×

سورة الفتح باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة الفتح

ترجمة معاني سورة الفتح باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة الفتح مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Al Fath in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة الفتح باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 29 - رقم السورة 48 - الصفحة 511.

بسم الله الرحمن الرحيم

إِنَّا فَتَحْنَا لَكَ فَتْحًا مُّبِينًا (1)
Ndithudi Ife takupambanitsa iwe,kupambana kwenikweni
لِّيَغْفِرَ لَكَ اللَّهُ مَا تَقَدَّمَ مِن ذَنبِكَ وَمَا تَأَخَّرَ وَيُتِمَّ نِعْمَتَهُ عَلَيْكَ وَيَهْدِيَكَ صِرَاطًا مُّسْتَقِيمًا (2)
Kuti Mulungu akukhululukire machimo ako akale ndi am’tsogolo omwe, ndi kumaliza ubwino wake pa iwe ndi kukutsogolera ku njira yoyenera
وَيَنصُرَكَ اللَّهُ نَصْرًا عَزِيزًا (3)
Ndikuti Mulungu athe kukuthandiza ndi chithandizo chokwanira
هُوَ الَّذِي أَنزَلَ السَّكِينَةَ فِي قُلُوبِ الْمُؤْمِنِينَ لِيَزْدَادُوا إِيمَانًا مَّعَ إِيمَانِهِمْ ۗ وَلِلَّهِ جُنُودُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا (4)
Ndiye amene adatumiza chisomo m’mitima mwa anthu okhulupirira kuti chikhulupiriro chawo chikhoza kukhala chokhazikika za Mulungu ndi zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi waluntha
لِّيُدْخِلَ الْمُؤْمِنِينَ وَالْمُؤْمِنَاتِ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا وَيُكَفِّرَ عَنْهُمْ سَيِّئَاتِهِمْ ۚ وَكَانَ ذَٰلِكَ عِندَ اللَّهِ فَوْزًا عَظِيمًا (5)
Kuti akhoza kulowetsa amuna ndi akazi okhulupirira ku minda imene pansi pake pali mitsinje yamadzi oyenda kuti akhale komweko mpaka kalekale ndi kuwakhululukira machimo awo ndipo pamaso pa Mulungu, ndiko kupambana kwenikweni kumeneku
وَيُعَذِّبَ الْمُنَافِقِينَ وَالْمُنَافِقَاتِ وَالْمُشْرِكِينَ وَالْمُشْرِكَاتِ الظَّانِّينَ بِاللَّهِ ظَنَّ السَّوْءِ ۚ عَلَيْهِمْ دَائِرَةُ السَّوْءِ ۖ وَغَضِبَ اللَّهُ عَلَيْهِمْ وَلَعَنَهُمْ وَأَعَدَّ لَهُمْ جَهَنَّمَ ۖ وَسَاءَتْ مَصِيرًا (6)
Ndipo akhoza kulanga anthu a chinyengo, aamuna ndi aakazi ndi anthu opembedza mafano, amuna ndi akazi amene amaganiza zoipa za Mulungu. Kwa iwo kudzadza mavuto ndipo mkwiyo wa Mulungu uli pa iwo. Iye wawatemberera iwo ndipo wakonzekera Gahena omwe ndi malo oipa kukhalako
وَلِلَّهِ جُنُودُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَكَانَ اللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمًا (7)
Mulungu zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Mulungu ndi wamphamvu ndi wa nzeru
إِنَّا أَرْسَلْنَاكَ شَاهِدًا وَمُبَشِّرًا وَنَذِيرًا (8)
Ndithudi takutumiza iwe ngati Mboni, ngati Wolalikira uthenga wabwino ndiponso ngati Mchenjezi
لِّتُؤْمِنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ وَتُعَزِّرُوهُ وَتُوَقِّرُوهُ وَتُسَبِّحُوهُ بُكْرَةً وَأَصِيلًا (9)
Ndi cholinga chakuti inu anthu mukhoza kukhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndi kuti mumuthandize ndi kumulemekeza iye ndipo kuti muzilemekeza Mulungu m’mawa ndi madzulo
إِنَّ الَّذِينَ يُبَايِعُونَكَ إِنَّمَا يُبَايِعُونَ اللَّهَ يَدُ اللَّهِ فَوْقَ أَيْدِيهِمْ ۚ فَمَن نَّكَثَ فَإِنَّمَا يَنكُثُ عَلَىٰ نَفْسِهِ ۖ وَمَنْ أَوْفَىٰ بِمَا عَاهَدَ عَلَيْهُ اللَّهَ فَسَيُؤْتِيهِ أَجْرًا عَظِيمًا (10)
Ndithudi onse amene amalumbira kuti ali pambuyo pako, iwo amalumbira kuti ali pambuyo pa Mulungu. Ndipo dzanja la Mulungu ndi loposa manja awo. Ndipo aliyense amene aphwanya lonjezo lake, Iye akungodzipondereza yekha ndipo aliyense amene akwaniritsa lonjezo limene adachita ndi Mulungu, Iye adzamulipira iye mphotho yopambana
سَيَقُولُ لَكَ الْمُخَلَّفُونَ مِنَ الْأَعْرَابِ شَغَلَتْنَا أَمْوَالُنَا وَأَهْلُونَا فَاسْتَغْفِرْ لَنَا ۚ يَقُولُونَ بِأَلْسِنَتِهِم مَّا لَيْسَ فِي قُلُوبِهِمْ ۚ قُلْ فَمَن يَمْلِكُ لَكُم مِّنَ اللَّهِ شَيْئًا إِنْ أَرَادَ بِكُمْ ضَرًّا أَوْ أَرَادَ بِكُمْ نَفْعًا ۚ بَلْ كَانَ اللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرًا (11)
Maarabu okhala m’chipululu amene adatsalira m’mbuyo adzati kwa iwe, “Ife tidatangwanika ndi chuma ndi mabanja athu, motero tipemphere chikhululukiro.” Iwo amangonena ndi milomo yawo zimene m’mitima mwawo mulibe. Nena, “Kodi ndani angakuyankhulireni inu kwa Mulungu ngati Iye atafuna kukuonongani kapena atafuna kuti akuchitireni zabwino? Iyayi, Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita.”
بَلْ ظَنَنتُمْ أَن لَّن يَنقَلِبَ الرَّسُولُ وَالْمُؤْمِنُونَ إِلَىٰ أَهْلِيهِمْ أَبَدًا وَزُيِّنَ ذَٰلِكَ فِي قُلُوبِكُمْ وَظَنَنتُمْ ظَنَّ السَّوْءِ وَكُنتُمْ قَوْمًا بُورًا (12)
Iyayi! Inu munali kuganiza kuti Mtumwi pamodzi ndi onse okhulupirira sadzabwerera ku mabanja awo ndipo zimenezo zinali zokusangalatsani inu ndipo inu munali kuganiza maganizo oipa ndipo inu munali anthu opanda pake opita ku chionongeko
وَمَن لَّمْ يُؤْمِن بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ فَإِنَّا أَعْتَدْنَا لِلْكَافِرِينَ سَعِيرًا (13)
Ndipo aliyense amene sakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake, ndithudi, Ife tawakonzera anthu osakhulupirira moto woyaka
وَلِلَّهِ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ يَغْفِرُ لِمَن يَشَاءُ وَيُعَذِّبُ مَن يَشَاءُ ۚ وَكَانَ اللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا (14)
wa Mulungu ndi Ufumu wakumwamba ndi padziko lapansi. Iye amakhululukirira amene wamufuna ndipo amalanga aliyense amene wamufuna. Ndipo Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha
سَيَقُولُ الْمُخَلَّفُونَ إِذَا انطَلَقْتُمْ إِلَىٰ مَغَانِمَ لِتَأْخُذُوهَا ذَرُونَا نَتَّبِعْكُمْ ۖ يُرِيدُونَ أَن يُبَدِّلُوا كَلَامَ اللَّهِ ۚ قُل لَّن تَتَّبِعُونَا كَذَٰلِكُمْ قَالَ اللَّهُ مِن قَبْلُ ۖ فَسَيَقُولُونَ بَلْ تَحْسُدُونَنَا ۚ بَلْ كَانُوا لَا يَفْقَهُونَ إِلَّا قَلِيلًا (15)
Iwo amene adatsala m’mbuyo adzati, pamene adzaona inu muli kukonzeka kukatenga katundu amene mwapeza pa nkhondo, “Tiloleni kuti tipite nanu.” Iwo afuna kusintha mawu a Mulungu. Nena, “Ndikosatheka! Inu simudzapita nafe. Mulungu ananena kale za inu.” Ndipo iwo adzati, “Iyayi! Inu muli kutichitira ife nsanje.” “Iyayi! Koma iwo sazindikira koma pang’ono pokha.”
قُل لِّلْمُخَلَّفِينَ مِنَ الْأَعْرَابِ سَتُدْعَوْنَ إِلَىٰ قَوْمٍ أُولِي بَأْسٍ شَدِيدٍ تُقَاتِلُونَهُمْ أَوْ يُسْلِمُونَ ۖ فَإِن تُطِيعُوا يُؤْتِكُمُ اللَّهُ أَجْرًا حَسَنًا ۖ وَإِن تَتَوَلَّوْا كَمَا تَوَلَّيْتُم مِّن قَبْلُ يُعَذِّبْكُمْ عَذَابًا أَلِيمًا (16)
Nena kwa iwo amene amakhala m’chipululu ndipo adakhalira m’mbuyo kuti, “Inu mudzaitanidwa, kuti mumenyane ndi anthu amphamvu kwambiri ndipo inu mudzamenyana nawo mpaka pamene adzagonja. Ndipo ngati inu mumvera, Mulungu adzakulipirani mphotho ya mtengo wapatali ndipo ngati inu muthawa, Iye adzakulangani inu ndi chilango chowawa.”
لَّيْسَ عَلَى الْأَعْمَىٰ حَرَجٌ وَلَا عَلَى الْأَعْرَجِ حَرَجٌ وَلَا عَلَى الْمَرِيضِ حَرَجٌ ۗ وَمَن يُطِعِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ يُدْخِلْهُ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ ۖ وَمَن يَتَوَلَّ يُعَذِّبْهُ عَذَابًا أَلِيمًا (17)
Palibe cholakwa kapena mlandu kwa wakhungu, kapena cholakwa kapena mlandu kwa wopunduka ndipo palibe cholakwa kapena mlandu kwa wodwala ngati iwo sapita nawo. Aliyense amene amvera Mulungu ndi Mtumwi wake, Mulungu adzamulandira ku minda imene ili ndi mitsinje yoyenda madzi pansi pake ndipo aliyense amene athawa, Mulungu adzamulanga ndi chilango chowawa
۞ لَّقَدْ رَضِيَ اللَّهُ عَنِ الْمُؤْمِنِينَ إِذْ يُبَايِعُونَكَ تَحْتَ الشَّجَرَةِ فَعَلِمَ مَا فِي قُلُوبِهِمْ فَأَنزَلَ السَّكِينَةَ عَلَيْهِمْ وَأَثَابَهُمْ فَتْحًا قَرِيبًا (18)
Ndithudi Mulungu adasangalala ndi anthu okhulupirira pamene iwo adakulonjeza patsinde pa mtengo kuti adzakhala ndi iwe ndipo Iye adadziwa zimene zidali m’mitima mwawo. Ndipo Iye adatumiza madalitso kwa iwo ndipo adawalipirira mwamsanga mphotho yopambana
وَمَغَانِمَ كَثِيرَةً يَأْخُذُونَهَا ۗ وَكَانَ اللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمًا (19)
Ndipo iwo adzalanda katundu wambiri. Ndipo Mulungu ndi Wamphamvu ndi Waluntha
وَعَدَكُمُ اللَّهُ مَغَانِمَ كَثِيرَةً تَأْخُذُونَهَا فَعَجَّلَ لَكُمْ هَٰذِهِ وَكَفَّ أَيْدِيَ النَّاسِ عَنكُمْ وَلِتَكُونَ آيَةً لِّلْمُؤْمِنِينَ وَيَهْدِيَكُمْ صِرَاطًا مُّسْتَقِيمًا (20)
Mulungu wakulonjeza katundu wambiri amene udzalandira ndipo wakupatsiratu, ndipo Iye wamanga manja ya anthu kuti asakukhudze, kuti chikhale chizindikiro kwa anthu okhulupirira ndipo kuti Iye akutsogolere ku njira yoyenera
وَأُخْرَىٰ لَمْ تَقْدِرُوا عَلَيْهَا قَدْ أَحَاطَ اللَّهُ بِهَا ۚ وَكَانَ اللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرًا (21)
Ndi zina zomwe iwe siudazipeze ndithudi,Mulungu wazizungulira. Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
وَلَوْ قَاتَلَكُمُ الَّذِينَ كَفَرُوا لَوَلَّوُا الْأَدْبَارَ ثُمَّ لَا يَجِدُونَ وَلِيًّا وَلَا نَصِيرًا (22)
Ngati anthu osakhulupirira amenyana nanu, ndithudi, iwo adzathawa, ndipo iwo sadzapeza wina aliyense wowateteza kapena kuwathandiza
سُنَّةَ اللَّهِ الَّتِي قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلُ ۖ وَلَن تَجِدَ لِسُنَّةِ اللَّهِ تَبْدِيلًا (23)
Amenewa ndiwo machitidwe a Mulungu kuyambira kalekale. Ndipo inu simudzapeza chosintha m’machitidwe a Mulungu
وَهُوَ الَّذِي كَفَّ أَيْدِيَهُمْ عَنكُمْ وَأَيْدِيَكُمْ عَنْهُم بِبَطْنِ مَكَّةَ مِن بَعْدِ أَنْ أَظْفَرَكُمْ عَلَيْهِمْ ۚ وَكَانَ اللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرًا (24)
Ndipo ndiye amene adamanga manja awo kuti asakukhudzeni inu ndipo manja anu kuti asawakhudze iwo m’kati mwa Makka pamene Iye adakupambanitsani inu. Ndipo Mulungu amaona zonse zimene mumachita
هُمُ الَّذِينَ كَفَرُوا وَصَدُّوكُمْ عَنِ الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ وَالْهَدْيَ مَعْكُوفًا أَن يَبْلُغَ مَحِلَّهُ ۚ وَلَوْلَا رِجَالٌ مُّؤْمِنُونَ وَنِسَاءٌ مُّؤْمِنَاتٌ لَّمْ تَعْلَمُوهُمْ أَن تَطَئُوهُمْ فَتُصِيبَكُم مِّنْهُم مَّعَرَّةٌ بِغَيْرِ عِلْمٍ ۖ لِّيُدْخِلَ اللَّهُ فِي رَحْمَتِهِ مَن يَشَاءُ ۚ لَوْ تَزَيَّلُوا لَعَذَّبْنَا الَّذِينَ كَفَرُوا مِنْهُمْ عَذَابًا أَلِيمًا (25)
Iwo ndiwo amene sadakhulupirire ndipo adakutchingani kuti musalowe mu Mzikiti Wolemekezeka ndi kukuletsani kuti nyama za nsembe zisakafike pa malo operekerapo nsembe. Koma pakadakhala kuti panalibe anthu aamuna okhulupirira ndi aakazi okhulupirira, amene simuwadziwa, inu mukadawapondereza kotero kuti china chake choipa chikadadza pa inu chifukwa cha iwo, kuti Mulungu aonetse chisomo chake kwa aliyense amene Iye wamufuna. Koma iwo akadapatukana wina ndi mnzake, Ife ndithudi tikadalanga ndi chilango choopsa onse amene sadakhulupirire amene anali pakati pawo
إِذْ جَعَلَ الَّذِينَ كَفَرُوا فِي قُلُوبِهِمُ الْحَمِيَّةَ حَمِيَّةَ الْجَاهِلِيَّةِ فَأَنزَلَ اللَّهُ سَكِينَتَهُ عَلَىٰ رَسُولِهِ وَعَلَى الْمُؤْمِنِينَ وَأَلْزَمَهُمْ كَلِمَةَ التَّقْوَىٰ وَكَانُوا أَحَقَّ بِهَا وَأَهْلَهَا ۚ وَكَانَ اللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمًا (26)
Pamene iwo osakhulupirira adasunga chidani m’mitima mwawo, chidani cha nthawi ya chikunja, ndipo Mulungu adatumiza chisomo chake kwa Mtumwi wake ndi kwa anthu okhulupirira. Ndipo adawachititsa iwo kukhala omvera malamulo odziletsa ndipo adakhazikitsa bata kukhala pa iwo chifukwa adali oyenera kulilandira batalo. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse
لَّقَدْ صَدَقَ اللَّهُ رَسُولَهُ الرُّؤْيَا بِالْحَقِّ ۖ لَتَدْخُلُنَّ الْمَسْجِدَ الْحَرَامَ إِن شَاءَ اللَّهُ آمِنِينَ مُحَلِّقِينَ رُءُوسَكُمْ وَمُقَصِّرِينَ لَا تَخَافُونَ ۖ فَعَلِمَ مَا لَمْ تَعْلَمُوا فَجَعَلَ مِن دُونِ ذَٰلِكَ فَتْحًا قَرِيبًا (27)
Ndithudi Mulungu adzakwaniritsa masomphenya a Mtumwi wake. Ndithudi inu mudzalowa mu Mzikiti Wolemekezeka, ngati Mulungu afuna mopanda vuto ndipo ena adzameta mitu yawo ndiponso ena adzapungula tsitsi lawo ndipo mudzakhala opanda mantha. Iye adadziwa zimene inu simudadziwe ndipo adapereka moonjezera pa zimenezi, kupambana kwa msanga
هُوَ الَّذِي أَرْسَلَ رَسُولَهُ بِالْهُدَىٰ وَدِينِ الْحَقِّ لِيُظْهِرَهُ عَلَى الدِّينِ كُلِّهِ ۚ وَكَفَىٰ بِاللَّهِ شَهِيدًا (28)
Ndiye amene adatumiza Mtumwi wake ndi ulangizi ndiponso chipembedzo choonadi. Ndipo Iye wachipanga icho kuti chikhale chopambana zipembedzo zina zonse. Ndipo Mulungu ndi wokwana kukhala mboni
مُّحَمَّدٌ رَّسُولُ اللَّهِ ۚ وَالَّذِينَ مَعَهُ أَشِدَّاءُ عَلَى الْكُفَّارِ رُحَمَاءُ بَيْنَهُمْ ۖ تَرَاهُمْ رُكَّعًا سُجَّدًا يَبْتَغُونَ فَضْلًا مِّنَ اللَّهِ وَرِضْوَانًا ۖ سِيمَاهُمْ فِي وُجُوهِهِم مِّنْ أَثَرِ السُّجُودِ ۚ ذَٰلِكَ مَثَلُهُمْ فِي التَّوْرَاةِ ۚ وَمَثَلُهُمْ فِي الْإِنجِيلِ كَزَرْعٍ أَخْرَجَ شَطْأَهُ فَآزَرَهُ فَاسْتَغْلَظَ فَاسْتَوَىٰ عَلَىٰ سُوقِهِ يُعْجِبُ الزُّرَّاعَ لِيَغِيظَ بِهِمُ الْكُفَّارَ ۗ وَعَدَ اللَّهُ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ مِنْهُم مَّغْفِرَةً وَأَجْرًا عَظِيمًا (29)
Muhammad ndi Mtumwi wa Mulungu ndipo onse amene amamutsatira iye amakhala olimbika polimbana ndi anthu osakhulupirira koma amachitirana chisoni wokhaokha. Inu mumawaona ali nkupembedza pa mawondo awo ndi kugwetsa mphumi zawo kufunafuna chisomo chochokera kwa Mulungu ndi chisangalalo chake. Pamphumi pawo pali zizindikiro zimene zimadza chifukwa chakugunditsa mphumi zawo pansi. Awa ndi maonekedwe awo amene ali m’Chipangano Chakale. Koma maonekedwe awo amene ali mu Chipangano Chatsopano ali monga momwembewuimatulutsiransongayakendikuikhwimitsa. Ndipo iyo imalimba ndi kukhala yoimirira modabwitsa ndi kusangalatsa amene adaibzala. Kuti Iye akwiyitse osakhulupirira ndi izo. Mulungu walonjeza chikhululukiro ndi mphotho yaikulu kwa anthu okhulupirira ndiponso ochita ntchito zabwino
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس