×

سورة المعارج باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة المعارج

ترجمة معاني سورة المعارج باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة المعارج مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Maarij in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة المعارج باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 44 - رقم السورة 70 - الصفحة 568.

بسم الله الرحمن الرحيم

سَأَلَ سَائِلٌ بِعَذَابٍ وَاقِعٍ (1)
Wofunsa adafunsa za chilango chimene chichitike
لِّلْكَافِرِينَ لَيْسَ لَهُ دَافِعٌ (2)
Pa anthu onse osakhulupirira, chimene wina sangachiletse
مِّنَ اللَّهِ ذِي الْمَعَارِجِ (3)
Kuchokera kwa Ambuye, Mwini njira zokwerera kumwamba
تَعْرُجُ الْمَلَائِكَةُ وَالرُّوحُ إِلَيْهِ فِي يَوْمٍ كَانَ مِقْدَارُهُ خَمْسِينَ أَلْفَ سَنَةٍ (4)
Angelo ndi Mzimu amakwera kupita kwa Iye mtsiku limodzi limene lingafanizidwe ndi zaka zikwi makumi asanu
فَاصْبِرْ صَبْرًا جَمِيلًا (5)
Kotero pirira kupilira kwabwino
إِنَّهُمْ يَرَوْنَهُ بَعِيدًا (6)
Ndithudi! Iwo amaona kuti ili patali
وَنَرَاهُ قَرِيبًا (7)
Koma Ife tili kuliona lili pafupi
يَوْمَ تَكُونُ السَّمَاءُ كَالْمُهْلِ (8)
Tsiku limene kumwamba kudzaoneka ngati mkuwa wachiphalaphala
وَتَكُونُ الْجِبَالُ كَالْعِهْنِ (9)
Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya wouluka
وَلَا يَسْأَلُ حَمِيمٌ حَمِيمًا (10)
Ndipo palibe bwenzi amene adzafunse za bwenzi lake
يُبَصَّرُونَهُمْ ۚ يَوَدُّ الْمُجْرِمُ لَوْ يَفْتَدِي مِنْ عَذَابِ يَوْمِئِذٍ بِبَنِيهِ (11)
Iwo azidzawaona iwo. Munthu wochita zoipa adzafunitsitsa kuti mwina akhoza kudzipulumutsa ku chilango cha tsikuli popereka ana ake
وَصَاحِبَتِهِ وَأَخِيهِ (12)
Ndi mkazi wake ndi m’bale wake
وَفَصِيلَتِهِ الَّتِي تُؤْوِيهِ (13)
Ndi anansi ake amene adamusunga
وَمَن فِي الْأَرْضِ جَمِيعًا ثُمَّ يُنجِيهِ (14)
Ndipo zonse zimene zili padziko lapansi kuti mwina zikhoza kumupulumutsa
كَلَّا ۖ إِنَّهَا لَظَىٰ (15)
Kosatheka! Ndithudi udzakhala moto wa lawilawi wa ku Gahena
نَزَّاعَةً لِّلشَّوَىٰ (16)
wotentha mutu wonse
تَدْعُو مَنْ أَدْبَرَ وَتَوَلَّىٰ (17)
Udzaitana aliyense amene amakana choonadi
وَجَمَعَ فَأَوْعَىٰ (18)
Ndipo amangopanga chuma ndi kuchisunga
۞ إِنَّ الْإِنسَانَ خُلِقَ هَلُوعًا (19)
Ndithudi Munthu adalengedwa kukhala wosapirira
إِذَا مَسَّهُ الشَّرُّ جَزُوعًا (20)
Amakhala modandaula ngati mavuto amupeza
وَإِذَا مَسَّهُ الْخَيْرُ مَنُوعًا (21)
Ndipo amachita mwano ngati apeza zabwino
إِلَّا الْمُصَلِّينَ (22)
Kupatula okhawo amene amapemphera Al Ma’arij 619 nthawi zonse
الَّذِينَ هُمْ عَلَىٰ صَلَاتِهِمْ دَائِمُونَ (23)
Iwo amene amapemphera mowirikiza
وَالَّذِينَ فِي أَمْوَالِهِمْ حَقٌّ مَّعْلُومٌ (24)
Ndi iwo amene m’chuma chawo muli gawo limene amasiya padera
لِّلسَّائِلِ وَالْمَحْرُومِ (25)
Kuti apereke kwa anthu opempha ndi amene ali pa mavuto
وَالَّذِينَ يُصَدِّقُونَ بِيَوْمِ الدِّينِ (26)
Ndi iwo amene amakhulupirira kuti kudzakhala tsiku lachiweruzo
وَالَّذِينَ هُم مِّنْ عَذَابِ رَبِّهِم مُّشْفِقُونَ (27)
Ndi iwo amene amachita mantha ndi chilango cha Ambuye wawo
إِنَّ عَذَابَ رَبِّهِمْ غَيْرُ مَأْمُونٍ (28)
Ndithudi chilango cha Ambuye ndi chosatetezeka
وَالَّذِينَ هُمْ لِفُرُوجِهِمْ حَافِظُونَ (29)
Ndi iwo amene amadzisunga
إِلَّا عَلَىٰ أَزْوَاجِهِمْ أَوْ مَا مَلَكَتْ أَيْمَانُهُمْ فَإِنَّهُمْ غَيْرُ مَلُومِينَ (30)
Kupatula akazi awo ndi akapolo awo chifukwa iwo sadzadzudzulidwa
فَمَنِ ابْتَغَىٰ وَرَاءَ ذَٰلِكَ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْعَادُونَ (31)
Koma aliyense amene afuna kuposa awa, ndi wophwanya malamulo
وَالَّذِينَ هُمْ لِأَمَانَاتِهِمْ وَعَهْدِهِمْ رَاعُونَ (32)
Ndi iwo amene amasunga malonjezo ndi malamulo awo
وَالَّذِينَ هُم بِشَهَادَاتِهِمْ قَائِمُونَ (33)
Ndi iwo amene amapereka umboni woona nthawi zonse
وَالَّذِينَ هُمْ عَلَىٰ صَلَاتِهِمْ يُحَافِظُونَ (34)
Ndi iwo amene amalabadira mapemphero awo
أُولَٰئِكَ فِي جَنَّاتٍ مُّكْرَمُونَ (35)
Awa ndiwo amene adzalemekezeka m’minda ya Paradiso
فَمَالِ الَّذِينَ كَفَرُوا قِبَلَكَ مُهْطِعِينَ (36)
Kodi chachitika ndi chiyani kwa anthu osakhulupirira kuti azibwera mwaliwiro kudza kwa iwe
عَنِ الْيَمِينِ وَعَنِ الشِّمَالِ عِزِينَ (37)
Kuchokera kumbali ya dzanja lamanja ndi mbali yakumanzere mu unyinji wawo
أَيَطْمَعُ كُلُّ امْرِئٍ مِّنْهُمْ أَن يُدْخَلَ جَنَّةَ نَعِيمٍ (38)
Kodi aliyense wa iwo amayembekeza kukalowa m’munda wa chisangalalo
كَلَّا ۖ إِنَّا خَلَقْنَاهُم مِّمَّا يَعْلَمُونَ (39)
Kosatheka! Ndithudi Ife tawalenga kuchokera ku chinthu chimene sachidziwa
فَلَا أُقْسِمُ بِرَبِّ الْمَشَارِقِ وَالْمَغَارِبِ إِنَّا لَقَادِرُونَ (40)
Motero, Ine ndilumbira pa Ambuye wa malo onse a kum’mawa ndi kumadzulo kuti Ife tikhoza
عَلَىٰ أَن نُّبَدِّلَ خَيْرًا مِّنْهُمْ وَمَا نَحْنُ بِمَسْبُوقِينَ (41)
Kuika anthu ena abwino m’malo mwawo ndipo palibe chinthu chimene chingatiletse kutero
فَذَرْهُمْ يَخُوضُوا وَيَلْعَبُوا حَتَّىٰ يُلَاقُوا يَوْمَهُمُ الَّذِي يُوعَدُونَ (42)
Motero asiye ayambe adzinyenga ndi chisangalalo mpaka pamene adzakumana ndi tsiku lawo limene adalonjezedwa
يَوْمَ يَخْرُجُونَ مِنَ الْأَجْدَاثِ سِرَاعًا كَأَنَّهُمْ إِلَىٰ نُصُبٍ يُوفِضُونَ (43)
Tsiku limene adzatuluka mwansanga m’manda mwawo ngati anthu a pa mpikisano umene amalandirirapo mphotho
خَاشِعَةً أَبْصَارُهُمْ تَرْهَقُهُمْ ذِلَّةٌ ۚ ذَٰلِكَ الْيَوْمُ الَّذِي كَانُوا يُوعَدُونَ (44)
Atayang’ana maso awo pansi ndipo adzachititsidwa manyazi. Limeneli ndilo tsiku limene analonjezedwa
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس