وَالشَّمْسِ وَضُحَاهَا (1) Pali dzuwa ndi kuwala kwake |
وَالْقَمَرِ إِذَا تَلَاهَا (2) Ndi pali mwezi umene umatuluka dzuwa litalowa |
وَالنَّهَارِ إِذَا جَلَّاهَا (3) Ndi masana pamene kumayera |
وَاللَّيْلِ إِذَا يَغْشَاهَا (4) Ndi pali usiku umene umabisa |
وَالسَّمَاءِ وَمَا بَنَاهَا (5) Ndi pali Kumwamba ndi Iye amene adakulenga |
وَالْأَرْضِ وَمَا طَحَاهَا (6) Ndi pali dziko lapansi ndi Iye amene analitambasula |
وَنَفْسٍ وَمَا سَوَّاهَا (7) Ndi pali mzimu ndi Iye amene adaulenga |
فَأَلْهَمَهَا فُجُورَهَا وَتَقْوَاهَا (8) Ndi kumupatsa iye nzeru zodziwa choipa ndi chabwino |
قَدْ أَفْلَحَ مَن زَكَّاهَا (9) Ndithudi wopambana ndi amene amadziyeretsa |
وَقَدْ خَابَ مَن دَسَّاهَا (10) Ndipo wolephera ndiye amene wadzidetsa |
كَذَّبَتْ ثَمُودُ بِطَغْوَاهَا (11) Anthu a Thamoud adakana Mtumwi wawo poukiramoyerekedwa |
إِذِ انبَعَثَ أَشْقَاهَا (12) Pamenemunthuolakwakwambiri adayambitsa chipolowe |
فَقَالَ لَهُمْ رَسُولُ اللَّهِ نَاقَةَ اللَّهِ وَسُقْيَاهَا (13) Ndipo Mthenga wa Mulungu anati kwa iwo: “Samalirani ngamira ya ikazi ya Mulungu ndi tsiku lake lomwa madzi!” |
فَكَذَّبُوهُ فَعَقَرُوهَا فَدَمْدَمَ عَلَيْهِمْ رَبُّهُم بِذَنبِهِمْ فَسَوَّاهَا (14) Iwo sadakhulupirire ayi ndipo ngamirayo adaipha. Motero Ambuye wawo adawaononga chifukwa cha machimo awo ndipo adafafaniza onse mosasankha |
وَلَا يَخَافُ عُقْبَاهَا (15) Iye sadaope chotsatira chake |