×

Surah An-Nahl in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Nahl

Translation of the Meanings of Surah Nahl in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Nahl translated into Chichewa, Surah An-Nahl in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Nahl in Chichewa - نيانجا, Verses 128 - Surah Number 16 - Page 267.

بسم الله الرحمن الرحيم

أَتَىٰ أَمْرُ اللَّهِ فَلَا تَسْتَعْجِلُوهُ ۚ سُبْحَانَهُ وَتَعَالَىٰ عَمَّا يُشْرِكُونَ (1)
Chiweruzo cha Mulungu chidzabwera, ndipo kotero musachifulumizitse. Kulemekezeka ndi kuyamikidwa kukhale kwa Iye kuposa zonse zimene akumufanizira
يُنَزِّلُ الْمَلَائِكَةَ بِالرُّوحِ مِنْ أَمْرِهِ عَلَىٰ مَن يَشَاءُ مِنْ عِبَادِهِ أَنْ أَنذِرُوا أَنَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا أَنَا فَاتَّقُونِ (2)
Iyeamatsitsaangelondimawuakeamalamulokwaakapolo ake amene wawafuna ndikuwauza kuti muwachenjeze iwo kuti, “Kulibe Mulungu wina koma Ine ndekha. Kotero ndiopeni Ine.”
خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ بِالْحَقِّ ۚ تَعَالَىٰ عَمَّا يُشْرِكُونَ (3)
Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi. Iye akhale kutali ndi zimene akumufanizira nazo
خَلَقَ الْإِنسَانَ مِن نُّطْفَةٍ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٌ مُّبِينٌ (4)
Iye ndiye adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna ndi la ukazi ndipo taonani iye amatsutsa poyera
وَالْأَنْعَامَ خَلَقَهَا ۗ لَكُمْ فِيهَا دِفْءٌ وَمَنَافِعُ وَمِنْهَا تَأْكُلُونَ (5)
Iye adakulengerani nyama ndipo mu izo mumapeza zofunda ndi zithandizo zina ndiponso nyamazo mumadya
وَلَكُمْ فِيهَا جَمَالٌ حِينَ تُرِيحُونَ وَحِينَ تَسْرَحُونَ (6)
Ndipo mumanyadira pamene mumazisaka kudza nazo ku nyumba kwanu madzulo ndi pamene mumapita nazo kuubusa kukazidyetsa m’mawa
وَتَحْمِلُ أَثْقَالَكُمْ إِلَىٰ بَلَدٍ لَّمْ تَكُونُوا بَالِغِيهِ إِلَّا بِشِقِّ الْأَنفُسِ ۚ إِنَّ رَبَّكُمْ لَرَءُوفٌ رَّحِيمٌ (7)
Ndipo izo zimanyamula katundu wanu wolemera kupita kumalo kumene inu simutha kukafikako kupatula movutikira. Ndithudi Ambuye wanu ndi Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha
وَالْخَيْلَ وَالْبِغَالَ وَالْحَمِيرَ لِتَرْكَبُوهَا وَزِينَةً ۚ وَيَخْلُقُ مَا لَا تَعْلَمُونَ (8)
Ndipo adalenga akavalo, abulu ndi mahatchi kuti muzikwera ndi kukongoletsa. Ndipo adalenganso zina zimene simuzidziwa
وَعَلَى اللَّهِ قَصْدُ السَّبِيلِ وَمِنْهَا جَائِرٌ ۚ وَلَوْ شَاءَ لَهَدَاكُمْ أَجْمَعِينَ (9)
Zili kwa Mulungu kusonyeza njira yoyenera, koma pali njirazinazopatukandipo Iyeakadafunaakadakutsogolerani nonse
هُوَ الَّذِي أَنزَلَ مِنَ السَّمَاءِ مَاءً ۖ لَّكُم مِّنْهُ شَرَابٌ وَمِنْهُ شَجَرٌ فِيهِ تُسِيمُونَ (10)
Iye ndiye amene amatsitsa madzi kuchokera ku mitambo omwe inu mumamwa ndipo amameretsa mitengo imene mumadyetsa ziweto
يُنبِتُ لَكُم بِهِ الزَّرْعَ وَالزَّيْتُونَ وَالنَّخِيلَ وَالْأَعْنَابَ وَمِن كُلِّ الثَّمَرَاتِ ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لِّقَوْمٍ يَتَفَكَّرُونَ (11)
Kudzera m’menemu, Iye amakumeretserani mbewu ndi mitengo ya mafuta, mitengo ya tende ndi mphesa ndiponso zipatso zina. Ndithudi! Mu ichi muli chizindikiro kwa anthu a maganizo abwino
وَسَخَّرَ لَكُمُ اللَّيْلَ وَالنَّهَارَ وَالشَّمْسَ وَالْقَمَرَ ۖ وَالنُّجُومُ مُسَخَّرَاتٌ بِأَمْرِهِ ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يَعْقِلُونَ (12)
Ndipo adakupeputsirani usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, mwalamulo lake. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira
وَمَا ذَرَأَ لَكُمْ فِي الْأَرْضِ مُخْتَلِفًا أَلْوَانُهُ ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لِّقَوْمٍ يَذَّكَّرُونَ (13)
Ndipo chilichonse chimene adakulengerani padziko lapansi adachilenga cha mitundu yosiyanasiyana. Kotero chilichonse chili ndi chisonyezo kwa anthu omwe amasangalala ndi matamando a Mulungu
وَهُوَ الَّذِي سَخَّرَ الْبَحْرَ لِتَأْكُلُوا مِنْهُ لَحْمًا طَرِيًّا وَتَسْتَخْرِجُوا مِنْهُ حِلْيَةً تَلْبَسُونَهَا وَتَرَى الْفُلْكَ مَوَاخِرَ فِيهِ وَلِتَبْتَغُوا مِن فَضْلِهِ وَلَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (14)
Iye ndiye amene adakupeputsirani nyanja kuti inu muzidya nyama yaiwisi kuchokera mu iyo ndi kutulutsa zovala zokongola zimene mumavala. Ndipo mumaona ngalawa zili kuyenda pa nyanja. Adalenga zonsezi kuti muzipezamo zokoma zake ndi kuti muzikhala othokoza
وَأَلْقَىٰ فِي الْأَرْضِ رَوَاسِيَ أَن تَمِيدَ بِكُمْ وَأَنْهَارًا وَسُبُلًا لَّعَلَّكُمْ تَهْتَدُونَ (15)
Ndipo Iye adakhazikitsa mapiri padziko lapansi kuti lisagwedezeke pamodzi ndi inu, mitsinje ndi misewu kuti mutsogozedwe munjira zabwino
وَعَلَامَاتٍ ۚ وَبِالنَّجْمِ هُمْ يَهْتَدُونَ (16)
Ndi zizindikiro zina zokutsogolerani, nyenyezi nazonso anthu amatsogozedwa nazo
أَفَمَن يَخْلُقُ كَمَن لَّا يَخْلُقُ ۗ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ (17)
Kodi Iye amene amalenga angafanane ndi Iye amene salenga? Kodi inu simungakumbukire
وَإِن تَعُدُّوا نِعْمَةَ اللَّهِ لَا تُحْصُوهَا ۗ إِنَّ اللَّهَ لَغَفُورٌ رَّحِيمٌ (18)
Ngati inu mutawerenga zokoma za Mulungu simungakwaniritse kuziwerenga. Ndithudi! Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
وَاللَّهُ يَعْلَمُ مَا تُسِرُّونَ وَمَا تُعْلِنُونَ (19)
Ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumabisa ndi zimene mumaonetsera
وَالَّذِينَ يَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ لَا يَخْلُقُونَ شَيْئًا وَهُمْ يُخْلَقُونَ (20)
Koma milungu yabodza imene anthu osakhulupirira amapembedza m’malo mwa Mulungu, siinalenge china chilichonse ayi chifukwa nayonso ndi yolengedwa
أَمْوَاتٌ غَيْرُ أَحْيَاءٍ ۖ وَمَا يَشْعُرُونَ أَيَّانَ يُبْعَثُونَ (21)
Iyo ndi yakufa, si yamoyo ayi ndiponso iyo siidziwa nthawi imene idzaukitsidwe
إِلَٰهُكُمْ إِلَٰهٌ وَاحِدٌ ۚ فَالَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ قُلُوبُهُم مُّنكِرَةٌ وَهُم مُّسْتَكْبِرُونَ (22)
Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi yekha. Koma iwo amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza, mitima yawo imakana ndipo iwo ndi odzikweza
لَا جَرَمَ أَنَّ اللَّهَ يَعْلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعْلِنُونَ ۚ إِنَّهُ لَا يُحِبُّ الْمُسْتَكْبِرِينَ (23)
Mosakayika, ndithudi, Mulungu amadziwa zonse zimene iwo amabisa ndi zimene amaonetsera. Ndithudi, Iye sakonda anthu odzikweza
وَإِذَا قِيلَ لَهُم مَّاذَا أَنزَلَ رَبُّكُمْ ۙ قَالُوا أَسَاطِيرُ الْأَوَّلِينَ (24)
Pamene amafunsidwa kuti, “Kodi Ambuye wanu wavumbulutsa zotani?” Iwo amati, “Nkhani zopeka za anthu a kalekale.”
لِيَحْمِلُوا أَوْزَارَهُمْ كَامِلَةً يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۙ وَمِنْ أَوْزَارِ الَّذِينَ يُضِلُّونَهُم بِغَيْرِ عِلْمٍ ۗ أَلَا سَاءَ مَا يَزِرُونَ (25)
Iwo adzanyamula katundu wawo okwanira pa tsiku la kuuka kwa akufa pamodzi ndi katundu wa iwo amene adawasocheretsa mu umbuli. Ndithudi zoipa ndi zimene akusenza
قَدْ مَكَرَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ فَأَتَى اللَّهُ بُنْيَانَهُم مِّنَ الْقَوَاعِدِ فَخَرَّ عَلَيْهِمُ السَّقْفُ مِن فَوْقِهِمْ وَأَتَاهُمُ الْعَذَابُ مِنْ حَيْثُ لَا يَشْعُرُونَ (26)
Iwo amene adalipo kale adakonza chiwembu koma Mulungu adaphwanya nyumba zawo kuyambira pa maziko ake ndipo denga lidawagwera kuchokera pamwamba pawo ndipo chilango chidadza pa iwo kuchokera ku mbali imene iwo sanali kuganiza
ثُمَّ يَوْمَ الْقِيَامَةِ يُخْزِيهِمْ وَيَقُولُ أَيْنَ شُرَكَائِيَ الَّذِينَ كُنتُمْ تُشَاقُّونَ فِيهِمْ ۚ قَالَ الَّذِينَ أُوتُوا الْعِلْمَ إِنَّ الْخِزْيَ الْيَوْمَ وَالسُّوءَ عَلَى الْكَافِرِينَ (27)
Ndipo patsiku la kuuka kwa akufa Iye adzawachititsa manyazi ndipo adzati, “Zili kuti zimene munkandifanizira nazo, zimene inu mumakangana ndi Aneneri chifukwa cha izo?” Iwo amene adapatsidwa nzeru adzati, “Ndithudi! Zochititsa manyazi ndiponso zoipa ziwagwera lero lino anthu osakhulupirira.”
الَّذِينَ تَتَوَفَّاهُمُ الْمَلَائِكَةُ ظَالِمِي أَنفُسِهِمْ ۖ فَأَلْقَوُا السَّلَمَ مَا كُنَّا نَعْمَلُ مِن سُوءٍ ۚ بَلَىٰ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (28)
Iwo amene angelo amawatenga ali odzipondereza okha, adzagonja mwachinyengo ponena kuti, “Ife sitinali kuchitachoipa.”Angeloadzati,“Indedi! Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene munali kuchita.”
فَادْخُلُوا أَبْوَابَ جَهَنَّمَ خَالِدِينَ فِيهَا ۖ فَلَبِئْسَ مَثْوَى الْمُتَكَبِّرِينَ (29)
“Kotero lowani m’zipata za Gahena, kumeneko mudzakhalako mpaka kalekale. Ndithudi ndi oipa malo a anthu odzikweza.”
۞ وَقِيلَ لِلَّذِينَ اتَّقَوْا مَاذَا أَنزَلَ رَبُّكُمْ ۚ قَالُوا خَيْرًا ۗ لِّلَّذِينَ أَحْسَنُوا فِي هَٰذِهِ الدُّنْيَا حَسَنَةٌ ۚ وَلَدَارُ الْآخِرَةِ خَيْرٌ ۚ وَلَنِعْمَ دَارُ الْمُتَّقِينَ (30)
Ndipo kwa anthu oopa zidzanenedwa kuti, “Kodi Ambuye wanu adavumbulutsa zotani?” Iwo adzati, “Zabwino.” Mphotho yabwino idzakhala ya iwo amene adachita ntchito zabwino m’moyo uno. Koma nyumba yabwino kwambiri ndi mphotho ya moyo umene uli nkudza ndi mtendere wabwino ndiponso nyumba ya anthu oopa Mulungu
جَنَّاتُ عَدْنٍ يَدْخُلُونَهَا تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ ۖ لَهُمْ فِيهَا مَا يَشَاءُونَ ۚ كَذَٰلِكَ يَجْزِي اللَّهُ الْمُتَّقِينَ (31)
Iwo adzalowa m’minda yamuyaya ndipo mitsinje idzayenda pansi pake. Iwo, kumeneko, adzapeza zonse zimene adzazifuna. Mmenemu ndi mmene Mulungu adzawalipirire anthu oopa Mulungu
الَّذِينَ تَتَوَفَّاهُمُ الْمَلَائِكَةُ طَيِّبِينَ ۙ يَقُولُونَ سَلَامٌ عَلَيْكُمُ ادْخُلُوا الْجَنَّةَ بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (32)
Iwo amene angelo amatenga miyoyo yawo ali kuchita zabwino, Angelo adzanena kuti, “Mtendere ukhale kwa inu. Lowani mu Paradiso, chifukwa cha ntchito zabwino zimene munkachita.”
هَلْ يَنظُرُونَ إِلَّا أَن تَأْتِيَهُمُ الْمَلَائِكَةُ أَوْ يَأْتِيَ أَمْرُ رَبِّكَ ۚ كَذَٰلِكَ فَعَلَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ وَمَا ظَلَمَهُمُ اللَّهُ وَلَٰكِن كَانُوا أَنفُسَهُمْ يَظْلِمُونَ (33)
Kodi iwo akudikira kuti angelo adze kwa iwo kapena kuti libwere lamulo kuchokera kwa Mulungu wanu? Chomwecho ndicho adachita iwo amene adalipo kale. Mulungu sadawapondereze koma iwo adadzipondereza okha
فَأَصَابَهُمْ سَيِّئَاتُ مَا عَمِلُوا وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (34)
Ndipo mavuto adawapeza iwo chifukwa cha zimene adachita ndipo adawazungulira masautso a zinthu zimene iwo amazikana
وَقَالَ الَّذِينَ أَشْرَكُوا لَوْ شَاءَ اللَّهُ مَا عَبَدْنَا مِن دُونِهِ مِن شَيْءٍ نَّحْنُ وَلَا آبَاؤُنَا وَلَا حَرَّمْنَا مِن دُونِهِ مِن شَيْءٍ ۚ كَذَٰلِكَ فَعَلَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ فَهَلْ عَلَى الرُّسُلِ إِلَّا الْبَلَاغُ الْمُبِينُ (35)
Ndipo anthu opembedza mafano amati, “Mulungu akadafuna, ife kapena makolo athu, sitikadapembedza milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni ayi ndiponso ife sitikadaletsa china chilichonse opanda chilolezo chake.” Mmenemo ndimo adachitira anthu amene adalipo kale iwo asanadze. Kodi Atumwi adapatsidwa china kupatula kupereka Uthenga momveka
وَلَقَدْ بَعَثْنَا فِي كُلِّ أُمَّةٍ رَّسُولًا أَنِ اعْبُدُوا اللَّهَ وَاجْتَنِبُوا الطَّاغُوتَ ۖ فَمِنْهُم مَّنْ هَدَى اللَّهُ وَمِنْهُم مَّنْ حَقَّتْ عَلَيْهِ الضَّلَالَةُ ۚ فَسِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَانظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُكَذِّبِينَ (36)
Ndithudi! Ife tidatumiza Mtumwi pakati pa mtundu uliwonse amene amanena kuti, “Pembedzani Mulungu ndipo mupewe milungu yabodza.” Pakati pawo padali ena amene Mulungu adawatsogolera ndi ena mwa iwo amene kusochera kwawo kudali koyenera. Yendani pa dziko lonse lapansi ndipo mukaone kuti adali bwanji mapeto a anthu osakhulupirira
إِن تَحْرِصْ عَلَىٰ هُدَاهُمْ فَإِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي مَن يُضِلُّ ۖ وَمَا لَهُم مِّن نَّاصِرِينَ (37)
Ngati iwe ufunitsitsa kuti iwo atsogozedwe, ndithudi, Mulungu satsogolera amene wamusocheretsa. Ndipo iwo sadzapeza owathandiza
وَأَقْسَمُوا بِاللَّهِ جَهْدَ أَيْمَانِهِمْ ۙ لَا يَبْعَثُ اللَّهُ مَن يَمُوتُ ۚ بَلَىٰ وَعْدًا عَلَيْهِ حَقًّا وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (38)
Iwo adalumbira mwamphamvu M’dzina la Mulungu kuti, “Mulungu sadzaukitsa munthu wakufa.” Inde, ndi lonjezo la Mulungu loona ndipo lidzakwaniritsidwa, koma anthu ambiri sadziwa
لِيُبَيِّنَ لَهُمُ الَّذِي يَخْتَلِفُونَ فِيهِ وَلِيَعْلَمَ الَّذِينَ كَفَرُوا أَنَّهُمْ كَانُوا كَاذِبِينَ (39)
Kuti Iye adzawaonetse zoonadi zimene iwo amatsutsana ndi kuti iwo amene sakhulupirira adziwe kuti adali onama
إِنَّمَا قَوْلُنَا لِشَيْءٍ إِذَا أَرَدْنَاهُ أَن نَّقُولَ لَهُ كُن فَيَكُونُ (40)
Ndithudi liwu lathu pa chinthu chimene tachifuna ndi lakuti timangonena, “Khala” ndipo chimakhala
وَالَّذِينَ هَاجَرُوا فِي اللَّهِ مِن بَعْدِ مَا ظُلِمُوا لَنُبَوِّئَنَّهُمْ فِي الدُّنْيَا حَسَنَةً ۖ وَلَأَجْرُ الْآخِرَةِ أَكْبَرُ ۚ لَوْ كَانُوا يَعْلَمُونَ (41)
Ndi iwo amene adasamuka ndi cholinga chokondweretsa Mulungu pambuyo poponderezedwa, Ife, ndithudi, tidzawakhazika padziko mwamtendere. Koma malipiro a tsiku lachiweruzo adzakhala aakulu kwambiri iwo akadadziwa
الَّذِينَ صَبَرُوا وَعَلَىٰ رَبِّهِمْ يَتَوَكَّلُونَ (42)
Iwo amene adapirira ndipo adaika chikhulupiriro mwa Ambuye wawo
وَمَا أَرْسَلْنَا مِن قَبْلِكَ إِلَّا رِجَالًا نُّوحِي إِلَيْهِمْ ۚ فَاسْأَلُوا أَهْلَ الذِّكْرِ إِن كُنتُمْ لَا تَعْلَمُونَ (43)
Iwe usanadze Ife sitidatumizepo, ena koma amuna amene tidawapatsa chivumbulutso chathu. Kotero afunse iwo odziwa mawu a Mulungu ngati iwe siukudziwa
بِالْبَيِّنَاتِ وَالزُّبُرِ ۗ وَأَنزَلْنَا إِلَيْكَ الذِّكْرَ لِتُبَيِّنَ لِلنَّاسِ مَا نُزِّلَ إِلَيْهِمْ وَلَعَلَّهُمْ يَتَفَكَّرُونَ (44)
Ndi zizindikiro zooneka ndiponso mabuku opatulika, Ife tavumbulutsa kwa iwe chikumbutso kuti ulalikire anthu zonse zimene zatumizidwa kwa iwo ndi kuti akhoza kulingirira
أَفَأَمِنَ الَّذِينَ مَكَرُوا السَّيِّئَاتِ أَن يَخْسِفَ اللَّهُ بِهِمُ الْأَرْضَ أَوْ يَأْتِيَهُمُ الْعَذَابُ مِنْ حَيْثُ لَا يَشْعُرُونَ (45)
Kodi iwo amene amakonza chiwembu ndi odzikhulupirira kuti Mulungu sangawakwirire m’nthaka kapena kuti chilango sichingagwe pa iwo kuchokera ku mbali imene sali kuiyembekezera
أَوْ يَأْخُذَهُمْ فِي تَقَلُّبِهِمْ فَمَا هُم بِمُعْجِزِينَ (46)
Kapena iwo ali ndi chikhulupiriro chakuti Iye sadzawagwira iwo m’maulendo awo pamene sangathe kuthawa
أَوْ يَأْخُذَهُمْ عَلَىٰ تَخَوُّفٍ فَإِنَّ رَبَّكُمْ لَرَءُوفٌ رَّحِيمٌ (47)
Kapena kuti Iye sangawapatse chionongeko cha pang’onopang’ono? Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha
أَوَلَمْ يَرَوْا إِلَىٰ مَا خَلَقَ اللَّهُ مِن شَيْءٍ يَتَفَيَّأُ ظِلَالُهُ عَنِ الْيَمِينِ وَالشَّمَائِلِ سُجَّدًا لِّلَّهِ وَهُمْ دَاخِرُونَ (48)
Kodi iwo sakuziona zinthu zimene Mulungu adalenga mmene zimagwetsera mithunzi yake kumbali ya dzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere, kumulambira Mulungu modzichepetsa
وَلِلَّهِ يَسْجُدُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ مِن دَابَّةٍ وَالْمَلَائِكَةُ وَهُمْ لَا يَسْتَكْبِرُونَ (49)
Ndipo kwa Mulungu zimagwada zinthu zonse za mlengalenga ndi za padziko lapansi ndi zonse za moyo ndi angelo, ndipo sizidzikweza
يَخَافُونَ رَبَّهُم مِّن فَوْقِهِمْ وَيَفْعَلُونَ مَا يُؤْمَرُونَ ۩ (50)
Izo zimaopa Ambuye wawo amene ali pamwamba pawo ndipo zimachita monga momwe zalamulidwira
۞ وَقَالَ اللَّهُ لَا تَتَّخِذُوا إِلَٰهَيْنِ اثْنَيْنِ ۖ إِنَّمَا هُوَ إِلَٰهٌ وَاحِدٌ ۖ فَإِيَّايَ فَارْهَبُونِ (51)
Mulungu adati, “Inu musapembedze milungu iwiri ayi. Ndithudi Iyendi Mulungummodziyekha. Koterondiopeni Ine.”
وَلَهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَلَهُ الدِّينُ وَاصِبًا ۚ أَفَغَيْرَ اللَّهِ تَتَّقُونَ (52)
Ndipo zonse zimene zili mlengalenga ndi m’dziko lapansi ndi zake ndipo Iye yekha ayenera kupembedzedwa basi. Kodi inu mudzaopa wina wake wosati Mulungu
وَمَا بِكُم مِّن نِّعْمَةٍ فَمِنَ اللَّهِ ۖ ثُمَّ إِذَا مَسَّكُمُ الضُّرُّ فَإِلَيْهِ تَجْأَرُونَ (53)
Ndipo zokoma zonse zimene mumalandira zimachokera kwa Mulungu. Ndipo pamene mavuto akupezani, inu mumapempha chithandizo kwa Iye
ثُمَّ إِذَا كَشَفَ الضُّرَّ عَنكُمْ إِذَا فَرِيقٌ مِّنكُم بِرَبِّهِمْ يُشْرِكُونَ (54)
Koma Iye akakuchotserani inu mavuto, taonani! Ena mwa inu mumaphatikiza Ambuye wanu ndi mafano mukamapembedza
لِيَكْفُرُوا بِمَا آتَيْنَاهُمْ ۚ فَتَمَتَّعُوا ۖ فَسَوْفَ تَعْلَمُونَ (55)
Motero iwo amakana zimene tawapatsa! Choncho basangalalani pang’ono koma posachedwapa mudzadziwa choonadi
وَيَجْعَلُونَ لِمَا لَا يَعْلَمُونَ نَصِيبًا مِّمَّا رَزَقْنَاهُمْ ۗ تَاللَّهِ لَتُسْأَلُنَّ عَمَّا كُنتُمْ تَفْتَرُونَ (56)
Ndipo iwo amapereka gawo lina la zinthu zimene tawapatsa ku zinthu zimene iwo sazidziwa. Pali Mulungu, inu mudzafunsidwa zinthu zonse zabodza zimene mumapeka
وَيَجْعَلُونَ لِلَّهِ الْبَنَاتِ سُبْحَانَهُ ۙ وَلَهُم مَّا يَشْتَهُونَ (57)
Ndipo iwo amamupatsa Mulungu ana aakazi. Ayeretsedwe Ambuye ndipo Iye akhale pamwamba pa zonse zimene amaziphatikiza ndi Iye ndi zimene iwo amafuna
وَإِذَا بُشِّرَ أَحَدُهُم بِالْأُنثَىٰ ظَلَّ وَجْهُهُ مُسْوَدًّا وَهُوَ كَظِيمٌ (58)
Ndipo pamene kubadwa kwa mwana wamkazi kumemezedwa kwa wina wa iwo, nkhope yake imada ndipo amadzadzidwa ndi chisoni
يَتَوَارَىٰ مِنَ الْقَوْمِ مِن سُوءِ مَا بُشِّرَ بِهِ ۚ أَيُمْسِكُهُ عَلَىٰ هُونٍ أَمْ يَدُسُّهُ فِي التُّرَابِ ۗ أَلَا سَاءَ مَا يَحْكُمُونَ (59)
Iye amadzibisa kuti asaonane ndi anthu ake chifukwa cha nkhani yoipa imene wauzidwa. Kodi mwanayu akhale naye ndi manyazi kapena kuti akamukwirire m’nthaka? Ndithudi chiweruzo chawo ndi choipa kwambiri
لِلَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ مَثَلُ السَّوْءِ ۖ وَلِلَّهِ الْمَثَلُ الْأَعْلَىٰ ۚ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (60)
Iwo amene sakhulupirira zatsiku lachiweruzo ali ndi mbiri yoipa pamene Mulungu ali ndi mbiri yaulemerero. Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndiponso ndi Wanzeru
وَلَوْ يُؤَاخِذُ اللَّهُ النَّاسَ بِظُلْمِهِم مَّا تَرَكَ عَلَيْهَا مِن دَابَّةٍ وَلَٰكِن يُؤَخِّرُهُمْ إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى ۖ فَإِذَا جَاءَ أَجَلُهُمْ لَا يَسْتَأْخِرُونَ سَاعَةً ۖ وَلَا يَسْتَقْدِمُونَ (61)
Akadakhala kuti Mulungu anali kulanga anthu msanga chifukwa cha zoipa zawo, palibe cholengedwa ndi chimodzi chomwe chimene Iye akadachisiya ndi moyo. Koma Iye amawasunga mpaka tsiku lokhazikitsidwa, ndipo ngati nthawi yawo ikwana, ngakhale ndi kamphindi kochepa, iwo sangaichedwetse kapena kuifulumizitsa
وَيَجْعَلُونَ لِلَّهِ مَا يَكْرَهُونَ وَتَصِفُ أَلْسِنَتُهُمُ الْكَذِبَ أَنَّ لَهُمُ الْحُسْنَىٰ ۖ لَا جَرَمَ أَنَّ لَهُمُ النَّارَ وَأَنَّهُم مُّفْرَطُونَ (62)
Iwo amamupatsa Mulungu zinthu zimene iwo amazida, ndipo malirime awo amanena bodza lakuti mphotho yabwino ili kuwayembekezera. Mosakayika kwawo ndi kumoto ndipo iwo adzakhala oyamba kuponyedwako ndipo adzasiyidwa m’menemo osasamalidwa
تَاللَّهِ لَقَدْ أَرْسَلْنَا إِلَىٰ أُمَمٍ مِّن قَبْلِكَ فَزَيَّنَ لَهُمُ الشَّيْطَانُ أَعْمَالَهُمْ فَهُوَ وَلِيُّهُمُ الْيَوْمَ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (63)
Pali Mulungu, ndithudi, Ife tidatumiza Atumwi ena, ku mibadwo ina, iwe usanadze. Koma Satana adasandutsa ntchito zawo zoipa kuti zikhale zabwino kwa iwo. Motero Satana ndiye bwenzi lawo. Chawo chidzakhala chilango chowawa zedi
وَمَا أَنزَلْنَا عَلَيْكَ الْكِتَابَ إِلَّا لِتُبَيِّنَ لَهُمُ الَّذِي اخْتَلَفُوا فِيهِ ۙ وَهُدًى وَرَحْمَةً لِّقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (64)
Ndipo Ife sitinavumbulutse Buku kwa iwe kupatula kuti iwe uwauze anthu poyera choonadi cha zinthu zimene ali kukangana ndiponso ngati chilangizo ndi dalitso kwa anthu okhulupirira moonadi
وَاللَّهُ أَنزَلَ مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَأَحْيَا بِهِ الْأَرْضَ بَعْدَ مَوْتِهَا ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لِّقَوْمٍ يَسْمَعُونَ (65)
Mulungu amatsitsa madzi kuchokera ku mtambo ndipo Iye amadzutsira nthaka pambuyo poti idafa. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu akumva
وَإِنَّ لَكُمْ فِي الْأَنْعَامِ لَعِبْرَةً ۖ نُّسْقِيكُم مِّمَّا فِي بُطُونِهِ مِن بَيْنِ فَرْثٍ وَدَمٍ لَّبَنًا خَالِصًا سَائِغًا لِّلشَّارِبِينَ (66)
Ndithudi! Mu nyama muli phunziro kwa inu. Ife timakupatsani kuti muzimwa zina mwa zomwe zili m’mimba mwake kuchokera pakati pa ndowe ndi magazi. Mkaka wabwino, chakumwa chabwino kwambiri kwa iwo amene amamwa
وَمِن ثَمَرَاتِ النَّخِيلِ وَالْأَعْنَابِ تَتَّخِذُونَ مِنْهُ سَكَرًا وَرِزْقًا حَسَنًا ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لِّقَوْمٍ يَعْقِلُونَ (67)
Ndipo kuchokera ku zipatso za mitengo ya tende ndi mitengo ya mphesa, inu mumapanga zakumwa zoledzeretsa ndiponso chakudya chabwino. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu amene ali ndi nzeru
وَأَوْحَىٰ رَبُّكَ إِلَى النَّحْلِ أَنِ اتَّخِذِي مِنَ الْجِبَالِ بُيُوتًا وَمِنَ الشَّجَرِ وَمِمَّا يَعْرِشُونَ (68)
Ambuye wako adauza njuchi kuti, “Mangani nyumba zanu m’mapiri, m’mitengo ndi m’ming’oma imene anthu amakonza.”
ثُمَّ كُلِي مِن كُلِّ الثَّمَرَاتِ فَاسْلُكِي سُبُلَ رَبِّكِ ذُلُلًا ۚ يَخْرُجُ مِن بُطُونِهَا شَرَابٌ مُّخْتَلِفٌ أَلْوَانُهُ فِيهِ شِفَاءٌ لِّلنَّاسِ ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لِّقَوْمٍ يَتَفَكَّرُونَ (69)
“Ndipo idyani zipatso za mitundu yonse, ndipo yendani m’njira za Ambuye wanu mosavutika.” Kuchokera m’mimba mwa njuchi, mumatuluka zakumwa zamitundu yosiyanasiyana ndipo m’menemo muli mankhwala ochiza anthu. Ndithudi mu izi muli zizindikiro kwa iwo amene amalingilira
وَاللَّهُ خَلَقَكُمْ ثُمَّ يَتَوَفَّاكُمْ ۚ وَمِنكُم مَّن يُرَدُّ إِلَىٰ أَرْذَلِ الْعُمُرِ لِكَيْ لَا يَعْلَمَ بَعْدَ عِلْمٍ شَيْئًا ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ قَدِيرٌ (70)
Mulungu ndiye amene adakulengani inu ndipo adzakuphani. Ndipo ena a inu amakalamba koti sangathe kuzidziwa zinthu zimene anali kuzidziwa kale. Ndithudi! Mulungu amadziwa chilichonse ndiponso ali ndi mphamvu zonse
وَاللَّهُ فَضَّلَ بَعْضَكُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ فِي الرِّزْقِ ۚ فَمَا الَّذِينَ فُضِّلُوا بِرَادِّي رِزْقِهِمْ عَلَىٰ مَا مَلَكَتْ أَيْمَانُهُمْ فَهُمْ فِيهِ سَوَاءٌ ۚ أَفَبِنِعْمَةِ اللَّهِ يَجْحَدُونَ (71)
Ndipo Mulungu wawalemekeza ena a inu kuposa ena powapatsa chuma chambiri. Ndipo iwo amene apatsidwa zambiri sadzapereka ngakhale zitavuta chotani chuma chawo kwa akapolo awo kuti mwina akhoza kufanana pa chuma. Kodi iwo amakana zokoma za Mulungu
وَاللَّهُ جَعَلَ لَكُم مِّنْ أَنفُسِكُمْ أَزْوَاجًا وَجَعَلَ لَكُم مِّنْ أَزْوَاجِكُم بَنِينَ وَحَفَدَةً وَرَزَقَكُم مِّنَ الطَّيِّبَاتِ ۚ أَفَبِالْبَاطِلِ يُؤْمِنُونَ وَبِنِعْمَتِ اللَّهِ هُمْ يَكْفُرُونَ (72)
Ndipo Mulungu wakupatsani akazi kuchoka pakati panu ndipo kudzera mwa iwo wakupatsani ana aamuna ndi zidzukulu ndipo Iye wakupatsani zinthu zabwino. Kodi iwo tsopano adzakhulupirira mu zinthu zabodza ndikukana ubwino wa Mulungu
وَيَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ مَا لَا يَمْلِكُ لَهُمْ رِزْقًا مِّنَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ شَيْئًا وَلَا يَسْتَطِيعُونَ (73)
Ndipo iwo amapembedza mafano mowonjezera pa Mulungu amene sangathe kuwapatsa chithandizo chilichonse kuchokera kumwamba kapena padziko lapansi
فَلَا تَضْرِبُوا لِلَّهِ الْأَمْثَالَ ۚ إِنَّ اللَّهَ يَعْلَمُ وَأَنتُمْ لَا تَعْلَمُونَ (74)
Motero musafanizire wina aliyense ndi Mulungu. Ndithudi Mulungu amadziwa pamene inu simudziwa chilichonse
۞ ضَرَبَ اللَّهُ مَثَلًا عَبْدًا مَّمْلُوكًا لَّا يَقْدِرُ عَلَىٰ شَيْءٍ وَمَن رَّزَقْنَاهُ مِنَّا رِزْقًا حَسَنًا فَهُوَ يُنفِقُ مِنْهُ سِرًّا وَجَهْرًا ۖ هَلْ يَسْتَوُونَ ۚ الْحَمْدُ لِلَّهِ ۚ بَلْ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (75)
Mulungu akupereka fanizo la kapolo amene ali mu ulamuliro wa bwana wake amene sangathe kuchita chilichonse ndi munthu wina, amene tamupatsa zinthu zabwino ndipo iye amapereka kuchokera ku zimene wapatsidwa mwamseri ndiponso moonekera. Kodi iwo angafanane? Kuyamikidwa konse kukhale kwa Mulungu, koma ambiri a iwo sazindikira
وَضَرَبَ اللَّهُ مَثَلًا رَّجُلَيْنِ أَحَدُهُمَا أَبْكَمُ لَا يَقْدِرُ عَلَىٰ شَيْءٍ وَهُوَ كَلٌّ عَلَىٰ مَوْلَاهُ أَيْنَمَا يُوَجِّههُّ لَا يَأْتِ بِخَيْرٍ ۖ هَلْ يَسْتَوِي هُوَ وَمَن يَأْمُرُ بِالْعَدْلِ ۙ وَهُوَ عَلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (76)
Ndipo Mulungu ali kuperekanso fanizo la anthu ena awiri, mmodzi wa iwo wosayankhula amene sangathe kuchita chilichonse, ndi wosathandiza Ambuye wake chifukwa kulikonse kumene amamutuma iye sabweretsa chabwino. Kodi iyeyu ndi wofanana ndi iye amene amalamula mwachilungamo ndipo ali m’njira yoyenera
وَلِلَّهِ غَيْبُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَمَا أَمْرُ السَّاعَةِ إِلَّا كَلَمْحِ الْبَصَرِ أَوْ هُوَ أَقْرَبُ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (77)
Zinsinsi zimene zili mlengalenga ndi pa dziko lapansi zonse ndi za Mulungu. Ntchito yokhudza ola lomaliza idzagwiridwa mu nthawi ngati kuphethira kwa diso kapena kufulumira koposerapo apa. Ndithudi Mulungu amatha kuchita chilichonse
وَاللَّهُ أَخْرَجَكُم مِّن بُطُونِ أُمَّهَاتِكُمْ لَا تَعْلَمُونَ شَيْئًا وَجَعَلَ لَكُمُ السَّمْعَ وَالْأَبْصَارَ وَالْأَفْئِدَةَ ۙ لَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (78)
Ndipo Mulungu adakutulutsani kuchokera m’mimba mwa amayi anu muli osadziwa china chilichonse ndipo adakupatsani makutu, maso, ndi mitima kuti muzithokoza
أَلَمْ يَرَوْا إِلَى الطَّيْرِ مُسَخَّرَاتٍ فِي جَوِّ السَّمَاءِ مَا يُمْسِكُهُنَّ إِلَّا اللَّهُ ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (79)
Kodi iwo saona mbalame zomwe zimauluka mlengalenga? Palibe wina amene amazigwira kuti zisagwe pansi koma Mulungu yekha. Ndithudi mu ichi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira
وَاللَّهُ جَعَلَ لَكُم مِّن بُيُوتِكُمْ سَكَنًا وَجَعَلَ لَكُم مِّن جُلُودِ الْأَنْعَامِ بُيُوتًا تَسْتَخِفُّونَهَا يَوْمَ ظَعْنِكُمْ وَيَوْمَ إِقَامَتِكُمْ ۙ وَمِنْ أَصْوَافِهَا وَأَوْبَارِهَا وَأَشْعَارِهَا أَثَاثًا وَمَتَاعًا إِلَىٰ حِينٍ (80)
Ndipo Mulungu wakupangirani nyumba zanu kuti muzikhalamo ndipo wakupangirani nyumba kuchokera kuzikopa za nyama, zomwe mumaona kuti zimakupepukirani ponyamula ndikumakhala pamodzi ndi ubweya umene mumakonzera zinthu zina zofunika
وَاللَّهُ جَعَلَ لَكُم مِّمَّا خَلَقَ ظِلَالًا وَجَعَلَ لَكُم مِّنَ الْجِبَالِ أَكْنَانًا وَجَعَلَ لَكُمْ سَرَابِيلَ تَقِيكُمُ الْحَرَّ وَسَرَابِيلَ تَقِيكُم بَأْسَكُمْ ۚ كَذَٰلِكَ يُتِمُّ نِعْمَتَهُ عَلَيْكُمْ لَعَلَّكُمْ تُسْلِمُونَ (81)
Ndipo Mulungu wakupangirani kuchokera ku zinthu zimene adalenga mthunzi ndipo wakupangirani malo othawirako m’mapiri ndipo Iye wakupangiraninso zovala kuti zizikutetezani kukatentha ndi zovala zokutetezani ngati chishango nthawi ya nkhondo. Mmenemo ndimo mmene amakwaniritsira ubwino wake pa inu kuti mukhale odzipereka mwahifuniro chake
فَإِن تَوَلَّوْا فَإِنَّمَا عَلَيْكَ الْبَلَاغُ الْمُبِينُ (82)
Koma ngati iwo samvera, udindo wako ndi kufikitsa uthenga moonekera
يَعْرِفُونَ نِعْمَتَ اللَّهِ ثُمَّ يُنكِرُونَهَا وَأَكْثَرُهُمُ الْكَافِرُونَ (83)
Iwo amazindikira ubwino wa Mulungu komabe amaukana ndipo ambiri a iwo ndi anthu osakhulupirira
وَيَوْمَ نَبْعَثُ مِن كُلِّ أُمَّةٍ شَهِيدًا ثُمَّ لَا يُؤْذَنُ لِلَّذِينَ كَفَرُوا وَلَا هُمْ يُسْتَعْتَبُونَ (84)
Ndipo patsiku limene Ife tidzadzutsa mboni kuchokerakumtunduuliwonse, iwoamenesanakhulupirire sadzapatsidwa mwayi
وَإِذَا رَأَى الَّذِينَ ظَلَمُوا الْعَذَابَ فَلَا يُخَفَّفُ عَنْهُمْ وَلَا هُمْ يُنظَرُونَ (85)
Ndipo pamene ochita zoipa adzaona chilango, mavuto awo sadzachepetsedwa ndipo sadzapatsidwa mpumulo
وَإِذَا رَأَى الَّذِينَ أَشْرَكُوا شُرَكَاءَهُمْ قَالُوا رَبَّنَا هَٰؤُلَاءِ شُرَكَاؤُنَا الَّذِينَ كُنَّا نَدْعُو مِن دُونِكَ ۖ فَأَلْقَوْا إِلَيْهِمُ الْقَوْلَ إِنَّكُمْ لَكَاذِبُونَ (86)
Ndipo anthu opembedza mafano akadzaona mafano awo, iwo adzati, “Oh Ambuye wathu! Awa ndi mafano athu amene tinali kupembedza kuonjezera pa inu.” Koma mafano awo adzayankha opembedzawo nati, “Ndithudi! Inu ndinu abodza.”
وَأَلْقَوْا إِلَى اللَّهِ يَوْمَئِذٍ السَّلَمَ ۖ وَضَلَّ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَفْتَرُونَ (87)
Patsiku limeneli, iwo adzaonetsera poyera kugonja kwawo kwa Mulungu ndipo mafano awo onse adzawathawira iwo
الَّذِينَ كَفَرُوا وَصَدُّوا عَن سَبِيلِ اللَّهِ زِدْنَاهُمْ عَذَابًا فَوْقَ الْعَذَابِ بِمَا كَانُوا يُفْسِدُونَ (88)
Kwa iwo amene sadakhulupirire ndipo adatsekereza anzawo kutsatira njira ya Mulungu, Ife tidzawaonjezera chilango kuonjezera pa chilango china, chifukwa cha ntchito zawo zoipa zimene anali kufalitsa
وَيَوْمَ نَبْعَثُ فِي كُلِّ أُمَّةٍ شَهِيدًا عَلَيْهِم مِّنْ أَنفُسِهِمْ ۖ وَجِئْنَا بِكَ شَهِيدًا عَلَىٰ هَٰؤُلَاءِ ۚ وَنَزَّلْنَا عَلَيْكَ الْكِتَابَ تِبْيَانًا لِّكُلِّ شَيْءٍ وَهُدًى وَرَحْمَةً وَبُشْرَىٰ لِلْمُسْلِمِينَ (89)
Ndipo patsikulo tidzadzutsa kuchokera ku mtundu uliwonse amene adzawachitira umboni wochokera pakati pawo. Ndipo tidzakubweretsa iwe kukhala mboni ya anthu awa. Ndipo takuvumbulutsira Buku lolongosola zonse, chilangizo, madalitso ndi nkhani yabwino kwa omwe amagonjera Mulungu
۞ إِنَّ اللَّهَ يَأْمُرُ بِالْعَدْلِ وَالْإِحْسَانِ وَإِيتَاءِ ذِي الْقُرْبَىٰ وَيَنْهَىٰ عَنِ الْفَحْشَاءِ وَالْمُنكَرِ وَالْبَغْيِ ۚ يَعِظُكُمْ لَعَلَّكُمْ تَذَكَّرُونَ (90)
Ndithudi Mulungu amalamulira chilungamo, kupirira pogwira ntchito ya Mulungu, ubwino ndi kupereka chaulere kwa abale. Ndipo amaletsa ntchito zoipa, zonyansa ndi kuponderezana. Iye ali kukuchenjezani kuti mukhale okumbukira
وَأَوْفُوا بِعَهْدِ اللَّهِ إِذَا عَاهَدتُّمْ وَلَا تَنقُضُوا الْأَيْمَانَ بَعْدَ تَوْكِيدِهَا وَقَدْ جَعَلْتُمُ اللَّهَ عَلَيْكُمْ كَفِيلًا ۚ إِنَّ اللَّهَ يَعْلَمُ مَا تَفْعَلُونَ (91)
Kwaniritsani pangano la Mulungu mukalonjeza ndipo musaphwanye malonjezo anu mutatsimikiza. Ndithudi inu mwamupanga Mulungu kukhala mboni yanu yodalirika. Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
وَلَا تَكُونُوا كَالَّتِي نَقَضَتْ غَزْلَهَا مِن بَعْدِ قُوَّةٍ أَنكَاثًا تَتَّخِذُونَ أَيْمَانَكُمْ دَخَلًا بَيْنَكُمْ أَن تَكُونَ أُمَّةٌ هِيَ أَرْبَىٰ مِنْ أُمَّةٍ ۚ إِنَّمَا يَبْلُوكُمُ اللَّهُ بِهِ ۚ وَلَيُبَيِّنَنَّ لَكُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ مَا كُنتُمْ فِيهِ تَخْتَلِفُونَ (92)
Musakhale ngati mkazi amene wadula ulusi wa nsalu imene amasoka italimba polumbira mwachinyengo pakati panu kuti mwina gulu lina lingakhale lopambana kuposa gulu linzake. Ndithudi mu ichi Mulungu amakuyesani. Ndipo patsiku la kuuka kwa akufa, Iye adzakuululirani zoona zokhazokha za izo zimene munali kusemphana maganizo
وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ لَجَعَلَكُمْ أُمَّةً وَاحِدَةً وَلَٰكِن يُضِلُّ مَن يَشَاءُ وَيَهْدِي مَن يَشَاءُ ۚ وَلَتُسْأَلُنَّ عَمَّا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (93)
Ndipo Mulungu akadafuna, akadakupangani inu kuti mukhale mtundu umodzi. Koma Iye amasocheretsa amene Iye wamufuna ndipo amamutsogolera Iye amene wamufuna. Ndithudi inu mudzafunsidwa za ntchito zanu zonse zimene munali kuchita
وَلَا تَتَّخِذُوا أَيْمَانَكُمْ دَخَلًا بَيْنَكُمْ فَتَزِلَّ قَدَمٌ بَعْدَ ثُبُوتِهَا وَتَذُوقُوا السُّوءَ بِمَا صَدَدتُّمْ عَن سَبِيلِ اللَّهِ ۖ وَلَكُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌ (94)
Musasandutse kulumbira kwanu kukhala chinyengo pakatipanuchifukwamwinaphazilingatererelitakhazikika ndipo inu mungalawe zoipa chifukwa chakutsekereza njira ya Mulungu ndipo chanu chidzakhala chilango chachikulu
وَلَا تَشْتَرُوا بِعَهْدِ اللَّهِ ثَمَنًا قَلِيلًا ۚ إِنَّمَا عِندَ اللَّهِ هُوَ خَيْرٌ لَّكُمْ إِن كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (95)
Musagulitse lonjezo la Mulungu ndi mtengo wochepa. Ndithudi zinthu zimene zili kwa Mulungu ndi zabwino inu mukadadziwa
مَا عِندَكُمْ يَنفَدُ ۖ وَمَا عِندَ اللَّهِ بَاقٍ ۗ وَلَنَجْزِيَنَّ الَّذِينَ صَبَرُوا أَجْرَهُم بِأَحْسَنِ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (96)
Zinthuzimenezilindiinundizakuthakomazimenezili kwa Mulungu ndi zosatha. Ndithudi Ife tidzalipira anthu omwe amapirira malipiro abwino kwambiri molingana ndi zimene anali kuchita
مَنْ عَمِلَ صَالِحًا مِّن ذَكَرٍ أَوْ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَلَنُحْيِيَنَّهُ حَيَاةً طَيِّبَةً ۖ وَلَنَجْزِيَنَّهُمْ أَجْرَهُم بِأَحْسَنِ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (97)
Aliyense amene achita zabwino, mwamuna kapena mkazi, ndipo ali okhulupirira, ndithudi, tidzampatsa moyo wabwino ndipo tidzawalipira malipiro abwino kwambiri molingana ndi zimene ankachita
فَإِذَا قَرَأْتَ الْقُرْآنَ فَاسْتَعِذْ بِاللَّهِ مِنَ الشَّيْطَانِ الرَّجِيمِ (98)
Motero ukafuna kuwerenga Korani, pempha chitetezo cha Mulungu kuti akuteteze kwa Satana wotembereredwa
إِنَّهُ لَيْسَ لَهُ سُلْطَانٌ عَلَى الَّذِينَ آمَنُوا وَعَلَىٰ رَبِّهِمْ يَتَوَكَّلُونَ (99)
Ndithudi! Satana alibe mphamvu pa anthu okhulupirira amene amaika chikhulupiliro chawo mwa Ambuye wawo
إِنَّمَا سُلْطَانُهُ عَلَى الَّذِينَ يَتَوَلَّوْنَهُ وَالَّذِينَ هُم بِهِ مُشْرِكُونَ (100)
Mphamvu zake zili pa okhawo amene amapalana naye ubwenzi, ndiponso iwo amene amapembedza milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni
وَإِذَا بَدَّلْنَا آيَةً مَّكَانَ آيَةٍ ۙ وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا يُنَزِّلُ قَالُوا إِنَّمَا أَنتَ مُفْتَرٍ ۚ بَلْ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (101)
Ndipo pamene Ife tisintha Vesi m’malo mwa linzake, Mulungu yekha amadziwa kwambiri zimene akuvumbulutsa. Iwo amati, “Iwe ndiwe wabodza.” Iyayi koma ambiri mwa iwo sadziwa
قُلْ نَزَّلَهُ رُوحُ الْقُدُسِ مِن رَّبِّكَ بِالْحَقِّ لِيُثَبِّتَ الَّذِينَ آمَنُوا وَهُدًى وَبُشْرَىٰ لِلْمُسْلِمِينَ (102)
Nena, “Ndi Mzimu Woyera umene wabweretsa chivumbulutso kuchokera kwa Ambuye wako mwachoonadi, ndi cholinga choti chiwalimbikitse anthu amene amakhulupirira, ndi malangizo ndiponso nkhani yabwino kwa Asilamu.”
وَلَقَدْ نَعْلَمُ أَنَّهُمْ يَقُولُونَ إِنَّمَا يُعَلِّمُهُ بَشَرٌ ۗ لِّسَانُ الَّذِي يُلْحِدُونَ إِلَيْهِ أَعْجَمِيٌّ وَهَٰذَا لِسَانٌ عَرَبِيٌّ مُّبِينٌ (103)
Ndithudi Ife tikudziwa kuti iwo amanena kuti, “Ndi munthu amene akumuphunzitsa iye.” Koma munthu amene amamuganizira, kuti ndiye amene anamuphunzitsa amayankhula chiyankhulo cha chilendo pamene Korani iyi ndi chiyankhulo cha Chiarabu chomveka
إِنَّ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِآيَاتِ اللَّهِ لَا يَهْدِيهِمُ اللَّهُ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (104)
Ndithudi! Iwo amene sakhulupirira mawu a Mulungu, Mulungu sadzawatsogolera ndipo iwo adzapeza chilango chowawa
إِنَّمَا يَفْتَرِي الْكَذِبَ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِآيَاتِ اللَّهِ ۖ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْكَاذِبُونَ (105)
Ndithudi ndi okhawo amene sakukhulupirira mavesi a Mulungu amene amapeka bodza ndipo iwo ndi abodza
مَن كَفَرَ بِاللَّهِ مِن بَعْدِ إِيمَانِهِ إِلَّا مَنْ أُكْرِهَ وَقَلْبُهُ مُطْمَئِنٌّ بِالْإِيمَانِ وَلَٰكِن مَّن شَرَحَ بِالْكُفْرِ صَدْرًا فَعَلَيْهِمْ غَضَبٌ مِّنَ اللَّهِ وَلَهُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌ (106)
Aliyense amene sakhulupirira Mulungu pambuyo pokhulupirira kupatula amene wakakamizidwa koma mtima wake uli wokhazikika ndi chikhulupiriro, koma iwo amene ayamba kusakhulupirira mu mtima mwawo, mkwiyo wochokera kwa Mulungu udzadza pa iwo ndipo adzapeza chilango chachikulu
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمُ اسْتَحَبُّوا الْحَيَاةَ الدُّنْيَا عَلَى الْآخِرَةِ وَأَنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الْكَافِرِينَ (107)
Ichi ndi chifukwa chakuti anthu otero adakonda moyo wa padziko lapansi kwambiri kuposa moyo umene uli nkudza. Ndipo Mulungu satsogolera anthu osakhulupirira
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ طَبَعَ اللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمْ وَسَمْعِهِمْ وَأَبْصَارِهِمْ ۖ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْغَافِلُونَ (108)
Amenewa ndiwo amene mitima yawo, makutu awo ndi maso awo atsekedwa ndi Mulungu ndipo ndi osamva ayi
لَا جَرَمَ أَنَّهُمْ فِي الْآخِرَةِ هُمُ الْخَاسِرُونَ (109)
Palibe chikayiko kuti iwo, m’moyo umene uli nkudza, sadzapeza chilichonse ndipo adzakhala olephera
ثُمَّ إِنَّ رَبَّكَ لِلَّذِينَ هَاجَرُوا مِن بَعْدِ مَا فُتِنُوا ثُمَّ جَاهَدُوا وَصَبَرُوا إِنَّ رَبَّكَ مِن بَعْدِهَا لَغَفُورٌ رَّحِيمٌ (110)
Ndipo, ndithudi, Ambuye wako, kwa iwo amene adasamuka kwawo pambuyo povutitsidwa ndipo apitirira kumenya nkhondo ndi kupirira, ndithudi, Ambuye wako, pambuyo pa zimenezo ndi Wokhululukira kwambiri ndiponso wachisoni
۞ يَوْمَ تَأْتِي كُلُّ نَفْسٍ تُجَادِلُ عَن نَّفْسِهَا وَتُوَفَّىٰ كُلُّ نَفْسٍ مَّا عَمِلَتْ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (111)
Pa tsiku limene munthu aliyense adzadza kudzadzidandaulira yekha, ndipo aliyense adzalandira dipo lolingana ndi ntchito zake ndipo iwo sadzaponderezedwa ayi
وَضَرَبَ اللَّهُ مَثَلًا قَرْيَةً كَانَتْ آمِنَةً مُّطْمَئِنَّةً يَأْتِيهَا رِزْقُهَا رَغَدًا مِّن كُلِّ مَكَانٍ فَكَفَرَتْ بِأَنْعُمِ اللَّهِ فَأَذَاقَهَا اللَّهُ لِبَاسَ الْجُوعِ وَالْخَوْفِ بِمَا كَانُوا يَصْنَعُونَ (112)
Ndipo Mulungu wapereka chitsanzo cha Mzinda umene udali wabata ndi wamtendere, chakudya chake chidali chambiri chimene chimachokera kumbali zosiyanasiyana koma anthu ake adakana zokoma za Mulungu. Kotero Mulungu adaulawitsa Mzindawo vuto la njala ndi mantha chifukwa cha zimene iwo amachita
وَلَقَدْ جَاءَهُمْ رَسُولٌ مِّنْهُمْ فَكَذَّبُوهُ فَأَخَذَهُمُ الْعَذَابُ وَهُمْ ظَالِمُونَ (113)
Ndithudi! Kudadza kwa iwo Mtumwi wa mtundu wawo koma iwo adamukana. Choncho chilango chathu chidawapeza iwo ali kuchita zoipa
فَكُلُوا مِمَّا رَزَقَكُمُ اللَّهُ حَلَالًا طَيِّبًا وَاشْكُرُوا نِعْمَتَ اللَّهِ إِن كُنتُمْ إِيَّاهُ تَعْبُدُونَ (114)
Motero idyani zinthu zabwino ndi zololedwa zimene Mulungu wakupatsani inu. Ndipo thokozani chisomo cha Mulungu ngati ndiye yekha amene mumapembedza
إِنَّمَا حَرَّمَ عَلَيْكُمُ الْمَيْتَةَ وَالدَّمَ وَلَحْمَ الْخِنزِيرِ وَمَا أُهِلَّ لِغَيْرِ اللَّهِ بِهِ ۖ فَمَنِ اضْطُرَّ غَيْرَ بَاغٍ وَلَا عَادٍ فَإِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (115)
Iye wakuletsani kudya zinthu zofa zokha, liwende, nyama ya nkhumba, ndiponso nyama iliyonse imene yaphedwa m’dzina la mulungu wina wosati Mulungu mmodzi yekha. Koma ngati wina akakamizidwa kudya zina za izi, osati mofuna yekha kapena mofuna kuphwanya malamulo, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira ndi wachifundo chosatha
وَلَا تَقُولُوا لِمَا تَصِفُ أَلْسِنَتُكُمُ الْكَذِبَ هَٰذَا حَلَالٌ وَهَٰذَا حَرَامٌ لِّتَفْتَرُوا عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ ۚ إِنَّ الَّذِينَ يَفْتَرُونَ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ لَا يُفْلِحُونَ (116)
Ndipo musanene bodza ndi malirime anu ponena kuti, “Ichi ndi chololedwa kapena ichi ndi choletsedwa” ndi cholinga chomupekera Mulungu bodza. Ndithudi amene akupekera Mulungu bodza sadzapambana
مَتَاعٌ قَلِيلٌ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (117)
Chisangalalo cha kanthawi kochepa kwambiri koma iwo adzapeza chilango chowawa
وَعَلَى الَّذِينَ هَادُوا حَرَّمْنَا مَا قَصَصْنَا عَلَيْكَ مِن قَبْلُ ۖ وَمَا ظَلَمْنَاهُمْ وَلَٰكِن كَانُوا أَنفُسَهُمْ يَظْلِمُونَ (118)
Ife tidawaletsa Ayuda kudya zakudya zimene takufotokozera kale. Ife sitidawapondereze ayi koma iwo adadzipondereza okha
ثُمَّ إِنَّ رَبَّكَ لِلَّذِينَ عَمِلُوا السُّوءَ بِجَهَالَةٍ ثُمَّ تَابُوا مِن بَعْدِ ذَٰلِكَ وَأَصْلَحُوا إِنَّ رَبَّكَ مِن بَعْدِهَا لَغَفُورٌ رَّحِيمٌ (119)
Ndipo, ndithudi! Ambuye wako, kwa anthu amene amachita zoipa mosazindikira ndi kulapa pambuyo pake ndikuchita zabwino, ndithudi, Ambuye wako pambuyo pa zimenezo ndi wokhululukira ndi wachisoni
إِنَّ إِبْرَاهِيمَ كَانَ أُمَّةً قَانِتًا لِّلَّهِ حَنِيفًا وَلَمْ يَكُ مِنَ الْمُشْرِكِينَ (120)
Ndithudi! Abrahamu adali chitsanzo cha makhalidwe abwino, wokhulupirika kwa Mulungu ndiponso wangwiro. Iye sadali mmodzi wa anthu opembedza mafano
شَاكِرًا لِّأَنْعُمِهِ ۚ اجْتَبَاهُ وَهَدَاهُ إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (121)
Iye adali wothokoza chisomo cha Mulungu ndipo Iye adamusankha iye ndi kum’tsogolera ku njira yoyenera
وَآتَيْنَاهُ فِي الدُّنْيَا حَسَنَةً ۖ وَإِنَّهُ فِي الْآخِرَةِ لَمِنَ الصَّالِحِينَ (122)
Ndipo Ife tidamupatsa zabwino m’moyo uno ndipo iye, m’moyo umene uli nkudza, adzakhala pakati pa anthu olungama
ثُمَّ أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ أَنِ اتَّبِعْ مِلَّةَ إِبْرَاهِيمَ حَنِيفًا ۖ وَمَا كَانَ مِنَ الْمُشْرِكِينَ (123)
Motero Ife tavumbulutsa kwa iwe kuti, “Tsatira chipembedzo cha Abrahamu amene sanali mmodzi wopembedza mafano.”
إِنَّمَا جُعِلَ السَّبْتُ عَلَى الَّذِينَ اخْتَلَفُوا فِيهِ ۚ وَإِنَّ رَبَّكَ لَيَحْكُمُ بَيْنَهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ فِيمَا كَانُوا فِيهِ يَخْتَلِفُونَ (124)
Tsiku la sabata lidakhazikitsidwira anthu amene adali kutsutsana pa za tsikuli ndipo ndithudi Ambuye wako adzaweruza zonse zimene anali kukangana pa tsiku lachiweruzo
ادْعُ إِلَىٰ سَبِيلِ رَبِّكَ بِالْحِكْمَةِ وَالْمَوْعِظَةِ الْحَسَنَةِ ۖ وَجَادِلْهُم بِالَّتِي هِيَ أَحْسَنُ ۚ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعْلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِ ۖ وَهُوَ أَعْلَمُ بِالْمُهْتَدِينَ (125)
Itanira anthu ku njira ya Ambuye wako mwanzeru ndi ulaliki wabwino. Tsutsana nawo m’njira yabwino. Ndithudi Ambuye wako amadziwa bwinobwino onse amene amasochera ku njira yake, ndiponso Iye amawadziwa bwino bwino iwo amene atsogozedwa
وَإِنْ عَاقَبْتُمْ فَعَاقِبُوا بِمِثْلِ مَا عُوقِبْتُم بِهِ ۖ وَلَئِن صَبَرْتُمْ لَهُوَ خَيْرٌ لِّلصَّابِرِينَ (126)
Ngati inu muli kulanga, langani monga momwe inu mwalangidwira. Koma ngati mutapirira, zimenezo ndi zabwino kwa anthu opirira
وَاصْبِرْ وَمَا صَبْرُكَ إِلَّا بِاللَّهِ ۚ وَلَا تَحْزَنْ عَلَيْهِمْ وَلَا تَكُ فِي ضَيْقٍ مِّمَّا يَمْكُرُونَ (127)
Khala opirira ndipo kupirira kwako ndi chifukwa cha Mulungu ndipo usadandaule za iwo ndiponso usakhale obanika chifukwa cha chiwembu chawo
إِنَّ اللَّهَ مَعَ الَّذِينَ اتَّقَوا وَّالَّذِينَ هُم مُّحْسِنُونَ (128)
Ndithudi Mulungu ali ndi iwo amene amamuopa Iye ndipo amachita ntchito zabwino
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas