الْحَمْدُ لِلَّهِ فَاطِرِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ جَاعِلِ الْمَلَائِكَةِ رُسُلًا أُولِي أَجْنِحَةٍ مَّثْنَىٰ وَثُلَاثَ وَرُبَاعَ ۚ يَزِيدُ فِي الْخَلْقِ مَا يَشَاءُ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (1) Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Namalenga wakumwamba ndi dziko lapansi, amene adalenga angelo, atumwi ouluka, amapiko awiri, atatu ndi anayi. Iye amachulukitsa zolengedwa mwachifuniro chake. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse |
مَّا يَفْتَحِ اللَّهُ لِلنَّاسِ مِن رَّحْمَةٍ فَلَا مُمْسِكَ لَهَا ۖ وَمَا يُمْسِكْ فَلَا مُرْسِلَ لَهُ مِن بَعْدِهِ ۚ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (2) Chimene Mulungu, mwachifundo chake, amapereka kwa anthu palibe amene angawalande, ndipo chilichonse chimene Iye awamana palibe wina amene angawapatse. Iye ndiye Mwini mphamvu ndiponso Mwini nzeru |
يَا أَيُّهَا النَّاسُ اذْكُرُوا نِعْمَتَ اللَّهِ عَلَيْكُمْ ۚ هَلْ مِنْ خَالِقٍ غَيْرُ اللَّهِ يَرْزُقُكُم مِّنَ السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ ۚ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ فَأَنَّىٰ تُؤْفَكُونَ (3) Oh anthu inu! Kumbukirani zokoma zimene Mulungu adakupatsani! Kodipali Namalengawinakupatula Mulungu amene akhoza kukupatsani zokoma kuchokera kumwamba kapena padziko lapansi? Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Nanga ndi chifukwa chiyani mumanyengedwa |
وَإِن يُكَذِّبُوكَ فَقَدْ كُذِّبَتْ رُسُلٌ مِّن قَبْلِكَ ۚ وَإِلَى اللَّهِ تُرْجَعُ الْأُمُورُ (4) Ndipo ngati akuti iwe ndi wabodza, ndithudi, Atumwi amene adadza iwe usanabadwe nawonso adatchulidwa kuti ndi abodza ndipo ndi kwa Mulungu kokha kumene zinthu zonse zidzabwerera |
يَا أَيُّهَا النَّاسُ إِنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ ۖ فَلَا تَغُرَّنَّكُمُ الْحَيَاةُ الدُّنْيَا ۖ وَلَا يَغُرَّنَّكُم بِاللَّهِ الْغَرُورُ (5) Anthu inu! Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona, kotero musalole zokoma za m’moyo uno kuti zikunyengeni ndiponso musalole mdyerekezi kuti akunyengeni zokhudza Mulungu |
إِنَّ الشَّيْطَانَ لَكُمْ عَدُوٌّ فَاتَّخِذُوهُ عَدُوًّا ۚ إِنَّمَا يَدْعُو حِزْبَهُ لِيَكُونُوا مِنْ أَصْحَابِ السَّعِيرِ (6) Ndithudi Satana ndi mdani wanu, kotero dziwani kuti iye ndi mdani wanu. Iye amangoitana gulu lake kuti akhoza kukakhala nalo ku moto woyaka |
الَّذِينَ كَفَرُوا لَهُمْ عَذَابٌ شَدِيدٌ ۖ وَالَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَأَجْرٌ كَبِيرٌ (7) Kwa iwo amene sakhulupirira, iwo adzalandira chilango chowawa ndipo iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, iwo adzakhululukidwa ndi kulandira mphotho yaikulu |
أَفَمَن زُيِّنَ لَهُ سُوءُ عَمَلِهِ فَرَآهُ حَسَنًا ۖ فَإِنَّ اللَّهَ يُضِلُّ مَن يَشَاءُ وَيَهْدِي مَن يَشَاءُ ۖ فَلَا تَذْهَبْ نَفْسُكَ عَلَيْهِمْ حَسَرَاتٍ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ بِمَا يَصْنَعُونَ (8) Kodi iye,amene zoipa zake zimaoneka ngati zabwino, moti akamaziona amati ndi zabwino? Ndithudi Mulungu amasocheretsa aliyense amene amamufuna ndiponso amatsogolera aliyense amene wamufuna. Kotero usavutike mu mtima mwako chifukwa cha iwo. Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene amachita |
وَاللَّهُ الَّذِي أَرْسَلَ الرِّيَاحَ فَتُثِيرُ سَحَابًا فَسُقْنَاهُ إِلَىٰ بَلَدٍ مَّيِّتٍ فَأَحْيَيْنَا بِهِ الْأَرْضَ بَعْدَ مَوْتِهَا ۚ كَذَٰلِكَ النُّشُورُ (9) Ndipo Mulungu ndiye amene amatumiza mphepo imene imayendetsa mtambo, ndipo timauyendetsa kudziko lakufa ndipo ndi iwo timapereka moyo ku nthaka ikafa. Kumeneko ndiko kuuka kwa akufa |
مَن كَانَ يُرِيدُ الْعِزَّةَ فَلِلَّهِ الْعِزَّةُ جَمِيعًا ۚ إِلَيْهِ يَصْعَدُ الْكَلِمُ الطَّيِّبُ وَالْعَمَلُ الصَّالِحُ يَرْفَعُهُ ۚ وَالَّذِينَ يَمْكُرُونَ السَّيِّئَاتِ لَهُمْ عَذَابٌ شَدِيدٌ ۖ وَمَكْرُ أُولَٰئِكَ هُوَ يَبُورُ (10) Aliyense amene afuna ulemu ndi mphamvu ndi kwa Mulungu kumene kuli ulemu ndi mphamvu. Kwa Iye ndiko kumene kumapita mawu abwino ndipo ntchito zabwino amazinyamula. Akakhala iwo amene amakonza ntchito zoipa, iwo adzalandira chilango chowawa ndipo chikonzero chawo chidzafafanizidwa |
وَاللَّهُ خَلَقَكُم مِّن تُرَابٍ ثُمَّ مِن نُّطْفَةٍ ثُمَّ جَعَلَكُمْ أَزْوَاجًا ۚ وَمَا تَحْمِلُ مِنْ أُنثَىٰ وَلَا تَضَعُ إِلَّا بِعِلْمِهِ ۚ وَمَا يُعَمَّرُ مِن مُّعَمَّرٍ وَلَا يُنقَصُ مِنْ عُمُرِهِ إِلَّا فِي كِتَابٍ ۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى اللَّهِ يَسِيرٌ (11) Ndipo Mulungu adakulengani inu kuchokera ku dothi, kenaka adakulengani kuchokera ku dontho la umuna ndipo adakupangani inu awiriawiri ndipo palibe mkazi amene amaima kapena kubala kupatula ndi chilolezo chake. Ndipo palibe aliyense amene moyo wake umapitirizidwa kapena kuchepetsedwa kupatula zimene zidalembedwa m’Buku Lopatulika. Ndithudi zimenezi ndi za pafupi ndi Mulungu |
وَمَا يَسْتَوِي الْبَحْرَانِ هَٰذَا عَذْبٌ فُرَاتٌ سَائِغٌ شَرَابُهُ وَهَٰذَا مِلْحٌ أُجَاجٌ ۖ وَمِن كُلٍّ تَأْكُلُونَ لَحْمًا طَرِيًّا وَتَسْتَخْرِجُونَ حِلْيَةً تَلْبَسُونَهَا ۖ وَتَرَى الْفُلْكَ فِيهِ مَوَاخِرَ لِتَبْتَغُوا مِن فَضْلِهِ وَلَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (12) Ndiponyanjaziwirisizingakhalezofananakwenikweni. Ina ndi ya madzi ozuna amene amatha ludzu chifukwa cha kukoma kwake, okoma kumwa; ndipo ina ndi yamchere, imene imatentha chifukwa cha mchere. Komabe kuchokera mu zonse inu mumadya zakudya zabwino ndipo mumatulutsamo zinthu zosangalatsa zimene mumavala. Ndipo inu mumaona zombo zilikuyenda m’mafunde kuti inu muthe kufunafuna zokoma za Mulungu ndiponso kuti muzithokoza |
يُولِجُ اللَّيْلَ فِي النَّهَارِ وَيُولِجُ النَّهَارَ فِي اللَّيْلِ وَسَخَّرَ الشَّمْسَ وَالْقَمَرَ كُلٌّ يَجْرِي لِأَجَلٍ مُّسَمًّى ۚ ذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبُّكُمْ لَهُ الْمُلْكُ ۚ وَالَّذِينَ تَدْعُونَ مِن دُونِهِ مَا يَمْلِكُونَ مِن قِطْمِيرٍ (13) Iye amasanduliza usiku kuti ukhale usana ndipo amasanduliza usana kuti ukhale usiku ndipo Iye adalamula dzuwa ndi mwezi kumvera malamulo ake. Iye adalamula chilichonse kuti chiziyenda m’njira yake mpaka pa tsiku lokhazikitsidwa. Iye ndi Mulungu,Ambuye wanu; wake ndi Ufumu ndipo iwo amene mumapembedza poonjezera pa Mulungu salamulira chinthu ngakhale chaching’ono |
إِن تَدْعُوهُمْ لَا يَسْمَعُوا دُعَاءَكُمْ وَلَوْ سَمِعُوا مَا اسْتَجَابُوا لَكُمْ ۖ وَيَوْمَ الْقِيَامَةِ يَكْفُرُونَ بِشِرْكِكُمْ ۚ وَلَا يُنَبِّئُكَ مِثْلُ خَبِيرٍ (14) Ngati inu muwapempha iwo sadzamva kupempha kwanu ndipo ngati iwo akadamva iwo sangathe kuyankha mapemphero anu. Ndipo pa tsiku lachiweruzo iwo adzakukanani inu. Ndipo palibe wina amene angakuuzeni inu kuposa Iye amene amadziwa chilichonse |
۞ يَا أَيُّهَا النَّاسُ أَنتُمُ الْفُقَرَاءُ إِلَى اللَّهِ ۖ وَاللَّهُ هُوَ الْغَنِيُّ الْحَمِيدُ (15) Anthu inu! Ndinu amene mumafuna Mulungu ndipo Mulungu ndiye amene ali woima payekha ndi woyamikiridwa |
إِن يَشَأْ يُذْهِبْكُمْ وَيَأْتِ بِخَلْقٍ جَدِيدٍ (16) Ngati Iye atafuna akhoza kukuchotsani ndi kubweretsa m’badwo wina watsopano |
وَمَا ذَٰلِكَ عَلَى اللَّهِ بِعَزِيزٍ (17) Ndipo kutero si kovuta kwa Mulungu |
وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزْرَ أُخْرَىٰ ۚ وَإِن تَدْعُ مُثْقَلَةٌ إِلَىٰ حِمْلِهَا لَا يُحْمَلْ مِنْهُ شَيْءٌ وَلَوْ كَانَ ذَا قُرْبَىٰ ۗ إِنَّمَا تُنذِرُ الَّذِينَ يَخْشَوْنَ رَبَّهُم بِالْغَيْبِ وَأَقَامُوا الصَّلَاةَ ۚ وَمَن تَزَكَّىٰ فَإِنَّمَا يَتَزَكَّىٰ لِنَفْسِهِ ۚ وَإِلَى اللَّهِ الْمَصِيرُ (18) Ndipo mzimu wolemedwa sungathe kunyamula katundu wa mzimu wina wolemedwa ndipo ngati mzimu wina wolemedwa utalilira mzimu wina wolemedwa kuti uunyamulire katundu wake, winawo siungathe kunyamula katunduyo ngakhale kuti mizimuyo itakhala pa chibale. Achenjeze okhawo amene amaopa Ambuye wawo mwamseri ndipo amakwaniritsa mapemphero, ndipo aliyense amene adziyeretsa, amatero populumutsa mzimu wake. Ndi kwa Mulungu kokha kumene onse adzabwerera |
وَمَا يَسْتَوِي الْأَعْمَىٰ وَالْبَصِيرُ (19) Ndipo anthu akhungu ndi openya safanana |
وَلَا الظُّلُمَاتُ وَلَا النُّورُ (20) Ngakhalenso usiku ndi usana sizifanana |
وَلَا الظِّلُّ وَلَا الْحَرُورُ (21) Ngakhalenso mthunzi wozizira kwambiri ndi kutentha kwa dzuwa sizingafanane |
وَمَا يَسْتَوِي الْأَحْيَاءُ وَلَا الْأَمْوَاتُ ۚ إِنَّ اللَّهَ يُسْمِعُ مَن يَشَاءُ ۖ وَمَا أَنتَ بِمُسْمِعٍ مَّن فِي الْقُبُورِ (22) Ndipo zamoyo ndi zakufa sizifanana. Ndithudi Mulungu akhoza kumupanga aliyense amene wamufuna kuti amve koma iwe siungathe kuwauza iwo amene ali m’manda kuti amve |
إِنْ أَنتَ إِلَّا نَذِيرٌ (23) Iwe ndiwe wochenjeza kwambiri |
إِنَّا أَرْسَلْنَاكَ بِالْحَقِّ بَشِيرًا وَنَذِيرًا ۚ وَإِن مِّنْ أُمَّةٍ إِلَّا خَلَا فِيهَا نَذِيرٌ (24) Ndithudi Ife takutumiza iwe ndi choonadi ngati wotenga nkhani zabwino ndi mchenjezi ndipo palibe mtundu wa anthu umene sadakhale ndi mchenjezi pakati pawo kalelo |
وَإِن يُكَذِّبُوكَ فَقَدْ كَذَّبَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ جَاءَتْهُمْ رُسُلُهُم بِالْبَيِّنَاتِ وَبِالزُّبُرِ وَبِالْكِتَابِ الْمُنِيرِ (25) Ndipo ngati iwo akuti iwe ndiwe wabodza, nawonso amene adalipo kale, adawatcha Atumwi awo kuti ndi abodza. Atumwi awo adadza kwa iwo ndi chiphunzitso chomveka ndi mawu opatulika ndi Buku la muuni |
ثُمَّ أَخَذْتُ الَّذِينَ كَفَرُوا ۖ فَكَيْفَ كَانَ نَكِيرِ (26) Kotero ndidawalanga anthu onse amene sadakhulupirire. Kodi chilango changa chidali chotani |
أَلَمْ تَرَ أَنَّ اللَّهَ أَنزَلَ مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَأَخْرَجْنَا بِهِ ثَمَرَاتٍ مُّخْتَلِفًا أَلْوَانُهَا ۚ وَمِنَ الْجِبَالِ جُدَدٌ بِيضٌ وَحُمْرٌ مُّخْتَلِفٌ أَلْوَانُهَا وَغَرَابِيبُ سُودٌ (27) Kodi inu simuona mmene Mulungu amagwetsera mvula kuchokera ku mitambo? Ndi mvulayo Ife timameretsa mbewu za maonekedwe osiyanasiyana. Ndipo m’mapiri muli njira zoyera ndi zofiira, zooneka m’maonekedwe osiyanasiyana ndi zina zakuda |
وَمِنَ النَّاسِ وَالدَّوَابِّ وَالْأَنْعَامِ مُخْتَلِفٌ أَلْوَانُهُ كَذَٰلِكَ ۗ إِنَّمَا يَخْشَى اللَّهَ مِنْ عِبَادِهِ الْعُلَمَاءُ ۗ إِنَّ اللَّهَ عَزِيزٌ غَفُورٌ (28) Pali kusiyana m’maonekedwe pakati pa anthu, zolengedwa ndi zinyama. Iwo amene amaopa Mulungu pakati pa akapolo ake ndiwo amene ali ndi nzeru chifukwa Mulungu ndi wamphamvu zambiri ndi wokhululukira nthawi zonse |
إِنَّ الَّذِينَ يَتْلُونَ كِتَابَ اللَّهِ وَأَقَامُوا الصَّلَاةَ وَأَنفَقُوا مِمَّا رَزَقْنَاهُمْ سِرًّا وَعَلَانِيَةً يَرْجُونَ تِجَارَةً لَّن تَبُورَ (29) Iwo amene amawerenga Buku la Mulungu, amene amapitiriza kupemphera nthawi zonse ndipo amapereka chaulere pa katundu amene tawapatsa mwamseri kapena poyera, ayenera kukhulupirira m’malonda amene sadzatha ayi |
لِيُوَفِّيَهُمْ أُجُورَهُمْ وَيَزِيدَهُم مِّن فَضْلِهِ ۚ إِنَّهُ غَفُورٌ شَكُورٌ (30) Kuti Iye akhoza kuwalipira mphotho zawo zonse ndi kuwapatsa zambiri kudzera m’chisomo chake. Ndithudi Iye ndi wokhululukira amene amachulukitsa malipiro |
وَالَّذِي أَوْحَيْنَا إِلَيْكَ مِنَ الْكِتَابِ هُوَ الْحَقُّ مُصَدِّقًا لِّمَا بَيْنَ يَدَيْهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ بِعِبَادِهِ لَخَبِيرٌ بَصِيرٌ (31) Ndipo chimene tavumbulutsa kwa iwe kuchokera m’Buku ndi choonadi chimene chitsimikiza zimene zidalipo kale. Ndithudi Mulungu amadziwa ndipo amaona zochita za akapolo ake |
ثُمَّ أَوْرَثْنَا الْكِتَابَ الَّذِينَ اصْطَفَيْنَا مِنْ عِبَادِنَا ۖ فَمِنْهُمْ ظَالِمٌ لِّنَفْسِهِ وَمِنْهُم مُّقْتَصِدٌ وَمِنْهُمْ سَابِقٌ بِالْخَيْرَاتِ بِإِذْنِ اللَّهِ ۚ ذَٰلِكَ هُوَ الْفَضْلُ الْكَبِيرُ (32) Ndipo tidapereka Buku kuti lisungidwe ndi anthu amene adali pakati pa akapolo athu. Ndipo pakati pawo pali munthu amene amataya mzimu wake ndipo pakati pawo pali iye amene amaima pakati ndi pakati ndiponso pakati pawo pali iye amene amakhala patsogolo pochita ntchito zabwino ndi chilolezo cha Mulungu. Umenewu ndiwo ubwino wopambana |
جَنَّاتُ عَدْنٍ يَدْخُلُونَهَا يُحَلَّوْنَ فِيهَا مِنْ أَسَاوِرَ مِن ذَهَبٍ وَلُؤْلُؤًا ۖ وَلِبَاسُهُمْ فِيهَا حَرِيرٌ (33) Iwo adzalowa m’minda yokhalitsa ndipo azidzavala zibangiri zagolide ndi nkhombe ndipo zovala zawo zidzakhala za silika |
وَقَالُوا الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي أَذْهَبَ عَنَّا الْحَزَنَ ۖ إِنَّ رَبَّنَا لَغَفُورٌ شَكُورٌ (34) Ndipoiwoadzati,“Kuyamikidwakonsendikwa Mulungu amene wachotsa chisoni pakati pathu. Ndithudi Ambuye wathu ndi wokhululukira ndiponso amene amachulukitsa malipiro.” |
الَّذِي أَحَلَّنَا دَارَ الْمُقَامَةِ مِن فَضْلِهِ لَا يَمَسُّنَا فِيهَا نَصَبٌ وَلَا يَمَسُّنَا فِيهَا لُغُوبٌ (35) “Amene watikhazika m’nyumba yokhalamo mpaka kalekale mwachisomo chake. Palibe mavuto amene adzatipeza kuno ndiponso sitidzakhala otopa.” |
وَالَّذِينَ كَفَرُوا لَهُمْ نَارُ جَهَنَّمَ لَا يُقْضَىٰ عَلَيْهِمْ فَيَمُوتُوا وَلَا يُخَفَّفُ عَنْهُم مِّنْ عَذَابِهَا ۚ كَذَٰلِكَ نَجْزِي كُلَّ كَفُورٍ (36) Akakhala iwo amene sakhulupirira, iwo adzakhala kumoto wa ku Gahena. Iwo siudzawamaliza kuti afe ayi, ndipo chilango chawo sichidzachepetsedwa. Kotero ndi mmene timalipirira aliyense wosayamika |
وَهُمْ يَصْطَرِخُونَ فِيهَا رَبَّنَا أَخْرِجْنَا نَعْمَلْ صَالِحًا غَيْرَ الَّذِي كُنَّا نَعْمَلُ ۚ أَوَلَمْ نُعَمِّرْكُم مَّا يَتَذَكَّرُ فِيهِ مَن تَذَكَّرَ وَجَاءَكُمُ النَّذِيرُ ۖ فَذُوقُوا فَمَا لِلظَّالِمِينَ مِن نَّصِيرٍ (37) Ndipo iwo adzalira pofuna chipulumutso nati, “Ambuye wathu! Tichotseni kuno. Ife tikachita zinthu zabwino kusiyana ndi zimene tinali kuchita”. “Kodi Ife sitidakusungeni ndi moyo nthawi yaitali kuti iye amene amalabadira akadazindikira za zimenezi? Ndipo kwa inu kudadza mchenjezi kotero lawani chilango chifukwa munthu wochimwa alibe woti angamuthandize” |
إِنَّ اللَّهَ عَالِمُ غَيْبِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ إِنَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (38) Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zobisika zakumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndithudi Iye amaona zimene zili m’mitima mwa anthu |
هُوَ الَّذِي جَعَلَكُمْ خَلَائِفَ فِي الْأَرْضِ ۚ فَمَن كَفَرَ فَعَلَيْهِ كُفْرُهُ ۖ وَلَا يَزِيدُ الْكَافِرِينَ كُفْرُهُمْ عِندَ رَبِّهِمْ إِلَّا مَقْتًا ۖ وَلَا يَزِيدُ الْكَافِرِينَ كُفْرُهُمْ إِلَّا خَسَارًا (39) Ndiye amene adakusankhani kukhala oweruza pa dziko. Kotero aliyense amene sakhulupirira, kusakhulupirira kwake kudzamupweteka yekha. Ndipo kusakhulupirira kwawo sikuonjezera china chilichonse kwa Ambuye wawo kupatula chidani chokha. Ndipo kusakhulupirira kwawo sikuonjezera china chilichonse kwa iwo kupatula kutayika |
قُلْ أَرَأَيْتُمْ شُرَكَاءَكُمُ الَّذِينَ تَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ أَرُونِي مَاذَا خَلَقُوا مِنَ الْأَرْضِ أَمْ لَهُمْ شِرْكٌ فِي السَّمَاوَاتِ أَمْ آتَيْنَاهُمْ كِتَابًا فَهُمْ عَلَىٰ بَيِّنَتٍ مِّنْهُ ۚ بَلْ إِن يَعِدُ الظَّالِمُونَ بَعْضُهُم بَعْضًا إِلَّا غُرُورًا (40) Nena, “Kodi mudayamba mwaganiza za mafano anu amene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu? Tandilangizani gawo limodzi la dziko limene mafanowo adalenga? Kodi kapena iwo ali ndi gawo kumwamba? Kodi kapena Ife tidawapatsa Buku Lopatulika limene iwo amatsatira chiphunzitso chake? Iyayi! Anthu ochimwa sakwaniritsa malonjezo pakati pawo koma kunyengana basi.” |
۞ إِنَّ اللَّهَ يُمْسِكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ أَن تَزُولَا ۚ وَلَئِن زَالَتَا إِنْ أَمْسَكَهُمَا مِنْ أَحَدٍ مِّن بَعْدِهِ ۚ إِنَّهُ كَانَ حَلِيمًا غَفُورًا (41) Ndithudi ndi Mulungu amene amayang’anira kumwamba ndi dziko lapansi kuti zingaonongeke ndipo izo zitaonongeka palibe wina amene akhoza kuzikonzanso kupatula Iye yekha. Ndithudi Iye ndi wopirira ndi wokhululukira |
وَأَقْسَمُوا بِاللَّهِ جَهْدَ أَيْمَانِهِمْ لَئِن جَاءَهُمْ نَذِيرٌ لَّيَكُونُنَّ أَهْدَىٰ مِنْ إِحْدَى الْأُمَمِ ۖ فَلَمَّا جَاءَهُمْ نَذِيرٌ مَّا زَادَهُمْ إِلَّا نُفُورًا (42) Ndipo iwo adalumbira motchula Mulungu ndi molimbika kuti ngati kungadze kwa iwo Mtumwi iwo adzalandira ulangizi wake kuposa mtundu wina uliwonse. Koma pamene Mtumwi adadza kwa iwo, kubwera kwake kudaonjezera kuipa kwawo |
اسْتِكْبَارًا فِي الْأَرْضِ وَمَكْرَ السَّيِّئِ ۚ وَلَا يَحِيقُ الْمَكْرُ السَّيِّئُ إِلَّا بِأَهْلِهِ ۚ فَهَلْ يَنظُرُونَ إِلَّا سُنَّتَ الْأَوَّلِينَ ۚ فَلَن تَجِدَ لِسُنَّتِ اللَّهِ تَبْدِيلًا ۖ وَلَن تَجِدَ لِسُنَّتِ اللَّهِ تَحْوِيلًا (43) Chifukwa cha mwano ndi chiwembu chimene anali kukonza ndi chifukwa chakukonza chiwembucho, choipa chidagwa pa onse amene adakonza chiwembucho. Kodi iwo ayembekeza kusamalidwa mosiyana ndi anthu akale? Ndipo inu simudzapeza chosintha m’machitidwe a Mulungu |
أَوَلَمْ يَسِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَيَنظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ وَكَانُوا أَشَدَّ مِنْهُمْ قُوَّةً ۚ وَمَا كَانَ اللَّهُ لِيُعْجِزَهُ مِن شَيْءٍ فِي السَّمَاوَاتِ وَلَا فِي الْأَرْضِ ۚ إِنَّهُ كَانَ عَلِيمًا قَدِيرًا (44) Kodi iwo sadayende padziko lapansi ndi kuona zimene zidawachitikira anthu amene adalipo kale pamene mitundu ya anthuwo idali yamphamvu kuposa iwo? Kulibe chinthu kumwamba kapena padziko lapansi chimene chingakhumudwitse Mulungu chifukwa Iye amadziwa chilichonse ndipo ndi mwini mphamvu zonse |
وَلَوْ يُؤَاخِذُ اللَّهُ النَّاسَ بِمَا كَسَبُوا مَا تَرَكَ عَلَىٰ ظَهْرِهَا مِن دَابَّةٍ وَلَٰكِن يُؤَخِّرُهُمْ إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى ۖ فَإِذَا جَاءَ أَجَلُهُمْ فَإِنَّ اللَّهَ كَانَ بِعِبَادِهِ بَصِيرًا (45) Ndipo Mulungu akamalanga anthu chifukwa cha zoipa zimene amachita, sipakadakhala cholengedwa chimene chikadakhala ndi moyo padziko lapansi. Koma Iye amazisunga mpaka pa nthawi ya malire awo. Ndipo pamene nthawi yawo ikwana, ndithudi, Mulungu amaona akapolo ake onse |