الم (1) Alif Lam Mim |
تَنزِيلُ الْكِتَابِ لَا رَيْبَ فِيهِ مِن رَّبِّ الْعَالَمِينَ (2) Ichi ndi chivumbulutso cha Buku Lopatulika limene mulibe zokayikitsa ndi chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse |
أَمْ يَقُولُونَ افْتَرَاهُ ۚ بَلْ هُوَ الْحَقُّ مِن رَّبِّكَ لِتُنذِرَ قَوْمًا مَّا أَتَاهُم مِّن نَّذِيرٍ مِّن قَبْلِكَ لَعَلَّهُمْ يَهْتَدُونَ (3) Kodi kapena iwo amati wapeka yekha? Iyayi, ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wake kuti uchenjeze anthu amene kuyambira kale mchenjezi sanadze kwa iwo, kuti iwo akhoza kutsatira njira yoyenera |
اللَّهُ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ وَمَا بَيْنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ ثُمَّ اسْتَوَىٰ عَلَى الْعَرْشِ ۖ مَا لَكُم مِّن دُونِهِ مِن وَلِيٍّ وَلَا شَفِيعٍ ۚ أَفَلَا تَتَذَكَّرُونَ (4) Mulungu ndiye amene adalenga kumwamba ndi dziko Sajda 439 lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo m’masiku asanu ndi limodzi. Ndipo atatero Iye adabuka pa mpando wake wachifumu. Inu mulibe wokuyang’anirani kapena wokuthandizani kupatula Iye yekha. Kodi simungaganize |
يُدَبِّرُ الْأَمْرَ مِنَ السَّمَاءِ إِلَى الْأَرْضِ ثُمَّ يَعْرُجُ إِلَيْهِ فِي يَوْمٍ كَانَ مِقْدَارُهُ أَلْفَ سَنَةٍ مِّمَّا تَعُدُّونَ (5) Iye amalamulira zinthu kuchokera kumwamba mpaka pa dziko lapansi ndipo zidzakwera kudza kwa Iye m’tsiku limene muyeso wake ungathe kuyerekezedwa ndi zaka chikwi chimodzi mwa chiwerengero chomwe inu mumachidziwa |
ذَٰلِكَ عَالِمُ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ الْعَزِيزُ الرَّحِيمُ (6) Uyundiyewodziwazobisikandizooneka, Mwini mphamvu, ndi Mwini chisoni chosatha |
الَّذِي أَحْسَنَ كُلَّ شَيْءٍ خَلَقَهُ ۖ وَبَدَأَ خَلْقَ الْإِنسَانِ مِن طِينٍ (7) Amene adalenga chilichonse m’maonekedwe abwino. Ndipo adalenga munthu kuchokera ku dothi |
ثُمَّ جَعَلَ نَسْلَهُ مِن سُلَالَةٍ مِّن مَّاءٍ مَّهِينٍ (8) Ndipo adalenga ana ake kuchokera ku dontho lamadzi onyozeka |
ثُمَّ سَوَّاهُ وَنَفَخَ فِيهِ مِن رُّوحِهِ ۖ وَجَعَلَ لَكُمُ السَّمْعَ وَالْأَبْصَارَ وَالْأَفْئِدَةَ ۚ قَلِيلًا مَّا تَشْكُرُونَ (9) Ndipo iye adamuumba munthu mwaubwino ndipo adamuuzira Mzimu wake. Ndipo Iye adakupatsani inu makutu, maso ndi mitima, inu simuthokoza nthawi zambiri |
وَقَالُوا أَإِذَا ضَلَلْنَا فِي الْأَرْضِ أَإِنَّا لَفِي خَلْقٍ جَدِيدٍ ۚ بَلْ هُم بِلِقَاءِ رَبِّهِمْ كَافِرُونَ (10) Iwo adati, “Chiyani! Pamene ife taikidwa m’manda, kodi tingadzalengedwenso?” Ndithudi iwo adakana kuti adzakumana ndi Ambuye wawo |
۞ قُلْ يَتَوَفَّاكُم مَّلَكُ الْمَوْتِ الَّذِي وُكِّلَ بِكُمْ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُمْ تُرْجَعُونَ (11) Nena “Mngelo wa imfa, amene adasankhidwa kukuyang’anirani inu, adzakupangitsani kuti mufe. Kotero inu mudzabwerera kwa Ambuye wanu.” |
وَلَوْ تَرَىٰ إِذِ الْمُجْرِمُونَ نَاكِسُو رُءُوسِهِمْ عِندَ رَبِّهِمْ رَبَّنَا أَبْصَرْنَا وَسَمِعْنَا فَارْجِعْنَا نَعْمَلْ صَالِحًا إِنَّا مُوقِنُونَ (12) Iwe ukadangodzaona mmene anthu ochimwa adzagwetsera mitu yawo pamaso pa Ambuye wawo nati, “Ambuye wathu! Ife taona ndipo tamva. Tsopano tibwezereni pa dziko lapansi ndipo ife tidzagwira ntchito zachilungamo chifukwa ife, ndithudi, takhulupirira.” |
وَلَوْ شِئْنَا لَآتَيْنَا كُلَّ نَفْسٍ هُدَاهَا وَلَٰكِنْ حَقَّ الْقَوْلُ مِنِّي لَأَمْلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنَ الْجِنَّةِ وَالنَّاسِ أَجْمَعِينَ (13) Ife tikadafuna, ndithudi, tikadatsogolera mzimu uliwonse ku njira yoyenera. Koma kuti mawu ochokera kwa Ine adakwanitsidwa. “Ine ndidzadzadza Gahena ndi majini pamodzi ndi anthu.” |
فَذُوقُوا بِمَا نَسِيتُمْ لِقَاءَ يَوْمِكُمْ هَٰذَا إِنَّا نَسِينَاكُمْ ۖ وَذُوقُوا عَذَابَ الْخُلْدِ بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (14) Lawani chilango tsopano, chifukwa inu mudaiwala za tsikuli. Ndipo nafenso takuiwalani. Kotero inu lawani chilango chosatha chifukwa cha ntchito zanu zoipa |
إِنَّمَا يُؤْمِنُ بِآيَاتِنَا الَّذِينَ إِذَا ذُكِّرُوا بِهَا خَرُّوا سُجَّدًا وَسَبَّحُوا بِحَمْدِ رَبِّهِمْ وَهُمْ لَا يَسْتَكْبِرُونَ ۩ (15) Ndi okhawo amene amakhulupirira chiphunzitso chathu amene chiphunzitsocho chimati chikaphunzitsidwa, amagwa pansi kupembedza ndipo amayamikandikulemekeza Mulunguwawomodzichepetsa |
تَتَجَافَىٰ جُنُوبُهُمْ عَنِ الْمَضَاجِعِ يَدْعُونَ رَبَّهُمْ خَوْفًا وَطَمَعًا وَمِمَّا رَزَقْنَاهُمْ يُنفِقُونَ (16) Iwo amasiya makama awo ndi cholinga chopempha kwa Ambuye wawo mwamantha ndi mwa chikhulupiriro. Ndipo amapereka zaulere kuchokera ku chuma chimene tidawapatsa |
فَلَا تَعْلَمُ نَفْسٌ مَّا أُخْفِيَ لَهُم مِّن قُرَّةِ أَعْيُنٍ جَزَاءً بِمَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (17) Tsopano palibe munthu amene amadziwa madalitso amene ali kuwasungira m’nkhokwe ngati malipiro a ntchito zawo zabwino |
أَفَمَن كَانَ مُؤْمِنًا كَمَن كَانَ فَاسِقًا ۚ لَّا يَسْتَوُونَ (18) Kodi munthu wokhulupirira angafanane ndi munthu woswa malamulo ndi woipa? Iyayi, sangafanane |
أَمَّا الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ فَلَهُمْ جَنَّاتُ الْمَأْوَىٰ نُزُلًا بِمَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (19) Iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzalandira minda ngati malo awo okhala chifukwa cha ntchito zawo zabwino zimene anachita |
وَأَمَّا الَّذِينَ فَسَقُوا فَمَأْوَاهُمُ النَّارُ ۖ كُلَّمَا أَرَادُوا أَن يَخْرُجُوا مِنْهَا أُعِيدُوا فِيهَا وَقِيلَ لَهُمْ ذُوقُوا عَذَابَ النَّارِ الَّذِي كُنتُم بِهِ تُكَذِّبُونَ (20) Ndipo iwo amene amaswa malamulo, malo awo okhala ndi kumoto ndipo nthawi zonse zimene iwo adzafuna kuchokako, adzabwezedwanso komweko. Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti, “Lawani ululu wa moto umene munkati ndi bodza.” |
وَلَنُذِيقَنَّهُم مِّنَ الْعَذَابِ الْأَدْنَىٰ دُونَ الْعَذَابِ الْأَكْبَرِ لَعَلَّهُمْ يَرْجِعُونَ (21) Ndipo, ndithudi, Ife tidzawalawitsa, chilango cha m’moyo uno chisanadze, chilango choyamba kuti mwina akhoza kutembenuka |
وَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّن ذُكِّرَ بِآيَاتِ رَبِّهِ ثُمَّ أَعْرَضَ عَنْهَا ۚ إِنَّا مِنَ الْمُجْرِمِينَ مُنتَقِمُونَ (22) Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amati akakumbutsidwa chiphunzitso cha Ambuye wake, iye amabwerera m’mbuyo? Ndithudi Ife tidzalanga anthu ochimwa |
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ فَلَا تَكُن فِي مِرْيَةٍ مِّن لِّقَائِهِ ۖ وَجَعَلْنَاهُ هُدًى لِّبَنِي إِسْرَائِيلَ (23) Ndipo, ndithudi, Ife tidamupatsa Buku Mose ndipo musakayike za kulandira kwake ndipo tidalipanga ilo kukhala chotsogolera ana a Israyeli |
وَجَعَلْنَا مِنْهُمْ أَئِمَّةً يَهْدُونَ بِأَمْرِنَا لَمَّا صَبَرُوا ۖ وَكَانُوا بِآيَاتِنَا يُوقِنُونَ (24) Ndipo tidasankha pakati pawo, atsogoleri amene amapereka malangizo potsatira malamulo athu, pamene iwo anali kupirira ndi kukhulupirira mu chiphunzitso chathu |
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ يَفْصِلُ بَيْنَهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ فِيمَا كَانُوا فِيهِ يَخْتَلِفُونَ (25) Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa tsiku louka kwa akufa pa nkhani zimene anali kutsutsana |
أَوَلَمْ يَهْدِ لَهُمْ كَمْ أَهْلَكْنَا مِن قَبْلِهِم مِّنَ الْقُرُونِ يَمْشُونَ فِي مَسَاكِنِهِمْ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ ۖ أَفَلَا يَسْمَعُونَ (26) Kodi icho sichiwaphunzitsa phunziro kuti kodi ndi mibadwo ingati imene tidaononga iwo asanadze, m’nyumba zawo zimene amalowa ndi kutulukamo? Ndithudi mu izo muli chiphunzitso. Kodi iwo sangamve |
أَوَلَمْ يَرَوْا أَنَّا نَسُوقُ الْمَاءَ إِلَى الْأَرْضِ الْجُرُزِ فَنُخْرِجُ بِهِ زَرْعًا تَأْكُلُ مِنْهُ أَنْعَامُهُمْ وَأَنفُسُهُمْ ۖ أَفَلَا يُبْصِرُونَ (27) Kodi iwo saona kuti Ife timagwetsa mvula panthaka youma ndi kumeretsa mbewu zimene iwo ndi ziweto zawo zimadya? Kodi alibe maso oti angaone |
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْفَتْحُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (28) Iwo amafunsa kuti “Kodi chiweruzo chimenechi chidzachitika liti ngati zimene munenazi ndi zoona?” |
قُلْ يَوْمَ الْفَتْحِ لَا يَنفَعُ الَّذِينَ كَفَرُوا إِيمَانُهُمْ وَلَا هُمْ يُنظَرُونَ (29) Nena, “Pa tsiku lachiweruzo, chikhulupiriro cha iwo amene sakhulupirira sichidzawathandiza ndiponso sadzapeza mpumulo.” |
فَأَعْرِضْ عَنْهُمْ وَانتَظِرْ إِنَّهُم مُّنتَظِرُونَ (30) Kotero asiye okha ndipo dikira ndithudi nawonso ali kudikira |