وَيْلٌ لِّلْمُطَفِّفِينَ (1) Tsoka kwa iwo onse amene amagulitsa malonda awo monyenga |
الَّذِينَ إِذَا اكْتَالُوا عَلَى النَّاسِ يَسْتَوْفُونَ (2) Iwo amene amati ena akamawayesera zinthu amafuna kuti zikwanire muyeso wake |
وَإِذَا كَالُوهُمْ أَو وَّزَنُوهُمْ يُخْسِرُونَ (3) Koma pamene iwo ayesa kapena awayesera anthu ena amawanyenga |
أَلَا يَظُنُّ أُولَٰئِكَ أَنَّهُم مَّبْعُوثُونَ (4) Kodi iwo saganiza kuti adzaukitsidwa kwa akufa |
لِيَوْمٍ عَظِيمٍ (5) Patsiku lalikulu |
يَوْمَ يَقُومُ النَّاسُ لِرَبِّ الْعَالَمِينَ (6) Tsiku limene anthu a mitundu yonse adzaima pamaso pa Ambuye wa zolengedwa zonse |
كَلَّا إِنَّ كِتَابَ الْفُجَّارِ لَفِي سِجِّينٍ (7) Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu onse oipa chili mu Sijjin |
وَمَا أَدْرَاكَ مَا سِجِّينٌ (8) Kodi udzadziwa bwanji Sijjin ndi chiyani |
كِتَابٌ مَّرْقُومٌ (9) Ili ndi Buku lolembedwa |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (10) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira |
الَّذِينَ يُكَذِّبُونَ بِيَوْمِ الدِّينِ (11) Iwo amene amakana kuti kuli tsiku lachiweruzo |
وَمَا يُكَذِّبُ بِهِ إِلَّا كُلُّ مُعْتَدٍ أَثِيمٍ (12) Palibe wina amene amalikana tsikuli kupatula munthu wogona m’machimo |
إِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِ آيَاتُنَا قَالَ أَسَاطِيرُ الْأَوَّلِينَ (13) Pamene chivumbulutso chathu chinenedwa kwa iye, iye amati: “Izi ndizo nthano za anthu akale.” |
كَلَّا ۖ بَلْ ۜ رَانَ عَلَىٰ قُلُوبِهِم مَّا كَانُوا يَكْسِبُونَ (14) Iyayi! Koma m’mitima mwawo ndi mokutidwa ndi zintchito zimene amachita |
كَلَّا إِنَّهُمْ عَن رَّبِّهِمْ يَوْمَئِذٍ لَّمَحْجُوبُونَ (15) Iyayi! Ndithudi iwo sadzaloledwa kuona Ambuye wawo pa tsikuli |
ثُمَّ إِنَّهُمْ لَصَالُو الْجَحِيمِ (16) Ndipo iwo adzalowa ndi kulawa moto ku Gahena |
ثُمَّ يُقَالُ هَٰذَا الَّذِي كُنتُم بِهِ تُكَذِّبُونَ (17) Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti: “Chimenechi ndicho chilango chija munkachinena kuti sichidzakhalako.” |
كَلَّا إِنَّ كِتَابَ الْأَبْرَارِ لَفِي عِلِّيِّينَ (18) Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu olungama chimasungidwa mu Illiyyun |
وَمَا أَدْرَاكَ مَا عِلِّيُّونَ (19) Kodi mudzadziwa bwanji kuti Illiyin wapamwambayo ndi chiyani |
كِتَابٌ مَّرْقُومٌ (20) Ndi Al Mutaffifin 645 Buku lochita kulembedwa |
يَشْهَدُهُ الْمُقَرَّبُونَ (21) Limene limaonedwa ndi iwo okhawo amene ali kufupi ndi zofuna za Mulungu |
إِنَّ الْأَبْرَارَ لَفِي نَعِيمٍ (22) Ndithudi anthu onse olungama adzakhala ku malo a mtendere |
عَلَى الْأَرَائِكِ يَنظُرُونَ (23) Atakhala pa mipando ya wofowofo ndipo ali kuyang’ana uku ndi uku |
تَعْرِفُ فِي وُجُوهِهِمْ نَضْرَةَ النَّعِيمِ (24) Ndipo udzaona chisangalalo pa nkhope zawo |
يُسْقَوْنَ مِن رَّحِيقٍ مَّخْتُومٍ (25) Iwo adzapatsidwa kuti amwe vinyo weniweni amene sanatsegulidwepo |
خِتَامُهُ مِسْكٌ ۚ وَفِي ذَٰلِكَ فَلْيَتَنَافَسِ الْمُتَنَافِسُونَ (26) Womaliza wake adzakhala ndi fungo labwino ndipo pachifukwa cha ichi, aleke onse amene afuna kulimbikira kuti alimbike |
وَمِزَاجُهُ مِن تَسْنِيمٍ (27) Wosakanizidwa ndi madzi a Tasnim |
عَيْنًا يَشْرَبُ بِهَا الْمُقَرَّبُونَ (28) Kasupe amene anthu odala adzakhala ali kumwa |
إِنَّ الَّذِينَ أَجْرَمُوا كَانُوا مِنَ الَّذِينَ آمَنُوا يَضْحَكُونَ (29) Ndithudi! Anthu amene amachita zoipa, anali kuwaseka anthu amene anakhulupirira |
وَإِذَا مَرُّوا بِهِمْ يَتَغَامَزُونَ (30) Ndi kumacheulana iwo akamadutsa pakati pawo |
وَإِذَا انقَلَبُوا إِلَىٰ أَهْلِهِمُ انقَلَبُوا فَكِهِينَ (31) Ndipo iwo amati akabwerera kwa anthu awo amabwera ali kunyoza |
وَإِذَا رَأَوْهُمْ قَالُوا إِنَّ هَٰؤُلَاءِ لَضَالُّونَ (32) Ndipo amati akawaona iwo amati: “Ndithudi awa ndiwo anthu osochera.” |
وَمَا أُرْسِلُوا عَلَيْهِمْ حَافِظِينَ (33) Pamene iwo sadalamulidwe kuti akhale owayang’anira |
فَالْيَوْمَ الَّذِينَ آمَنُوا مِنَ الْكُفَّارِ يَضْحَكُونَ (34) Koma pa tsikuli anthu okhulupirira adzaseka anthu osakhulupirira |
عَلَى الْأَرَائِكِ يَنظُرُونَ (35) Ali pa mipando yawofowofo ndi kumayang’ana |
هَلْ ثُوِّبَ الْكُفَّارُ مَا كَانُوا يَفْعَلُونَ (36) Kodi anthu osakhulupirira, sanalipidwe mphotho yawo molingana ndi ntchito zawo |