×

سورة فصلت باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة فصلت

ترجمة معاني سورة فصلت باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة فصلت مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Fussilat in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة فصلت باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 54 - رقم السورة 41 - الصفحة 477.

بسم الله الرحمن الرحيم

حم (1)
Ha Mim
تَنزِيلٌ مِّنَ الرَّحْمَٰنِ الرَّحِيمِ (2)
Chivumbulutso chochokera kwa Mulungu, Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha
كِتَابٌ فُصِّلَتْ آيَاتُهُ قُرْآنًا عَرَبِيًّا لِّقَوْمٍ يَعْلَمُونَ (3)
Ndi Buku limene mawu ake ndi ofotokozedwa mwatsatanetsatane. Ndi Korani ya m’chiyankhulo cha Chiarabu, kwa anthu ozindikira
بَشِيرًا وَنَذِيرًا فَأَعْرَضَ أَكْثَرُهُمْ فَهُمْ لَا يَسْمَعُونَ (4)
Lopereka nkhani yabwino ndi chenjezo koma ambiri a iwo amabwerera m’mbuyo kotero sakumva chilichonse
وَقَالُوا قُلُوبُنَا فِي أَكِنَّةٍ مِّمَّا تَدْعُونَا إِلَيْهِ وَفِي آذَانِنَا وَقْرٌ وَمِن بَيْنِنَا وَبَيْنِكَ حِجَابٌ فَاعْمَلْ إِنَّنَا عَامِلُونَ (5)
Ndipo iwo amati, “Mitima yathu ndi yokutidwa ku zimene iwe uli kutiitanira ndipo makutu athu ndi ogontha ndipo chotchinga chili pakati pathu ndi iwe kotero iwe gwira ntchito yako ndipo nafenso tili kugwira yathu.”
قُلْ إِنَّمَا أَنَا بَشَرٌ مِّثْلُكُمْ يُوحَىٰ إِلَيَّ أَنَّمَا إِلَٰهُكُمْ إِلَٰهٌ وَاحِدٌ فَاسْتَقِيمُوا إِلَيْهِ وَاسْتَغْفِرُوهُ ۗ وَوَيْلٌ لِّلْمُشْرِكِينَ (6)
Nena, “Ine ndine munthu monga inu nomwe. Koma zavumbulutsidwa kwa ine kuti Mulungu wanu ndi mmodzi yekha kotero tsatirani njira yoyenera yopita kwa Iye ndipo pemphani chikhululukiro chake. Tsoka kwa iwo amene amafanizira milungu ina ndi Mulungu weniweni.”
الَّذِينَ لَا يُؤْتُونَ الزَّكَاةَ وَهُم بِالْآخِرَةِ هُمْ كَافِرُونَ (7)
Iwo ndi amene sapereka chaulere chothandiza osauka ndipo sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ لَهُمْ أَجْرٌ غَيْرُ مَمْنُونٍ (8)
Ndithudi iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, kwa iwo kuli mphotho zosatha
۞ قُلْ أَئِنَّكُمْ لَتَكْفُرُونَ بِالَّذِي خَلَقَ الْأَرْضَ فِي يَوْمَيْنِ وَتَجْعَلُونَ لَهُ أَندَادًا ۚ ذَٰلِكَ رَبُّ الْعَالَمِينَ (9)
Nena, “Kodi, ndithudi, inu muli kumukana Iye amene adalenga dziko lapansi m’masiku awiri ndipo muli kumufanizirandienakukhalaofanananaye? IyendiAmbuye wa zolengedwa zonse.”
وَجَعَلَ فِيهَا رَوَاسِيَ مِن فَوْقِهَا وَبَارَكَ فِيهَا وَقَدَّرَ فِيهَا أَقْوَاتَهَا فِي أَرْبَعَةِ أَيَّامٍ سَوَاءً لِّلسَّائِلِينَ (10)
Iye adaika mu dziko lapansi mapiri okhazikika pamwamba pake ndipo adalidalitsa ilo ndi kulipatsa chakudya, chokwanira chilichonse m’masiku anayi ofanana
ثُمَّ اسْتَوَىٰ إِلَى السَّمَاءِ وَهِيَ دُخَانٌ فَقَالَ لَهَا وَلِلْأَرْضِ ائْتِيَا طَوْعًا أَوْ كَرْهًا قَالَتَا أَتَيْنَا طَائِعِينَ (11)
Ndipo atatero Iye adabuka kumwamba pamene kudali nkhungu ndipo Iye adati adayankhula mawu okhudza kumwamba ndi ku dziko lapansi kuti, “Idzani nonse mwanokha kapena mokakamizidwa.” Onse adati, “Tibwera mosakakamizidwa.”
فَقَضَاهُنَّ سَبْعَ سَمَاوَاتٍ فِي يَوْمَيْنِ وَأَوْحَىٰ فِي كُلِّ سَمَاءٍ أَمْرَهَا ۚ وَزَيَّنَّا السَّمَاءَ الدُّنْيَا بِمَصَابِيحَ وَحِفْظًا ۚ ذَٰلِكَ تَقْدِيرُ الْعَزِيزِ الْعَلِيمِ (12)
Ndipo Iye adakonza ndi kulenga maiko asanu ndi awiri m’masiku awiri ndipo adapereka ku dziko lililonse ulamuliro. Ndipo Ife tidaika ku muyamba wapansi nyenyezi zokongola kuti zizilonda. Umenewo ndi ulamuliro wa Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru
فَإِنْ أَعْرَضُوا فَقُلْ أَنذَرْتُكُمْ صَاعِقَةً مِّثْلَ صَاعِقَةِ عَادٍ وَثَمُودَ (13)
Koma ngati iwo abwerera m’mbuyo, nena, “Ine ndakuchenjezani inu za chilango chonga ngati chimene chidadza pa anthu a Aad ndi Thamoud.”
إِذْ جَاءَتْهُمُ الرُّسُلُ مِن بَيْنِ أَيْدِيهِمْ وَمِنْ خَلْفِهِمْ أَلَّا تَعْبُدُوا إِلَّا اللَّهَ ۖ قَالُوا لَوْ شَاءَ رَبُّنَا لَأَنزَلَ مَلَائِكَةً فَإِنَّا بِمَا أُرْسِلْتُم بِهِ كَافِرُونَ (14)
Ndipo pamene Atumwi awo adadza kwa iwo kuchokera ku mbali zonse, nati, “Musapembedze wina aliyense koma Mulungu.” Iwo adati, “Ngati Ambuye wathu akadafuna, Iye ndithudi, akadatumiza Angelo. Kotero ife, ndithudi, sitikhulupirira zimene inu mwatumidwa.”
فَأَمَّا عَادٌ فَاسْتَكْبَرُوا فِي الْأَرْضِ بِغَيْرِ الْحَقِّ وَقَالُوا مَنْ أَشَدُّ مِنَّا قُوَّةً ۖ أَوَلَمْ يَرَوْا أَنَّ اللَّهَ الَّذِي خَلَقَهُمْ هُوَ أَشَدُّ مِنْهُمْ قُوَّةً ۖ وَكَانُوا بِآيَاتِنَا يَجْحَدُونَ (15)
Akakhala anthu a Aad, iwo adanyada kopambana padziko ndipo adati, “Kodi ali ndi mphamvu zopambana zathu ndani?” Kodi iwo saona kuti Mulungu amene adawalenga, ali ndi mphamvu zambiri zoposa zawo? Ndipo iwo anali kukana chivumbulutso chathu
فَأَرْسَلْنَا عَلَيْهِمْ رِيحًا صَرْصَرًا فِي أَيَّامٍ نَّحِسَاتٍ لِّنُذِيقَهُمْ عَذَابَ الْخِزْيِ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۖ وَلَعَذَابُ الْآخِرَةِ أَخْزَىٰ ۖ وَهُمْ لَا يُنصَرُونَ (16)
Kotero Ife tidawatumizira mphepo yamkuntho m’masiku a tsoka, ndi cholinga choti alawe chilango chochititsa manyazi m’dziko lino koma, ndithudi, chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi chochititsa manyazi zedi ndipo iwo sadzathandizidwa ayi
وَأَمَّا ثَمُودُ فَهَدَيْنَاهُمْ فَاسْتَحَبُّوا الْعَمَىٰ عَلَى الْهُدَىٰ فَأَخَذَتْهُمْ صَاعِقَةُ الْعَذَابِ الْهُونِ بِمَا كَانُوا يَكْسِبُونَ (17)
Akakhala anthu a Thamoud Ife tidawalangiza njira yoyenera koma iwo adasankha kuchita zoipa m’malo mochita zabwino kotero kwa iwo kudadza chilango chochititsa manyazi chifukwa cha ntchito zawo
وَنَجَّيْنَا الَّذِينَ آمَنُوا وَكَانُوا يَتَّقُونَ (18)
Ndipo Ife tidapulumutsa iwo amene adakhulupirira ndi amene amaopa Mulungu ndi kulewa zoipa
وَيَوْمَ يُحْشَرُ أَعْدَاءُ اللَّهِ إِلَى النَّارِ فَهُمْ يُوزَعُونَ (19)
Ndipo pa tsiku limene adani ake a Mulungu adzasonkhanitsidwa kupita kumoto, iwo adzaikidwa m’magulumagulu
حَتَّىٰ إِذَا مَا جَاءُوهَا شَهِدَ عَلَيْهِمْ سَمْعُهُمْ وَأَبْصَارُهُمْ وَجُلُودُهُم بِمَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (20)
Mpaka pamene wo atafika ku malo a moto makutu awo, maso awo ndi makungu awo adzapereka umboni wowaneneza pa zimene anali kuchita
وَقَالُوا لِجُلُودِهِمْ لِمَ شَهِدتُّمْ عَلَيْنَا ۖ قَالُوا أَنطَقَنَا اللَّهُ الَّذِي أَنطَقَ كُلَّ شَيْءٍ وَهُوَ خَلَقَكُمْ أَوَّلَ مَرَّةٍ وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (21)
Ndipo iwo adzati kwa makungu awo, “Bwanji inu muli kupereka umboni wotineneza?” Iwo adzati, “Mulungu, amene amayankhulitsa chilichonse, watiyankhulitsa ife ndipo Iye ndiye amene adakulengani inu poyamba ndipo nonse mudzabwerera kwa Iye.”
وَمَا كُنتُمْ تَسْتَتِرُونَ أَن يَشْهَدَ عَلَيْكُمْ سَمْعُكُمْ وَلَا أَبْصَارُكُمْ وَلَا جُلُودُكُمْ وَلَٰكِن ظَنَنتُمْ أَنَّ اللَّهَ لَا يَعْلَمُ كَثِيرًا مِّمَّا تَعْمَلُونَ (22)
Ndipo inu simunadzibise ku makutu anu, maso anu ndi makungu anu kuti zisadzapereke umboni wokunenezani koma inu mumaganiza kuti Mulungu sadziwa zonse zimene munali kuchita
وَذَٰلِكُمْ ظَنُّكُمُ الَّذِي ظَنَنتُم بِرَبِّكُمْ أَرْدَاكُمْ فَأَصْبَحْتُم مِّنَ الْخَاسِرِينَ (23)
Ndipo ndi maganizo anu amene inu munali kuganiza okhudza Ambuye wanu amene wakubweretsani ku chionongeko tsopano muli m’gulu la anthu otayika
فَإِن يَصْبِرُوا فَالنَّارُ مَثْوًى لَّهُمْ ۖ وَإِن يَسْتَعْتِبُوا فَمَا هُم مِّنَ الْمُعْتَبِينَ (24)
Ndipo ngati iwo apirira komabe ku moto ndiko kudzakhala kumalo kwawo. Ndipo ngati apempha chikhululukiro pempho lawo lidzakanidwa
۞ وَقَيَّضْنَا لَهُمْ قُرَنَاءَ فَزَيَّنُوا لَهُم مَّا بَيْنَ أَيْدِيهِمْ وَمَا خَلْفَهُمْ وَحَقَّ عَلَيْهِمُ الْقَوْلُ فِي أُمَمٍ قَدْ خَلَتْ مِن قَبْلِهِم مِّنَ الْجِنِّ وَالْإِنسِ ۖ إِنَّهُمْ كَانُوا خَاسِرِينَ (25)
Ndipo Ife tawasankhira anzawo amene adapanga kuti aziona zopusa zakale ndi zatsopano kukhala zinthu zokondweretsa kwa iwo. Ndipo chiweruzo chimene chidadza ku mtundu wa majini ndi kwa anthu amene adalipo kale chakwaniritsidwa kwa iwo. Ndithudi iwo ndi otayika kwambiri
وَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا لَا تَسْمَعُوا لِهَٰذَا الْقُرْآنِ وَالْغَوْا فِيهِ لَعَلَّكُمْ تَغْلِبُونَ (26)
Ndipo iwo amene sakhulupirira amati, “Musamvetsere Koraniyi koma m’malo mwake muzipanga phokoso kuti mwina mukhoza kuigonjetsa.”
فَلَنُذِيقَنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا عَذَابًا شَدِيدًا وَلَنَجْزِيَنَّهُمْ أَسْوَأَ الَّذِي كَانُوا يَعْمَلُونَ (27)
Koma, ndithudi, Ife tidzawalawitsa anthu osakhulupirira chilango chowawa, ndipo, ndithudi, Ife tidzawalipira chifukwa cha ntchito zawo zoipa zimene anali kuchita
ذَٰلِكَ جَزَاءُ أَعْدَاءِ اللَّهِ النَّارُ ۖ لَهُمْ فِيهَا دَارُ الْخُلْدِ ۖ جَزَاءً بِمَا كَانُوا بِآيَاتِنَا يَجْحَدُونَ (28)
Amenewo ndiwo malipiro a adani a Mulungu. Moto ndiwo malo awo a nthawi zonse. Malipiro okwanira malinga ndi ntchito zawo zoipa zimene anali kuchita pokana zizindikiro zathu
وَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا رَبَّنَا أَرِنَا اللَّذَيْنِ أَضَلَّانَا مِنَ الْجِنِّ وَالْإِنسِ نَجْعَلْهُمَا تَحْتَ أَقْدَامِنَا لِيَكُونَا مِنَ الْأَسْفَلِينَ (29)
Ndipo iwo osakhulupirira adzati, “Ambuye wathu! Tilangizeni iwo amene ali pakati pa majini ndi anthu amene adatisocheretsa ife ndipo ife tidzawapondaponda ndi mapazi athu kuti iwo akhale a pansi kwambiri.”
إِنَّ الَّذِينَ قَالُوا رَبُّنَا اللَّهُ ثُمَّ اسْتَقَامُوا تَتَنَزَّلُ عَلَيْهِمُ الْمَلَائِكَةُ أَلَّا تَخَافُوا وَلَا تَحْزَنُوا وَأَبْشِرُوا بِالْجَنَّةِ الَّتِي كُنتُمْ تُوعَدُونَ (30)
Ndithudi iwo amene amati, “Ambuye wathu ndi Mulungu ndipo amapitiriza kutsatira njira yoyenera.” Kwa iwo angelo amadza nati, “Musaope ndipo musadandaule ayi. Koma landirani nkhani yabwino yokhudza Paradiso imene inu mudalonjezedwa!”
نَحْنُ أَوْلِيَاؤُكُمْ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَفِي الْآخِرَةِ ۖ وَلَكُمْ فِيهَا مَا تَشْتَهِي أَنفُسُكُمْ وَلَكُمْ فِيهَا مَا تَدَّعُونَ (31)
Ife tinali abwenzi anu m’moyo uno ndiponso ndi m’moyo umene uli nkudza. M’menemu inu mudzapeza chilichonse chimene mufuna ndipo m’menemo inu mudzalandira chilichonse chimene mupempha
نُزُلًا مِّنْ غَفُورٍ رَّحِيمٍ (32)
Mphatso yamtengo wapatali yachokera kwa Iye amene amakhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha
وَمَنْ أَحْسَنُ قَوْلًا مِّمَّن دَعَا إِلَى اللَّهِ وَعَمِلَ صَالِحًا وَقَالَ إِنَّنِي مِنَ الْمُسْلِمِينَ (33)
Kodi amayankhula bwino ndani kuposa iye amene amati; ‘Ambuye wanga ndi Mulungu’ amaitanira anthu kunjira ya Mulungu amene amachita ntchito zabwino ndipo amati, “Ine ndine mmodzi wa Asilamu?”
وَلَا تَسْتَوِي الْحَسَنَةُ وَلَا السَّيِّئَةُ ۚ ادْفَعْ بِالَّتِي هِيَ أَحْسَنُ فَإِذَا الَّذِي بَيْنَكَ وَبَيْنَهُ عَدَاوَةٌ كَأَنَّهُ وَلِيٌّ حَمِيمٌ (34)
Ntchito zabwino ndi ntchito zoipa sizifanana. Kotero gonjetsani choipa pochita chabwino ndipo, ndithudi, iye amene ali mdani wako adzakhala ngati bwenzi lako lapamtima
وَمَا يُلَقَّاهَا إِلَّا الَّذِينَ صَبَرُوا وَمَا يُلَقَّاهَا إِلَّا ذُو حَظٍّ عَظِيمٍ (35)
Koma palibe wina amene adzalandira zimenezi kupatula yekhayo amene amapirira kwambiri ndipo amadziletsa. Ndipo palibe wina amene angalandire kuposa iwo amene ali ndi mwayi wochuluka
وَإِمَّا يَنزَغَنَّكَ مِنَ الشَّيْطَانِ نَزْغٌ فَاسْتَعِذْ بِاللَّهِ ۖ إِنَّهُ هُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (36)
Ndipo ngati iwe uyesedwa ndi Satana, funafuna chitetezo cha Mulungu. Ndithudi Iye ndiye amene amamva ndipo amadziwa chinthu china chilichonse
وَمِنْ آيَاتِهِ اللَّيْلُ وَالنَّهَارُ وَالشَّمْسُ وَالْقَمَرُ ۚ لَا تَسْجُدُوا لِلشَّمْسِ وَلَا لِلْقَمَرِ وَاسْجُدُوا لِلَّهِ الَّذِي خَلَقَهُنَّ إِن كُنتُمْ إِيَّاهُ تَعْبُدُونَ (37)
Ndipo pakati pa zizindikiro zake pali usiku ndi usana ndiponso dzuwa ndi mwezi. Musagwadire dzuwa kapena mwezi koma mugwadire Mulungu amene adazilenga izo ngati ndiye amene inu mumamupembedza
فَإِنِ اسْتَكْبَرُوا فَالَّذِينَ عِندَ رَبِّكَ يُسَبِّحُونَ لَهُ بِاللَّيْلِ وَالنَّهَارِ وَهُمْ لَا يَسْأَمُونَ ۩ (38)
Koma ngati iwo ndi amwano palibe kanthu chifukwa pamaso pa Ambuye wako pali iwo amene amamulemekeza Iye usiku ndi usana ndipo satopa ayi
وَمِنْ آيَاتِهِ أَنَّكَ تَرَى الْأَرْضَ خَاشِعَةً فَإِذَا أَنزَلْنَا عَلَيْهَا الْمَاءَ اهْتَزَّتْ وَرَبَتْ ۚ إِنَّ الَّذِي أَحْيَاهَا لَمُحْيِي الْمَوْتَىٰ ۚ إِنَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (39)
Ndipo pakati pa zizindikiro zake pali choti inu mumaona nthaka ili youma koma pamene Ife titumiza pa nthakayo madzi, iyo imakhala ndi moyo ndipo imakhala ndi zomera zambiri. Ndithudi, Iye amapereka moyo ku nthaka youma, ndithudi, akhoza kuperekanso moyo kwa anthu amene adafa. Ndithudi Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
إِنَّ الَّذِينَ يُلْحِدُونَ فِي آيَاتِنَا لَا يَخْفَوْنَ عَلَيْنَا ۗ أَفَمَن يُلْقَىٰ فِي النَّارِ خَيْرٌ أَم مَّن يَأْتِي آمِنًا يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۚ اعْمَلُوا مَا شِئْتُمْ ۖ إِنَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (40)
Ndithudi onse amene sakhulupirira chivumbulutso chathu sadzatha kubisala. Kodi iye amene aponyedwa ku moto ndi wabwino kapena iye amene adzapulumutsidwa pa tsiku lachiweruzo? Chitani monga momwe mufunira. Ndithudi Iye amaona zonse zimene mumachita
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا بِالذِّكْرِ لَمَّا جَاءَهُمْ ۖ وَإِنَّهُ لَكِتَابٌ عَزِيزٌ (41)
Ndithudi iwo amene amakana uthenga pamene udza kwa iwo adzalangidwa. Ndithudi ili ndi Buku lolemekezeka kwambiri
لَّا يَأْتِيهِ الْبَاطِلُ مِن بَيْنِ يَدَيْهِ وَلَا مِنْ خَلْفِهِ ۖ تَنزِيلٌ مِّنْ حَكِيمٍ حَمِيدٍ (42)
Bodza silingalowemo kuchokera kumbali ina iliyonse. Ichi ndi chivumbulutso chochokera kwa Mwini nzeru ndi olemekezeka
مَّا يُقَالُ لَكَ إِلَّا مَا قَدْ قِيلَ لِلرُّسُلِ مِن قَبْلِكَ ۚ إِنَّ رَبَّكَ لَذُو مَغْفِرَةٍ وَذُو عِقَابٍ أَلِيمٍ (43)
Palibe chimene chili kunenedwa kwa iwe kupatula chokhacho chimene chidanenedwa kwa Atumwi kale. Ndithudi Ambuye wako ndi Mwini kukhululukira ndiponso Mwini chilango chowawa
وَلَوْ جَعَلْنَاهُ قُرْآنًا أَعْجَمِيًّا لَّقَالُوا لَوْلَا فُصِّلَتْ آيَاتُهُ ۖ أَأَعْجَمِيٌّ وَعَرَبِيٌّ ۗ قُلْ هُوَ لِلَّذِينَ آمَنُوا هُدًى وَشِفَاءٌ ۖ وَالَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ فِي آذَانِهِمْ وَقْرٌ وَهُوَ عَلَيْهِمْ عَمًى ۚ أُولَٰئِكَ يُنَادَوْنَ مِن مَّكَانٍ بَعِيدٍ (44)
NdipoIfetikadatumizaBukulaKoranimuchiyankhulo china osati Chiarabu, iwo akadanena kuti, “Kodi bwanji mawu ake sali kufotokozeredwa bwinobwino? Chiyani! Chiyankhulo cha chilendo osati Chiarabu!” Nena, “Ilo ndi la iwo amene amakhulupirira, ndi chilangizo ndiponso mankhwala ochiritsa. Ndipo iwo amene sakhulupirira, makutu awo ndi ogontha ndipo ilo ndi khungu kwa iwo. Iwo ndiwo amene amaitanidwa kuchokera kutali.”
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ فَاخْتُلِفَ فِيهِ ۗ وَلَوْلَا كَلِمَةٌ سَبَقَتْ مِن رَّبِّكَ لَقُضِيَ بَيْنَهُمْ ۚ وَإِنَّهُمْ لَفِي شَكٍّ مِّنْهُ مُرِيبٍ (45)
Ndithudi Ife tidamupatsa Mose Buku koma panabuka mikangano yotsutsana za ilo. Koma pakanapanda mawu amene adanenedwa kale ndi Ambuye wako, onse akadaweruzidwa kale. Ndithudi iwo amakayika kwambiri
مَّنْ عَمِلَ صَالِحًا فَلِنَفْسِهِ ۖ وَمَنْ أَسَاءَ فَعَلَيْهَا ۗ وَمَا رَبُّكَ بِظَلَّامٍ لِّلْعَبِيدِ (46)
Aliyense amene amachita zabwino amachitira moyo wake zabwino ndipo aliyense amene amachita zoipa amadzikundikira yekha mavuto. Ndithudi Ambuye wako sapondereza akapolo ake
۞ إِلَيْهِ يُرَدُّ عِلْمُ السَّاعَةِ ۚ وَمَا تَخْرُجُ مِن ثَمَرَاتٍ مِّنْ أَكْمَامِهَا وَمَا تَحْمِلُ مِنْ أُنثَىٰ وَلَا تَضَعُ إِلَّا بِعِلْمِهِ ۚ وَيَوْمَ يُنَادِيهِمْ أَيْنَ شُرَكَائِي قَالُوا آذَنَّاكَ مَا مِنَّا مِن شَهِيدٍ (47)
Iye yekha ndiye amene amadziwa za ola. Ndipo palibe mtengo umene umabereka zipatso kapena chachikazi kuima kapena kubala popanda Iye kudziwa. Ndipo pa tsiku limene adzawafunsa onse kuti, “Kodi ali kuti amene munkati ndi anzanga?” Iwo adzayankha kuti, “Ife tili kunenetsa kwa Inu kuti palibe aliyense pakati pathu amene angachitire umboni.”
وَضَلَّ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَدْعُونَ مِن قَبْلُ ۖ وَظَنُّوا مَا لَهُم مِّن مَّحِيصٍ (48)
Ndipo mafano awo onse adzawathawira ndipo onse adzadziwa kuti alibe kothawira ayi
لَّا يَسْأَمُ الْإِنسَانُ مِن دُعَاءِ الْخَيْرِ وَإِن مَّسَّهُ الشَّرُّ فَيَئُوسٌ قَنُوطٌ (49)
Munthu satopa akamapempha zinthu zabwino koma ngati mavuto adza pa iye, amataya mtima ndipo amakhala ndi nkhawa
وَلَئِنْ أَذَقْنَاهُ رَحْمَةً مِّنَّا مِن بَعْدِ ضَرَّاءَ مَسَّتْهُ لَيَقُولَنَّ هَٰذَا لِي وَمَا أَظُنُّ السَّاعَةَ قَائِمَةً وَلَئِن رُّجِعْتُ إِلَىٰ رَبِّي إِنَّ لِي عِندَهُ لَلْحُسْنَىٰ ۚ فَلَنُنَبِّئَنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا بِمَا عَمِلُوا وَلَنُذِيقَنَّهُم مِّنْ عَذَابٍ غَلِيظٍ (50)
Ndipo, ndithudi, Ife tikamuonetsera chifundo chathu atazunzika, ndithudi iye adzati: “Ichi ndi chifukwa cha nzeru zanga ndipo ine sindiganiza kuti ola lidzadza. Ndipo ngati ine ndibwerera kwa Ambuye wanga, ndithudi ine ndidzalandira zabwino kuchokera kwa Iye.” Ndithudi, Ife tidzawauza onse amene samakhulupirira zonse zimene adachita ndipo, ndithudi, Ife tidzawapatsa chilango chowawa kwambiri
وَإِذَا أَنْعَمْنَا عَلَى الْإِنسَانِ أَعْرَضَ وَنَأَىٰ بِجَانِبِهِ وَإِذَا مَسَّهُ الشَّرُّ فَذُو دُعَاءٍ عَرِيضٍ (51)
Ndipo Ife tikamulangiza munthu chifundo chathu, iye amatembenuka ndi kuyamba kuchita zakezake koma ngati vuto lidza pa iye, amapemphera mosalekeza
قُلْ أَرَأَيْتُمْ إِن كَانَ مِنْ عِندِ اللَّهِ ثُمَّ كَفَرْتُم بِهِ مَنْ أَضَلُّ مِمَّنْ هُوَ فِي شِقَاقٍ بَعِيدٍ (52)
Nena, “Ndiuzeni ngati ilo ndi lochokera kwa Mulungu ndipo inu muli kulikana. Kodi ndani amene angakhale wolakwa kwambiri kuposa iye amene amatsutsa mowirikiza?”
سَنُرِيهِمْ آيَاتِنَا فِي الْآفَاقِ وَفِي أَنفُسِهِمْ حَتَّىٰ يَتَبَيَّنَ لَهُمْ أَنَّهُ الْحَقُّ ۗ أَوَلَمْ يَكْفِ بِرَبِّكَ أَنَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ شَهِيدٌ (53)
Ife tidzawaonetsa zizindikiro zathu za mlengalenga ndi za m’mizimu yawo, mpaka iwo atazindikira bwinobwino kuti ndi choonadi chenicheni. Kodi sizikwanira kuti Ambuye wanu ndiye mboni wa chinthu china chilichonse
أَلَا إِنَّهُمْ فِي مِرْيَةٍ مِّن لِّقَاءِ رَبِّهِمْ ۗ أَلَا إِنَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ مُّحِيطٌ (54)
Ndithudi! Tsopano iwo ali okayika pa zakukumana ndi Ambuye wawo. Ndithudi, ndiye amene wazungulira zinthu zonse
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس