×

سورة النجم باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة النجم

ترجمة معاني سورة النجم باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة النجم مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Najm in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة النجم باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 62 - رقم السورة 53 - الصفحة 526.

بسم الله الرحمن الرحيم

وَالنَّجْمِ إِذَا هَوَىٰ (1)
Ndi pali nyenyezi pamene ili kulowa
مَا ضَلَّ صَاحِبُكُمْ وَمَا غَوَىٰ (2)
M’bale wanu sadasochere kapena kuti ndi wolakwa
وَمَا يَنطِقُ عَنِ الْهَوَىٰ (3)
Ndipo iye sayankhula zofuna zake
إِنْ هُوَ إِلَّا وَحْيٌ يُوحَىٰ (4)
Icho ndi chochita kuuzidwa kwa iye
عَلَّمَهُ شَدِيدُ الْقُوَىٰ (5)
Iye adaphunzitsidwa ndi Iye amene ali ndi mphamvu
ذُو مِرَّةٍ فَاسْتَوَىٰ (6)
Wopanda chilema chilichonse, kotero adadzuka ndi kukhala wokhazikika
وَهُوَ بِالْأُفُقِ الْأَعْلَىٰ (7)
Pamene iye anali patali kwambiri mu mlengalenga
ثُمَّ دَنَا فَتَدَلَّىٰ (8)
Ndipo adasendera ndi kudza pafupi
فَكَانَ قَابَ قَوْسَيْنِ أَوْ أَدْنَىٰ (9)
Ndipo adali pa mtunda wolingana kuponya mipaliro iwiri kapena kucheperapo
فَأَوْحَىٰ إِلَىٰ عَبْدِهِ مَا أَوْحَىٰ (10)
Motero Iye adaulula Uthenga kwa kapolo wake kudzera mwa Gabriyele
مَا كَذَبَ الْفُؤَادُ مَا رَأَىٰ (11)
Mtima wake wa Mtumwi siudaname ponena zimene iye adaona
أَفَتُمَارُونَهُ عَلَىٰ مَا يَرَىٰ (12)
Kodi inu mudzatsutsana naye pa zimene iye adaona
وَلَقَدْ رَآهُ نَزْلَةً أُخْرَىٰ (13)
Ndithudi iye adamuona iye pamene anali kutsika kachiwiri
عِندَ سِدْرَةِ الْمُنتَهَىٰ (14)
Pafupi ndi mtengo wa Sidrah
عِندَهَا جَنَّةُ الْمَأْوَىٰ (15)
Pafupi pake pali munda womwe ndi malo opumirako
إِذْ يَغْشَى السِّدْرَةَ مَا يَغْشَىٰ (16)
Ndipo chimene chimaphimba chidakuta mtengo wa Sidrah
مَا زَاغَ الْبَصَرُ وَمَا طَغَىٰ (17)
Maso ake sadayang’ane kumbali kapena kupyola muyeso
لَقَدْ رَأَىٰ مِنْ آيَاتِ رَبِّهِ الْكُبْرَىٰ (18)
Ndithudi iye adaona zizindikiro zazikulu kwambiri za Ambuye wake
أَفَرَأَيْتُمُ اللَّاتَ وَالْعُزَّىٰ (19)
Kodi inu maganiza za Lat ndi Uzza
وَمَنَاةَ الثَّالِثَةَ الْأُخْرَىٰ (20)
Ndi Manat wachitatu wamkazi
أَلَكُمُ الذَّكَرُ وَلَهُ الْأُنثَىٰ (21)
Kwa inu amuna ndipo kwa Iye akazi
تِلْكَ إِذًا قِسْمَةٌ ضِيزَىٰ (22)
Ndithudi kumeneku ndiko kugawa kosalungama
إِنْ هِيَ إِلَّا أَسْمَاءٌ سَمَّيْتُمُوهَا أَنتُمْ وَآبَاؤُكُم مَّا أَنزَلَ اللَّهُ بِهَا مِن سُلْطَانٍ ۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا الظَّنَّ وَمَا تَهْوَى الْأَنفُسُ ۖ وَلَقَدْ جَاءَهُم مِّن رَّبِّهِمُ الْهُدَىٰ (23)
Awa ndi mayina chabe amene inu mwapeka, inu ndi atate anu, amene Mulungu sadakulamuleni ndi pang’ono pomwe. Iwo amangotsatira nkhani zakumva chabe zimene mitima yawo imafuna pamene, ndithudi, kwadza kale kwa iwo ulangizi wochokera kwa Ambuye wawo
أَمْ لِلْإِنسَانِ مَا تَمَنَّىٰ (24)
Kodi munthu angapeze zonse zimene amafuna
فَلِلَّهِ الْآخِرَةُ وَالْأُولَىٰ (25)
Koma Mulungu ndiye Mwini moyo umene uli nkudza ndi moyo wakale
۞ وَكَم مِّن مَّلَكٍ فِي السَّمَاوَاتِ لَا تُغْنِي شَفَاعَتُهُمْ شَيْئًا إِلَّا مِن بَعْدِ أَن يَأْذَنَ اللَّهُ لِمَن يَشَاءُ وَيَرْضَىٰ (26)
Ndipo kuli angelo ambiri amene ali kumwamba amene kukhala pakati kwawo sikudzathandiza chilichonse kupatula pokhapo pamene Mulungu apereka chilolezo kwa amene Iye wamufuna ndi kukondweretsedwa naye
إِنَّ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ لَيُسَمُّونَ الْمَلَائِكَةَ تَسْمِيَةَ الْأُنثَىٰ (27)
Ndithudi iwo amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza, amatcha angelo ndi mayina achikazi
وَمَا لَهُم بِهِ مِنْ عِلْمٍ ۖ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا الظَّنَّ ۖ وَإِنَّ الظَّنَّ لَا يُغْنِي مِنَ الْحَقِّ شَيْئًا (28)
Pamene iwo sadziwa chilichonse cha izo. Iwo satsatira china chilichonse koma nkhani zabodza ndipo, ndithudi, nkhani zabodza si mlowam’malo wa choonadi
فَأَعْرِضْ عَن مَّن تَوَلَّىٰ عَن ذِكْرِنَا وَلَمْ يُرِدْ إِلَّا الْحَيَاةَ الدُّنْيَا (29)
Motero mupewe wina aliyense amene salabadira chikumbutso chathu ndipo safuna china chilichonse koma moyo wa padziko lino lapansi
ذَٰلِكَ مَبْلَغُهُم مِّنَ الْعِلْمِ ۚ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعْلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِ وَهُوَ أَعْلَمُ بِمَنِ اهْتَدَىٰ (30)
Uko ndiko kuchuluka kwa nzeru zawo. Ndithudi Ambuye wako ndiye amadziwa bwino onse amene amasochera ku njira yoyenera ndipo amadziwa kwambiri iye amene amatsata njira yoyenera
وَلِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ لِيَجْزِيَ الَّذِينَ أَسَاءُوا بِمَا عَمِلُوا وَيَجْزِيَ الَّذِينَ أَحْسَنُوا بِالْحُسْنَى (31)
Ndipo Mulungu ndiye mwini wake wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi, ndipo akhoza kulanga onse amene amachita zoipa molingana ndi ntchito zawo ndiponso kuti akhoza kulipira onse amene amachita zabwino ndi mphotho yabwino kwambiri
الَّذِينَ يَجْتَنِبُونَ كَبَائِرَ الْإِثْمِ وَالْفَوَاحِشَ إِلَّا اللَّمَمَ ۚ إِنَّ رَبَّكَ وَاسِعُ الْمَغْفِرَةِ ۚ هُوَ أَعْلَمُ بِكُمْ إِذْ أَنشَأَكُم مِّنَ الْأَرْضِ وَإِذْ أَنتُمْ أَجِنَّةٌ فِي بُطُونِ أُمَّهَاتِكُمْ ۖ فَلَا تُزَكُّوا أَنفُسَكُمْ ۖ هُوَ أَعْلَمُ بِمَنِ اتَّقَىٰ (32)
Iwo amene amapewa machimo a akuluakulu ndi chigololo kupatula machimo a ang’onoang’ono, ndithudi, Ambuye wako ndi Mwini chikhululukiro. Iye amakudziwani bwino pamene amakulengani kuchokera ku dothi ndi pamene mukutidwa m’mimba mwa amayi anu. Motero musadziyeretse nokha. Al Najm 567 Iye amadziwa bwino kwambiri aliyense amene amalewa zoipa
أَفَرَأَيْتَ الَّذِي تَوَلَّىٰ (33)
Kodi iwe wamuona amene amabwerera m’mbuyo
وَأَعْطَىٰ قَلِيلًا وَأَكْدَىٰ (34)
Amene adapereka pang’ono ndipo anasiya kupereka
أَعِندَهُ عِلْمُ الْغَيْبِ فَهُوَ يَرَىٰ (35)
Kodi iye amadziwa za zinthu zobisika kuti akhoza kuziona
أَمْ لَمْ يُنَبَّأْ بِمَا فِي صُحُفِ مُوسَىٰ (36)
Kodi kapena iye sadauzidwe za mawu amene ali m’mabuku a Mose
وَإِبْرَاهِيمَ الَّذِي وَفَّىٰ (37)
Ndiponso za Abrahamu amene adakwaniritsa malamulo
أَلَّا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزْرَ أُخْرَىٰ (38)
Kuti palibe munthu amene adzasenza katundu wa mnzake
وَأَن لَّيْسَ لِلْإِنسَانِ إِلَّا مَا سَعَىٰ (39)
Ndipo kuti munthu sadzapeza chilichonse kupatula chimene wachigwirira ntchito
وَأَنَّ سَعْيَهُ سَوْفَ يُرَىٰ (40)
Ndipo kuti ntchito zake zidzaoneka
ثُمَّ يُجْزَاهُ الْجَزَاءَ الْأَوْفَىٰ (41)
Pamenepo iye adzalipidwa malipiro ake oyenera
وَأَنَّ إِلَىٰ رَبِّكَ الْمُنتَهَىٰ (42)
Ndipo kuti kwa Ambuye wanu ndi kumene nonse mudzapita
وَأَنَّهُ هُوَ أَضْحَكَ وَأَبْكَىٰ (43)
Ndipo kuti Ndiye amene amawachititsa anthu kuseka ndi kuwaliritsa
وَأَنَّهُ هُوَ أَمَاتَ وَأَحْيَا (44)
Ndipo kuti Ndiye amene amapereka imfa ndi moyo
وَأَنَّهُ خَلَقَ الزَّوْجَيْنِ الذَّكَرَ وَالْأُنثَىٰ (45)
Ndiponso kuti Iye adalenga zinthu ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi
مِن نُّطْفَةٍ إِذَا تُمْنَىٰ (46)
Kuchokera ku madontho a umuna umene umatuluka
وَأَنَّ عَلَيْهِ النَّشْأَةَ الْأُخْرَىٰ (47)
Ndipo kuti kwa Iye kuli chilengedwe chachiwiri
وَأَنَّهُ هُوَ أَغْنَىٰ وَأَقْنَىٰ (48)
Ndipo kuti Ndiye amene amapereka chuma ndi chisangalalo
وَأَنَّهُ هُوَ رَبُّ الشِّعْرَىٰ (49)
Ndipo kuti Iye ndiye Ambuye wa nyenyezi yamphamvu yotchedwa Sirius
وَأَنَّهُ أَهْلَكَ عَادًا الْأُولَىٰ (50)
Kuti ndiye amene adaononga anthu akale a mphamvu kwambiri a mtundu wa a Aad kale
وَثَمُودَ فَمَا أَبْقَىٰ (51)
Ndi anthu a mtundu wa a Thamoud. Ndipo Iye sadasiye wina aliyense
وَقَوْمَ نُوحٍ مِّن قَبْلُ ۖ إِنَّهُمْ كَانُوا هُمْ أَظْلَمَ وَأَطْغَىٰ (52)
Ndi anthu a Nowa amakedzana ndithudi iwo adali osalungama ndi oswa malamulo mwamwano
وَالْمُؤْتَفِكَةَ أَهْوَىٰ (53)
Ndipo iye adaononga mizinda yomwe idali yogonjetsedwa
فَغَشَّاهَا مَا غَشَّىٰ (54)
Kotero iwo adawavundikira nd chimene chidawavundikira
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكَ تَتَمَارَىٰ (55)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wako zimene udzazikayikira
هَٰذَا نَذِيرٌ مِّنَ النُّذُرِ الْأُولَىٰ (56)
Uyu ndi mchenjezi wotsatizana ndi achenjezi a makedzana
أَزِفَتِ الْآزِفَةُ (57)
Tsiku louka kwa akufa lili pafupi
لَيْسَ لَهَا مِن دُونِ اللَّهِ كَاشِفَةٌ (58)
Palibe wina kupatula Mulungu amene akhoza kulipherera
أَفَمِنْ هَٰذَا الْحَدِيثِ تَعْجَبُونَ (59)
Kodi inu mulikudabwa pa zimene zili kulakatulidwa
وَتَضْحَكُونَ وَلَا تَبْكُونَ (60)
Ndipo inu muli kuseka m’malo mwakulira
وَأَنتُمْ سَامِدُونَ (61)
Ndi kumapitirizabe kuchita zinthu zopanda pake
فَاسْجُدُوا لِلَّهِ وَاعْبُدُوا ۩ (62)
Motero gunditsani nkhope zanu pansi ndipo pembedzani Mulungu mmodzi yekha
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس