هَلْ أَتَىٰ عَلَى الْإِنسَانِ حِينٌ مِّنَ الدَّهْرِ لَمْ يَكُن شَيْئًا مَّذْكُورًا (1) Kodi sipadali nthawi imene munthu sanali kanthu kena kali konse kodziwika |
إِنَّا خَلَقْنَا الْإِنسَانَ مِن نُّطْفَةٍ أَمْشَاجٍ نَّبْتَلِيهِ فَجَعَلْنَاهُ سَمِيعًا بَصِيرًا (2) Ndithudi Ife tidamulenga munthu kuchokera ku madontho a umuna umene unasakanizidwa ndi ukazi ndi cholinga chomuyesa motero Ife tidamupanga iye kukhala wakumva ndi woona |
إِنَّا هَدَيْنَاهُ السَّبِيلَ إِمَّا شَاكِرًا وَإِمَّا كَفُورًا (3) Ndithudi Ife tamulangiza njira yabwino kaya iye akhala wothokoza kapena wosathokoza |
إِنَّا أَعْتَدْنَا لِلْكَافِرِينَ سَلَاسِلَ وَأَغْلَالًا وَسَعِيرًا (4) Ndithudi tawakonzera anthu osakhulupirira unyolo ndi magoli ndi moto wa lawilawi |
إِنَّ الْأَبْرَارَ يَشْرَبُونَ مِن كَأْسٍ كَانَ مِزَاجُهَا كَافُورًا (5) Ndithudi anthu onse angwiro adzamwa chakumwa chosakanizidwa ndi madzi ochokera pa kasupe wa ku Paradiso chotchedwa Kafur |
عَيْنًا يَشْرَبُ بِهَا عِبَادُ اللَّهِ يُفَجِّرُونَهَا تَفْجِيرًا (6) Kasupe amene akapolo a Mulungu adzamwapo, amene amatumphutsa madzi ochuluka |
يُوفُونَ بِالنَّذْرِ وَيَخَافُونَ يَوْمًا كَانَ شَرُّهُ مُسْتَطِيرًا (7) Iwo amene amakwaniritsa malonjezo awo ndipo amakhala ndi mantha ndi tsiku limene zoipa zidzasefukira ponseponse |
وَيُطْعِمُونَ الطَّعَامَ عَلَىٰ حُبِّهِ مِسْكِينًا وَيَتِيمًا وَأَسِيرًا (8) Ndipo amapereka chakudya chifukwa cha chikondi cha Mulungu, kwa anthu aumphawi, amasiye ndi kwa akaidi |
إِنَّمَا نُطْعِمُكُمْ لِوَجْهِ اللَّهِ لَا نُرِيدُ مِنكُمْ جَزَاءً وَلَا شُكُورًا (9) Ife tili kukudyetsani chifukwa cha Mulungu basi. Ife sitifuna malipiro kapena mayamiko kuchokera kwa inu |
إِنَّا نَخَافُ مِن رَّبِّنَا يَوْمًا عَبُوسًا قَمْطَرِيرًا (10) Ndithudi ife tiopa tsiku loopsa ndi laululu limene lidzasanduliza nkhope kuoneka monyasa, limene lili nkudza kuchokera kwa Ambuye wathu |
فَوَقَاهُمُ اللَّهُ شَرَّ ذَٰلِكَ الْيَوْمِ وَلَقَّاهُمْ نَضْرَةً وَسُرُورًا (11) Motero Mulungu awapulumutsa iwo ku zoipa za tsiku limeneli ndi kuwapatsa nyali yokongola kuti akhale mosavutika ndi mwachisangalalo |
وَجَزَاهُم بِمَا صَبَرُوا جَنَّةً وَحَرِيرًا (12) Ndipo mphotho yawo idzakhala munda wa Paradiso ndi zovala za silika chifukwa chopirira kwawo |
مُّتَّكِئِينَ فِيهَا عَلَى الْأَرَائِكِ ۖ لَا يَرَوْنَ فِيهَا شَمْسًا وَلَا زَمْهَرِيرًا (13) Ali kukhala m’Paradiso, pamipando yawofowofo, iwo sadzamva kutentha kwa dzuwa kapena kuzizira kwambiri |
وَدَانِيَةً عَلَيْهِمْ ظِلَالُهَا وَذُلِّلَتْ قُطُوفُهَا تَذْلِيلًا (14) Ndipo mithunzi idzakhala pafupi ndi iwo ndipo zipatso zidzalendewera mu matsanzi kuti asamavutike pothyola |
وَيُطَافُ عَلَيْهِم بِآنِيَةٍ مِّن فِضَّةٍ وَأَكْوَابٍ كَانَتْ قَوَارِيرَا (15) Ndipo pakati pawo padzaperekedwa zikho zozungulira za siliva ndi matambula a magalasi |
قَوَارِيرَ مِن فِضَّةٍ قَدَّرُوهَا تَقْدِيرًا (16) Matambula oonetsa zinthu zomwe zili m’kati mwake, opangidwa kuchokera ku siliva. Iwo adzathiramo chakumwa molingana ndi chilakolako chawo |
وَيُسْقَوْنَ فِيهَا كَأْسًا كَانَ مِزَاجُهَا زَنجَبِيلًا (17) Ndipo iwo adzapatsidwa chakumwa kuchokera mu zikho zodzala ndi madzi osakaniza ndi Zanjabil |
عَيْنًا فِيهَا تُسَمَّىٰ سَلْسَبِيلًا (18) Kasupe amene ali komweko wotchedwa Salsabil |
۞ وَيَطُوفُ عَلَيْهِمْ وِلْدَانٌ مُّخَلَّدُونَ إِذَا رَأَيْتَهُمْ حَسِبْتَهُمْ لُؤْلُؤًا مَّنثُورًا (19) Ndipo adzazunguliridwa ndi ana owatumikira a misinkhu yofanana. Ndipo ngati iwe utawaona ukhoza kuganiza kuti ndi ndolo zomwazikamwazika |
وَإِذَا رَأَيْتَ ثَمَّ رَأَيْتَ نَعِيمًا وَمُلْكًا كَبِيرًا (20) Ndipo pamene iwe uona kumeneko, udzaona madalitso ndi ufumu waukulu |
عَالِيَهُمْ ثِيَابُ سُندُسٍ خُضْرٌ وَإِسْتَبْرَقٌ ۖ وَحُلُّوا أَسَاوِرَ مِن فِضَّةٍ وَسَقَاهُمْ رَبُّهُمْ شَرَابًا طَهُورًا (21) Iwo adzavala nsalu zokongola za silika zooneka ngati msipu zopetedwa ndi golide. Iwo adzavala zibangiri za siliva ndipo Ambuye wawo adzawapatsa chakumwa chabwino |
إِنَّ هَٰذَا كَانَ لَكُمْ جَزَاءً وَكَانَ سَعْيُكُم مَّشْكُورًا (22) Ndithudi iyi ndi mphotho yanu ndipo kupirira kwanu kwalandiridwa |
إِنَّا نَحْنُ نَزَّلْنَا عَلَيْكَ الْقُرْآنَ تَنزِيلًا (23) Ndithudi ndife amene tavumbulutsa kwa iwe pang’ono pang’ono, Buku lolemekezeka la Korani |
فَاصْبِرْ لِحُكْمِ رَبِّكَ وَلَا تُطِعْ مِنْهُمْ آثِمًا أَوْ كَفُورًا (24) Motero pirira ndipo tsatira malamulo a Ambuye wako ndipo usamvere zonena za munthu wochimwa kapena wosakhulupirira amene ali pakati pawo |
وَاذْكُرِ اسْمَ رَبِّكَ بُكْرَةً وَأَصِيلًا (25) Ndipo uzilemekeza dzina la Ambuye wako m’mawa ndi madzulo |
وَمِنَ اللَّيْلِ فَاسْجُدْ لَهُ وَسَبِّحْهُ لَيْلًا طَوِيلًا (26) Ndi m’gawo lina la usiku, uzimupembedza Iye ndipo uzimulemekeza Iye usiku wonse |
إِنَّ هَٰؤُلَاءِ يُحِبُّونَ الْعَاجِلَةَ وَيَذَرُونَ وَرَاءَهُمْ يَوْمًا ثَقِيلًا (27) Ndithudi! Awa amakonda kwambiri moyo wa msanga msanga wa masiku ano, ndipo amaiwala tsiku limenelidzakhalalovuta |
نَّحْنُ خَلَقْنَاهُمْ وَشَدَدْنَا أَسْرَهُمْ ۖ وَإِذَا شِئْنَا بَدَّلْنَا أَمْثَالَهُمْ تَبْدِيلًا (28) Ndifeamenetidawalengandipo tinaika mphamvu m’ziwalo zawo. Koma ngati Ife titafuna, tikhoza kulenga anthu ena kuti alowe m’malo mwawo |
إِنَّ هَٰذِهِ تَذْكِرَةٌ ۖ فَمَن شَاءَ اتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِ سَبِيلًا (29) Ndithudi! Ili ndi chenjezo motero aliyense amene afuna, mulekeni kuti atsatire njira yoyenera yopita kwa Ambuye wake |
وَمَا تَشَاءُونَ إِلَّا أَن يَشَاءَ اللَّهُ ۚ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمًا (30) Koma inu simudzatha kutero pokhapokha ndi chifuniro cha Mulungu. Ndithudi Mulungu ndiye Mwini kudziwa ndi Mwini nzeru |
يُدْخِلُ مَن يَشَاءُ فِي رَحْمَتِهِ ۚ وَالظَّالِمِينَ أَعَدَّ لَهُمْ عَذَابًا أَلِيمًا (31) Iye adzaonetsa chisomo chake kwa aliyense amene Iye wamufuna. Koma anthu ochimwa, Iye wawakonzera iwo chilango chowawa |