اقْرَأْ بِاسْمِ رَبِّكَ الَّذِي خَلَقَ (1) Werenga! M’dzina la Ambuye wako amene analenga |
خَلَقَ الْإِنسَانَ مِنْ عَلَقٍ (2) Yemwe adalenga munthu kuchokera ku kadontho kamagazi oundana |
اقْرَأْ وَرَبُّكَ الْأَكْرَمُ (3) werenga! Ndipo Ambuye wako ndiye wopereka mowoolowa manja |
الَّذِي عَلَّمَ بِالْقَلَمِ (4) Amene anaphunzitsa ndi cholembera |
عَلَّمَ الْإِنسَانَ مَا لَمْ يَعْلَمْ (5) Anaphunzitsa munthu chimene sanali kuchidziwa |
كَلَّا إِنَّ الْإِنسَانَ لَيَطْغَىٰ (6) Iyayi! Ndithudi, munthu amalakwa mopyola muyeso |
أَن رَّآهُ اسْتَغْنَىٰ (7) Chifukwa amaganiza kuti iye ndi oima payekha |
إِنَّ إِلَىٰ رَبِّكَ الرُّجْعَىٰ (8) Ndithudi! Nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu |
أَرَأَيْتَ الَّذِي يَنْهَىٰ (9) Kodi mwamuona munthu amene amaletsa |
عَبْدًا إِذَا صَلَّىٰ (10) Kapolo pamene akupemphera |
أَرَأَيْتَ إِن كَانَ عَلَى الْهُدَىٰ (11) Kodi mwamuona ngati iye alikutsatira chilangizo chabwino |
أَوْ أَمَرَ بِالتَّقْوَىٰ (12) Kapena kulamulira machitidwe abwino |
أَرَأَيْتَ إِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ (13) Ndiuze ngati iye akana choonadi ndipo salabadira |
أَلَمْ يَعْلَم بِأَنَّ اللَّهَ يَرَىٰ (14) Kodi iye sadziwa kuti Mulungu amaona zinthu zonse |
كَلَّا لَئِن لَّمْ يَنتَهِ لَنَسْفَعًا بِالنَّاصِيَةِ (15) Iyayi! Ngati iye sasiya, Ife tidzamududuluza pogwira tsitsi la pa mphumi pake |
نَاصِيَةٍ كَاذِبَةٍ خَاطِئَةٍ (16) Mphumi yabodza ndi yochimwa |
فَلْيَدْعُ نَادِيَهُ (17) Ndipo mulekeni iye aitane anzake oti amuthandize |
سَنَدْعُ الزَّبَانِيَةَ (18) Ife tidzaitana osunga Gahena |
كَلَّا لَا تُطِعْهُ وَاسْجُدْ وَاقْتَرِب ۩ (19) Iyayi! Usamumvere iye. Gunditsa mphumi yako pansi ndipo idza pafupi ndi Mulungu |