إِذَا جَاءَكَ الْمُنَافِقُونَ قَالُوا نَشْهَدُ إِنَّكَ لَرَسُولُ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ يَعْلَمُ إِنَّكَ لَرَسُولُهُ وَاللَّهُ يَشْهَدُ إِنَّ الْمُنَافِقِينَ لَكَاذِبُونَ (1) Pamene anthu a chinyengo amadza kwa iwe amati: “Ife tichitira umboni kuti iwe, ndithudi, ndiwe Mtumwi wa Mulungu. Inde Mulungu amadziwa kuti iwe, ndithudi, ndiwe Mtumwi wake ndipo Mulungu achitira umboni kuti anthu achinyengo, ndithudi, ndi abodza |
اتَّخَذُوا أَيْمَانَهُمْ جُنَّةً فَصَدُّوا عَن سَبِيلِ اللَّهِ ۚ إِنَّهُمْ سَاءَ مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (2) Iwo asandutsa malonjezo awo ngati tchingo. Motero iwo amaletsa anthu ena kuti atsatire njira ya Mulungu. Ndithudi zimene iwo amachita ndi zoipa |
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ آمَنُوا ثُمَّ كَفَرُوا فَطُبِعَ عَلَىٰ قُلُوبِهِمْ فَهُمْ لَا يَفْقَهُونَ (3) Ichi ndi chifukwa chakuti iwo adakhulupirirapoyambandipopambuyopakeadayambanso kusakhulupirira. Motero mitima yawo idatsekedwa ndipo sazindikira china chilichonse |
۞ وَإِذَا رَأَيْتَهُمْ تُعْجِبُكَ أَجْسَامُهُمْ ۖ وَإِن يَقُولُوا تَسْمَعْ لِقَوْلِهِمْ ۖ كَأَنَّهُمْ خُشُبٌ مُّسَنَّدَةٌ ۖ يَحْسَبُونَ كُلَّ صَيْحَةٍ عَلَيْهِمْ ۚ هُمُ الْعَدُوُّ فَاحْذَرْهُمْ ۚ قَاتَلَهُمُ اللَّهُ ۖ أَنَّىٰ يُؤْفَكُونَ (4) Ndipo pamene iwe uwaona, matupi awo amakusangalatsa ndipo pamene iwo alankhula, iwe umamvera zonena zawo. Iwo ali ngati matabwa amene aimikidwa pa chipupa. Iwo amaganiza kuti mawu onse amene amveka amanena za iwo. Iwo ndi adani kotero chenjera nawo. Matemberero a Mulungu akhale pa iwo! Kodi iwo asocheretsedwa bwanji kunjira yoyenera |
وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ تَعَالَوْا يَسْتَغْفِرْ لَكُمْ رَسُولُ اللَّهِ لَوَّوْا رُءُوسَهُمْ وَرَأَيْتَهُمْ يَصُدُّونَ وَهُم مُّسْتَكْبِرُونَ (5) Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: “Bwerani kuti mwina Mtumwi wa Mulungu akupemphereni chikhululukiro kuchokera kwa Mulungu, ” iwo amabwerera m’mbuyo ndipo iwe umawaona ali kutembenuza nkhope zawo mwachipongwe |
سَوَاءٌ عَلَيْهِمْ أَسْتَغْفَرْتَ لَهُمْ أَمْ لَمْ تَسْتَغْفِرْ لَهُمْ لَن يَغْفِرَ اللَّهُ لَهُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الْفَاسِقِينَ (6) Ndi chimodzimodzi kwa iwo kaya iwe uwapemphera chikhululukiro kapena ayi Mulungu sadzawakhululukira Al Munafiqun 601 iwo. Ndithudi Mulungu satsogolera anthu ophwanya malamulo |
هُمُ الَّذِينَ يَقُولُونَ لَا تُنفِقُوا عَلَىٰ مَنْ عِندَ رَسُولِ اللَّهِ حَتَّىٰ يَنفَضُّوا ۗ وَلِلَّهِ خَزَائِنُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَلَٰكِنَّ الْمُنَافِقِينَ لَا يَفْقَهُونَ (7) Iwo ndiwo amene amati: “Musawapatse china chilichonse anthu amene ali ndi Mtumwi wa Mulungu kuti amuthawe.” Koma Mulungu ndiye Mwini wa chuma cha mlengalenga ndi padziko lapansi koma anthu achinyengo sadziwa zimenezi |
يَقُولُونَ لَئِن رَّجَعْنَا إِلَى الْمَدِينَةِ لَيُخْرِجَنَّ الْأَعَزُّ مِنْهَا الْأَذَلَّ ۚ وَلِلَّهِ الْعِزَّةُ وَلِرَسُولِهِ وَلِلْمُؤْمِنِينَ وَلَٰكِنَّ الْمُنَافِقِينَ لَا يَعْلَمُونَ (8) Iwo amati: “Ngati tibwerera ku Medina, ndithudi, anthu a mphamvu, adzathamangitsa anthu kuchoka ku Mzindawo.” Koma ulemu, mphamvu ndi ulemerero ndi wa Mulungu, Mtumwi wake ndi okhulupilira koma anthu a chinyengo sadziwa chimenechi |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تُلْهِكُمْ أَمْوَالُكُمْ وَلَا أَوْلَادُكُمْ عَن ذِكْرِ اللَّهِ ۚ وَمَن يَفْعَلْ ذَٰلِكَ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْخَاسِرُونَ (9) oh inu okhulupirira! Musalole chuma kapena ana anu kuti akusokonezeni pokukumbukira Mulungu. Ndipo aliyense amene achita motero, ndithudi, ndi wotayika |
وَأَنفِقُوا مِن مَّا رَزَقْنَاكُم مِّن قَبْلِ أَن يَأْتِيَ أَحَدَكُمُ الْمَوْتُ فَيَقُولَ رَبِّ لَوْلَا أَخَّرْتَنِي إِلَىٰ أَجَلٍ قَرِيبٍ فَأَصَّدَّقَ وَأَكُن مِّنَ الصَّالِحِينَ (10) Ndipo perekani kuchokera ku katundu amene takupatsani imfa isanadze pa wina wa inu kuti iye asanene kuti: “Oh Ambuye wanga! Inu mukadandibweza mwa kanthawi kochepa, ine ndikadapereka chaulere chochuluka kuchokera ku chuma changa ndikukhala mmodzi wa anthu ochita zabwino.” |
وَلَن يُؤَخِّرَ اللَّهُ نَفْسًا إِذَا جَاءَ أَجَلُهَا ۚ وَاللَّهُ خَبِيرٌ بِمَا تَعْمَلُونَ (11) Ndipo Mulungu sapereka nthawi kwa wina pamene nthawi yake itakwana. Ndipo Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita |