هَلْ أَتَاكَ حَدِيثُ الْغَاشِيَةِ (1) Kodi wamva za chinthu chachikulu chimene chili nkudza |
وُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ خَاشِعَةٌ (2) Nkhope zina, patsiku limeneli, zidzachititsidwa manyazi |
عَامِلَةٌ نَّاصِبَةٌ (3) Pogwira ntchito zotopetsa |
تَصْلَىٰ نَارًا حَامِيَةً (4) Iwo adzalowa kumoto woyaka |
تُسْقَىٰ مِنْ عَيْنٍ آنِيَةٍ (5) Iwo adzapatsidwa madzi oti amwe kuchokera kuchitsime cha moto |
لَّيْسَ لَهُمْ طَعَامٌ إِلَّا مِن ضَرِيعٍ (6) Sadzakhala ndi chakudya china koma chiphe cha mtengo waminga |
لَّا يُسْمِنُ وَلَا يُغْنِي مِن جُوعٍ (7) Chimene sichidzawapatsa thanzi kapena kuthetsa njala |
وُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ نَّاعِمَةٌ (8) Nkhope zina, pa tsikuli, zidzakhala zosangalala |
لِّسَعْيِهَا رَاضِيَةٌ (9) Adzakondwa chifukwa cha ntchito zawo |
فِي جَنَّةٍ عَالِيَةٍ (10) Atakhala m’minda ya pamwamba |
لَّا تَسْمَعُ فِيهَا لَاغِيَةً (11) Kumene iwo sadzamva zoononga kapena za bodza |
فِيهَا عَيْنٌ جَارِيَةٌ (12) Mudzakhala kasupe wa madzi oyenda |
فِيهَا سُرُرٌ مَّرْفُوعَةٌ (13) Ndi mipando yonyamuka ya wofowofo |
وَأَكْوَابٌ مَّوْضُوعَةٌ (14) Ndi zikho zomwera zitaikidwa pambali pake |
وَنَمَارِقُ مَصْفُوفَةٌ (15) Ndi makushoni yoikidwa m’mizere |
وَزَرَابِيُّ مَبْثُوثَةٌ (16) Ndi mikeka yoyalidwa bwino pansi pake |
أَفَلَا يَنظُرُونَ إِلَى الْإِبِلِ كَيْفَ خُلِقَتْ (17) Kodi iwo saona mmene ngamira zidalengedwera |
وَإِلَى السَّمَاءِ كَيْفَ رُفِعَتْ (18) Ndi Kumwamba mmene kudakwezedwera |
وَإِلَى الْجِبَالِ كَيْفَ نُصِبَتْ (19) Ndi mapiri mmene adalengedwera mokhazikika |
وَإِلَى الْأَرْضِ كَيْفَ سُطِحَتْ (20) Ndi dziko mmene adalitambasulira |
فَذَكِّرْ إِنَّمَا أَنتَ مُذَكِّرٌ (21) Motero akumbutse, chifukwa udindo wako ndi wowakumbutsa |
لَّسْتَ عَلَيْهِم بِمُصَيْطِرٍ (22) Iwe sindiwe munthu wowakakamiza ayi |
إِلَّا مَن تَوَلَّىٰ وَكَفَرَ (23) Kupatula iye Al Fajr 651 amene abwerera m’mbuyo ndi kuyamba kusakhulupirira |
فَيُعَذِّبُهُ اللَّهُ الْعَذَابَ الْأَكْبَرَ (24) Motero Mulungu adzamulanga chilango chachikulu |
إِنَّ إِلَيْنَا إِيَابَهُمْ (25) Ndithudi onse adzabwerera kwa Ife |
ثُمَّ إِنَّ عَلَيْنَا حِسَابَهُم (26) Ndipo, ndithudi, chiwerengero cha zochita zawo chidzakhala kwa Ife |