uwachenjeza kapena ayi ndipo iwo sadzakhulupirira |
إِنَّمَا تُنذِرُ مَنِ اتَّبَعَ الذِّكْرَ وَخَشِيَ الرَّحْمَٰنَ بِالْغَيْبِ ۖ فَبَشِّرْهُ بِمَغْفِرَةٍ وَأَجْرٍ كَرِيمٍ (11) Ukhoza kumuchenjeza yekhayo amene watsatira chikumbutso ndi kuopa Mwini Chisoni ngakhale kuti iye sangamuone. Kwa iye umuuze nkhani yabwino ya chikhululukiro ndi mphotho yopambana |
إِنَّا نَحْنُ نُحْيِي الْمَوْتَىٰ وَنَكْتُبُ مَا قَدَّمُوا وَآثَارَهُمْ ۚ وَكُلَّ شَيْءٍ أَحْصَيْنَاهُ فِي إِمَامٍ مُّبِينٍ (12) Ndife amene tidzadzutsa anthu akufa ndi kulemba ntchito zonse za anthu ndi zizindikiro zimene asiya m’mbuyo: Talemba zonse mooneka bwino kwambiri m’buku |
وَاضْرِبْ لَهُم مَّثَلًا أَصْحَابَ الْقَرْيَةِ إِذْ جَاءَهَا الْمُرْسَلُونَ (13) Apatse chitsanzo cha anthu a mu mzinda umene mudadza Atumwi |
إِذْ أَرْسَلْنَا إِلَيْهِمُ اثْنَيْنِ فَكَذَّبُوهُمَا فَعَزَّزْنَا بِثَالِثٍ فَقَالُوا إِنَّا إِلَيْكُم مُّرْسَلُونَ (14) Pamene Ife tidawatumizira iwo awiri, iwo adawakana. Motero Ife tidatumizanso wina wachitatu, ndipo iwo adati, “Ndithudi ife tatumizidwa kwa inu.” |
قَالُوا مَا أَنتُمْ إِلَّا بَشَرٌ مِّثْلُنَا وَمَا أَنزَلَ الرَّحْمَٰنُ مِن شَيْءٍ إِنْ أَنتُمْ إِلَّا تَكْذِبُونَ (15) Iwo adati, “Inu ndinu anthu ngati ife tomwe. Mwini chisoni sadavumbulutse china chilichonse! Inu muli kunama basi.” |
قَالُوا رَبُّنَا يَعْلَمُ إِنَّا إِلَيْكُمْ لَمُرْسَلُونَ (16) Iwo adati, “Ambuye wathu akudziwa kuti ife tatumidwa.” |
وَمَا عَلَيْنَا إِلَّا الْبَلَاغُ الْمُبِينُ (17) “Udindo wathu ndi wongokuchenjezani basi.” |
قَالُوا إِنَّا تَطَيَّرْنَا بِكُمْ ۖ لَئِن لَّمْ تَنتَهُوا لَنَرْجُمَنَّكُمْ وَلَيَمَسَّنَّكُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٌ (18) Anthu adati, “Tili kuona malodza. Ngati mupitiriza tikuponyani miyala ndipo chilango chowawa chizadza pa inu.” |
قَالُوا طَائِرُكُم مَّعَكُمْ ۚ أَئِن ذُكِّرْتُم ۚ بَلْ أَنتُمْ قَوْمٌ مُّسْرِفُونَ (19) Iwo adati, “Malodza anu akhale ndi inu! Kodi chifukwa chakuti mwachenjezedwa? Iyayi koma inu ndinu anthu ochimwa kwambiri |
وَجَاءَ مِنْ أَقْصَى الْمَدِينَةِ رَجُلٌ يَسْعَىٰ قَالَ يَا قَوْمِ اتَّبِعُوا الْمُرْسَلِينَ (20) Nthawi yomweyo munthu wina adadza ali kuthamanga kuchokera kumbali ina ya mzinda. Iye adati, “Anthu anga! Tsatirani iwo amene atumidwa ndi Mulungu.” |
اتَّبِعُوا مَن لَّا يَسْأَلُكُمْ أَجْرًا وَهُم مُّهْتَدُونَ (21) “Atsatireni iwo amene safuna malipiro kuchokera kwa inu pokukumbutsani mawu a Mulungu ndipo ndi otsogozedwa bwino.” |
وَمَا لِيَ لَا أَعْبُدُ الَّذِي فَطَرَنِي وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (22) “Kodi pali chifukwa chotani chimene chingandilepheretse ine kuti ndim’pembedze Iye amene adandilenga popeza ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera?” |
أَأَتَّخِذُ مِن دُونِهِ آلِهَةً إِن يُرِدْنِ الرَّحْمَٰنُ بِضُرٍّ لَّا تُغْنِ عَنِّي شَفَاعَتُهُمْ شَيْئًا وَلَا يُنقِذُونِ (23) “Kodi ine ndizipembedza milungu ina osati Iyeyo? Ngati ndi chifuniro cha Mwini chisoni kundizunza, kukhala pakati kwawo sikudzandithandiza ndipo iwo sadzandipulumutsa ayi.” |
إِنِّي إِذًا لَّفِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (24) “Ndithudi ine ndikadatero, ndikadakhala mu chisokonezo choonekeratu.” |
إِنِّي آمَنتُ بِرَبِّكُمْ فَاسْمَعُونِ (25) Ndithudi ine ndakhulupirira mwa Ambuye wanu choncho ndimvereni.” |
قِيلَ ادْخُلِ الْجَنَّةَ ۖ قَالَ يَا لَيْتَ قَوْمِي يَعْلَمُونَ (26) Kudanenedwa kwa iye kuti, “Lowa mu Paradiso.” Iye adafuula kuti, “Akadakhala kuti anthu anga adadziwa.” |
بِمَا غَفَرَ لِي رَبِّي وَجَعَلَنِي مِنَ الْمُكْرَمِينَ (27) “Mmene Ambuye wanga wandionetsera chifundo chake kundiika mugulu la olemekezeka.” |
۞ وَمَا أَنزَلْنَا عَلَىٰ قَوْمِهِ مِن بَعْدِهِ مِن جُندٍ مِّنَ السَّمَاءِ وَمَا كُنَّا مُنزِلِينَ (28) Ndipo Ife sitidatumize padziko lapansi, kwa anthu ake, gulu lochokera kumwamba kuti lilimbane nawo ndipo sikudali koyenera kuti Ife tichite choncho |
إِن كَانَتْ إِلَّا صَيْحَةً وَاحِدَةً فَإِذَا هُمْ خَامِدُونَ (29) Udali mkuwo umodzi ndipo Oh! Onse adaonongedwa |
يَا حَسْرَةً عَلَى الْعِبَادِ ۚ مَا يَأْتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (30) Kalanga akapolo anga! Iwo amaseka pofuna kunyoza Mtumwi aliyense amene adadza kwa iwo |
أَلَمْ يَرَوْا كَمْ أَهْلَكْنَا قَبْلَهُم مِّنَ الْقُرُونِ أَنَّهُمْ إِلَيْهِمْ لَا يَرْجِعُونَ (31) Kodi iwo sadaone mibadwo yakale imene tidaiononga zaka zikwizikwi iwo asanabadwe? Ndipo iwo sadzabwereranso |
وَإِن كُلٌّ لَّمَّا جَمِيعٌ لَّدَيْنَا مُحْضَرُونَ (32) onse, popanda opatuka, adzadza kwa Ife |
وَآيَةٌ لَّهُمُ الْأَرْضُ الْمَيْتَةُ أَحْيَيْنَاهَا وَأَخْرَجْنَا مِنْهَا حَبًّا فَمِنْهُ يَأْكُلُونَ (33) Chizindikiro kwa iwo ndi nthaka yakufa imene tidaidzutsa ndipo timatulutsa m’nthakamo nthangala zomwe iwo amadya |
وَجَعَلْنَا فِيهَا جَنَّاتٍ مِّن نَّخِيلٍ وَأَعْنَابٍ وَفَجَّرْنَا فِيهَا مِنَ الْعُيُونِ (34) Taika m’nthakamo minda ya mitengo ya tende ndi ya mphesa ndipo timathirira ndi madzi a m’kasupe |
لِيَأْكُلُوا مِن ثَمَرِهِ وَمَا عَمِلَتْهُ أَيْدِيهِمْ ۖ أَفَلَا يَشْكُرُونَ (35) Moti akhoza kumadya zipatso zake. Si manja awo amene adapanga zimenezi ayi. Kodi sangathokoze |
سُبْحَانَ الَّذِي خَلَقَ الْأَزْوَاجَ كُلَّهَا مِمَّا تُنبِتُ الْأَرْضُ وَمِنْ أَنفُسِهِمْ وَمِمَّا لَا يَعْلَمُونَ (36) Ulemerero ukhale kwa Iye amene adalenga zinthu ziwiriziwiri, (chachimuna ndi chachikazi) zimene zimamera m’nthaka ndi zina za mtundu wawo ndi zinanso zimene sazidziwa |
وَآيَةٌ لَّهُمُ اللَّيْلُ نَسْلَخُ مِنْهُ النَّهَارَ فَإِذَا هُم مُّظْلِمُونَ (37) Chizindikiro cha kwa iwo ndi usiku. Kuchokera ku iwo timachotsa usana ndipo iwo amakhala mu mdima |
وَالشَّمْسُ تَجْرِي لِمُسْتَقَرٍّ لَّهَا ۚ ذَٰلِكَ تَقْدِيرُ الْعَزِيزِ الْعَلِيمِ (38) Dzuwa limayenda mofulumira kupita kumalo ake okapuma. Umenewu ndiwo ulamuliro wa Mwini Mphamvu zonse ndiponso Wodziwa chilichonse |
وَالْقَمَرَ قَدَّرْنَاهُ مَنَازِلَ حَتَّىٰ عَادَ كَالْعُرْجُونِ الْقَدِيمِ (39) Ndipo mwezi tidaulamulira kuti uyende mumsewu wake mpaka pamene ukamabwerera ngati nthawi yoyamba m’maonekedwe |
لَا الشَّمْسُ يَنبَغِي لَهَا أَن تُدْرِكَ الْقَمَرَ وَلَا اللَّيْلُ سَابِقُ النَّهَارِ ۚ وَكُلٌّ فِي فَلَكٍ يَسْبَحُونَ (40) Dzuwa sililoledwa kupitirira mwezi ndipo usiku siupyola usana. Chilichonse chimayenda mumsewu wake |
وَآيَةٌ لَّهُمْ أَنَّا حَمَلْنَا ذُرِّيَّتَهُمْ فِي الْفُلْكِ الْمَشْحُونِ (41) Ndipo chizindikiro china kwa iwo ndi chakuti tidanyamula makolo awo mu chombo chonyamula katundu |
وَخَلَقْنَا لَهُم مِّن مِّثْلِهِ مَا يَرْكَبُونَ (42) Tidalenga zombo za mtundu umenewu kuti iwo azikweramo |
وَإِن نَّشَأْ نُغْرِقْهُمْ فَلَا صَرِيخَ لَهُمْ وَلَا هُمْ يُنقَذُونَ (43) Timawamiza tikafuna ndipo palibe amene angawathandize ndipo sangathe kupulumutsidwa |
إِلَّا رَحْمَةً مِّنَّا وَمَتَاعًا إِلَىٰ حِينٍ (44) Kupatula kudzera m’chifundo chathu ndi kuwapatsa chisangalalo cha kanthawi kochepa |
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ اتَّقُوا مَا بَيْنَ أَيْدِيكُمْ وَمَا خَلْفَكُمْ لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (45) Pamene zinenedwa kwa iwo kuti, “Opani chinthu chimene chili patsogolo panu ndi pambuyo panu kuti mwina Mulungu angakuonetsereni chifundo” ndipo iwo samvera ayi |
وَمَا تَأْتِيهِم مِّنْ آيَةٍ مِّنْ آيَاتِ رَبِّهِمْ إِلَّا كَانُوا عَنْهَا مُعْرِضِينَ (46) Ndithudi palibe chizindikiro chochokera kwa Ambuye wawo chimene iwo amachivomera. Ndipo iwo salabadira |
وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ أَنفِقُوا مِمَّا رَزَقَكُمُ اللَّهُ قَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا لِلَّذِينَ آمَنُوا أَنُطْعِمُ مَن لَّوْ يَشَاءُ اللَّهُ أَطْعَمَهُ إِنْ أَنتُمْ إِلَّا فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (47) Ndipo pamene auzidwa kuti, “Perekani gawo la chopereka chaulere pa zinthu zimene Mulungu wakupatsani.” Anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ife tizidyetsa iwo amene Mulungu atafuna akhoza kuwadyetsa? Ndithudi inu ndi osochera kwambiri.” |
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْوَعْدُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (48) Iwo amanenanso kuti, “Kodi lonjezo limeneli la tsiku lachiweruzo lidzatsimikizidwa liti, ngati zimene uli kunenazi ndi zoona?” |
مَا يَنظُرُونَ إِلَّا صَيْحَةً وَاحِدَةً تَأْخُذُهُمْ وَهُمْ يَخِصِّمُونَ (49) Angodikira mkokomo umodzi wokha basi umene udzadza pa nthawi imene iwo ali kutsutsana |
فَلَا يَسْتَطِيعُونَ تَوْصِيَةً وَلَا إِلَىٰ أَهْلِهِمْ يَرْجِعُونَ (50) Iwo sadzakhala ndi mwayi wosiya mawu kapena kubwerera kwa abale awo |
وَنُفِخَ فِي الصُّورِ فَإِذَا هُم مِّنَ الْأَجْدَاثِ إِلَىٰ رَبِّهِمْ يَنسِلُونَ (51) Pamene lipenga lidzamveka, taona, kuchokera ku manda, anthu adzathamanga kupita kwa Ambuye wawo |
قَالُوا يَا وَيْلَنَا مَن بَعَثَنَا مِن مَّرْقَدِنَا ۜ ۗ هَٰذَا مَا وَعَدَ الرَّحْمَٰنُ وَصَدَقَ الْمُرْسَلُونَ (52) “Tsoka kwa ife!” Iwo adzatero. “Ndani amene watidzutsa kuchokera kumalo athu a mpumulo?” Ichi ndi chimene Ambuye wachifundo adalonjeza. “Atumwi adanenadi zoona!” |
إِن كَانَتْ إِلَّا صَيْحَةً وَاحِدَةً فَإِذَا هُمْ جَمِيعٌ لَّدَيْنَا مُحْضَرُونَ (53) Ndithudi ndi mfuwu umodzi wokha, onse panthawiyo, adzasonkhanitsidwa kwa Ife |
فَالْيَوْمَ لَا تُظْلَمُ نَفْسٌ شَيْئًا وَلَا تُجْزَوْنَ إِلَّا مَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (54) Patsiku limeneli sipadzakhala mzimu umene siudzaweruzidwa ndipo inu mudzalandira mphotho molingana ndi ntchito zanu |
إِنَّ أَصْحَابَ الْجَنَّةِ الْيَوْمَ فِي شُغُلٍ فَاكِهُونَ (55) Pa tsiku limeneli anthu okhala ku Paradiso adzakhala osangalala kwambiri |
هُمْ وَأَزْوَاجُهُمْ فِي ظِلَالٍ عَلَى الْأَرَائِكِ مُتَّكِئُونَ (56) Iwo pamodzi ndi akazi awo, adzakhala m’mithunzi ya nkhalango, pa mipando yawofowofo |
لَهُمْ فِيهَا فَاكِهَةٌ وَلَهُم مَّا يَدَّعُونَ (57) Iwo adzapeza m’menemo zipatso ndi zina zonse zimene adzafuna |
سَلَامٌ قَوْلًا مِّن رَّبٍّ رَّحِيمٍ (58) “Mtendere” ndiwo mawu amene adzachokere kwa Mulungu, Mwini Chisoni |
وَامْتَازُوا الْيَوْمَ أَيُّهَا الْمُجْرِمُونَ (59) Ndipo Iye adzati, “Khalani kutali inu oipa tsiku lalero?” |
۞ أَلَمْ أَعْهَدْ إِلَيْكُمْ يَا بَنِي آدَمَ أَن لَّا تَعْبُدُوا الشَّيْطَانَ ۖ إِنَّهُ لَكُمْ عَدُوٌّ مُّبِينٌ (60) “Kodi Ine sindidakuchenjezeni, inu ana a Adamu, kuti musamagwadire Satana, chifukwa iyeyu ndi mdani wanu woonekeratu?” |
وَأَنِ اعْبُدُونِي ۚ هَٰذَا صِرَاطٌ مُّسْتَقِيمٌ (61) “Ndi kuti muzindipembedza Ine? Ndithudi imeneyo ndiyo njira yoyenera.” |
وَلَقَدْ أَضَلَّ مِنكُمْ جِبِلًّا كَثِيرًا ۖ أَفَلَمْ تَكُونُوا تَعْقِلُونَ (62) Koma iye adasocheretsa anthu ambiri. Kodi mudalibe nzeru |
هَٰذِهِ جَهَنَّمُ الَّتِي كُنتُمْ تُوعَدُونَ (63) Imeneyi ndiyo Gahena imene munali kulonjezedwa |
اصْلَوْهَا الْيَوْمَ بِمَا كُنتُمْ تَكْفُرُونَ (64) Lowani m’menemo tsiku lalero ngati chilango, chifukwa chakusakhulupirira kwanu |
الْيَوْمَ نَخْتِمُ عَلَىٰ أَفْوَاهِهِمْ وَتُكَلِّمُنَا أَيْدِيهِمْ وَتَشْهَدُ أَرْجُلُهُم بِمَا كَانُوا يَكْسِبُونَ (65) Lero, Ife titseka pakamwa pawo, ndipo manja awo ndi amene ayankhule ndi Ife ndiponso miyendo yawo ichitira umboni pa ntchito zoipa zimene anali kuchita |
وَلَوْ نَشَاءُ لَطَمَسْنَا عَلَىٰ أَعْيُنِهِمْ فَاسْتَبَقُوا الصِّرَاطَ فَأَنَّىٰ يُبْصِرُونَ (66) Chikadakhala cholinga chathu, tikadawachititsa khungu kuti azivutika poyenda. Nanga akadaona bwanji machimo awo |
وَلَوْ نَشَاءُ لَمَسَخْنَاهُمْ عَلَىٰ مَكَانَتِهِمْ فَمَا اسْتَطَاعُوا مُضِيًّا وَلَا يَرْجِعُونَ (67) Chikadakhala cholinga chathu, tikadawasintha kuti asanduke china chake pamalo pamene adaimirira, kuti asapite patsogolo kapena kubwerera m’mbuyo |
وَمَن نُّعَمِّرْهُ نُنَكِّسْهُ فِي الْخَلْقِ ۖ أَفَلَا يَعْقِلُونَ (68) Aliyense amene timamukalambitsa, timam’bwezera ku ubwana. Kodi iwo sangazindikire chimenechi |
وَمَا عَلَّمْنَاهُ الشِّعْرَ وَمَا يَنبَغِي لَهُ ۚ إِنْ هُوَ إِلَّا ذِكْرٌ وَقُرْآنٌ مُّبِينٌ (69) Ife sitidamuphunzitse iye ndakatulo ayi ndiponso si koyenera kuti akhale mlakatuli. Ichi si china koma chikumbutso ndi dongosolo la Korani |
لِّيُنذِرَ مَن كَانَ حَيًّا وَيَحِقَّ الْقَوْلُ عَلَى الْكَافِرِينَ (70) Limene lichenjeza anthu a moyo ndi kupereka chiweruzo kwa anthu osakhulupirira |
أَوَلَمْ يَرَوْا أَنَّا خَلَقْنَا لَهُم مِّمَّا عَمِلَتْ أَيْدِينَا أَنْعَامًا فَهُمْ لَهَا مَالِكُونَ (71) Kodi iwo saona kuti pakati pa zinthu zimene tidalenga ndi manja athu tidawalengera nyama zimene iwo amazilamulira |
وَذَلَّلْنَاهَا لَهُمْ فَمِنْهَا رَكُوبُهُمْ وَمِنْهَا يَأْكُلُونَ (72) Tidalamula zimenezi kuti zizimvera malamulo awo kuti akhoza kumakwera ndi zina zoti azidya |
وَلَهُمْ فِيهَا مَنَافِعُ وَمَشَارِبُ ۖ أَفَلَا يَشْكُرُونَ (73) Ndipo amapezanso phindu lina lolekana. Iwo amamwa mkaka kuchokera ku izo. Kodi iwo sangathokoze |
وَاتَّخَذُوا مِن دُونِ اللَّهِ آلِهَةً لَّعَلَّهُمْ يُنصَرُونَ (74) Iwo akhazikitsa milungu ina powonjezera pa Mulungu weniweni, poganiza kuti mwina akhoza kuthandizidwa |
لَا يَسْتَطِيعُونَ نَصْرَهُمْ وَهُمْ لَهُمْ جُندٌ مُّحْضَرُونَ (75) Milunguyo siingawathandize. Iwo adzatengedwa mwankhondo kunka ku chilango |
فَلَا يَحْزُنكَ قَوْلُهُمْ ۘ إِنَّا نَعْلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعْلِنُونَ (76) Usalole kuti mawu awo akumvetse chisoni. Ife tikudziwa zonse zimene azibisa ndi zonse zimene akuzionetsa |
أَوَلَمْ يَرَ الْإِنسَانُ أَنَّا خَلَقْنَاهُ مِن نُّطْفَةٍ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٌ مُّبِينٌ (77) Kodi munthu, sadziwa kuti tidamulenga kuchokera ku dontho la umuna? Koma iye ndi otsutsana ndi Ife poyera |
وَضَرَبَ لَنَا مَثَلًا وَنَسِيَ خَلْقَهُ ۖ قَالَ مَن يُحْيِي الْعِظَامَ وَهِيَ رَمِيمٌ (78) Iye amatifanizira Ife ndi zina zake ndipo amaiwala za chilengedwe chake. Iye amafunsa kuti, “Kodi ndani amene adzapereka moyo ku mafupa oola?” |
قُلْ يُحْيِيهَا الَّذِي أَنشَأَهَا أَوَّلَ مَرَّةٍ ۖ وَهُوَ بِكُلِّ خَلْقٍ عَلِيمٌ (79) Nena “Iye amene adawalenga poyamba adzawapatsa moyo. Iye amadziwa chilichonse cha zolengedwa zake.” |
الَّذِي جَعَلَ لَكُم مِّنَ الشَّجَرِ الْأَخْضَرِ نَارًا فَإِذَا أَنتُم مِّنْهُ تُوقِدُونَ (80) Iye amene amakupatsani moto kuchokera ku mtengo wauwisi umene inu mumawunikira |
أَوَلَيْسَ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ بِقَادِرٍ عَلَىٰ أَن يَخْلُقَ مِثْلَهُم ۚ بَلَىٰ وَهُوَ الْخَلَّاقُ الْعَلِيمُ (81) Kodi Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, alibe mphamvu zolenga china chake chofanana nazo? Ndithudi ali nazo. Iye ndi Mlengi amene amadziwa chinthu china chilichonse |
إِنَّمَا أَمْرُهُ إِذَا أَرَادَ شَيْئًا أَن يَقُولَ لَهُ كُن فَيَكُونُ (82) Ndithudi pamene Iye afuna chinthu amangonena kuti, “Chikhale” ndipo chimakhaladi |
فَسُبْحَانَ الَّذِي بِيَدِهِ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيْءٍ وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (83) Ulemerero ukhale kwa Iye amene ali ndi ulamuliro pa chinthu china chilichonse; ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera |