وَالسَّمَاءِ ذَاتِ الْبُرُوجِ (1) Pali kumwamba kumene kuli nyenyezi zikulu zikulu |
وَالْيَوْمِ الْمَوْعُودِ (2) Pali tsiku lolonjezedwa |
وَشَاهِدٍ وَمَشْهُودٍ (3) Pali tsiku la umboni ndi tsiku loperekedwa umboni |
قُتِلَ أَصْحَابُ الْأُخْدُودِ (4) wotembereredwa anali anthu amene anakumba ngalande |
النَّارِ ذَاتِ الْوَقُودِ (5) Imene munali moto woyaka |
إِذْ هُمْ عَلَيْهَا قُعُودٌ (6) Pamene akhala moizungulira |
وَهُمْ عَلَىٰ مَا يَفْعَلُونَ بِالْمُؤْمِنِينَ شُهُودٌ (7) Ndipo iwo adachitira umboni pa zomwe amachitira anthu okhulupirira |
وَمَا نَقَمُوا مِنْهُمْ إِلَّا أَن يُؤْمِنُوا بِاللَّهِ الْعَزِيزِ الْحَمِيدِ (8) Iwo analibe mlandu wina uliwonse ndi anthuwa kupatula kuti anali kukhulupirira mwa Mulungu mmodzi yekha, Mwini mphamvu zonse, Mwini kuyamikidwa |
الَّذِي لَهُ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ شَهِيدٌ (9) Mwini Ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi! Ndipo Mulungu ndi mboni pa chilichonse |
إِنَّ الَّذِينَ فَتَنُوا الْمُؤْمِنِينَ وَالْمُؤْمِنَاتِ ثُمَّ لَمْ يَتُوبُوا فَلَهُمْ عَذَابُ جَهَنَّمَ وَلَهُمْ عَذَابُ الْحَرِيقِ (10) Ndithudi onse amene adazunza amuna okhulupirira, ndi akazi okhulupilira ndipo salapa machimo awo, adzalandira chilango chowawa cha moto woyaka wa ku Gahena |
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ لَهُمْ جَنَّاتٌ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ ۚ ذَٰلِكَ الْفَوْزُ الْكَبِيرُ (11) Ndithu onse amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino adzakhala m’minda imene ili ndi mitsinje ya madzi oyenda. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu |
إِنَّ بَطْشَ رَبِّكَ لَشَدِيدٌ (12) Ndithudi chilango cha Ambuye wako ndi chowawa |
إِنَّهُ هُوَ يُبْدِئُ وَيُعِيدُ (13) Ndithudi Iye ndiye amene amayambitsa chilengedwe ndipo adzachibwereza patsiku louka kwa akufa |
وَهُوَ الْغَفُورُ الْوَدُودُ (14) Ndipo Iye ndi wokhululuka ndi wachikondi chodzadza |
ذُو الْعَرْشِ الْمَجِيدُ (15) Mwini wake wa Mpando wachifumu, Wolemekezeka |
فَعَّالٌ لِّمَا يُرِيدُ (16) Iye amachita chimene afuna |
هَلْ أَتَاكَ حَدِيثُ الْجُنُودِ (17) Kodi iwe siudamve za asirikali |
فِرْعَوْنَ وَثَمُودَ (18) A Farao ndi a Thamoud |
بَلِ الَّذِينَ كَفَرُوا فِي تَكْذِيبٍ (19) Iyayi! Koma anthu osakhulupirira amazikana |
وَاللَّهُ مِن وَرَائِهِم مُّحِيطٌ (20) Ndipo Mulungu amawazungulira onse |
بَلْ هُوَ قُرْآنٌ مَّجِيدٌ (21) Iyayi! Ili ndi Buku loyera la Korani |
فِي لَوْحٍ مَّحْفُوظٍ (22) Lolembedwa m’Buku lotetezedwa |