قَدْ أَفْلَحَ الْمُؤْمِنُونَ (1) Anthu okhulupirira ndiwo opambana |
الَّذِينَ هُمْ فِي صَلَاتِهِمْ خَاشِعُونَ (2) Iwo amene amadzichepetsa akamapemphera |
وَالَّذِينَ هُمْ عَنِ اللَّغْوِ مُعْرِضُونَ (3) Ndi iwo amene amalewa nkhani zabodza |
وَالَّذِينَ هُمْ لِلزَّكَاةِ فَاعِلُونَ (4) Ndipo amapereka zaulere kwa anthu osauka |
وَالَّذِينَ هُمْ لِفُرُوجِهِمْ حَافِظُونَ (5) Ndi iwo amene amadziteteza ku chiwerewere |
إِلَّا عَلَىٰ أَزْوَاجِهِمْ أَوْ مَا مَلَكَتْ أَيْمَانُهُمْ فَإِنَّهُمْ غَيْرُ مَلُومِينَ (6) Kupatula kwa akazi awo kapena akapolo awo akazi, chifukwa iwo sangadzudzulidwe |
فَمَنِ ابْتَغَىٰ وَرَاءَ ذَٰلِكَ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْعَادُونَ (7) Koma amene angafune zina pamwamba pa zimene tawaloleza anthu otere ndi ochimwa |
وَالَّذِينَ هُمْ لِأَمَانَاتِهِمْ وَعَهْدِهِمْ رَاعُونَ (8) Amene amakwaniritsa malonjezo ndi mapangano awo |
وَالَّذِينَ هُمْ عَلَىٰ صَلَوَاتِهِمْ يُحَافِظُونَ (9) Ndi iwo amene amasunga mapemphero awo |
أُولَٰئِكَ هُمُ الْوَارِثُونَ (10) Amenewa ndithudi ndiwo amene adzalowa |
الَّذِينَ يَرِثُونَ الْفِرْدَوْسَ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (11) Iwo adzalowa ku Paradiso ya pamwamba ndipo adzakhalamo mpaka kalekale |
وَلَقَدْ خَلَقْنَا الْإِنسَانَ مِن سُلَالَةٍ مِّن طِينٍ (12) Ndithudi Ife tidapanga munthu kuchokera ku dothi labwino |
ثُمَّ جَعَلْنَاهُ نُطْفَةً فِي قَرَارٍ مَّكِينٍ (13) Titatero tidamukonza iye kukhala dontho la umuna m’malo otetezedwa mu msana |
ثُمَّ خَلَقْنَا النُّطْفَةَ عَلَقَةً فَخَلَقْنَا الْعَلَقَةَ مُضْغَةً فَخَلَقْنَا الْمُضْغَةَ عِظَامًا فَكَسَوْنَا الْعِظَامَ لَحْمًا ثُمَّ أَنشَأْنَاهُ خَلْقًا آخَرَ ۚ فَتَبَارَكَ اللَّهُ أَحْسَنُ الْخَالِقِينَ (14) dontho la umunali tidalipanga kukhala dontho la magazi ndipo dontho lamagazili tidalipanga kukhala m’bulu wa mnofu. Ndipo mnofu umenewu tidaukonza kukhala mafupa ndipo tidakuta mafupa ndi mnofu. Kotero tidamupanga iye kukhala chilengedwe china. odalitsa akhale Mulungu, Namalenga wabwino kwambiri mwa onse |
ثُمَّ إِنَّكُم بَعْدَ ذَٰلِكَ لَمَيِّتُونَ (15) Ndipo pambuyo pake inu nonse mudzafa |
ثُمَّ إِنَّكُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ تُبْعَثُونَ (16) Ndipo mudzapatsidwanso moyo patsiku la kuuka kwa akufa |
وَلَقَدْ خَلَقْنَا فَوْقَكُمْ سَبْعَ طَرَائِقَ وَمَا كُنَّا عَنِ الْخَلْقِ غَافِلِينَ (17) Ife tidalenga miyamba isanu ndi iwiri pamwamba panu ndipo kwa zolengedwa zathu. Ndipo Ife sitikhala osalabadira ayi |
وَأَنزَلْنَا مِنَ السَّمَاءِ مَاءً بِقَدَرٍ فَأَسْكَنَّاهُ فِي الْأَرْضِ ۖ وَإِنَّا عَلَىٰ ذَهَابٍ بِهِ لَقَادِرُونَ (18) Ife timatumiza madzi kuchokera kumwamba m’muyeso wokwana ndipo timawalowetsa pansi pa nthaka. Ndipo Ife tili ndi mphamvu yowachotsa madziwo |
فَأَنشَأْنَا لَكُم بِهِ جَنَّاتٍ مِّن نَّخِيلٍ وَأَعْنَابٍ لَّكُمْ فِيهَا فَوَاكِهُ كَثِيرَةٌ وَمِنْهَا تَأْكُلُونَ (19) Ndipo Ife timakutulutsirani mmenemo minda ya tende ndi mphesa, m’mene muli zipatso zanu zambiri zimene zina mwa izo mumadya |
وَشَجَرَةً تَخْرُجُ مِن طُورِ سَيْنَاءَ تَنبُتُ بِالدُّهْنِ وَصِبْغٍ لِّلْآكِلِينَ (20) Mtengo umene umamera pa phiri la Sinai, umapereka mafuta ndiponso ndiwo kwa anthu |
وَإِنَّ لَكُمْ فِي الْأَنْعَامِ لَعِبْرَةً ۖ نُّسْقِيكُم مِّمَّا فِي بُطُونِهَا وَلَكُمْ فِيهَا مَنَافِعُ كَثِيرَةٌ وَمِنْهَا تَأْكُلُونَ (21) M’nyama namonso muli chizindikiro choonetsa mphamvu zathu. Inu timakumwetsani zimene zili m’mimba mwake ndipo mumadya nyama yake ndiponso mumapeza phindu lambiri |
وَعَلَيْهَا وَعَلَى الْفُلْكِ تُحْمَلُونَ (22) Ndipo pa izo ndi m’zombo zimene zimayenda pa nyanja, inu mumanyamulidwa |
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوْمِهِ فَقَالَ يَا قَوْمِ اعْبُدُوا اللَّهَ مَا لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرُهُ ۖ أَفَلَا تَتَّقُونَ (23) Tidamutumiza Nowa kwa anthu ake ndipo iye adati, “Tumikirani Mulungu anthu anga chifukwa mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Iye?” |
فَقَالَ الْمَلَأُ الَّذِينَ كَفَرُوا مِن قَوْمِهِ مَا هَٰذَا إِلَّا بَشَرٌ مِّثْلُكُمْ يُرِيدُ أَن يَتَفَضَّلَ عَلَيْكُمْ وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ لَأَنزَلَ مَلَائِكَةً مَّا سَمِعْنَا بِهَٰذَا فِي آبَائِنَا الْأَوَّلِينَ (24) Akuluakulu osakhulupirira a anthu ake adati, “Munthu uyu ndi wolingana ndi inu, iye ali kungodziyenereza kuti ndi wopambana pakati panu.” Mulungu akadafuna, akadatumiza angelo. Ndiponso zinthu za mtundu uwu sitidamvepo kuchokera kwa makolo athu akalekale |
إِنْ هُوَ إِلَّا رَجُلٌ بِهِ جِنَّةٌ فَتَرَبَّصُوا بِهِ حَتَّىٰ حِينٍ (25) Ndithudi ameneyu ndi wopenga, ndipo mumuyang’anire pa kanthawi.” |
قَالَ رَبِّ انصُرْنِي بِمَا كَذَّبُونِ (26) Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kundikana.” |
فَأَوْحَيْنَا إِلَيْهِ أَنِ اصْنَعِ الْفُلْكَ بِأَعْيُنِنَا وَوَحْيِنَا فَإِذَا جَاءَ أَمْرُنَا وَفَارَ التَّنُّورُ ۙ فَاسْلُكْ فِيهَا مِن كُلٍّ زَوْجَيْنِ اثْنَيْنِ وَأَهْلَكَ إِلَّا مَن سَبَقَ عَلَيْهِ الْقَوْلُ مِنْهُمْ ۖ وَلَا تُخَاطِبْنِي فِي الَّذِينَ ظَلَمُوا ۖ إِنَّهُم مُّغْرَقُونَ (27) Ife tidavumbulutsa chifuniro chathu kwa iye ponena kuti, “Khoma chombo chimene Ife tidzayang’anira molingana ndi chilangizo chathu. Pamene chiweruzo chathu chidza ndipo madzi asefukira kuchokera ku ng’anjo, utenge zolengedwa ziwiriziwiri, zazimuna ndi zazikazi ndiponso kuchokera kwa iwo a m’nyumba mwako kupatula okhawo amene adanenedwa kuti adzaonongeka. Usandipemphe kuti ndipulumutse iwo amene adachita zoipa chifukwa iwo adzamizidwa.” |
فَإِذَا اسْتَوَيْتَ أَنتَ وَمَن مَّعَكَ عَلَى الْفُلْكِ فَقُلِ الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي نَجَّانَا مِنَ الْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (28) Ndipo pamene iwe ndi iwo amene akutsata iwe mulowa m’chombo, nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu amene watipulumutsa ife kuchoka ku mtundu wa anthu oipa.” |
وَقُل رَّبِّ أَنزِلْنِي مُنزَلًا مُّبَارَكًا وَأَنتَ خَيْرُ الْمُنزِلِينَ (29) Ndipo nena: “Ambuye wanga! Ndithandizeni kuti ndikafike pamalo podalitsika chifukwa Inu ndinu wabwino wa onse amene amafikitsa pamalo okocheza.” |
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ وَإِن كُنَّا لَمُبْتَلِينَ (30) Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro zooneka. Ndithudi Ife timawaika anthu m’mayesero |
ثُمَّ أَنشَأْنَا مِن بَعْدِهِمْ قَرْنًا آخَرِينَ (31) Potero Ife tidapanga mtundu wa anthu a tsopano pambuyo pawo |
فَأَرْسَلْنَا فِيهِمْ رَسُولًا مِّنْهُمْ أَنِ اعْبُدُوا اللَّهَ مَا لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرُهُ ۖ أَفَلَا تَتَّقُونَ (32) Ndipo tidatumiza kwa iwo Mtumwi wa mtundu wawo amene adati, “Tumikirani Mulungu chifukwa inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Mulungu?” |
وَقَالَ الْمَلَأُ مِن قَوْمِهِ الَّذِينَ كَفَرُوا وَكَذَّبُوا بِلِقَاءِ الْآخِرَةِ وَأَتْرَفْنَاهُمْ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا مَا هَٰذَا إِلَّا بَشَرٌ مِّثْلُكُمْ يَأْكُلُ مِمَّا تَأْكُلُونَ مِنْهُ وَيَشْرَبُ مِمَّا تَشْرَبُونَ (33) Koma akuluakulu a anthu osakhulupirira a anthu ake, amene adakana za moyo umene uli nkudza ndi amene tidawapatsa zinthu zabwino za m’moyo uno adati, “Munthu uyu ndi munthu monga inu nomwe amene akudya zimene mumadya inu ndi kumwa zimene inu mumamwa.” |
وَلَئِنْ أَطَعْتُم بَشَرًا مِّثْلَكُمْ إِنَّكُمْ إِذًا لَّخَاسِرُونَ (34) “Ngati inu mumvera munthu wonga inu nomwe, ndithudi, inu mudzatayika.” |
أَيَعِدُكُمْ أَنَّكُمْ إِذَا مِتُّمْ وَكُنتُمْ تُرَابًا وَعِظَامًا أَنَّكُم مُّخْرَجُونَ (35) “Kodi iye ali kukuopsezani kuti pamene inu mutafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa mudzadzuka ndi kukhalanso ndi moyo?” |
۞ هَيْهَاتَ هَيْهَاتَ لِمَا تُوعَدُونَ (36) “Zimene inu muli kuopsezedwa nazo zili kutali.” |
إِنْ هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا الدُّنْيَا نَمُوتُ وَنَحْيَا وَمَا نَحْنُ بِمَبْعُوثِينَ (37) “Kulibenso moyo wina koma moyo wathu wapadziko lapansi basi. Ife timafa ndi kukhala ndi moyo ndipo ife sitidzadzukanso ayi.” |
إِنْ هُوَ إِلَّا رَجُلٌ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا وَمَا نَحْنُ لَهُ بِمُؤْمِنِينَ (38) “Munthu uyu ndi odziyenereza amene ali kunena za Mulungu zimene sizili zoona ayi. Ife sitidzamukhulupirira.” |
قَالَ رَبِّ انصُرْنِي بِمَا كَذَّبُونِ (39) Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kunditsutsa.” |
قَالَ عَمَّا قَلِيلٍ لَّيُصْبِحُنَّ نَادِمِينَ (40) Iye adati, “Posachedwapa iwo adzanong’oneza bombono.” |
فَأَخَذَتْهُمُ الصَّيْحَةُ بِالْحَقِّ فَجَعَلْنَاهُمْ غُثَاءً ۚ فَبُعْدًا لِّلْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (41) Chilango chathu chidawapeza mwachilungamo ndipo tidawafafaniza monga zinyalala. Chionongeko kwa anthu onse ochimwa |
ثُمَّ أَنشَأْنَا مِن بَعْدِهِمْ قُرُونًا آخَرِينَ (42) Atapita awa tidalenganso mitundu ina ya anthu |
مَا تَسْبِقُ مِنْ أُمَّةٍ أَجَلَهَا وَمَا يَسْتَأْخِرُونَ (43) Palibeanthuameneangafulumizitsekapenakuchedwetsa chionongeko chawo |
ثُمَّ أَرْسَلْنَا رُسُلَنَا تَتْرَىٰ ۖ كُلَّ مَا جَاءَ أُمَّةً رَّسُولُهَا كَذَّبُوهُ ۚ فَأَتْبَعْنَا بَعْضَهُم بَعْضًا وَجَعَلْنَاهُمْ أَحَادِيثَ ۚ فَبُعْدًا لِّقَوْمٍ لَّا يُؤْمِنُونَ (44) Ndipo Ife tidatumiza Atumwi ena motsagana ndipo nthawi iliyonse Mtumwi amadza kwa iwo ndipo amamukana nati ndi wabodza. Ndipo Ife tidawaononga ena pambuyo pawo ndipo tidawapanga iwo kukhala chitsanzo cha mbiri ya anthu olakwa. Ichi chidali chionongeko cha anthu osakhulupirira |
ثُمَّ أَرْسَلْنَا مُوسَىٰ وَأَخَاهُ هَارُونَ بِآيَاتِنَا وَسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (45) Ndipo Ife tidamutumiza Mose pamodzi ndi m’bale wake Aroni ndi zizindikiro ndiponso ulamuliro wathu |
إِلَىٰ فِرْعَوْنَ وَمَلَئِهِ فَاسْتَكْبَرُوا وَكَانُوا قَوْمًا عَالِينَ (46) Kwa Farawo ndi nduna zake ndipo iwo adawalandira mwamwano chifukwa iwo adali anthu a chipongwe |
فَقَالُوا أَنُؤْمِنُ لِبَشَرَيْنِ مِثْلِنَا وَقَوْمُهُمَا لَنَا عَابِدُونَ (47) Ndipo iwo adati, “Kodi ife tikhulupirire anthu awiri olingana ndi ife amene anthu awo ndi akapolo athu?” |
فَكَذَّبُوهُمَا فَكَانُوا مِنَ الْمُهْلَكِينَ (48) Iwo adawakana iwo kotero iwo adalandira chionongeko |
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ لَعَلَّهُمْ يَهْتَدُونَ (49) Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku la Chipangano Chakale kuti anthu ake akhoza kutsogozedwa bwino |
وَجَعَلْنَا ابْنَ مَرْيَمَ وَأُمَّهُ آيَةً وَآوَيْنَاهُمَا إِلَىٰ رَبْوَةٍ ذَاتِ قَرَارٍ وَمَعِينٍ (50) Ife tidamupanga mwana wamwamuna wa Maria pamodzi ndi amayi ake kukhala chizindikiro kwa anthu onse ndipo tidawapatsa mnthunzi pa malo okwera ndi malo a mtendere amene anali kuthiriridwa ndi madzi a pa kasupe |
يَا أَيُّهَا الرُّسُلُ كُلُوا مِنَ الطَّيِّبَاتِ وَاعْمَلُوا صَالِحًا ۖ إِنِّي بِمَا تَعْمَلُونَ عَلِيمٌ (51) Oh Atumwi! Idyani zinthu zabwino ndipo muzichita ntchito zabwino. Ndithudi Ine ndimadziwa zonse zimene mumachita |
وَإِنَّ هَٰذِهِ أُمَّتُكُمْ أُمَّةً وَاحِدَةً وَأَنَا رَبُّكُمْ فَاتَّقُونِ (52) Ndithudi chipembedzo chanu ndi chimodzi ndipo Ine ndine Ambuye wanu. Kotero ndiopeni Ine |
فَتَقَطَّعُوا أَمْرَهُم بَيْنَهُمْ زُبُرًا ۖ كُلُّ حِزْبٍ بِمَا لَدَيْهِمْ فَرِحُونَ (53) Koma anthu adagawanika m’magulu osiyanasiyana, gulu lililonse limasangalala ndi ziphunzitso zawo |
فَذَرْهُمْ فِي غَمْرَتِهِمْ حَتَّىٰ حِينٍ (54) Alekeni ayambe achimwa mpaka pamene imfa iwapeza |
أَيَحْسَبُونَ أَنَّمَا نُمِدُّهُم بِهِ مِن مَّالٍ وَبَنِينَ (55) Kodi iwo amaganiza kuti popeza tawapatsa chuma ndi ana |
نُسَارِعُ لَهُمْ فِي الْخَيْرَاتِ ۚ بَل لَّا يَشْعُرُونَ (56) Ndiye kuti Ife tili kuwafunira zabwino? Iyayi. Iwo sadziwa kanthu ayi |
إِنَّ الَّذِينَ هُم مِّنْ خَشْيَةِ رَبِّهِم مُّشْفِقُونَ (57) Ndithudi iwo ndi anthu amene amaopa Ambuye wawo |
وَالَّذِينَ هُم بِآيَاتِ رَبِّهِمْ يُؤْمِنُونَ (58) Amene amakhulupirira zizindikiro za Ambuye wawo |
وَالَّذِينَ هُم بِرَبِّهِمْ لَا يُشْرِكُونَ (59) Amene sapembedza wina aliyense poonjezera pa Ambuye wawo |
وَالَّذِينَ يُؤْتُونَ مَا آتَوا وَّقُلُوبُهُمْ وَجِلَةٌ أَنَّهُمْ إِلَىٰ رَبِّهِمْ رَاجِعُونَ (60) Amene amapereka chaulere mitima ili yoopa Ambuye wawo chifukwa chakuti adzabwerera kwa Iye |
أُولَٰئِكَ يُسَارِعُونَ فِي الْخَيْرَاتِ وَهُمْ لَهَا سَابِقُونَ (61) Awa ndiwo amene amapikisana wina ndi mnzake pochita zabwino ndipo amakhala oyamba pozindikira |
وَلَا نُكَلِّفُ نَفْسًا إِلَّا وُسْعَهَا ۖ وَلَدَيْنَا كِتَابٌ يَنطِقُ بِالْحَقِّ ۚ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (62) Ife sitinyamulitsa mzimu wina uliwonse katundu amene iwo sangathe kunyamula. M’buku lathu mudalembedwa zoona zokhazokha. Ndipo palibe munthu amene adzaponderezedwa |
بَلْ قُلُوبُهُمْ فِي غَمْرَةٍ مِّنْ هَٰذَا وَلَهُمْ أَعْمَالٌ مِّن دُونِ ذَٰلِكَ هُمْ لَهَا عَامِلُونَ (63) Koma mitima ya anthu osakhulupirira siyizidziwa zimenezi ayi. Iwo ali ndi ntchito zina zoipa kupatula zimene iwo amachita |
حَتَّىٰ إِذَا أَخَذْنَا مُتْرَفِيهِم بِالْعَذَابِ إِذَا هُمْ يَجْأَرُونَ (64) Koma pamene chilango chathu chidza pa iwo amene amakhala mu mtendere, iwo adzafuula kufuna chithandizo |
لَا تَجْأَرُوا الْيَوْمَ ۖ إِنَّكُم مِّنَّا لَا تُنصَرُونَ (65) Musalire tsiku la lero chifukwa inu simudzalandira chithandizo china chilichonse kuchokera kwa Ife |
قَدْ كَانَتْ آيَاتِي تُتْلَىٰ عَلَيْكُمْ فَكُنتُمْ عَلَىٰ أَعْقَابِكُمْ تَنكِصُونَ (66) Chivumbulutso changa chinali kulakatulidwa kwa inu nthawi zambiri koma inu munali kuthawa ndi kuchikana mwamwano |
مُسْتَكْبِرِينَ بِهِ سَامِرًا تَهْجُرُونَ (67) Inu mumachinyoza usana ndi usiku uliwonse |
أَفَلَمْ يَدَّبَّرُوا الْقَوْلَ أَمْ جَاءَهُم مَّا لَمْ يَأْتِ آبَاءَهُمُ الْأَوَّلِينَ (68) Kodi iwo sangathe kulingalira mozama pa mawu a Mulungu kapena pali china chake chimene chidavumbulutsidwa kwa iwo chimene sichidavumbulutsidwe kwa makolo awo |
أَمْ لَمْ يَعْرِفُوا رَسُولَهُمْ فَهُمْ لَهُ مُنكِرُونَ (69) Kapena iwo sadziwa kuti akukana Mtumwi wawo |
أَمْ يَقُولُونَ بِهِ جِنَّةٌ ۚ بَلْ جَاءَهُم بِالْحَقِّ وَأَكْثَرُهُمْ لِلْحَقِّ كَارِهُونَ (70) Kapena iwo akuti Iye ndi wopenga? Koma iye wawabweretsera iwo onse zoonadi. Koma ambiri amakana choonadi |
وَلَوِ اتَّبَعَ الْحَقُّ أَهْوَاءَهُمْ لَفَسَدَتِ السَّمَاوَاتُ وَالْأَرْضُ وَمَن فِيهِنَّ ۚ بَلْ أَتَيْنَاهُم بِذِكْرِهِمْ فَهُمْ عَن ذِكْرِهِم مُّعْرِضُونَ (71) Kukadakhala kuti choonadi chimatsatira zofuna zawo, ndithudi, kumwamba, dziko lapansi ndi onse okhala m’menemo akadaonongeka. Ife tawapatsa chikumbutso komabe iwo safuna kumvera chikumbutsocho |
أَمْ تَسْأَلُهُمْ خَرْجًا فَخَرَاجُ رَبِّكَ خَيْرٌ ۖ وَهُوَ خَيْرُ الرَّازِقِينَ (72) Kapena iwe uli kuwapemphera mphotho? Chithandizo cha Ambuye wawo ndicho chabwino. Ndipo Iye ndiye wopereka moolowa manja kuposa onse amene amapereka |
وَإِنَّكَ لَتَدْعُوهُمْ إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (73) Ndithudi iwe uli kuwaitana kuti adze kunjira yoyenera |
وَإِنَّ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ عَنِ الصِّرَاطِ لَنَاكِبُونَ (74) Ndithudi iwo amene amakana moyo umene uli nkudza adzakhala ali kusochera ku njira yoyenerayi |
۞ وَلَوْ رَحِمْنَاهُمْ وَكَشَفْنَا مَا بِهِم مِّن ضُرٍّ لَّلَجُّوا فِي طُغْيَانِهِمْ يَعْمَهُونَ (75) Ngati Ife tikadawalangiza chisoni chathu ndi kuwachotsera mavuto, iwo akadakhala ali kulakwabe m’njira zawo zoipa ndi kusokonezeka ndi zoipazo |
وَلَقَدْ أَخَذْنَاهُم بِالْعَذَابِ فَمَا اسْتَكَانُوا لِرَبِّهِمْ وَمَا يَتَضَرَّعُونَ (76) Ndithudi tidawalanga kale koma iwo sadafunefune Ambuye wawo kapena kukhala odzichepetsa pamaso pake |
حَتَّىٰ إِذَا فَتَحْنَا عَلَيْهِم بَابًا ذَا عَذَابٍ شَدِيدٍ إِذَا هُمْ فِيهِ مُبْلِسُونَ (77) Mpaka pamene tidzawatsekulira khomo la chilango chowawa, iwo adzakhala okhumudwa |
وَهُوَ الَّذِي أَنشَأَ لَكُمُ السَّمْعَ وَالْأَبْصَارَ وَالْأَفْئِدَةَ ۚ قَلِيلًا مَّا تَشْكُرُونَ (78) Iye ndiye amene adakupatsani makutu, maso ndi mitima. Komabe inu simuthokoza mokwanira |
وَهُوَ الَّذِي ذَرَأَكُمْ فِي الْأَرْضِ وَإِلَيْهِ تُحْشَرُونَ (79) Iye ndiye amene adakulengani ndi kukuchulukitsani padziko lapansi ndipo nonsenu mudzasonkhanitsidwa kudza pamaso pake |
وَهُوَ الَّذِي يُحْيِي وَيُمِيتُ وَلَهُ اخْتِلَافُ اللَّيْلِ وَالنَّهَارِ ۚ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (80) Iye ndiye amene amapereka moyo ndiponso imfa ndipo ndi Iyenso amene amasithanitsa usiku ndi usana. Kodi simungazindikire |
بَلْ قَالُوا مِثْلَ مَا قَالَ الْأَوَّلُونَ (81) Iwo amanena zimene anthu akale ankanena |
قَالُوا أَإِذَا مِتْنَا وَكُنَّا تُرَابًا وَعِظَامًا أَإِنَّا لَمَبْعُوثُونَ (82) Iwo amati, “Pamene ife tafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa, kodi tidzadzukanso ndi kukhala ndi moyo?” |
لَقَدْ وُعِدْنَا نَحْنُ وَآبَاؤُنَا هَٰذَا مِن قَبْلُ إِنْ هَٰذَا إِلَّا أَسَاطِيرُ الْأَوَّلِينَ (83) Ndithudi ife tidalonjedzedwa zimenezi kale pamodzi ndi makolo athu. Izi si zina ayi koma nkhani zabodza za anthu a makedzana |
قُل لِّمَنِ الْأَرْضُ وَمَن فِيهَا إِن كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (84) Nena, “Kodi Mwini wake wa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo ndani? Ndiuzeni ngati mumudziwa.” |
سَيَقُولُونَ لِلَّهِ ۚ قُلْ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ (85) Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Kodi inu simungachenjezedwe?” |
قُلْ مَن رَّبُّ السَّمَاوَاتِ السَّبْعِ وَرَبُّ الْعَرْشِ الْعَظِيمِ (86) Nena, “Kodi Ambuye wa miyamba isanu ndi iwiri ndiponso Mwini Ufumu ndani?” |
سَيَقُولُونَ لِلَّهِ ۚ قُلْ أَفَلَا تَتَّقُونَ (87) Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Nanga kodi simungasiye kuchita zoipa?” |
قُلْ مَن بِيَدِهِ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيْءٍ وَهُوَ يُجِيرُ وَلَا يُجَارُ عَلَيْهِ إِن كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (88) Nena, “Kodi ulamuliro wa zinthu zonse zili m’manja mwa yani? Kodi ndani amene amaziteteza zonse pamene Iye safuna chitetezo cha wina aliyense ngati inu mukudziwa?” |
سَيَقُولُونَ لِلَّهِ ۚ قُلْ فَأَنَّىٰ تُسْحَرُونَ (89) Iwo adzati, “M’manja mwa Mulungu.” Nena, “Nanga ndi chifukwa chiyani inu mwanyengedwa?” |
بَلْ أَتَيْنَاهُم بِالْحَقِّ وَإِنَّهُمْ لَكَاذِبُونَ (90) Iyayi, Ife tawavumbulutsira choonadi. Koma onsewa ndi anthu abodza |
مَا اتَّخَذَ اللَّهُ مِن وَلَدٍ وَمَا كَانَ مَعَهُ مِنْ إِلَٰهٍ ۚ إِذًا لَّذَهَبَ كُلُّ إِلَٰهٍ بِمَا خَلَقَ وَلَعَلَا بَعْضُهُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ ۚ سُبْحَانَ اللَّهِ عَمَّا يَصِفُونَ (91) Palibe nthawi imene Mulungu adabala mwana ndipo kulibe Mulungu wina woonjezera pa Iye. Ngati izi zikadakhala choncho, bwezi Mulungu aliyense akumatenga zolengedwa zake zokha ndi kumaziika pamwamba pa zolengedwa za Mulungu wina. Ulemerero ukhale kwa Mulungu woposa zina zilizonse |
عَالِمِ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ فَتَعَالَىٰ عَمَّا يُشْرِكُونَ (92) Iye amadziwa zonse zooneka ndiponso zobisika. Mulungu akhale wopambana milungu ina imene iwo amaitumikira |
قُل رَّبِّ إِمَّا تُرِيَنِّي مَا يُوعَدُونَ (93) Nena, “Ambuye wanga! Ngati Inu mukadandionetsa chilango chimene muli kuwopseza |
رَبِّ فَلَا تَجْعَلْنِي فِي الْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (94) Ambuye wanga! Pulumutsani ndipo musandisiye ine pakati pa mtundu wa anthu oipawu.” |
وَإِنَّا عَلَىٰ أَن نُّرِيَكَ مَا نَعِدُهُمْ لَقَادِرُونَ (95) Ndithudi, Ife tili ndi mphamvu zoti ukhoza kuona chilango chimene tawaopseza |
ادْفَعْ بِالَّتِي هِيَ أَحْسَنُ السَّيِّئَةَ ۚ نَحْنُ أَعْلَمُ بِمَا يَصِفُونَ (96) Dzitetezeni ndi chabwino pothamangitsa choipa. Ife tili kudziwa zonse zimene ali kukunamizirani |
وَقُل رَّبِّ أَعُوذُ بِكَ مِنْ هَمَزَاتِ الشَّيَاطِينِ (97) Ndipo iwe unene kuti, “Ambuye wanga, Ine ndili kufuna chitetezo chanu pothawa zoipa za Satana.” |
وَأَعُوذُ بِكَ رَبِّ أَن يَحْضُرُونِ (98) “Ambuye! Ine ndili kupempha chitetezo chanu kuti asabwere kumene ndili ine.” |
حَتَّىٰ إِذَا جَاءَ أَحَدَهُمُ الْمَوْتُ قَالَ رَبِّ ارْجِعُونِ (99) Mpaka pamene imfa idza kwa munthu wolakwa iye adzati, “Ambuye wanga! Bwezeni.” |
لَعَلِّي أَعْمَلُ صَالِحًا فِيمَا تَرَكْتُ ۚ كَلَّا ۚ إِنَّهَا كَلِمَةٌ هُوَ قَائِلُهَا ۖ وَمِن وَرَائِهِم بَرْزَخٌ إِلَىٰ يَوْمِ يُبْعَثُونَ (100) “Kuti ndikachite ntchitozabwinozimenendidalepherakuchita.” Kosatheka! Amenewa ndiwo mawu chabe amene akungolankhula. Kumbuyo kwawo kudzakhala chipupa mpaka pa tsiku la kuuka kwa akufa |
فَإِذَا نُفِخَ فِي الصُّورِ فَلَا أَنسَابَ بَيْنَهُمْ يَوْمَئِذٍ وَلَا يَتَسَاءَلُونَ (101) Ndipo pamene lipenga lidzaombedwa, pa tsiku limeneli, ubale wawo wonse udzathera pomwepo ndiponso sadzafunsana chithandizo chochokera kwa wina ndi mnzake |
فَمَن ثَقُلَتْ مَوَازِينُهُ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (102) Aliyense amene muyeso wake udzakhala wolemera, adzapambana |
وَمَنْ خَفَّتْ مَوَازِينُهُ فَأُولَٰئِكَ الَّذِينَ خَسِرُوا أَنفُسَهُمْ فِي جَهَنَّمَ خَالِدُونَ (103) Koma aliyense amene muyeso wake udzakhala wopepuka adzataya moyo wake ndipo adzakhala ku Gahena nthawi zonse |
تَلْفَحُ وُجُوهَهُمُ النَّارُ وَهُمْ فِيهَا كَالِحُونَ (104) Moto udzatentha nkhope zawo ndipo izo zidzakwinyikakwinyika chifukwa chaululu |
أَلَمْ تَكُنْ آيَاتِي تُتْلَىٰ عَلَيْكُمْ فَكُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ (105) “Kodi chivumbulutso chathu sichidalakatulidwe kwa inu? Kodi simudachikane?” |
قَالُوا رَبَّنَا غَلَبَتْ عَلَيْنَا شِقْوَتُنَا وَكُنَّا قَوْمًا ضَالِّينَ (106) Iwo adzati, “Ambuye wathu! Zilakolako zathu zidatigonjetsa ife ndipo tidali anthu osochera.” |
رَبَّنَا أَخْرِجْنَا مِنْهَا فَإِنْ عُدْنَا فَإِنَّا ظَالِمُونَ (107) “Ambuye wathu! tipulumutseni ife ku ichi. Ngati ife tidzabwereranso ku zoipa, ndithudi, ife tidzakhala anthu oipa kwambiri.” |
قَالَ اخْسَئُوا فِيهَا وَلَا تُكَلِّمُونِ (108) Iye adzati, “Khalani mu icho mwamanyazi ndipo musandiyankhulitse Ine ayi.” |
إِنَّهُ كَانَ فَرِيقٌ مِّنْ عِبَادِي يَقُولُونَ رَبَّنَا آمَنَّا فَاغْفِرْ لَنَا وَارْحَمْنَا وَأَنتَ خَيْرُ الرَّاحِمِينَ (109) Ndithudi padali gulu la Atumiki anga amene adati, “Ambuye wathu! Ife timakhulupirira mwa inu. Tikhululukireni ndipo mutichitire chisoni. Inu ndinu wabwino pochita chisoni kuposa a chisoni onse.” |
فَاتَّخَذْتُمُوهُمْ سِخْرِيًّا حَتَّىٰ أَنسَوْكُمْ ذِكْرِي وَكُنتُم مِّنْهُمْ تَضْحَكُونَ (110) Koma inu munali kuwanyogodola mpaka pamene inu mudandiiwala Ine ndipo inu munali kuwaseka iwo |
إِنِّي جَزَيْتُهُمُ الْيَوْمَ بِمَا صَبَرُوا أَنَّهُمْ هُمُ الْفَائِزُونَ (111) Ndithudi lero Ine ndawalipira chifukwa cha kupirira kwawo ndipo iwo ndi amene apambana |
قَالَ كَمْ لَبِثْتُمْ فِي الْأَرْضِ عَدَدَ سِنِينَ (112) Ndipo Iye adzafunsa kuti, “Kodi inu munakhala padziko lapansi zaka zingati?” |
قَالُوا لَبِثْنَا يَوْمًا أَوْ بَعْضَ يَوْمٍ فَاسْأَلِ الْعَادِّينَ (113) Iwo adzayankha kuti, “Takhala tsiku limodzi kapena mphindi zochepa zokha. Afunseni iwo amene amasunga chiwerengero.” |
قَالَ إِن لَّبِثْتُمْ إِلَّا قَلِيلًا ۖ لَّوْ أَنَّكُمْ كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (114) Iye adzawayankha kuti, “Inu mukadadziwa ndi nthawi yochepa kwambiri imene inu munakhala.” |
أَفَحَسِبْتُمْ أَنَّمَا خَلَقْنَاكُمْ عَبَثًا وَأَنَّكُمْ إِلَيْنَا لَا تُرْجَعُونَ (115) “Kodi inu mumaganiza kuti tidangokulengani inu opanda cholinga ndipo kuti simudzabwerera kwa Ife?” |
فَتَعَالَى اللَّهُ الْمَلِكُ الْحَقُّ ۖ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ رَبُّ الْعَرْشِ الْكَرِيمِ (116) Motero alemekezeke Mulungu, Mfumu ya chilungamo. Palibe Mulungu wina koma Iye yekha, Ambuye wa Mpando wolemekezeka ndi Wachifumu |
وَمَن يَدْعُ مَعَ اللَّهِ إِلَٰهًا آخَرَ لَا بُرْهَانَ لَهُ بِهِ فَإِنَّمَا حِسَابُهُ عِندَ رَبِّهِ ۚ إِنَّهُ لَا يُفْلِحُ الْكَافِرُونَ (117) Aliyense amene apembedza mulungu wina woonjezera pa Mulungu, pamene Iye alibe umboni wa chimenecho, Ambuye wake adzamufunsa. Ndithudi anthu osakhulupirira sadzapambana ayi |
وَقُل رَّبِّ اغْفِرْ وَارْحَمْ وَأَنتَ خَيْرُ الرَّاحِمِينَ (118) Nena, “Ambuye wanga! Ndikhululukireni machimo anga ndipo mundichitire chisoni chifukwa Inu ndinu wachisoni choposa a chisoni onse.” |