عَمَّ يَتَسَاءَلُونَ (1) Kodi akufunsana nkhani zotani |
عَنِ النَّبَإِ الْعَظِيمِ (2) Ali kufunsana za nkhani ija yaikulu |
الَّذِي هُمْ فِيهِ مُخْتَلِفُونَ (3) Nkhani imene akusiyana maganizo pakati pawo |
كَلَّا سَيَعْلَمُونَ (4) Iyayi, iwo adzadziwa posachedwa |
ثُمَّ كَلَّا سَيَعْلَمُونَ (5) Iyayi, iwo adzadziwa posachedwapa |
أَلَمْ نَجْعَلِ الْأَرْضَ مِهَادًا (6) Kodi Ife sitidapange dziko lapansi monga ngati kama |
وَالْجِبَالَ أَوْتَادًا (7) Ndi mapiri ngati zikhomo |
وَخَلَقْنَاكُمْ أَزْوَاجًا (8) Ndipo Ife tidakulengani inu awiri awiri |
وَجَعَلْنَا نَوْمَكُمْ سُبَاتًا (9) Ndipo tidapanga tulo kukhala ngati mpumulo wanu |
وَجَعَلْنَا اللَّيْلَ لِبَاسًا (10) Ndipo tidapanga usiku kukhala chophimba |
وَجَعَلْنَا النَّهَارَ مَعَاشًا (11) Ndipo tinapanga usana kukhala kopezera zofuna zanu |
وَبَنَيْنَا فَوْقَكُمْ سَبْعًا شِدَادًا (12) Ndipo tidamanga mlengalenga miyamba isanu ndi iwiri |
وَجَعَلْنَا سِرَاجًا وَهَّاجًا (13) Ndipo tidakhazikitsa mmenemo nyali yowala |
وَأَنزَلْنَا مِنَ الْمُعْصِرَاتِ مَاءً ثَجَّاجًا (14) Ndipo tidatumiza mvula yambiri kuchokera ku mitambo ya mvula |
لِّنُخْرِجَ بِهِ حَبًّا وَنَبَاتًا (15) Kuti timeretse chakudya ndi mbewu |
وَجَنَّاتٍ أَلْفَافًا (16) Ndipo minda ya zomera zothinana |
إِنَّ يَوْمَ الْفَصْلِ كَانَ مِيقَاتًا (17) Ndithudi tsiku la chiweruzo lidakhazikitsidwa kale |
يَوْمَ يُنفَخُ فِي الصُّورِ فَتَأْتُونَ أَفْوَاجًا (18) Tsiku limene lipenga lidzalira ndipo inu mudzadza mu magulumagulu |
وَفُتِحَتِ السَّمَاءُ فَكَانَتْ أَبْوَابًا (19) Ndipomumlengalengamudzatsegulidwa ndipo mudzakhala ngati makomo |
وَسُيِّرَتِ الْجِبَالُ فَكَانَتْ سَرَابًا (20) Ndipo mapiri onse adzayendetsedwa ndi kukhala ngati nthunzi yamadzi |
إِنَّ جَهَنَّمَ كَانَتْ مِرْصَادًا (21) Ndithudi Gahena ili kuwayembekezera |
لِّلطَّاغِينَ مَآبًا (22) Mudzi wa anthu ophwanya malamulo |
لَّابِثِينَ فِيهَا أَحْقَابًا (23) Kumeneko ndiko kumene adzakhale mpaka kalekale |
لَّا يَذُوقُونَ فِيهَا بَرْدًا وَلَا شَرَابًا (24) Kumeneko sadzalawa chozizira kapena kumwa china chilichonse |
إِلَّا حَمِيمًا وَغَسَّاقًا (25) Kupatula Al-Naba 637 madzi owira ndi mafinya |
جَزَاءً وِفَاقًا (26) Mphotho yoyeneradi |
إِنَّهُمْ كَانُوا لَا يَرْجُونَ حِسَابًا (27) Chifukwa, ndithudi, iwo sanali kuopa chidzudzulo chathu |
وَكَذَّبُوا بِآيَاتِنَا كِذَّابًا (28) Ndipo iwo moyerekedwa anali kukana chivumbulutso chathu |
وَكُلَّ شَيْءٍ أَحْصَيْنَاهُ كِتَابًا (29) Ndipo Ife tidalemba m’Buku zonse zimene anali kuchita |
فَذُوقُوا فَلَن نَّزِيدَكُمْ إِلَّا عَذَابًا (30) Motero inu lawani! Inu simudzalandira china chilichonse koma manzunzo ochuluka |
إِنَّ لِلْمُتَّقِينَ مَفَازًا (31) Ndithudi kwa anthu oopa Mulungu kudzakhala kupambana |
حَدَائِقَ وَأَعْنَابًا (32) Minda ndi m’minda ya mphesa |
وَكَوَاعِبَ أَتْرَابًا (33) Ndi a namwali akulu akulu ofanana zaka |
وَكَأْسًا دِهَاقًا (34) Ndi chikho chodzadza |
لَّا يَسْمَعُونَ فِيهَا لَغْوًا وَلَا كِذَّابًا (35) Kumeneko iwo sadzamva mawu opanda pake kapena nkhani zabodza |
جَزَاءً مِّن رَّبِّكَ عَطَاءً حِسَابًا (36) Imeneyi ndiyo mphotho yochokera kwa Ambuye wako ndipo ndi mphotho yokwanira |
رَّبِّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا الرَّحْمَٰنِ ۖ لَا يَمْلِكُونَ مِنْهُ خِطَابًا (37) Ambuye wa Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, Mwini chisoni chosatha ndipo iwo sadzatha kulankhula naye |
يَوْمَ يَقُومُ الرُّوحُ وَالْمَلَائِكَةُ صَفًّا ۖ لَّا يَتَكَلَّمُونَ إِلَّا مَنْ أَذِنَ لَهُ الرَّحْمَٰنُ وَقَالَ صَوَابًا (38) Patsiku limene Mzimu ndi angelo adzaima pa mizere ndipo palibe amene adzalankhula kupatula yekhayo amene adzalandira chilolezo cha Mwini chifundo chosatha ndipo adzanena chinthu chimene chili choona |
ذَٰلِكَ الْيَوْمُ الْحَقُّ ۖ فَمَن شَاءَ اتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِ مَآبًا (39) Ndithudi tsiku limeneli ndi loona, motero iye amene afuna, mulekeni atsatire njira yobwerera kwa Ambuye wake |
إِنَّا أَنذَرْنَاكُمْ عَذَابًا قَرِيبًا يَوْمَ يَنظُرُ الْمَرْءُ مَا قَدَّمَتْ يَدَاهُ وَيَقُولُ الْكَافِرُ يَا لَيْتَنِي كُنتُ تُرَابًا (40) Ndithudi takuchenjezani za chilango chowawa chimene chili nkudza posachedwa. Tsiku limene munthu adzayang’ana ntchito zimene manja ake adatsogoza, ndipo osakhulupirira adzati: “Kalanga ine, ndikanakhala dothi.” |