×

Surah Al-Isra in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Al Isra

Translation of the Meanings of Surah Al Isra in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Al Isra translated into Chichewa, Surah Al-Isra in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Al Isra in Chichewa - نيانجا, Verses 111 - Surah Number 17 - Page 282.

بسم الله الرحمن الرحيم

سُبْحَانَ الَّذِي أَسْرَىٰ بِعَبْدِهِ لَيْلًا مِّنَ الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ إِلَى الْمَسْجِدِ الْأَقْصَى الَّذِي بَارَكْنَا حَوْلَهُ لِنُرِيَهُ مِنْ آيَاتِنَا ۚ إِنَّهُ هُوَ السَّمِيعُ الْبَصِيرُ (1)
Ulemerero ukhale kwa Iye amene adayendetsa kapolo wake nthawi ya usiku kuchoka ku Mzikiti Wolemekezeka kupita ku Mzikiti wakutali umene malo ake ozungulira tidawadalitsa; kuti timuonetse zina za zizindikiro zathu. Ndithudi Iye ndiwakumva ndipo woona zonse
وَآتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ وَجَعَلْنَاهُ هُدًى لِّبَنِي إِسْرَائِيلَ أَلَّا تَتَّخِذُوا مِن دُونِي وَكِيلًا (2)
Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku ndipo tidalipanga ilo kukhala chilangizo cha ana a Israyeli ponena kuti, “Musasankhe wina aliyense kupatula Ine kukhala wokutetezani.”
ذُرِّيَّةَ مَنْ حَمَلْنَا مَعَ نُوحٍ ۚ إِنَّهُ كَانَ عَبْدًا شَكُورًا (3)
oh inu ana a iwo amene tidawanyamula pamodzi ndi Nowa! Ndithudi Iye adali kapolo wothokoza kwambiri
وَقَضَيْنَا إِلَىٰ بَنِي إِسْرَائِيلَ فِي الْكِتَابِ لَتُفْسِدُنَّ فِي الْأَرْضِ مَرَّتَيْنِ وَلَتَعْلُنَّ عُلُوًّا كَبِيرًا (4)
Ife tidavumbulutsa kwa ana a Israyeli, m’Buku kuti, mosakayika, inu mudzabweretsa chisokonezo padziko kachiwiri ndipo mudzakhala ankhanza ndi odzikweza kwambiri
فَإِذَا جَاءَ وَعْدُ أُولَاهُمَا بَعَثْنَا عَلَيْكُمْ عِبَادًا لَّنَا أُولِي بَأْسٍ شَدِيدٍ فَجَاسُوا خِلَالَ الدِّيَارِ ۚ وَكَانَ وَعْدًا مَّفْعُولًا (5)
Ndipo litadza pangano loyamba, Ife tidzakutumizirani akapolo athu a gulu la nkhondo ankhongono zedi. Iwo amalowa m’katikati mwa nyumba zanu. Ndipo linali lonjezo limene linakwaniritsidwa
ثُمَّ رَدَدْنَا لَكُمُ الْكَرَّةَ عَلَيْهِمْ وَأَمْدَدْنَاكُم بِأَمْوَالٍ وَبَنِينَ وَجَعَلْنَاكُمْ أَكْثَرَ نَفِيرًا (6)
Titatero tidakupatsani mphamvu powagonjetsa iwo. Ndipo tidakuonjezerani chuma ndi ana ndipo tidakupangani kukhala anthu ambiri amphamvu
إِنْ أَحْسَنتُمْ أَحْسَنتُمْ لِأَنفُسِكُمْ ۖ وَإِنْ أَسَأْتُمْ فَلَهَا ۚ فَإِذَا جَاءَ وَعْدُ الْآخِرَةِ لِيَسُوءُوا وُجُوهَكُمْ وَلِيَدْخُلُوا الْمَسْجِدَ كَمَا دَخَلُوهُ أَوَّلَ مَرَّةٍ وَلِيُتَبِّرُوا مَا عَلَوْا تَتْبِيرًا (7)
Ngati inu muchita zabwino, mukudzichitira nokha ubwinowo, koma ngati muchita zoipa, mukudzichitiranso nokha. Ndipo pamene pangano lomaliza lidza, Ife tidzalola adani anu kuti akumvetseni chisoni ndi kulowa mu Mzikiti wanu monga momwe adaloweramo koyamba ndi kukantha kwenikweni onse amene adawapeza
عَسَىٰ رَبُّكُمْ أَن يَرْحَمَكُمْ ۚ وَإِنْ عُدتُّمْ عُدْنَا ۘ وَجَعَلْنَا جَهَنَّمَ لِلْكَافِرِينَ حَصِيرًا (8)
Mwina Ambuye wanu adzakuchitirani chifundo koma ngati inu mubwerera kuuchimo, nafenso tidzabwezera kukanthani. Ife takonza Gahena kukhala ndende ya anthu osakhulupirira
إِنَّ هَٰذَا الْقُرْآنَ يَهْدِي لِلَّتِي هِيَ أَقْوَمُ وَيُبَشِّرُ الْمُؤْمِنِينَ الَّذِينَ يَعْمَلُونَ الصَّالِحَاتِ أَنَّ لَهُمْ أَجْرًا كَبِيرًا (9)
Ndithudi Korani ino imatsogolera ku zinthu zabwino ndipo imawauza anthu okhulupirira, amene amachita zabwino, kuti adzakhala ndi malipiro aakulu
وَأَنَّ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ أَعْتَدْنَا لَهُمْ عَذَابًا أَلِيمًا (10)
Ndipo iwo amene sakhulupirira za tsiku lotsiriza Ife tawakonzera chilango chowawa
وَيَدْعُ الْإِنسَانُ بِالشَّرِّ دُعَاءَهُ بِالْخَيْرِ ۖ وَكَانَ الْإِنسَانُ عَجُولًا (11)
Ndipo munthu amapempha zoipa monga momwe amapemphera zabwino ndipo munthu ndi wopupuluma
وَجَعَلْنَا اللَّيْلَ وَالنَّهَارَ آيَتَيْنِ ۖ فَمَحَوْنَا آيَةَ اللَّيْلِ وَجَعَلْنَا آيَةَ النَّهَارِ مُبْصِرَةً لِّتَبْتَغُوا فَضْلًا مِّن رَّبِّكُمْ وَلِتَعْلَمُوا عَدَدَ السِّنِينَ وَالْحِسَابَ ۚ وَكُلَّ شَيْءٍ فَصَّلْنَاهُ تَفْصِيلًا (12)
Ndipo tidapanga usiku ndi usana kukhala zizindikiro zathu ziwiri. Ndipo tidakuta chizindikiro chausiku ndi mdima pamene tidaika chizindikiro chamasana kukhala chooneka kuti inu muzifunafuna zabwino zochokera kwa Ambuye wanu, komanso kuti mudziwe kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero. Ndipo zinthu zonse tazifotokoza momveka
وَكُلَّ إِنسَانٍ أَلْزَمْنَاهُ طَائِرَهُ فِي عُنُقِهِ ۖ وَنُخْرِجُ لَهُ يَوْمَ الْقِيَامَةِ كِتَابًا يَلْقَاهُ مَنشُورًا (13)
Ndipo Ife tidamangirira ntchito za munthu aliyense pakhosi lake ndipo patsiku lachiweruzo tidzamutulutsira buku limene adzalipeze lili lotsekulidwa
اقْرَأْ كِتَابَكَ كَفَىٰ بِنَفْسِكَ الْيَوْمَ عَلَيْكَ حَسِيبًا (14)
werenga Buku lako. Lero pakwana kuti mzimu wako udziwerengere wokha zonse zimene unkachita
مَّنِ اهْتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهْتَدِي لِنَفْسِهِ ۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيْهَا ۚ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزْرَ أُخْرَىٰ ۗ وَمَا كُنَّا مُعَذِّبِينَ حَتَّىٰ نَبْعَثَ رَسُولًا (15)
Aliyense amene achita zabwino atero podzipulumutsa yekha. Ndipo aliyense amene achita zoipa, atero podzipweteka yekha. Palibe amene adzanyamula katundu wa mnzake. Ndipo Ife sitilanga pokhapokha ngati tatumiza Mtumwi
وَإِذَا أَرَدْنَا أَن نُّهْلِكَ قَرْيَةً أَمَرْنَا مُتْرَفِيهَا فَفَسَقُوا فِيهَا فَحَقَّ عَلَيْهَا الْقَوْلُ فَدَمَّرْنَاهَا تَدْمِيرًا (16)
Ndipo pamene Ife tifuna kuononga Mzinda, poyamba timatumiza ulamuliro wathu kwa anthu ake opeza bwino. Ndipo iwo amauphwanya, ndipo motero liwu la chilango limatsimikiza pa iwo. Ndipo Ife timauononga kwambiri
وَكَمْ أَهْلَكْنَا مِنَ الْقُرُونِ مِن بَعْدِ نُوحٍ ۗ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ بِذُنُوبِ عِبَادِهِ خَبِيرًا بَصِيرًا (17)
Kodi ndi mibadwo ingati ya anthu imene taononga pambuyo pa Nowa? Ambuye wako wakwana kukhala Wozindikira ndi woona zolakwa za akapolo ake
مَّن كَانَ يُرِيدُ الْعَاجِلَةَ عَجَّلْنَا لَهُ فِيهَا مَا نَشَاءُ لِمَن نُّرِيدُ ثُمَّ جَعَلْنَا لَهُ جَهَنَّمَ يَصْلَاهَا مَذْمُومًا مَّدْحُورًا (18)
Aliyense amene afuna chisangalalo cha msanga Ife timapereka msanga chimene Ife tifuna kwa amene Ife tamufuna. Ndipo pambuyo pake tamukonzera iye Gahena, imene adzalowa monyozedwa ndi mokankhidwa
وَمَنْ أَرَادَ الْآخِرَةَ وَسَعَىٰ لَهَا سَعْيَهَا وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَأُولَٰئِكَ كَانَ سَعْيُهُم مَّشْكُورًا (19)
Ndipo yense amene afuna moyo umene uli nkudza, ndi kumaugwirira ntchito zake molimbika, ndipo ndi wokhulupirira, amenewo ndi amene ntchito zawo zidzakhala zoyamikidwa
كُلًّا نُّمِدُّ هَٰؤُلَاءِ وَهَٰؤُلَاءِ مِنْ عَطَاءِ رَبِّكَ ۚ وَمَا كَانَ عَطَاءُ رَبِّكَ مَحْظُورًا (20)
Ife timapereka kuchokera ku mphatso za Ambuye wako. Ndipo mphatso za Ambuye wako sizokanizidwa kwa aliyense
انظُرْ كَيْفَ فَضَّلْنَا بَعْضَهُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ ۚ وَلَلْآخِرَةُ أَكْبَرُ دَرَجَاتٍ وَأَكْبَرُ تَفْضِيلًا (21)
Taona mmene tawalemekezera ena kuposa anzawo ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza uli ndi ulemu wambiri ndipo ndi waukulu poyerekeza
لَّا تَجْعَلْ مَعَ اللَّهِ إِلَٰهًا آخَرَ فَتَقْعُدَ مَذْمُومًا مَّخْذُولًا (22)
Musasankhe mulungu wina ndi kumuphatikiza ndi Mulungu weniweni chifukwa mungadzakhale ndi manyazi ndi wopanda wokuthandizani
۞ وَقَضَىٰ رَبُّكَ أَلَّا تَعْبُدُوا إِلَّا إِيَّاهُ وَبِالْوَالِدَيْنِ إِحْسَانًا ۚ إِمَّا يَبْلُغَنَّ عِندَكَ الْكِبَرَ أَحَدُهُمَا أَوْ كِلَاهُمَا فَلَا تَقُل لَّهُمَا أُفٍّ وَلَا تَنْهَرْهُمَا وَقُل لَّهُمَا قَوْلًا كَرِيمًا (23)
Ndipo Ambuye wako walamula kuti musapembedze wina aliyense koma Iye yekha. Ndipo kuti muwachitire makolo anu zabwino. Ngati wina wa iwo kapena onse akalamba ali kukhala nanu, musawakalipire ayi, koma muziwayankhula ndi mawu aulemu
وَاخْفِضْ لَهُمَا جَنَاحَ الذُّلِّ مِنَ الرَّحْمَةِ وَقُل رَّبِّ ارْحَمْهُمَا كَمَا رَبَّيَانِي صَغِيرًا (24)
Onetsani kudzichepetsa ndi chisoni ndipo munene kuti, “Ambuye wanga! Achitireni chifundo monga momwe iwo adandilerera pamene ine ndidali wamng’ono.”
رَّبُّكُمْ أَعْلَمُ بِمَا فِي نُفُوسِكُمْ ۚ إِن تَكُونُوا صَالِحِينَ فَإِنَّهُ كَانَ لِلْأَوَّابِينَ غَفُورًا (25)
Ambuye wanu amadziwa kwambiri zonse zimene zili m’mitima mwanu. Ngati muli abwino ndithudi Iye ali wokhululukira kwa anthu amene amadza kwa Iye nthawi zonse modzichepetsa ndi kulapa
وَآتِ ذَا الْقُرْبَىٰ حَقَّهُ وَالْمِسْكِينَ وَابْنَ السَّبِيلِ وَلَا تُبَذِّرْ تَبْذِيرًا (26)
Ndipo apatseni abale anu ndi anthu ovutika gawo lawo lowayenera ndiponso a paulendo amene avutika. Ndipo musapereke chuma chanu moononga
إِنَّ الْمُبَذِّرِينَ كَانُوا إِخْوَانَ الشَّيَاطِينِ ۖ وَكَانَ الشَّيْطَانُ لِرَبِّهِ كَفُورًا (27)
Ndithudi anthu oononga ndi abale a Satana ndipo Satana, kwa Ambuye wake, ndi wosayamika
وَإِمَّا تُعْرِضَنَّ عَنْهُمُ ابْتِغَاءَ رَحْمَةٍ مِّن رَّبِّكَ تَرْجُوهَا فَقُل لَّهُمْ قَوْلًا مَّيْسُورًا (28)
Ndipo ngati iwe siuwathandiza ndipo uli kuyembekezera chisomo chochokera kwa Ambuye wako, yankhula nawo mwachifundo ndi mawu oleza
وَلَا تَجْعَلْ يَدَكَ مَغْلُولَةً إِلَىٰ عُنُقِكَ وَلَا تَبْسُطْهَا كُلَّ الْبَسْطِ فَتَقْعُدَ مَلُومًا مَّحْسُورًا (29)
Ndipo musakhale oumira kapena opereka moononga chifukwa mungadzudzulidwe kapena kukhala osauka kwambiri
إِنَّ رَبَّكَ يَبْسُطُ الرِّزْقَ لِمَن يَشَاءُ وَيَقْدِرُ ۚ إِنَّهُ كَانَ بِعِبَادِهِ خَبِيرًا بَصِيرًا (30)
Ndithudi Ambuye wako amapereka zambiri kwa aliyense amene wamufuna ndipo amanyalapsa. Ndithudi Iye, kwa akapolo ake, ndi wodziwa ndi woona
وَلَا تَقْتُلُوا أَوْلَادَكُمْ خَشْيَةَ إِمْلَاقٍ ۖ نَّحْنُ نَرْزُقُهُمْ وَإِيَّاكُمْ ۚ إِنَّ قَتْلَهُمْ كَانَ خِطْئًا كَبِيرًا (31)
Ndipo musawaphe ana anu chifukwa choopa umphawi. Ife timawapatsa zosowa zawo ndi inu nomwe. Ndithudi kuwapha iwo ndi tchimo lalikulu
وَلَا تَقْرَبُوا الزِّنَا ۖ إِنَّهُ كَانَ فَاحِشَةً وَسَاءَ سَبِيلًا (32)
Ndipo musayandikire chigololo. Ndithudi icho ndi chonyansa ndiponso njira yoipa
وَلَا تَقْتُلُوا النَّفْسَ الَّتِي حَرَّمَ اللَّهُ إِلَّا بِالْحَقِّ ۗ وَمَن قُتِلَ مَظْلُومًا فَقَدْ جَعَلْنَا لِوَلِيِّهِ سُلْطَانًا فَلَا يُسْرِف فِّي الْقَتْلِ ۖ إِنَّهُ كَانَ مَنصُورًا (33)
Ndipo musaphe wina aliyense amene Mulungu waletsa pokhapokha ngati pali chifukwa chololedwa. Ndipo aliyense amene waphedwa mopanda chilungamo, Ife tamupatsa m’bale wake mphamvu zobwezera kapena kukhululuka pa imfa yake. Koma m’bale wakeyo asapyole muyeso pa kubwezeraku. Ndithudi iye ndi wotetezedwa
وَلَا تَقْرَبُوا مَالَ الْيَتِيمِ إِلَّا بِالَّتِي هِيَ أَحْسَنُ حَتَّىٰ يَبْلُغَ أَشُدَّهُ ۚ وَأَوْفُوا بِالْعَهْدِ ۖ إِنَّ الْعَهْدَ كَانَ مَسْئُولًا (34)
Ndipo musachiyandikire chuma cha mwana wamasiye kupatula ngati muli ndi cholinga chochisamala mpaka pamene mwini wake adzafike pa msinkhu woti akhoza kuchisamalira yekha. Ndipo kwaniritsani lonjezo lililonse. Ndithudi! mudzafunsidwa za lonjezoli
وَأَوْفُوا الْكَيْلَ إِذَا كِلْتُمْ وَزِنُوا بِالْقِسْطَاسِ الْمُسْتَقِيمِ ۚ ذَٰلِكَ خَيْرٌ وَأَحْسَنُ تَأْوِيلًا (35)
Ndipo kwaniritsani muyeso pamene muyesa zinthu ndipo yesani mwachilungamo polinga zinthu pa sikelo. Zimenezo ndizo zabwino ndipo ndi mapeto abwino kwambiri
وَلَا تَقْفُ مَا لَيْسَ لَكَ بِهِ عِلْمٌ ۚ إِنَّ السَّمْعَ وَالْبَصَرَ وَالْفُؤَادَ كُلُّ أُولَٰئِكَ كَانَ عَنْهُ مَسْئُولًا (36)
Ndipo musatsatire zinthu zimene simuzidziwa. Ndithudi kumvera kapena kuyang’ana kapenanso kuganizira kwa mumtima mwa munthu kudzafufuzidwa pa tsiku lachiweruzo
وَلَا تَمْشِ فِي الْأَرْضِ مَرَحًا ۖ إِنَّكَ لَن تَخْرِقَ الْأَرْضَ وَلَن تَبْلُغَ الْجِبَالَ طُولًا (37)
Ndipo musayende modzitukumula pa dziko lapansi, ndithudi, inu simungathe kuboola nthaka ndi kufika kutalika kwa mapiri
كُلُّ ذَٰلِكَ كَانَ سَيِّئُهُ عِندَ رَبِّكَ مَكْرُوهًا (38)
Kuipa kwa zonsezi sikukondweretsa Ambuye wako
ذَٰلِكَ مِمَّا أَوْحَىٰ إِلَيْكَ رَبُّكَ مِنَ الْحِكْمَةِ ۗ وَلَا تَجْعَلْ مَعَ اللَّهِ إِلَٰهًا آخَرَ فَتُلْقَىٰ فِي جَهَنَّمَ مَلُومًا مَّدْحُورًا (39)
Ili ndi gawo la luntha limene Ambuye wako wakuuza iwe. Ndipo usatumikire mulungu wina kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa mwina iwe ungaponyedwe ku Gahena, modzudzulidwa ndi mokankhidwa
أَفَأَصْفَاكُمْ رَبُّكُم بِالْبَنِينَ وَاتَّخَذَ مِنَ الْمَلَائِكَةِ إِنَاثًا ۚ إِنَّكُمْ لَتَقُولُونَ قَوْلًا عَظِيمًا (40)
Kodi Ambuye wanu wakusankhirani inu ana aamuna ndipo wadzisankhira Iye mwini ana aakazi kuchokera kwa Angelo? Ndithudi! Inu mukuyankhula mawu oopsa
وَلَقَدْ صَرَّفْنَا فِي هَٰذَا الْقُرْآنِ لِيَذَّكَّرُوا وَمَا يَزِيدُهُمْ إِلَّا نُفُورًا (41)
Ndithudi Ife tafotokoza chinthu chilichonse m’Korani iyi kuti iwo achenjezedwe, koma iyo siili kuonjezera chilichonse koma kuipidwa
قُل لَّوْ كَانَ مَعَهُ آلِهَةٌ كَمَا يَقُولُونَ إِذًا لَّابْتَغَوْا إِلَىٰ ذِي الْعَرْشِ سَبِيلًا (42)
Nena, “Kukadakhala kuti kuli milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni, monga momwe akunenera, iyo ikadapeza njira yoti ikhale pafupi ndi Mulungu.”
سُبْحَانَهُ وَتَعَالَىٰ عَمَّا يَقُولُونَ عُلُوًّا كَبِيرًا (43)
Kuyamikidwa ndi kukhala pamwamba, kukhale kwake! Kuchokera ku bodza lalikulu limene iwo ali nkunena
تُسَبِّحُ لَهُ السَّمَاوَاتُ السَّبْعُ وَالْأَرْضُ وَمَن فِيهِنَّ ۚ وَإِن مِّن شَيْءٍ إِلَّا يُسَبِّحُ بِحَمْدِهِ وَلَٰكِن لَّا تَفْقَهُونَ تَسْبِيحَهُمْ ۗ إِنَّهُ كَانَ حَلِيمًا غَفُورًا (44)
Miyamba isanu ndi iwiri, dziko lapansi ndi zonse zimene zimakhala m’menemo zimamulemekeza Iye ndipo palibe chinthu chomwe sichimulemekeza Mulungu. Koma inu simumva mayamiko. Ndithudi Iye ndi woleza mtima ndipo ndi wokhululukira nthawi zonse
وَإِذَا قَرَأْتَ الْقُرْآنَ جَعَلْنَا بَيْنَكَ وَبَيْنَ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ حِجَابًا مَّسْتُورًا (45)
Pamene iwe umawerenga Korani, Ife timaika, pakati pa iwe ndi iwo amene sakhulupirira za moyo umene uli nkudza tchingo losaoneka
وَجَعَلْنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمْ أَكِنَّةً أَن يَفْقَهُوهُ وَفِي آذَانِهِمْ وَقْرًا ۚ وَإِذَا ذَكَرْتَ رَبَّكَ فِي الْقُرْآنِ وَحْدَهُ وَلَّوْا عَلَىٰ أَدْبَارِهِمْ نُفُورًا (46)
Ndipo Ife taika zophimba m’mitima mwawo kuti mwina angaizindikire ndi m’makutu mwawo kuti asaimvetse. Ndipo pamene iwe utchula Ambuye wako yekha mu Korani iwo amatembenuka kuthawa mosangalala
نَّحْنُ أَعْلَمُ بِمَا يَسْتَمِعُونَ بِهِ إِذْ يَسْتَمِعُونَ إِلَيْكَ وَإِذْ هُمْ نَجْوَىٰ إِذْ يَقُولُ الظَّالِمُونَ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا رَجُلًا مَّسْحُورًا (47)
Ife timadziwa kwambiri zimene iwo akumva ndi pamene amamvetsera kwa iwe. Ndipo pamene amanong’onezana, taona anthu oipa, amanena kuti: “Inu mukutsatira munthu wolodzedwa.”
انظُرْ كَيْفَ ضَرَبُوا لَكَ الْأَمْثَالَ فَضَلُّوا فَلَا يَسْتَطِيعُونَ سَبِيلًا (48)
Taona mmene akuperekera zitsanzo zokhudza iwe. Motero iwo asochera ndipo sangathe kupeza njira
وَقَالُوا أَإِذَا كُنَّا عِظَامًا وَرُفَاتًا أَإِنَّا لَمَبْعُوثُونَ خَلْقًا جَدِيدًا (49)
Ndipo iwo amati, “Kodi pamene ife tidzasanduka mafupa ndi zidutswa zopereseka kodi tidzaukitsidwanso kukhala chilengedwe chatsopano?”
۞ قُلْ كُونُوا حِجَارَةً أَوْ حَدِيدًا (50)
Nena, “Khalani miyala kapena zitsulo.”
أَوْ خَلْقًا مِّمَّا يَكْبُرُ فِي صُدُورِكُمْ ۚ فَسَيَقُولُونَ مَن يُعِيدُنَا ۖ قُلِ الَّذِي فَطَرَكُمْ أَوَّلَ مَرَّةٍ ۚ فَسَيُنْغِضُونَ إِلَيْكَ رُءُوسَهُمْ وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هُوَ ۖ قُلْ عَسَىٰ أَن يَكُونَ قَرِيبًا (51)
“Kapena cholengedwa china chimene ndi chachikulu m’mitima mwanu.” Iwo adzati, “Ndani amene adzatibwezeranso?” Nena, “Iye amene adakulengani poyamba.” Ndipo iwo adzapukusa mitu yawo ndipo kwa iwe adzafunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitika liti?” Nena, “Mwina zili pafupi.”
يَوْمَ يَدْعُوكُمْ فَتَسْتَجِيبُونَ بِحَمْدِهِ وَتَظُنُّونَ إِن لَّبِثْتُمْ إِلَّا قَلِيلًا (52)
Pa tsiku limene Iye adzakuitanani ndipo inu mudzamuyankha ndi matamando ake ndi kumvera, pamenepo inu mudzaganiza kuti simudakhale nthawi yaitali koma yochepa
وَقُل لِّعِبَادِي يَقُولُوا الَّتِي هِيَ أَحْسَنُ ۚ إِنَّ الشَّيْطَانَ يَنزَغُ بَيْنَهُمْ ۚ إِنَّ الشَّيْطَانَ كَانَ لِلْإِنسَانِ عَدُوًّا مُّبِينًا (53)
Auze akapolo anga kuti aziyankhula zokhazo zimene zili zabwino. Ndithudi Satana amafesa chidani pakati pawo. Ndithudi Satana, kwa munthu, ndi mdani woonekeratu
رَّبُّكُمْ أَعْلَمُ بِكُمْ ۖ إِن يَشَأْ يَرْحَمْكُمْ أَوْ إِن يَشَأْ يُعَذِّبْكُمْ ۚ وَمَا أَرْسَلْنَاكَ عَلَيْهِمْ وَكِيلًا (54)
Ambuye wanu amadziwa kwambiri za inu ndipo ngati Iye afuna adzakuchitirani chifundo kapena ngati Iye afuna adzakulangani. Ndipo Ife sitidakutumize iwe kuti ukhale wowayang’anira iwo ayi
وَرَبُّكَ أَعْلَمُ بِمَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۗ وَلَقَدْ فَضَّلْنَا بَعْضَ النَّبِيِّينَ عَلَىٰ بَعْضٍ ۖ وَآتَيْنَا دَاوُودَ زَبُورًا (55)
Ambuye wako amadziwa kwambiri zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi ndipo, ndithudi, Ife tidalemekeza Aneneri ena kuposa anzawo ndipo kwa Davide, Ife tidamupatsa Buku la Masalimo
قُلِ ادْعُوا الَّذِينَ زَعَمْتُم مِّن دُونِهِ فَلَا يَمْلِكُونَ كَشْفَ الضُّرِّ عَنكُمْ وَلَا تَحْوِيلًا (56)
Nena, “Aitaneni onse amene mumadzinyengeza nawo mowonjezera pa Iye. Iwo alibe mphamvu zochotsa mavuto anu kapena kuwasintha ndi kupatsa munthu wina.”
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ يَدْعُونَ يَبْتَغُونَ إِلَىٰ رَبِّهِمُ الْوَسِيلَةَ أَيُّهُمْ أَقْرَبُ وَيَرْجُونَ رَحْمَتَهُ وَيَخَافُونَ عَذَابَهُ ۚ إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ كَانَ مَحْذُورًا (57)
Iwo amene amawapembedza nawonso amafunafuna njira yodziyandikiritsira kwa Ambuye wawo, kuti ndani amene angakhale pafupi kwambiri ndi Mulungu ndipo amafunafuna mtendere wa Mulungu ndikuopa chilango chake. Ndithudi chilango cha Ambuye wako ndi chofuna kuopedwa
وَإِن مِّن قَرْيَةٍ إِلَّا نَحْنُ مُهْلِكُوهَا قَبْلَ يَوْمِ الْقِيَامَةِ أَوْ مُعَذِّبُوهَا عَذَابًا شَدِيدًا ۚ كَانَ ذَٰلِكَ فِي الْكِتَابِ مَسْطُورًا (58)
Ndipo palibe mzinda umene Ife sitingauononge kapena kuulanga ndi chilango choopsa tsiku lachiweruzo lisanadze. Izi zidalembedwa m’Buku
وَمَا مَنَعَنَا أَن نُّرْسِلَ بِالْآيَاتِ إِلَّا أَن كَذَّبَ بِهَا الْأَوَّلُونَ ۚ وَآتَيْنَا ثَمُودَ النَّاقَةَ مُبْصِرَةً فَظَلَمُوا بِهَا ۚ وَمَا نُرْسِلُ بِالْآيَاتِ إِلَّا تَخْوِيفًا (59)
Ndipo palibe chimene chimatiletsa Ife kutumiza zizindikiro kupatula kuti anthu a mvula zakale sadazikhulupirire izo. Ndipo kwa anthu a Thamoud, Ife tidawapatsa ngamira yaikazi kukhala chizindikiro chooneka ndi maso komabe iwo adaichitira zoipa. Ndipo Ife sititumiza zizindikiro kupatula ndi cholinga chofuna kuchenjeza ndi kuwachititsa mantha
وَإِذْ قُلْنَا لَكَ إِنَّ رَبَّكَ أَحَاطَ بِالنَّاسِ ۚ وَمَا جَعَلْنَا الرُّؤْيَا الَّتِي أَرَيْنَاكَ إِلَّا فِتْنَةً لِّلنَّاسِ وَالشَّجَرَةَ الْمَلْعُونَةَ فِي الْقُرْآنِ ۚ وَنُخَوِّفُهُمْ فَمَا يَزِيدُهُمْ إِلَّا طُغْيَانًا كَبِيرًا (60)
Ndipo pamene tidakuuza kuti, “Ndithudi! Ambuye wako wawazungulira anthu. Ndipo Ife sitidapange masomphenya amene tidakuonetsa iwe koma kukhala mayeso kwa anthu chimodzimodzinso mtengo wotembereredwa umene watchulidwa m’Korani. Ife timawachenjeza ndi kuwachititsa mantha koma sizili kuwathandiza koma kuonjezera kusakhulupirira.”
وَإِذْ قُلْنَا لِلْمَلَائِكَةِ اسْجُدُوا لِآدَمَ فَسَجَدُوا إِلَّا إِبْلِيسَ قَالَ أَأَسْجُدُ لِمَنْ خَلَقْتَ طِينًا (61)
Ndipo pamene ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Onse adamugwadira iye kupatula Satana. Iye adayankha kuti, “Kodi ine ndimugwadire iye amene Inu mudamupanga kuchokera ku dothi?”
قَالَ أَرَأَيْتَكَ هَٰذَا الَّذِي كَرَّمْتَ عَلَيَّ لَئِنْ أَخَّرْتَنِ إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ لَأَحْتَنِكَنَّ ذُرِّيَّتَهُ إِلَّا قَلِيلًا (62)
Iye adati, “Mukumuona! Uyu ndiye amene mwamulemekeza kuposa ine ndipo ngati inu mundisunga ndi moyo mpaka patsiku louka kwa akufa, ine ndidzawasokoneza ana ake kupatula ochepa.”
قَالَ اذْهَبْ فَمَن تَبِعَكَ مِنْهُمْ فَإِنَّ جَهَنَّمَ جَزَاؤُكُمْ جَزَاءً مَّوْفُورًا (63)
Mulungu adati, “Pita, ndipo aliyense wa iwo amene adzakutsatira, ndithudi, Gahena ndiyo idzakhala malipiro ake ndipo ndi malipiro okwana.”
وَاسْتَفْزِزْ مَنِ اسْتَطَعْتَ مِنْهُم بِصَوْتِكَ وَأَجْلِبْ عَلَيْهِم بِخَيْلِكَ وَرَجِلِكَ وَشَارِكْهُمْ فِي الْأَمْوَالِ وَالْأَوْلَادِ وَعِدْهُمْ ۚ وَمَا يَعِدُهُمُ الشَّيْطَانُ إِلَّا غُرُورًا (64)
“Ndipo anyengerere amene ungawathe mwa iwo ndi mawu ako, ndipo menyana nawo ndi asirikali ako okwera akavalo ndi oyenda pansi, ndipo gawana nawo chuma ndi ana ndipo alonjeze.” Koma Satana sawalonjeza china chilichonse koma chinyengo
إِنَّ عِبَادِي لَيْسَ لَكَ عَلَيْهِمْ سُلْطَانٌ ۚ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ وَكِيلًا (65)
“Ndithudi pa akapolo anga angwiro, iwe siudzakhala ndi mphamvu ina iliyonse pa iwo yowasokoneza. Ambuye wako ndi wokwana kukhala Mtetezi.”
رَّبُّكُمُ الَّذِي يُزْجِي لَكُمُ الْفُلْكَ فِي الْبَحْرِ لِتَبْتَغُوا مِن فَضْلِهِ ۚ إِنَّهُ كَانَ بِكُمْ رَحِيمًا (66)
Ambuye wanu ndiye amene amayendetsa zombo pa nyanja kuti mufunefune zokoma zake. Ndithudi Iye ali wachisoni ndi inu
وَإِذَا مَسَّكُمُ الضُّرُّ فِي الْبَحْرِ ضَلَّ مَن تَدْعُونَ إِلَّا إِيَّاهُ ۖ فَلَمَّا نَجَّاكُمْ إِلَى الْبَرِّ أَعْرَضْتُمْ ۚ وَكَانَ الْإِنسَانُ كَفُورًا (67)
Ndipo akakupezani mavuto pamene mulipanyanja, iwoamenemumawapembedzamowonjezera pa Iye amakuthawirani kupatula Iye yekha. Koma ngati Iye akupulumutsani kufika pa mtunda, mumatembenuka. Ndithudi, munthu ndi wamwano
أَفَأَمِنتُمْ أَن يَخْسِفَ بِكُمْ جَانِبَ الْبَرِّ أَوْ يُرْسِلَ عَلَيْكُمْ حَاصِبًا ثُمَّ لَا تَجِدُوا لَكُمْ وَكِيلًا (68)
Kodi inu muli ndi chikhulupiriro chakuti Iye sangakumizeni m’dera lililonse la pamtunda kapena kuti sangakutumizireni mphepo yamkuntho? Pamenepo inu simudzapeza wina aliyense wokuthandizani
أَمْ أَمِنتُمْ أَن يُعِيدَكُمْ فِيهِ تَارَةً أُخْرَىٰ فَيُرْسِلَ عَلَيْكُمْ قَاصِفًا مِّنَ الرِّيحِ فَيُغْرِقَكُم بِمَا كَفَرْتُمْ ۙ ثُمَّ لَا تَجِدُوا لَكُمْ عَلَيْنَا بِهِ تَبِيعًا (69)
Kapena inu mukukhulupirira kuti sangakubwezereninso m’nyanjamo kachiwiri ndi kukutumizirani mphepo yamkuntho, ndikukumizani chifukwa chakusakhulupirira kwanu ndipo kuti inu simudzapeza wokuthandizani polimbana ndi Ife
۞ وَلَقَدْ كَرَّمْنَا بَنِي آدَمَ وَحَمَلْنَاهُمْ فِي الْبَرِّ وَالْبَحْرِ وَرَزَقْنَاهُم مِّنَ الطَّيِّبَاتِ وَفَضَّلْنَاهُمْ عَلَىٰ كَثِيرٍ مِّمَّنْ خَلَقْنَا تَفْضِيلًا (70)
Ndithudi Ife tawalemekeza ana a Adamu, ndipo Ife tawanyamula pamtunda ndi pa nyanja ndipo tawapatsa zinthu zabwino ndiponso tawalemekeza kuposa zina zimene talenga ndi ulemu wapadera
يَوْمَ نَدْعُو كُلَّ أُنَاسٍ بِإِمَامِهِمْ ۖ فَمَنْ أُوتِيَ كِتَابَهُ بِيَمِينِهِ فَأُولَٰئِكَ يَقْرَءُونَ كِتَابَهُمْ وَلَا يُظْلَمُونَ فَتِيلًا (71)
Ndipo kumbukira tsiku limene tidzaitana mtundu uliwonse wa anthu pamodzi ndi Atsogoleri awo. Ndipo yemwe adzapatsidwa Buku lake ku dzanja lamanja iwo adzawerenga Bukulo mwa chisangalalo ndipo sadzaponderezedwa ngakhale ndi pang’onong’ono pomwe
وَمَن كَانَ فِي هَٰذِهِ أَعْمَىٰ فَهُوَ فِي الْآخِرَةِ أَعْمَىٰ وَأَضَلُّ سَبِيلًا (72)
Koma iye amene ali wakhungu m’moyo uno adzakhalanso wakhungu m’moyo umene uli nkudza ndipo adzasochera kwambiri
وَإِن كَادُوا لَيَفْتِنُونَكَ عَنِ الَّذِي أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ لِتَفْتَرِيَ عَلَيْنَا غَيْرَهُ ۖ وَإِذًا لَّاتَّخَذُوكَ خَلِيلًا (73)
Ndithudi iwo adali pafupi kuti akusokoneze ku zimene takuvumbulutsira iwe kuti utinamizire zina ndipo zikadatero akadakupala ubwenzi
وَلَوْلَا أَن ثَبَّتْنَاكَ لَقَدْ كِدتَّ تَرْكَنُ إِلَيْهِمْ شَيْئًا قَلِيلًا (74)
Ngati Ife tikadapanda kulimbikitsa chikhulupiriro chako, padatsala pang’ono kuti uwatsatire
إِذًا لَّأَذَقْنَاكَ ضِعْفَ الْحَيَاةِ وَضِعْفَ الْمَمَاتِ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ عَلَيْنَا نَصِيرًا (75)
Ndipo zikadatero Ife tikadakulawitsa chilango chachikulu m’moyo uno ndi chilango chachikulu m’moyo umene uli nkudza. Kotero siukadapeza wina aliyense wokuthandiza ku mkwiyo wathu
وَإِن كَادُوا لَيَسْتَفِزُّونَكَ مِنَ الْأَرْضِ لِيُخْرِجُوكَ مِنْهَا ۖ وَإِذًا لَّا يَلْبَثُونَ خِلَافَكَ إِلَّا قَلِيلًا (76)
Ndithudi adatsala pang’ono kukuchititsa mantha m’dziko ndi cholinga choti akuchotse m’menemo. Zikadatheka kutero iwo sakadakhala pambuyo pako, koma kwa kanthawi kochepa
سُنَّةَ مَن قَدْ أَرْسَلْنَا قَبْلَكَ مِن رُّسُلِنَا ۖ وَلَا تَجِدُ لِسُنَّتِنَا تَحْوِيلًا (77)
Umenewu ndiwo mwambo wa Atumwi amene tidatumiza iwe usanadze ndipo iwe siudzapeza kusintha kulikonse m’mwambo wathu
أَقِمِ الصَّلَاةَ لِدُلُوكِ الشَّمْسِ إِلَىٰ غَسَقِ اللَّيْلِ وَقُرْآنَ الْفَجْرِ ۖ إِنَّ قُرْآنَ الْفَجْرِ كَانَ مَشْهُودًا (78)
Chita mapemphero kuyambira nthawi yopendekera dzuwakufikirausikundipowerenga Koranim’mapemphero a m’mbandakucha. Ndithudi kuwerenga Korani nthawi ya m’mbandakucha kumachitilidwa umboni
وَمِنَ اللَّيْلِ فَتَهَجَّدْ بِهِ نَافِلَةً لَّكَ عَسَىٰ أَن يَبْعَثَكَ رَبُّكَ مَقَامًا مَّحْمُودًا (79)
Ndipo m’kati mwa usiku, pemphera ndi kuwerenga Korani ndi mapemphero oonjezera kwa iwe. Mwina Ambuye wako angadzakuike pamalo wotamandika
وَقُل رَّبِّ أَدْخِلْنِي مُدْخَلَ صِدْقٍ وَأَخْرِجْنِي مُخْرَجَ صِدْقٍ وَاجْعَل لِّي مِن لَّدُنكَ سُلْطَانًا نَّصِيرًا (80)
Nena, “Ambuye ndilowetseni kulowa kwa bwino ndipo nditulutseni mwaubwino. Ndipo ndipatseni kuchokera kwa Inu mphamvu yondithandiza.”
وَقُلْ جَاءَ الْحَقُّ وَزَهَقَ الْبَاطِلُ ۚ إِنَّ الْبَاطِلَ كَانَ زَهُوقًا (81)
Nena, “Choonadi chadza ndipo bodza latha. Ndithudi bodza liyenera kutha.”
وَنُنَزِّلُ مِنَ الْقُرْآنِ مَا هُوَ شِفَاءٌ وَرَحْمَةٌ لِّلْمُؤْمِنِينَ ۙ وَلَا يَزِيدُ الظَّالِمِينَ إِلَّا خَسَارًا (82)
Ndipo titumiza kuchokera m’Korani mankhwala ochiza ndiponso chisoni kwa onse okhulupirira, ndipo imaonjezera kwa anthu osakhulupirira chionongeko
وَإِذَا أَنْعَمْنَا عَلَى الْإِنسَانِ أَعْرَضَ وَنَأَىٰ بِجَانِبِهِ ۖ وَإِذَا مَسَّهُ الشَّرُّ كَانَ يَئُوسًا (83)
Ndipo tikam’patsa munthu zokoma zathu, iye amatembenuka ndi kuchita mwano ndipo amakhala kutali ndi njira yoyenera. Ndipo zikam’peza zoipa amakhala wotaya mtima kwambiri
قُلْ كُلٌّ يَعْمَلُ عَلَىٰ شَاكِلَتِهِ فَرَبُّكُمْ أَعْلَمُ بِمَنْ هُوَ أَهْدَىٰ سَبِيلًا (84)
Nena, “Munthu aliyense amachita molingana ndi chikhalidwe chake koma Ambuye wanu amadziwa yemwe watsogozedwa bwino panjira yachilungamo.”
وَيَسْأَلُونَكَ عَنِ الرُّوحِ ۖ قُلِ الرُّوحُ مِنْ أَمْرِ رَبِّي وَمَا أُوتِيتُم مِّنَ الْعِلْمِ إِلَّا قَلِيلًا (85)
IwoakukufunsazaMzimu.Ndiponena,“Ambuyewanga ndiye amene adziwa za iwo. Ndipo inu simudapatsidwe nzeru koma pang’ono pokha.”
وَلَئِن شِئْنَا لَنَذْهَبَنَّ بِالَّذِي أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ بِهِ عَلَيْنَا وَكِيلًا (86)
Ndithudi Ife tikadafuna, tikadakulanda chimene tavumbulutsa kwa iwe ndipo iwe siukadapeza wina aliyense wokuteteza kwa Ife m’malo mwako
إِلَّا رَحْمَةً مِّن رَّبِّكَ ۚ إِنَّ فَضْلَهُ كَانَ عَلَيْكَ كَبِيرًا (87)
Kupatula chifundo chochokera kwa Ambuye wako, ndithudi ubwino wake pa iwe ndi waukulu zedi
قُل لَّئِنِ اجْتَمَعَتِ الْإِنسُ وَالْجِنُّ عَلَىٰ أَن يَأْتُوا بِمِثْلِ هَٰذَا الْقُرْآنِ لَا يَأْتُونَ بِمِثْلِهِ وَلَوْ كَانَ بَعْضُهُمْ لِبَعْضٍ ظَهِيرًا (88)
Nena, “Ngati anthu ndi majini akadagwirizana kubweretsa chofanana ndi Korani ino, iwo sakadabweretsa chofanana nayo ngakhale kuti iwo akadathandizana.”
وَلَقَدْ صَرَّفْنَا لِلنَّاسِ فِي هَٰذَا الْقُرْآنِ مِن كُلِّ مَثَلٍ فَأَبَىٰ أَكْثَرُ النَّاسِ إِلَّا كُفُورًا (89)
Ndithudi talongosola kwa anthu mu Korani ino chitsanzo chilichonse. Komabe anthu ambiri akana choonadi ndi kukhala osakhulupirira
وَقَالُوا لَن نُّؤْمِنَ لَكَ حَتَّىٰ تَفْجُرَ لَنَا مِنَ الْأَرْضِ يَنبُوعًا (90)
Iwo amati, “Ife sitidzakukhulupirira iwe mpaka pamene utatitumphutsira kasupe kuchokera pansi.”
أَوْ تَكُونَ لَكَ جَنَّةٌ مِّن نَّخِيلٍ وَعِنَبٍ فَتُفَجِّرَ الْأَنْهَارَ خِلَالَهَا تَفْجِيرًا (91)
“Kapena utakhala ndi munda wa tende ndi mphesa ndipo m’kati mwake utumphutse mitsinjeyaikulu.”
أَوْ تُسْقِطَ السَّمَاءَ كَمَا زَعَمْتَ عَلَيْنَا كِسَفًا أَوْ تَأْتِيَ بِاللَّهِ وَالْمَلَائِكَةِ قَبِيلًا (92)
“Kapenaugwetsemtambopaifemonga momwe udatilonjezera kapena utibweretsere Mulungu pamodzi ndi angelo pamaso pathu.”
أَوْ يَكُونَ لَكَ بَيْتٌ مِّن زُخْرُفٍ أَوْ تَرْقَىٰ فِي السَّمَاءِ وَلَن نُّؤْمِنَ لِرُقِيِّكَ حَتَّىٰ تُنَزِّلَ عَلَيْنَا كِتَابًا نَّقْرَؤُهُ ۗ قُلْ سُبْحَانَ رَبِّي هَلْ كُنتُ إِلَّا بَشَرًا رَّسُولًا (93)
“Kapena ukhale ndi nyumba yokongoletsedwa bwino kwambiri kapena ukwere kumwamba. Komabe ife sitidzakukhulupirira kukwera kwako mpaka pamene utatitsitsira ife Buku kuti tiziwerenga.” Nena, “Alemekezeke Ambuye wanga! Ndithudi ine sindine aliyense koma munthu amene watumizidwa ngati Mtumwi.”
وَمَا مَنَعَ النَّاسَ أَن يُؤْمِنُوا إِذْ جَاءَهُمُ الْهُدَىٰ إِلَّا أَن قَالُوا أَبَعَثَ اللَّهُ بَشَرًا رَّسُولًا (94)
Ndipo palibe chimene chidawaletsa anthu kukhala okhulupirira pamene malangizo adadza kwa iwo koma mwano chifukwa iwo amati, “Kodi Mulungu watumiza munthu kukhala Mtumwi?”
قُل لَّوْ كَانَ فِي الْأَرْضِ مَلَائِكَةٌ يَمْشُونَ مُطْمَئِنِّينَ لَنَزَّلْنَا عَلَيْهِم مِّنَ السَّمَاءِ مَلَكًا رَّسُولًا (95)
Nena, “Ngati angelo akadakhala pa dziko lapansi, namayenda mwamtendere, ndithudi, Ife tikadatumiza kwa iwo mngelo kuchoka kumwamba ngati Mtumwi.”
قُلْ كَفَىٰ بِاللَّهِ شَهِيدًا بَيْنِي وَبَيْنَكُمْ ۚ إِنَّهُ كَانَ بِعِبَادِهِ خَبِيرًا بَصِيرًا (96)
Nena, “Mulungu ndi wokwana kukhala mboni pakati pa ine ndi inu. Ndithudi! Iye ndi wodziwa ndi woona zonse za akapolo ake.”
وَمَن يَهْدِ اللَّهُ فَهُوَ الْمُهْتَدِ ۖ وَمَن يُضْلِلْ فَلَن تَجِدَ لَهُمْ أَوْلِيَاءَ مِن دُونِهِ ۖ وَنَحْشُرُهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمْ عُمْيًا وَبُكْمًا وَصُمًّا ۖ مَّأْوَاهُمْ جَهَنَّمُ ۖ كُلَّمَا خَبَتْ زِدْنَاهُمْ سَعِيرًا (97)
Ndipo aliyense amene Mulungu wamutsogolera , atsogozedwa bwino koma iye amene Iye amusocheza wotere iwe siungamupezere mtetezi wina aliyense kupatula Iye yekha. Ndipo Ife tidzawasonkhanitsa onse pa tsiku la kuuka kwa akufa, akuyenda pa nkhope zawo, akhungu, abububu ndi agonthi, malo awo adzakhala Gahena ndipo pamene malawi ake azikazima tizidzawaonjezera moto
ذَٰلِكَ جَزَاؤُهُم بِأَنَّهُمْ كَفَرُوا بِآيَاتِنَا وَقَالُوا أَإِذَا كُنَّا عِظَامًا وَرُفَاتًا أَإِنَّا لَمَبْعُوثُونَ خَلْقًا جَدِيدًا (98)
Amenewo ndiwo malipiro awo chifukwa iwo sadakhulupirire mawu athu ndipo adati, “Pamene ife tidzasanduka mafupa ndi kufufutika, kodi tidzaukitsidwa kukhala chilengedwe chatsopano?”
۞ أَوَلَمْ يَرَوْا أَنَّ اللَّهَ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ قَادِرٌ عَلَىٰ أَن يَخْلُقَ مِثْلَهُمْ وَجَعَلَ لَهُمْ أَجَلًا لَّا رَيْبَ فِيهِ فَأَبَى الظَّالِمُونَ إِلَّا كُفُورًا (99)
Kodi iwo saona kuti Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ali ndi mphamvu yolenga zofanana ndi iwo? Ndipo Iye adawaikira iwo nthawi yosakayikitsa. Komabe anthu ochimwa amakana choonadi ndikusankha kusakhulupirira
قُل لَّوْ أَنتُمْ تَمْلِكُونَ خَزَائِنَ رَحْمَةِ رَبِّي إِذًا لَّأَمْسَكْتُمْ خَشْيَةَ الْإِنفَاقِ ۚ وَكَانَ الْإِنسَانُ قَتُورًا (100)
Nena, “Ngati mukadakhala ndi nkhokwe za chifundo cha Ambuye wanga, ndithudi, inu mukanazibisa poopa kuti zingathe.” Ndithudi munthu ndi waumbombo
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَىٰ تِسْعَ آيَاتٍ بَيِّنَاتٍ ۖ فَاسْأَلْ بَنِي إِسْرَائِيلَ إِذْ جَاءَهُمْ فَقَالَ لَهُ فِرْعَوْنُ إِنِّي لَأَظُنُّكَ يَا مُوسَىٰ مَسْحُورًا (101)
Ndithudi Ife tidamupatsa Mose zizindikiro zisanu ndi zinayi zooneka. Afunse ana a Israyeli pamene iye adadza kwa iwo ndipo Farawo adati kwa iye, “Iwe Mose, ndithudi, ine ndili kukuganizira kuti ndiwe wolodzedwa.”
قَالَ لَقَدْ عَلِمْتَ مَا أَنزَلَ هَٰؤُلَاءِ إِلَّا رَبُّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ بَصَائِرَ وَإِنِّي لَأَظُنُّكَ يَا فِرْعَوْنُ مَثْبُورًا (102)
Iye adati, “Ndithudi iwe uli kudziwa bwinobwino kuti zizindikiro izi sizinatumizidwe ndi wina koma Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ngati umboni wooneka ndi maso. Ndipo, ndithudi, ine ndiganiza kuti iwe, Farawo, ndiwe woonongeka.”
فَأَرَادَ أَن يَسْتَفِزَّهُم مِّنَ الْأَرْضِ فَأَغْرَقْنَاهُ وَمَن مَّعَهُ جَمِيعًا (103)
Farawo anafunitsitsa kuti awapirikitse m’dziko. Koma Ife tidamumiza pamodzi ndi onse amene adali naye
وَقُلْنَا مِن بَعْدِهِ لِبَنِي إِسْرَائِيلَ اسْكُنُوا الْأَرْضَ فَإِذَا جَاءَ وَعْدُ الْآخِرَةِ جِئْنَا بِكُمْ لَفِيفًا (104)
Ndipo pambuyo pake Ife tidati kwa ana a Israyeli, “Khalani m’dziko ndipo pamene lonjezo lomaliza lidzadza, Ife tidzakusonkhanitsani kukhala malo amodzi.”
وَبِالْحَقِّ أَنزَلْنَاهُ وَبِالْحَقِّ نَزَلَ ۗ وَمَا أَرْسَلْنَاكَ إِلَّا مُبَشِّرًا وَنَذِيرًا (105)
Ifetavumbulutsa Bukula Koranim’choonadindipondi m’choonadi latsika. Ndipo Ife takutumiza iwe osati wina kuti ukalalikire nkhani za bwino ndi kupereka chenjezo
وَقُرْآنًا فَرَقْنَاهُ لِتَقْرَأَهُ عَلَى النَّاسِ عَلَىٰ مُكْثٍ وَنَزَّلْنَاهُ تَنزِيلًا (106)
Ndi Buku la Korani limene tagawa m’zigawo kuti iwe uwerenge kwa anthu mwakanthawi. Ife talivumbulutsa pang’onopang’ono
قُلْ آمِنُوا بِهِ أَوْ لَا تُؤْمِنُوا ۚ إِنَّ الَّذِينَ أُوتُوا الْعِلْمَ مِن قَبْلِهِ إِذَا يُتْلَىٰ عَلَيْهِمْ يَخِرُّونَ لِلْأَذْقَانِ سُجَّدًا (107)
Nena, “Zili kwa inu kulikhulupirira kapena kusalikhulupirira. Ndithudi! Iwo amene adapatsidwa nzeru ilo lisadadze, likamawerengedwa kwa iwo, amagwetsa mphumi zawo pansi.”
وَيَقُولُونَ سُبْحَانَ رَبِّنَا إِن كَانَ وَعْدُ رَبِّنَا لَمَفْعُولًا (108)
Ndipo iwo amati, “Ulemerero ndi wa Ambuye wathu! Ndithudi lonjezo la Ambuye wathu likwaniritsidwe.”
وَيَخِرُّونَ لِلْأَذْقَانِ يَبْكُونَ وَيَزِيدُهُمْ خُشُوعًا ۩ (109)
Ndipo iwo amagwa pansi pa zipumi zawo, ali kulira ndipo limawaonjezera kudzichepetsa
قُلِ ادْعُوا اللَّهَ أَوِ ادْعُوا الرَّحْمَٰنَ ۖ أَيًّا مَّا تَدْعُوا فَلَهُ الْأَسْمَاءُ الْحُسْنَىٰ ۚ وَلَا تَجْهَرْ بِصَلَاتِكَ وَلَا تُخَافِتْ بِهَا وَابْتَغِ بَيْنَ ذَٰلِكَ سَبِيلًا (110)
Nena, “Muitaneni Mulungu kapena Mwini chifundo chosatha, m’dzina lililonse limene mungamuitanire, chifukwa Iye ali ndi mayina abwino. Ndipo musanene mapemphero anu mokweza kapena motsitsa koma sankhani mawu a pakati ndi pakati.”
وَقُلِ الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي لَمْ يَتَّخِذْ وَلَدًا وَلَمْ يَكُن لَّهُ شَرِيكٌ فِي الْمُلْكِ وَلَمْ يَكُن لَّهُ وَلِيٌّ مِّنَ الذُّلِّ ۖ وَكَبِّرْهُ تَكْبِيرًا (111)
Nena, “Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, amene sanabale mwana wamwamuna ndipo alibe mnzake womuthandiza mu Ufumu wake, ndipo Iye siwopanda mphamvu kuti angakhale ndi womuthandiza. Motero mulemekezeni Iye ndi ulemu woyenera Iye yekha.”
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas