×

سورة الصافات باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة الصافات

ترجمة معاني سورة الصافات باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة الصافات مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Assaaffat in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة الصافات باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 182 - رقم السورة 37 - الصفحة 446.

بسم الله الرحمن الرحيم

وَالصَّافَّاتِ صَفًّا (1)
Pali iwo amene amasonkhana kukhala pa maudindo osiyanasiyana
فَالزَّاجِرَاتِ زَجْرًا (2)
Pali iwo amene amayendetsa mitambo mwa ubwino
فَالتَّالِيَاتِ ذِكْرًا (3)
Pali iwo amene amabweretsa m’Buku ndi Korani kuchokera kwa Mulungu kupita nalo kwa anthu ake
إِنَّ إِلَٰهَكُمْ لَوَاحِدٌ (4)
Ndithudi Mulungu wanu ndi mmodzi yekha
رَّبُّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا وَرَبُّ الْمَشَارِقِ (5)
Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi wa zonse zimene zili m’menemo ndi Ambuye wa dera lililonse lotulukira dzuwa
إِنَّا زَيَّنَّا السَّمَاءَ الدُّنْيَا بِزِينَةٍ الْكَوَاكِبِ (6)
Ndithudi Ife tidakongoletsa mtambo woyandikira kwambiri ndi nyenyezi
وَحِفْظًا مِّن كُلِّ شَيْطَانٍ مَّارِدٍ (7)
Ndi kulonda Satana wofukira
لَّا يَسَّمَّعُونَ إِلَى الْمَلَإِ الْأَعْلَىٰ وَيُقْذَفُونَ مِن كُلِّ جَانِبٍ (8)
Kotero iwo sangathe kumvetsera zokambidwa za gulu lapamwamba chifukwa iwo amapirikitsidwa kuchokera kumbali iliyonse
دُحُورًا ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ وَاصِبٌ (9)
Atapirikitsidwa, chawo chidzakhala chilango chosatha
إِلَّا مَنْ خَطِفَ الْخَطْفَةَ فَأَتْبَعَهُ شِهَابٌ ثَاقِبٌ (10)
Kupatula yekhayo amene amakwatula zinthu mwakuba, ndipo amathamangitsidwa ndi moto woyaka ndi wowala kwambiri
فَاسْتَفْتِهِمْ أَهُمْ أَشَدُّ خَلْقًا أَم مَّنْ خَلَقْنَا ۚ إِنَّا خَلَقْنَاهُم مِّن طِينٍ لَّازِبٍ (11)
Ndipo tawafunsa, “Kodi iwo ndi a mphamvu kuposa zolengedwa zina zimene tidalenga?” Iwo tidawalenga kuchokera ku dothi lonyata la makande
بَلْ عَجِبْتَ وَيَسْخَرُونَ (12)
Iyayi, iwe udadabwa pamene iwo anali kunyoza
وَإِذَا ذُكِّرُوا لَا يَذْكُرُونَ (13)
Ndipo iwo akamaweruzidwa, iwo safuna kuweruzidwa
وَإِذَا رَأَوْا آيَةً يَسْتَسْخِرُونَ (14)
Ndipo iwo akaona chizindikiro chochokera kwa Mulungu amachisandutsa ngati chinthu choseweretsa
وَقَالُوا إِنْ هَٰذَا إِلَّا سِحْرٌ مُّبِينٌ (15)
Ndipo amati, “Ichi si china ayi koma matsenga woonekera poyera.”
أَإِذَا مِتْنَا وَكُنَّا تُرَابًا وَعِظَامًا أَإِنَّا لَمَبْعُوثُونَ (16)
“Chiyani! Ife tikafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, kodi tidzaukitsidwa?”
أَوَآبَاؤُنَا الْأَوَّلُونَ (17)
“Ndiponso makolo athu amakedzana?”
قُلْ نَعَمْ وَأَنتُمْ دَاخِرُونَ (18)
Nena, “Inde mudzachititsidwa manyazi.”
فَإِنَّمَا هِيَ زَجْرَةٌ وَاحِدَةٌ فَإِذَا هُمْ يَنظُرُونَ (19)
Ndipo udzakhala mfuwu umodzi ndipo taona iwo adzakhala ali kupenyetsetsana
وَقَالُوا يَا وَيْلَنَا هَٰذَا يَوْمُ الدِّينِ (20)
Iwo adzati, “Tsoka kwa ife! Ili ndi tsiku lachiweruzo.”
هَٰذَا يَوْمُ الْفَصْلِ الَّذِي كُنتُم بِهِ تُكَذِّبُونَ (21)
“Ili ndi tsiku lachiweruzo limene inu mumati ndi bodza.”
۞ احْشُرُوا الَّذِينَ ظَلَمُوا وَأَزْوَاجَهُمْ وَمَا كَانُوا يَعْبُدُونَ (22)
(Kudzanenedwa kuti); “Bweretsani anthu ochimwa pamodzi ndi anzawo ndi zinthu zimene iwo anali kupembedza.”
مِن دُونِ اللَّهِ فَاهْدُوهُمْ إِلَىٰ صِرَاطِ الْجَحِيمِ (23)
“Kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo atsogolereni ku njira ya kumoto.”
وَقِفُوهُمْ ۖ إِنَّهُم مَّسْئُولُونَ (24)
“Ndipo aimitseni. Ndithudi, iwo ayenera kufunsidwa.”
مَا لَكُمْ لَا تَنَاصَرُونَ (25)
“Kodi mwatani? Nanga ndi chifukwa chiyani inu simuli kuthandizana?”
بَلْ هُمُ الْيَوْمَ مُسْتَسْلِمُونَ (26)
Iyayi! Koma iwo lero ndi odzipereka
وَأَقْبَلَ بَعْضُهُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ يَتَسَاءَلُونَ (27)
Ndipo iwo adzafunsana wina ndi mnzake
قَالُوا إِنَّكُمْ كُنتُمْ تَأْتُونَنَا عَنِ الْيَمِينِ (28)
Iwo adzati, “Ndinu amene munali kubwera kwa ife kuchokera kudzanja lamanja.”
قَالُوا بَل لَّمْ تَكُونُوا مُؤْمِنِينَ (29)
Iwo adzayankha kuti, “Iyayi, Inuyo simunali okhulupirira.”
وَمَا كَانَ لَنَا عَلَيْكُم مِّن سُلْطَانٍ ۖ بَلْ كُنتُمْ قَوْمًا طَاغِينَ (30)
“Ndipo ife tidalibe ulamuliro pa inu. Iyayi! Inu mudali osamva.”
فَحَقَّ عَلَيْنَا قَوْلُ رَبِّنَا ۖ إِنَّا لَذَائِقُونَ (31)
“Kotero chiweruzo cha Ambuye wathu chadza pa ife. Ndithudi tsopano tidzachilawa.”
فَأَغْوَيْنَاكُمْ إِنَّا كُنَّا غَاوِينَ (32)
“Choncho ife tidakusocheretsani chifukwa nafenso tidali osochera.”
فَإِنَّهُمْ يَوْمَئِذٍ فِي الْعَذَابِ مُشْتَرِكُونَ (33)
Ndipo, ndithudi, patsiku limeneli onse adzalandirana chilango pakati pa wina ndi mnzake
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَفْعَلُ بِالْمُجْرِمِينَ (34)
Ndithudi mmenemo ndi mmene timachitira ndi anthu olakwa
إِنَّهُمْ كَانُوا إِذَا قِيلَ لَهُمْ لَا إِلَٰهَ إِلَّا اللَّهُ يَسْتَكْبِرُونَ (35)
Ndithudi pamene iwo, adauzidwa kuti, “Kulibe mulungu wina koma Mulungu weniweni, iwo anali kudzitukumula.”
وَيَقُولُونَ أَئِنَّا لَتَارِكُو آلِهَتِنَا لِشَاعِرٍ مَّجْنُونٍ (36)
Ndipo adanena kuti, “Kodi ife tisiye milungu yathu chifukwa cha Mlakatuli wamisala?”
بَلْ جَاءَ بِالْحَقِّ وَصَدَّقَ الْمُرْسَلِينَ (37)
Iyayi. Iye wadza ndi choonadi ndipo ali kutsimikizira uthenga wa Atumwi amene adadza kale
إِنَّكُمْ لَذَائِقُو الْعَذَابِ الْأَلِيمِ (38)
Ndithudi, inu mudzalangidwa kwambiri
وَمَا تُجْزَوْنَ إِلَّا مَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (39)
Ndipo inu mudzalandira mphotho molingana ndi ntchito zanu
إِلَّا عِبَادَ اللَّهِ الْمُخْلَصِينَ (40)
Kupatula akapolo osankhidwa a Mulungu
أُولَٰئِكَ لَهُمْ رِزْقٌ مَّعْلُومٌ (41)
Kwa iwo mphotho yawo ndi yodziwika
فَوَاكِهُ ۖ وَهُم مُّكْرَمُونَ (42)
Zipatso ndipo iwo adzalemekezeka kwambiri
فِي جَنَّاتِ النَّعِيمِ (43)
M’minda ya chisangalalo
عَلَىٰ سُرُرٍ مُّتَقَابِلِينَ (44)
Atakhala pa mipando ya chifumu moyang’anizana
يُطَافُ عَلَيْهِم بِكَأْسٍ مِّن مَّعِينٍ (45)
Pakati pawo padzaperekedwa chikho cha vinyo wabwino
بَيْضَاءَ لَذَّةٍ لِّلشَّارِبِينَ (46)
oyera ndiponso okoma kwa iwo amene amamwa
لَا فِيهَا غَوْلٌ وَلَا هُمْ عَنْهَا يُنزَفُونَ (47)
Simudzakhala mavuto mu icho ndipo sichidzawatopetsa
وَعِندَهُمْ قَاصِرَاتُ الطَّرْفِ عِينٌ (48)
Ndipo pakati pawo padzakhala akazi angwiro opanda chimasomaso
كَأَنَّهُنَّ بَيْضٌ مَّكْنُونٌ (49)
Okhala ngati mazira osamalidwa bwino
فَأَقْبَلَ بَعْضُهُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ يَتَسَاءَلُونَ (50)
Ndipo adzadza kwa anzawo ndi kumafunsana wina ndi mnzake
قَالَ قَائِلٌ مِّنْهُمْ إِنِّي كَانَ لِي قَرِينٌ (51)
Wina wochokera pakati pawo adzayankhula nati, “Ndithudi ine ndinali ndi bwenzi langa.”
يَقُولُ أَإِنَّكَ لَمِنَ الْمُصَدِّقِينَ (52)
“Amene amakonda kunena kuti; “Kodi ndiwe mmodzi mwa okhulupirira?”
أَإِذَا مِتْنَا وَكُنَّا تُرَابًا وَعِظَامًا أَإِنَّا لَمَدِينُونَ (53)
“Kodi ife tikafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa, tidzatengedwa kupita ku chiweruzo
قَالَ هَلْ أَنتُم مُّطَّلِعُونَ (54)
Iye adati, “Kodi iwe ungaone pansi?”
فَاطَّلَعَ فَرَآهُ فِي سَوَاءِ الْجَحِيمِ (55)
Motero adayang’ana pansi ndipo adamuona iye ali pakati pa moto wa ku Gahena
قَالَ تَاللَّهِ إِن كِدتَّ لَتُرْدِينِ (56)
Iye adati, “Pali Mulungu! Iwe udatsala pang’ono kundipweteka.”
وَلَوْلَا نِعْمَةُ رَبِّي لَكُنتُ مِنَ الْمُحْضَرِينَ (57)
“Ndipo kukadapanda chisomo cha Ambuye wanga ine, ndithudi, ndikadakhala mmodzi wa iwo.”
أَفَمَا نَحْنُ بِمَيِّتِينَ (58)
“Kodi ndiye kuti ife sitidzafa?”
إِلَّا مَوْتَتَنَا الْأُولَىٰ وَمَا نَحْنُ بِمُعَذَّبِينَ (59)
“Kupatula kufa koyamba, kodi ife sitidzalangidwa?”
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (60)
Ndithudi uku ndiko kupambana kwenikweni
لِمِثْلِ هَٰذَا فَلْيَعْمَلِ الْعَامِلُونَ (61)
Pofuna kupeza zotere, alekereni alimbikire amene akufuna kuti alimbikirewo
أَذَٰلِكَ خَيْرٌ نُّزُلًا أَمْ شَجَرَةُ الزَّقُّومِ (62)
Kodi chimenechi ndi chabwino kapena mtengo wa Zaqqum
إِنَّا جَعَلْنَاهَا فِتْنَةً لِّلظَّالِمِينَ (63)
Ndithudi tazipanga izi kukhala mayesero kwa anthu olakwa
إِنَّهَا شَجَرَةٌ تَخْرُجُ فِي أَصْلِ الْجَحِيمِ (64)
Ndithudi umenewu ndi mtengo umene umamera pansi pa Gahena
طَلْعُهَا كَأَنَّهُ رُءُوسُ الشَّيَاطِينِ (65)
Zipatso zake zili ngati mitu ya a Satana
فَإِنَّهُمْ لَآكِلُونَ مِنْهَا فَمَالِئُونَ مِنْهَا الْبُطُونَ (66)
Ndithudi iwo adzadya zimenezi ndi kukhutitsa mimba zawo ndi zipatsozo
ثُمَّ إِنَّ لَهُمْ عَلَيْهَا لَشَوْبًا مِّنْ حَمِيمٍ (67)
Ndithudi iwo akadzadya, adzamwa chakumwa chokonzedwa ndi madzi owira
ثُمَّ إِنَّ مَرْجِعَهُمْ لَإِلَى الْجَحِيمِ (68)
Ndithudi iwo adzapita ku Gahena
إِنَّهُمْ أَلْفَوْا آبَاءَهُمْ ضَالِّينَ (69)
Ndithudi iwo adapeza makolo awo ali osochera
فَهُمْ عَلَىٰ آثَارِهِمْ يُهْرَعُونَ (70)
Kotero iwo ali kutsatira mapazi awo
وَلَقَدْ ضَلَّ قَبْلَهُمْ أَكْثَرُ الْأَوَّلِينَ (71)
Ndithudi makolo awo adasochera iwo asanadze
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا فِيهِم مُّنذِرِينَ (72)
Ndipo, ndithudi, ife tidatumiza Atumwi pakati pawo
فَانظُرْ كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الْمُنذَرِينَ (73)
Ndipo taona zimene zidadza kwa iwo amene adachenjezedwa
إِلَّا عِبَادَ اللَّهِ الْمُخْلَصِينَ (74)
Kupatula akapolo osankhidwa a Mulungu omwe ndi anthu olungama
وَلَقَدْ نَادَانَا نُوحٌ فَلَنِعْمَ الْمُجِيبُونَ (75)
Ndipo ndithudi Nowa adatipempha Ife ndipo Ife timayankha bwino pa amene amayankha
وَنَجَّيْنَاهُ وَأَهْلَهُ مِنَ الْكَرْبِ الْعَظِيمِ (76)
Ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi banja lake ku chilango choopsa
وَجَعَلْنَا ذُرِّيَّتَهُ هُمُ الْبَاقِينَ (77)
Ndipo tidapulumutsanso ana ake
وَتَرَكْنَا عَلَيْهِ فِي الْآخِرِينَ (78)
Ndipo tidakhazikitsa ulemu pa iye pakati pa mitundu yonse yamtsogolo
سَلَامٌ عَلَىٰ نُوحٍ فِي الْعَالَمِينَ (79)
Mtendere ukhale kwa Nowa kuchokera kwa zolengedwa zonse
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (80)
Ndithudi mmenemo ndi mmene timalipirira anthu ochita zabwino
إِنَّهُ مِنْ عِبَادِنَا الْمُؤْمِنِينَ (81)
Ndithudi iye adali mmodzi mwa akapolo athu okhulupirira
ثُمَّ أَغْرَقْنَا الْآخَرِينَ (82)
Ndipo ena onse tidawamiza
۞ وَإِنَّ مِن شِيعَتِهِ لَإِبْرَاهِيمَ (83)
Ndithudi pakati pa iwo amene amatsatira njira yake adali Abrahamu
إِذْ جَاءَ رَبَّهُ بِقَلْبٍ سَلِيمٍ (84)
Pamene iye adadza kwa Ambuye wake ndi mtima woyera
إِذْ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوْمِهِ مَاذَا تَعْبُدُونَ (85)
Pamene iye adati kwa atate wake ndi anthu a mtundu wake, “Kodi ndi chiyani chimene inu muli kupembedza?”
أَئِفْكًا آلِهَةً دُونَ اللَّهِ تُرِيدُونَ (86)
“Kodi mukufuna milungu yabodza kapena Mulungu weniweni?”
فَمَا ظَنُّكُم بِرَبِّ الْعَالَمِينَ (87)
“Kodi mukuganiza zotani za Ambuye wa zolengedwa zonse?”
فَنَظَرَ نَظْرَةً فِي النُّجُومِ (88)
Ndipo iye adayang’ana nyenyezi
فَقَالَ إِنِّي سَقِيمٌ (89)
Ndipo iye adati, “Ndithudi ndili kudwala.”
فَتَوَلَّوْا عَنْهُ مُدْبِرِينَ (90)
Kotero iwo adamusiya ndi kubwerera
فَرَاغَ إِلَىٰ آلِهَتِهِمْ فَقَالَ أَلَا تَأْكُلُونَ (91)
Ndipoiyeadayang’anakwamilunguyawonati, “Kodi inu simudya?”
مَا لَكُمْ لَا تَنطِقُونَ (92)
“Kodi bwanji inu simuyankhula?”
فَرَاغَ عَلَيْهِمْ ضَرْبًا بِالْيَمِينِ (93)
Ndipo iye adadza pafupi ndi iyo ndi kuigwetsa ndi dzanja lake lamanja
فَأَقْبَلُوا إِلَيْهِ يَزِفُّونَ (94)
Nthawi yomweyo wopembedza mafano adadza kwa iye mwamsangamsanga
قَالَ أَتَعْبُدُونَ مَا تَنْحِتُونَ (95)
Iye adati, “Kodi mumapembedza zinthu zimene inu mwasema?”
وَاللَّهُ خَلَقَكُمْ وَمَا تَعْمَلُونَ (96)
“Pamene Mulungu ndiye amene adakulengani inu pamodzi ndi zosemasema zanuzi!”
قَالُوا ابْنُوا لَهُ بُنْيَانًا فَأَلْقُوهُ فِي الْجَحِيمِ (97)
Iwo adati, “Mupangireni ng’anjo ndipo muponyeni m’moto woyaka!”
فَأَرَادُوا بِهِ كَيْدًا فَجَعَلْنَاهُمُ الْأَسْفَلِينَ (98)
Iwo adachita chiwembu koma Ife tidawachititsa manyazi
وَقَالَ إِنِّي ذَاهِبٌ إِلَىٰ رَبِّي سَيَهْدِينِ (99)
Ndipo iye adati, “Ine ndithawira kwa Ambuye wanga. Ndipo Iye adzanditsogolera ine.”
رَبِّ هَبْ لِي مِنَ الصَّالِحِينَ (100)
“Ambuye wanga! Ndipatseni ana kuchokera kwa ochita ntchito zabwino.”
فَبَشَّرْنَاهُ بِغُلَامٍ حَلِيمٍ (101)
Ndipo Ife tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wamwamuna wopirira
فَلَمَّا بَلَغَ مَعَهُ السَّعْيَ قَالَ يَا بُنَيَّ إِنِّي أَرَىٰ فِي الْمَنَامِ أَنِّي أَذْبَحُكَ فَانظُرْ مَاذَا تَرَىٰ ۚ قَالَ يَا أَبَتِ افْعَلْ مَا تُؤْمَرُ ۖ سَتَجِدُنِي إِن شَاءَ اللَّهُ مِنَ الصَّابِرِينَ (102)
Ndipo pamene iye adakula mofika pa msinkhu woti angathe kuthandiza abambo ake, iye adati: “Mwana wanga! Ndithudi ine ndalota ndili kukupha ngati nsembe. Taganiza zimene uli kuziona.” Iye adati, “Atate wanga! Inu chitani monga momwe mwalamulidwira. Ngati Mulungu afuna, mudzandipeza ine wopirira!”
فَلَمَّا أَسْلَمَا وَتَلَّهُ لِلْجَبِينِ (103)
Ndipo pamene onse adadzipereka, ndipo adamugoneka iye chafufumimba
وَنَادَيْنَاهُ أَن يَا إِبْرَاهِيمُ (104)
Ndipo Ife tidamuitana ndipo tidati, “Iwe Abrahamu!”
قَدْ صَدَّقْتَ الرُّؤْيَا ۚ إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (105)
“Ndithudi wakwaniritsa maloto ako.” Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita zabwino
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ الْبَلَاءُ الْمُبِينُ (106)
Ndithudi awa adali mayesero oonekeratu
وَفَدَيْنَاهُ بِذِبْحٍ عَظِيمٍ (107)
Ndipo tidamupatsa iye nsembe yaikulu
وَتَرَكْنَا عَلَيْهِ فِي الْآخِرِينَ (108)
Ndipo Ife tidakhazikitsa ulemu pa iye pakati pa mibadwo yamtsogolo
سَلَامٌ عَلَىٰ إِبْرَاهِيمَ (109)
Mtendere ukhale pa Abrahamu
كَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (110)
Mmenemo ndi mmene timalipira mphotho kwa anthu ochita zabwino
إِنَّهُ مِنْ عِبَادِنَا الْمُؤْمِنِينَ (111)
Ndithudi iye adali mmodzi wa akapolo athu okhulupirira
وَبَشَّرْنَاهُ بِإِسْحَاقَ نَبِيًّا مِّنَ الصَّالِحِينَ (112)
Ndipo Ife tidamuuza nkhani yabwino ya Isake, Mtumwi, wochokera pakati pa anthu okhulupirira
وَبَارَكْنَا عَلَيْهِ وَعَلَىٰ إِسْحَاقَ ۚ وَمِن ذُرِّيَّتِهِمَا مُحْسِنٌ وَظَالِمٌ لِّنَفْسِهِ مُبِينٌ (113)
Ndipo Ife tidaika madalitso athu pa iye ndi pa Isake. Ndipo pakati pa ana awo pali ena ochita ntchito zabwino ndi ena amene ndi olakwa ndipo amadzipondereza okha
وَلَقَدْ مَنَنَّا عَلَىٰ مُوسَىٰ وَهَارُونَ (114)
Ndipo, ndithudi, Ife tidaonetsa chisomo chathu kwa Mose ndi Aroni
وَنَجَّيْنَاهُمَا وَقَوْمَهُمَا مِنَ الْكَرْبِ الْعَظِيمِ (115)
Ndipo tidawapulumutsa onse pamodzi ndi anthu awo ku mavuto oopsa
وَنَصَرْنَاهُمْ فَكَانُوا هُمُ الْغَالِبِينَ (116)
Ndipo Ife tidawathandiza kotero adali opambana
وَآتَيْنَاهُمَا الْكِتَابَ الْمُسْتَبِينَ (117)
Ndipo Ife tidawapatsa Buku Lopatulika limene limathandiza kufotokoza zinthu momveka bwino
وَهَدَيْنَاهُمَا الصِّرَاطَ الْمُسْتَقِيمَ (118)
Ndipo Ife tidawatsogolera ku njira yoyenera
وَتَرَكْنَا عَلَيْهِمَا فِي الْآخِرِينَ (119)
Ndipo Ife tidakhazikitsa ulemu kwa iwo pakati pa mibadwo ya mtsogolo
سَلَامٌ عَلَىٰ مُوسَىٰ وَهَارُونَ (120)
“Mtendere ukhale pa Mose ndi Aroni.”
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (121)
Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita ntchito zabwino
إِنَّهُمَا مِنْ عِبَادِنَا الْمُؤْمِنِينَ (122)
Ndithudi onse adali akapolo athu okhulupirira
وَإِنَّ إِلْيَاسَ لَمِنَ الْمُرْسَلِينَ (123)
Ndithudi Eliya anali mmodzi wa Atumwi
إِذْ قَالَ لِقَوْمِهِ أَلَا تَتَّقُونَ (124)
Pamene, iye adati kwa anthu ake, “Kodi inu simungaope Mulungu?”
أَتَدْعُونَ بَعْلًا وَتَذَرُونَ أَحْسَنَ الْخَالِقِينَ (125)
“Kodi muli kupembedza Bala ndi kusiya kupembedza Namalenga?”
اللَّهَ رَبَّكُمْ وَرَبَّ آبَائِكُمُ الْأَوَّلِينَ (126)
“Mulungu, Ambuye wanu ndi Ambuye wa makolo anu akale?”
فَكَذَّبُوهُ فَإِنَّهُمْ لَمُحْضَرُونَ (127)
Koma iwo adamukana iye ndipo ndithudi, iwo adzatengedwa
إِلَّا عِبَادَ اللَّهِ الْمُخْلَصِينَ (128)
Kupatula akapolo osankhidwa a Mulungu
وَتَرَكْنَا عَلَيْهِ فِي الْآخِرِينَ (129)
Ndithudi tidakhazikitsa ulemu kwa iye pakati pa mibadwo ya patsogolo
سَلَامٌ عَلَىٰ إِلْ يَاسِينَ (130)
“Mtendere ukhale ndi Eliya.”
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (131)
Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita ntchito zabwino
إِنَّهُ مِنْ عِبَادِنَا الْمُؤْمِنِينَ (132)
Ndithudi iye adali mmodzi wa akopolo athu okhulupirira
وَإِنَّ لُوطًا لَّمِنَ الْمُرْسَلِينَ (133)
Ndipo Loti adali mmodzi wa Atumwi
إِذْ نَجَّيْنَاهُ وَأَهْلَهُ أَجْمَعِينَ (134)
Pamene, Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi onse omutsatira
إِلَّا عَجُوزًا فِي الْغَابِرِينَ (135)
Kupatula mayi mmodzi wokalamba amene adali m’gulu la anthu otsalira m’mbuyo
ثُمَّ دَمَّرْنَا الْآخَرِينَ (136)
Ndipo Ife tidawaononga onse
وَإِنَّكُمْ لَتَمُرُّونَ عَلَيْهِم مُّصْبِحِينَ (137)
Ndithudi inu mumawadutsa nthawi ya m’mawa
وَبِاللَّيْلِ ۗ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (138)
Ndi nthawi yausiku, kodi inu simungazindikire
وَإِنَّ يُونُسَ لَمِنَ الْمُرْسَلِينَ (139)
Ndipo, ndithudi, Yona adali mmodzi wa Atumwi
إِذْ أَبَقَ إِلَى الْفُلْكِ الْمَشْحُونِ (140)
Pamene iye adathawa kupita ku chombo chodzadza kwambiri ndi katundu
فَسَاهَمَ فَكَانَ مِنَ الْمُدْحَضِينَ (141)
Iye adachita nawo mayere koma iye adali mmodzi wa olephera
فَالْتَقَمَهُ الْحُوتُ وَهُوَ مُلِيمٌ (142)
Ndipo nsomba idamumeza iye chifukwa adalakwa
فَلَوْلَا أَنَّهُ كَانَ مِنَ الْمُسَبِّحِينَ (143)
Koma kukadakhala kuti sadapemphe chikhululukiro cha Mulungu wolemekezeka
لَلَبِثَ فِي بَطْنِهِ إِلَىٰ يَوْمِ يُبْعَثُونَ (144)
Ndithudi iye akadakhalabe m’mimba mwa nsomba mpaka tsiku la kuuka kwa akufa
۞ فَنَبَذْنَاهُ بِالْعَرَاءِ وَهُوَ سَقِيمٌ (145)
Koma Ife tidakamuponya pa mtunda pamene iye anali kudwala
وَأَنبَتْنَا عَلَيْهِ شَجَرَةً مِّن يَقْطِينٍ (146)
Ndipo Ife tidameretsa chitsamba cha chipanda kuti chimere pamwamba pake
وَأَرْسَلْنَاهُ إِلَىٰ مِائَةِ أَلْفٍ أَوْ يَزِيدُونَ (147)
Ndipo tidamutumiza kwa anthu zikwi makumi khumi kapena kuposa apa
فَآمَنُوا فَمَتَّعْنَاهُمْ إِلَىٰ حِينٍ (148)
Ndipo onse adakhulupirira ndipo Ife tidawapatsa chisangalalo cha kanthawi kochepa
فَاسْتَفْتِهِمْ أَلِرَبِّكَ الْبَنَاتُ وَلَهُمُ الْبَنُونَ (149)
Ndipo tsopano afunseni kuti, “Kodi Ambuye wako ali ndi ana
أَمْ خَلَقْنَا الْمَلَائِكَةَ إِنَاثًا وَهُمْ شَاهِدُونَ (150)
Kapena kuti Ife tidalenga angelo kukhala akazi pamene iwo anali kuona
أَلَا إِنَّهُم مِّنْ إِفْكِهِمْ لَيَقُولُونَ (151)
Kodi iwo sanena zabodza pamene amati
وَلَدَ اللَّهُ وَإِنَّهُمْ لَكَاذِبُونَ (152)
“Mulungu wabereka mwana?” Ndithudi iwo ndi abodza
أَصْطَفَى الْبَنَاتِ عَلَى الْبَنِينَ (153)
Kodi iye adasankha ana aakazi m’malo mwa ana aamuna
مَا لَكُمْ كَيْفَ تَحْكُمُونَ (154)
Kodi mwatani? Kodi mumaweruza bwanji
أَفَلَا تَذَكَّرُونَ (155)
Kodi simungaganize bwino
أَمْ لَكُمْ سُلْطَانٌ مُّبِينٌ (156)
Kapena kodi inu muli ndi ulamuliro weniweni
فَأْتُوا بِكِتَابِكُمْ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (157)
Kotero bweretsani Buku lanu ngati ndinu olungama
وَجَعَلُوا بَيْنَهُ وَبَيْنَ الْجِنَّةِ نَسَبًا ۚ وَلَقَدْ عَلِمَتِ الْجِنَّةُ إِنَّهُمْ لَمُحْضَرُونَ (158)
Ndipo iwo akhazikitsa ubale pakati pa Mulungu ndi majini. Koma majini amadziwa kuti iwo adzatengedwa kupita kwa Iye
سُبْحَانَ اللَّهِ عَمَّا يَصِفُونَ (159)
Ulemerero ukhale kwa Mulungu. Iye ali pamwamba pa zimene amamuyerekeza nazo
إِلَّا عِبَادَ اللَّهِ الْمُخْلَصِينَ (160)
Kupatula akapolo a Mulungu, amene Iye amasankha
فَإِنَّكُمْ وَمَا تَعْبُدُونَ (161)
Ndithudi inu pamodzi ndi zimene mupembedza
مَا أَنتُمْ عَلَيْهِ بِفَاتِنِينَ (162)
Simungathe kusocheza wina aliyense
إِلَّا مَنْ هُوَ صَالِ الْجَحِيمِ (163)
Kupatula okhawo amene adzapita ku moto wa ku Gahena
وَمَا مِنَّا إِلَّا لَهُ مَقَامٌ مَّعْلُومٌ (164)
Aliyense wa Ife ali ndi malo ake ake
وَإِنَّا لَنَحْنُ الصَّافُّونَ (165)
Ndithudi ndife amene timaima pa mizere kupemphera
وَإِنَّا لَنَحْنُ الْمُسَبِّحُونَ (166)
Ndipo, ndithudi, ndife amene timamulemekeza
وَإِن كَانُوا لَيَقُولُونَ (167)
Ndipo, ndithudi, iwo anali kunena kuti
لَوْ أَنَّ عِندَنَا ذِكْرًا مِّنَ الْأَوَّلِينَ (168)
“Tikadakhala ndi chikumbutso monga chomwe chinali ndi anthu akale.”
لَكُنَّا عِبَادَ اللَّهِ الْمُخْلَصِينَ (169)
“Ife, ndithudi, tidakhala akapolo osankhidwa a Mulungu.”
فَكَفَرُوا بِهِ ۖ فَسَوْفَ يَعْلَمُونَ (170)
Koma iwo sakhulupilira mu izi komabe iwo adzadziwa
وَلَقَدْ سَبَقَتْ كَلِمَتُنَا لِعِبَادِنَا الْمُرْسَلِينَ (171)
Ndithudi mawu athu adatsogola kwa akapolo athu omwe ndi Atumwi athu
إِنَّهُمْ لَهُمُ الْمَنصُورُونَ (172)
Kuti iwo, ndithudi, adzathandizidwa
وَإِنَّ جُندَنَا لَهُمُ الْغَالِبُونَ (173)
Ndipo, ndithudi, gulu lathu lokha lidzakhala lopambana
فَتَوَلَّ عَنْهُمْ حَتَّىٰ حِينٍ (174)
Kotero uyambe wawasiya okha kwa kanthawi kochepa
وَأَبْصِرْهُمْ فَسَوْفَ يُبْصِرُونَ (175)
Ndipo uwaone ndipo iwo adzadzioneranso
أَفَبِعَذَابِنَا يَسْتَعْجِلُونَ (176)
Kodi iwo afuna kufulumizitsa chilango chathu
فَإِذَا نَزَلَ بِسَاحَتِهِمْ فَسَاءَ صَبَاحُ الْمُنذَرِينَ (177)
Koma pamene icho chidzadza pa iwo, udzakhala m’mawa woipa kwa iwo amene adachenjezedwa
وَتَوَلَّ عَنْهُمْ حَتَّىٰ حِينٍ (178)
Kotero uyambe wawasiya okha kwa kanthawi kochepa
وَأَبْصِرْ فَسَوْفَ يُبْصِرُونَ (179)
Ndipo uwaone ndipo nawo adzaona
سُبْحَانَ رَبِّكَ رَبِّ الْعِزَّةِ عَمَّا يَصِفُونَ (180)
Ulemerero ukhale kwa Ambuye wako, Ambuye wolemekezeka ndi wamphamvu, kuposa zimene ali kumukundikira
وَسَلَامٌ عَلَى الْمُرْسَلِينَ (181)
Ndipo mtendere ukhale kwa Atumwi onse
وَالْحَمْدُ لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (182)
Ndipo kuyamikidwa ndi kuthokoza konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس