×

سورة الأنبياء باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة الأنبياء

ترجمة معاني سورة الأنبياء باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة الأنبياء مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Anbiya in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة الأنبياء باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 112 - رقم السورة 21 - الصفحة 322.

بسم الله الرحمن الرحيم

اقْتَرَبَ لِلنَّاسِ حِسَابُهُمْ وَهُمْ فِي غَفْلَةٍ مُّعْرِضُونَ (1)
Chayandikira kwa anthu chiweruzo cha ntchito yawo ndi pamene iwo abwerera m’mbuyo monyoza
مَا يَأْتِيهِم مِّن ذِكْرٍ مِّن رَّبِّهِم مُّحْدَثٍ إِلَّا اسْتَمَعُوهُ وَهُمْ يَلْعَبُونَ (2)
Palibe chenjezo limene limadza kuchokera kwa Ambuye wawo limene iwo amalimvera kupatula pamene iwo ali kusewera
لَاهِيَةً قُلُوبُهُمْ ۗ وَأَسَرُّوا النَّجْوَى الَّذِينَ ظَلَمُوا هَلْ هَٰذَا إِلَّا بَشَرٌ مِّثْلُكُمْ ۖ أَفَتَأْتُونَ السِّحْرَ وَأَنتُمْ تُبْصِرُونَ (3)
Ndi mitima yotangwanika, iwo amene amachita zoipa amauzana mwamseri kuti, “Kodi uyu si munthu ngati inu? Kodi inu mukutsatira matsenga pamene muli kuona?”
قَالَ رَبِّي يَعْلَمُ الْقَوْلَ فِي السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ ۖ وَهُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (4)
Iye adati: “Ambuye wanga amadziwa chilichonse chimene chimanenedwa kumwamba ndi pa dziko lapansi ndipo Iye amamva zonse ndiponso amadziwa chinthu china chilichonse.”
بَلْ قَالُوا أَضْغَاثُ أَحْلَامٍ بَلِ افْتَرَاهُ بَلْ هُوَ شَاعِرٌ فَلْيَأْتِنَا بِآيَةٍ كَمَا أُرْسِلَ الْأَوَّلُونَ (5)
Koma ena amati, “Ichi si china koma maloto a bodza! Iyayi! Iye walipeka. Iyayi, iye ndi mlakatuli! Ndipo mulekeni atilangize ife chizindikiro china monga momwe Atumwi akale ankachitira.”
مَا آمَنَتْ قَبْلَهُم مِّن قَرْيَةٍ أَهْلَكْنَاهَا ۖ أَفَهُمْ يُؤْمِنُونَ (6)
Palibe umodzi wa mizinda imene tidaononga imene idakhulupirira iwo asanadze. Kodi iwo adzakhulupirira
وَمَا أَرْسَلْنَا قَبْلَكَ إِلَّا رِجَالًا نُّوحِي إِلَيْهِمْ ۖ فَاسْأَلُوا أَهْلَ الذِّكْرِ إِن كُنتُمْ لَا تَعْلَمُونَ (7)
Ndipo Ife, iwe usadabwere sitidatumize ena, koma amuna omwe timawapatsa chivumbulutso. Motero afunse anthu ozindikira ngati iwe siudziwa
وَمَا جَعَلْنَاهُمْ جَسَدًا لَّا يَأْكُلُونَ الطَّعَامَ وَمَا كَانُوا خَالِدِينَ (8)
Ife sitidawapange iwo ndi matupi amene samadya chakudya kapena amuyaya ayi
ثُمَّ صَدَقْنَاهُمُ الْوَعْدَ فَأَنجَيْنَاهُمْ وَمَن نَّشَاءُ وَأَهْلَكْنَا الْمُسْرِفِينَ (9)
Ndipo Ife tidakwaniritsa lonjezo lathu kwa iwo, ndipo tidawapulumutsa iwo pamodzi ndi ena amene Ife tidawafuna koma tidaonongeratu anthu onse ochimwa
لَقَدْ أَنزَلْنَا إِلَيْكُمْ كِتَابًا فِيهِ ذِكْرُكُمْ ۖ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (10)
Ndithudi tavumbulutsa Buku m’mene muli chikumbutso kwa inu. Kodi mulibe nzeru
وَكَمْ قَصَمْنَا مِن قَرْيَةٍ كَانَتْ ظَالِمَةً وَأَنشَأْنَا بَعْدَهَا قَوْمًا آخَرِينَ (11)
Kodi ndi mizinda ingati imene tidaononga imene idali yochita zoipa, ndipo m’malo mwawo tidaikamo anthu ena
فَلَمَّا أَحَسُّوا بَأْسَنَا إِذَا هُم مِّنْهَا يَرْكُضُونَ (12)
Ndipo pamene iwo adaona chilango chathu iwo adayesa kuthawa m’mizinda yawo
لَا تَرْكُضُوا وَارْجِعُوا إِلَىٰ مَا أُتْرِفْتُمْ فِيهِ وَمَسَاكِنِكُمْ لَعَلَّكُمْ تُسْأَلُونَ (13)
“Musathawe koma bwererani kumene mumakhala moyo wa chisangalalo ndi ku nyumba zanu kuti mukafunsidwe.”
قَالُوا يَا وَيْلَنَا إِنَّا كُنَّا ظَالِمِينَ (14)
Iwo anati, “Tsoka kwa ife! Ndithudi tinali kuchita zoipa.”
فَمَا زَالَت تِّلْكَ دَعْوَاهُمْ حَتَّىٰ جَعَلْنَاهُمْ حَصِيدًا خَامِدِينَ (15)
Koma kulira kwawo sikunathe mpaka pamene Ife tidawaononga ndi kukhala ngati munda umene wakololedwa
وَمَا خَلَقْنَا السَّمَاءَ وَالْأَرْضَ وَمَا بَيْنَهُمَا لَاعِبِينَ (16)
Sitidalengemwamasewerakumwambandidzikolapansi ndi zonse zimene zili pakati pake
لَوْ أَرَدْنَا أَن نَّتَّخِذَ لَهْوًا لَّاتَّخَذْنَاهُ مِن لَّدُنَّا إِن كُنَّا فَاعِلِينَ (17)
Ife tikadafuna kuti tisangalale tikadadzipangira tokha, ngati Ife tikadafunadi kutero
بَلْ نَقْذِفُ بِالْحَقِّ عَلَى الْبَاطِلِ فَيَدْمَغُهُ فَإِذَا هُوَ زَاهِقٌ ۚ وَلَكُمُ الْوَيْلُ مِمَّا تَصِفُونَ (18)
Iyayi! Ife timatumiza choonadi kuti chilimbane ndi bodza ndipo chimaliononga. Taonani, ilo latha. Ndipo tsoka kwa inu chifukwa cha zimene mumanena
وَلَهُ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَمَنْ عِندَهُ لَا يَسْتَكْبِرُونَ عَنْ عِبَادَتِهِ وَلَا يَسْتَحْسِرُونَ (19)
Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo onse amene ali pafupi pake sanyozera kumupembedza Iye ndipo satopa ayi
يُسَبِّحُونَ اللَّيْلَ وَالنَّهَارَ لَا يَفْتُرُونَ (20)
Iwo amamutamanda Iye masana ndi usiku ndipo sachita ulesi
أَمِ اتَّخَذُوا آلِهَةً مِّنَ الْأَرْضِ هُمْ يُنشِرُونَ (21)
Kodi iwo asankha milungu ya pa dziko lapansi imene imadzutsa anthu akufa
لَوْ كَانَ فِيهِمَا آلِهَةٌ إِلَّا اللَّهُ لَفَسَدَتَا ۚ فَسُبْحَانَ اللَّهِ رَبِّ الْعَرْشِ عَمَّا يَصِفُونَ (22)
Kukadakhala milungu ina kumeneko yoonjezera pa Mulungu weniweni, ndithudi, konse kukadaonongeka. Alemekezeke Mulungu, Mwini wa Mpando wa Chifumu, mu zimene akumunenera
لَا يُسْأَلُ عَمَّا يَفْعَلُ وَهُمْ يُسْأَلُونَ (23)
Iye sangafunsidwe pa ntchito zimene amachita pamene iwo adzafunsidwa
أَمِ اتَّخَذُوا مِن دُونِهِ آلِهَةً ۖ قُلْ هَاتُوا بُرْهَانَكُمْ ۖ هَٰذَا ذِكْرُ مَن مَّعِيَ وَذِكْرُ مَن قَبْلِي ۗ بَلْ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْلَمُونَ الْحَقَّ ۖ فَهُم مُّعْرِضُونَ (24)
Kodi kapena iwo asankha milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni? Nena, “Bweretsani umboni wanu”. Ichi ndi chikumbutso cha amene ndili nawo ndiponso iwo amakedzana. Koma ambiri a iwo sadziwa choonadi motero salabadira
وَمَا أَرْسَلْنَا مِن قَبْلِكَ مِن رَّسُولٍ إِلَّا نُوحِي إِلَيْهِ أَنَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا أَنَا فَاعْبُدُونِ (25)
Ndipo Ife sitidatumize iwe usadabadwe, Mtumwi wina aliyense amene sitinamuuze kuti, “Kulibe Mulungu wina koma Ine ndekha, kotero ndi pembedzeni Ine.”
وَقَالُوا اتَّخَذَ الرَّحْمَٰنُ وَلَدًا ۗ سُبْحَانَهُ ۚ بَلْ عِبَادٌ مُّكْرَمُونَ (26)
Iwo amati, “Mwini chisoni chosatha wabereka mwana wamwamuna.” Iye alemekezedwe! Amenewo si ena ayi koma akapolo ake olemekezeka
لَا يَسْبِقُونَهُ بِالْقَوْلِ وَهُم بِأَمْرِهِ يَعْمَلُونَ (27)
Iwo sayankhula pokhapokha Iye atayankhula, ndipo amachita zinthu potsatira malamulo ake
يَعْلَمُ مَا بَيْنَ أَيْدِيهِمْ وَمَا خَلْفَهُمْ وَلَا يَشْفَعُونَ إِلَّا لِمَنِ ارْتَضَىٰ وَهُم مِّنْ خَشْيَتِهِ مُشْفِقُونَ (28)
Iye amadziwa zonse zimene zili patsogolo pawo ndiponso zimene zili m’mbuyo mwawo ndipo iwo sangalankhulire wina aliyense chipulumutso kupatula amene Iye wamukonda ndipo iwo amanjenjemera chifukwa cha mantha pomuona Iye
۞ وَمَن يَقُلْ مِنْهُمْ إِنِّي إِلَٰهٌ مِّن دُونِهِ فَذَٰلِكَ نَجْزِيهِ جَهَنَّمَ ۚ كَذَٰلِكَ نَجْزِي الظَّالِمِينَ (29)
Ndipo ngati wina wa iwo atanena kuti, “Ndithudi ine ndine mulungu kuonjezera pa Iye.” Oteroyo adzalangidwa ndi moto wa ku Gahena. Mmenemo ndi mmene timalipirira anthu olakwa
أَوَلَمْ يَرَ الَّذِينَ كَفَرُوا أَنَّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ كَانَتَا رَتْقًا فَفَتَقْنَاهُمَا ۖ وَجَعَلْنَا مِنَ الْمَاءِ كُلَّ شَيْءٍ حَيٍّ ۖ أَفَلَا يُؤْمِنُونَ (30)
Kodi anthu osakhulupirira sadziwa kuti kumwamba ndi dziko lapansi chidali chinthu chimodzi chogwirana chimene tidachisiyanitsa? Ndipo tidapanga, chilichonse chamoyo, kuchokera ku madzi. Kodi iwo sangakhulupirire
وَجَعَلْنَا فِي الْأَرْضِ رَوَاسِيَ أَن تَمِيدَ بِهِمْ وَجَعَلْنَا فِيهَا فِجَاجًا سُبُلًا لَّعَلَّهُمْ يَهْتَدُونَ (31)
Ndipo Ife tidakhazikitsa mapiri pa dziko lapansi molimba kuti asagwedezeke pamodzi ndi iwo ndipo tidakhazikitsa misewu pa miyala kuti mwina atsogozedwe
وَجَعَلْنَا السَّمَاءَ سَقْفًا مَّحْفُوظًا ۖ وَهُمْ عَنْ آيَاتِهَا مُعْرِضُونَ (32)
Ndipo tidapanga kumwamba denga losungika bwino limene silingagwe. Komabe iwo amakana zizindikiro zake
وَهُوَ الَّذِي خَلَقَ اللَّيْلَ وَالنَّهَارَ وَالشَّمْسَ وَالْقَمَرَ ۖ كُلٌّ فِي فَلَكٍ يَسْبَحُونَ (33)
Iye ndiye amene adalenga usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi ndi china chilichonse chimene chimayenda mlengalenga
وَمَا جَعَلْنَا لِبَشَرٍ مِّن قَبْلِكَ الْخُلْدَ ۖ أَفَإِن مِّتَّ فَهُمُ الْخَالِدُونَ (34)
Palibe munthu, pambuyo pako amene tidamulenga kuti sadzafa. Ngati iweyo udzafa, kodi iwo adzakhala ndi moyo mpaka kalekale
كُلُّ نَفْسٍ ذَائِقَةُ الْمَوْتِ ۗ وَنَبْلُوكُم بِالشَّرِّ وَالْخَيْرِ فِتْنَةً ۖ وَإِلَيْنَا تُرْجَعُونَ (35)
Chilichonse cholengedwa chidzalawa imfa ndipo Ife tidzakuyesani ndi zinthu zoipa ndi zabwino ndipo ndi kwa Ife kumene nonse mudzabwerera
وَإِذَا رَآكَ الَّذِينَ كَفَرُوا إِن يَتَّخِذُونَكَ إِلَّا هُزُوًا أَهَٰذَا الَّذِي يَذْكُرُ آلِهَتَكُمْ وَهُم بِذِكْرِ الرَّحْمَٰنِ هُمْ كَافِرُونَ (36)
Pamene anthu osakhulupirira amakuona iwe, sakuganizira zabwino koma chipongwe ndipo amati, “Kodi uyu ndiye munthu amene amayankhula zoipa za milungu yanu?” Pamene iwo amakana zonse zokhudza Mwini chisoni chosatha
خُلِقَ الْإِنسَانُ مِنْ عَجَلٍ ۚ سَأُرِيكُمْ آيَاتِي فَلَا تَسْتَعْجِلُونِ (37)
Munthu adalengedwa kukhala opupuluma pochita zinthu. Ine ndidzakusonyezani zizindikiro zanga. Motero musandifulumizitse
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْوَعْدُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (38)
Iwo amati, “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene uli kunena ndi zoona?”
لَوْ يَعْلَمُ الَّذِينَ كَفَرُوا حِينَ لَا يَكُفُّونَ عَن وُجُوهِهِمُ النَّارَ وَلَا عَن ظُهُورِهِمْ وَلَا هُمْ يُنصَرُونَ (39)
Akadakhala kuti anthu osakhulupirira akudziwa tsiku limene iwo sadzakhala ndi mphamvu zophimba nkhope kapena misana yawo kudziteteza ku moto ndipo iwo sangathandizike
بَلْ تَأْتِيهِم بَغْتَةً فَتَبْهَتُهُمْ فَلَا يَسْتَطِيعُونَ رَدَّهَا وَلَا هُمْ يُنظَرُونَ (40)
Iyayi. Ilo lidzadza kwa iwo mwadzidzidzi ndipo adzadodoma ndi kusokonezeka ndipo iwo sadzatha kulibweza ndiponso sadzapatsidwa nthawi yopuma
وَلَقَدِ اسْتُهْزِئَ بِرُسُلٍ مِّن قَبْلِكَ فَحَاقَ بِالَّذِينَ سَخِرُوا مِنْهُم مَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (41)
Ndithudi Atumwi ena, adachitidwa chipongwe kale, koma anthu a chipongwe adafafanizidwa ndi chilango chimene iwo adachichitira chipongwe
قُلْ مَن يَكْلَؤُكُم بِاللَّيْلِ وَالنَّهَارِ مِنَ الرَّحْمَٰنِ ۗ بَلْ هُمْ عَن ذِكْرِ رَبِّهِم مُّعْرِضُونَ (42)
Nena, “Kodi ndani adzakutetezani inu nthawi ya usiku ndi nthawi ya masana ku mkwiyo wa Mwini chisoni?” Komabe iwo salabadira zokumbukira Ambuye wawo
أَمْ لَهُمْ آلِهَةٌ تَمْنَعُهُم مِّن دُونِنَا ۚ لَا يَسْتَطِيعُونَ نَصْرَ أَنفُسِهِمْ وَلَا هُم مِّنَّا يُصْحَبُونَ (43)
Kapena iwo ali ndi milungu ina yoti ingawateteze kwa Ife? Iyo siingathe kudziteteza yokha; ndiponso iwo sangatetezedwe kuchilango chathu
بَلْ مَتَّعْنَا هَٰؤُلَاءِ وَآبَاءَهُمْ حَتَّىٰ طَالَ عَلَيْهِمُ الْعُمُرُ ۗ أَفَلَا يَرَوْنَ أَنَّا نَأْتِي الْأَرْضَ نَنقُصُهَا مِنْ أَطْرَافِهَا ۚ أَفَهُمُ الْغَالِبُونَ (44)
Koma Ife tidapereka zokoma za m’moyo uno kwa anthuwa pamodzi ndi makolo awo mpaka pamene nthawi idawatalikira iwo. Kodi iwo saona kuti Ife timachepetsa dziko lawo kuchokera m’malire mwake? Kodi iwo ndiwo adzapambane
قُلْ إِنَّمَا أُنذِرُكُم بِالْوَحْيِ ۚ وَلَا يَسْمَعُ الصُّمُّ الدُّعَاءَ إِذَا مَا يُنذَرُونَ (45)
Nena, “Ine ndili kukuchenjezani ndi chivumbulutso, koma agonthi sadzamva kuitana pamene achenjezedwa
وَلَئِن مَّسَّتْهُمْ نَفْحَةٌ مِّنْ عَذَابِ رَبِّكَ لَيَقُولُنَّ يَا وَيْلَنَا إِنَّا كُنَّا ظَالِمِينَ (46)
Koma ngati katsoka kakang’ono kochokera kwa Ambuye wako kagwa pa iwo, ndithudi, iwo adzalira, “Tsoka kwa ife; ndithudi tidali anthu ochita zoipa.”
وَنَضَعُ الْمَوَازِينَ الْقِسْطَ لِيَوْمِ الْقِيَامَةِ فَلَا تُظْلَمُ نَفْسٌ شَيْئًا ۖ وَإِن كَانَ مِثْقَالَ حَبَّةٍ مِّنْ خَرْدَلٍ أَتَيْنَا بِهَا ۗ وَكَفَىٰ بِنَا حَاسِبِينَ (47)
Ndipo Ife tidzakhazikitsa miyeso yoyenera pa tsiku la kuuka kwa akufa ndipo aliyense sadzaponderezedwa pa china chilichonse. Ngakhale patakhala ntchito zazing’ono zolingana ngati kanthangala kakang’ono tidzazitulutsa kuti ziyesedwe. Ndipo Ife ndife okwana kuwerengera ntchito zonse
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَىٰ وَهَارُونَ الْفُرْقَانَ وَضِيَاءً وَذِكْرًا لِّلْمُتَّقِينَ (48)
Ndithudi Ife tidamupatsa Mose ndi Aroni muyeso ndi muuni wowala ndi chikumbutso kwa anthu angwiro
الَّذِينَ يَخْشَوْنَ رَبَّهُم بِالْغَيْبِ وَهُم مِّنَ السَّاعَةِ مُشْفِقُونَ (49)
Iwo amene amaopa Ambuye kuchokera m’maganizo a pansi penipeni pa mtima ndipo amaopa tsiku louka kwa akufa
وَهَٰذَا ذِكْرٌ مُّبَارَكٌ أَنزَلْنَاهُ ۚ أَفَأَنتُمْ لَهُ مُنكِرُونَ (50)
Ndipo ichi ndi chivumbulutso chodalitsika chimene tatumiza. Kodi mudzachikana
۞ وَلَقَدْ آتَيْنَا إِبْرَاهِيمَ رُشْدَهُ مِن قَبْلُ وَكُنَّا بِهِ عَالِمِينَ (51)
Ndithudi Ife tidamupatsa kale chilangizo Abrahamu ndipo tinali kumudziwa bwino
إِذْ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوْمِهِ مَا هَٰذِهِ التَّمَاثِيلُ الَّتِي أَنتُمْ لَهَا عَاكِفُونَ (52)
Pamene Iye adawauza abambo ake ndiponso anthu ake kuti, “Kodi mafano amene muli kuwapembedzawa ndi chiyani?”
قَالُوا وَجَدْنَا آبَاءَنَا لَهَا عَابِدِينَ (53)
Iwo adati, “Ife tidapeza makolo athu ali kuwapembedza.”
قَالَ لَقَدْ كُنتُمْ أَنتُمْ وَآبَاؤُكُمْ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (54)
Iye adati, “Ndithudi inu ndiponso makolo anu mwakhala muli kuchimwa kwambiri.”
قَالُوا أَجِئْتَنَا بِالْحَقِّ أَمْ أَنتَ مِنَ اللَّاعِبِينَ (55)
Iwo adati, “Kodi ndi zoona zimene wadza nazo kwa ife kapena ndi nthabwala chabe?”
قَالَ بَل رَّبُّكُمْ رَبُّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ الَّذِي فَطَرَهُنَّ وَأَنَا عَلَىٰ ذَٰلِكُم مِّنَ الشَّاهِدِينَ (56)
Iye adati, “Iyayi. Ambuye wanu ndi amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo muzimenezo ine ndichitira umboni.”
وَتَاللَّهِ لَأَكِيدَنَّ أَصْنَامَكُم بَعْدَ أَن تُوَلُّوا مُدْبِرِينَ (57)
“Ndilumbira pali Mulungu kuti ine ndidzachita chiwembu pa mafano anu inu mukangochoka.”
فَجَعَلَهُمْ جُذَاذًا إِلَّا كَبِيرًا لَّهُمْ لَعَلَّهُمْ إِلَيْهِ يَرْجِعُونَ (58)
Motero iye adaziphwanya zonse kukhala tizidutswa kupatula fano lalikulu kuti akhoza kudzalifunsa
قَالُوا مَن فَعَلَ هَٰذَا بِآلِهَتِنَا إِنَّهُ لَمِنَ الظَّالِمِينَ (59)
Iwo adati: “Kodi ndani amene wachita izi kwa milungu yathu? Ndithudi iye ali oipitsitsa.”
قَالُوا سَمِعْنَا فَتًى يَذْكُرُهُمْ يُقَالُ لَهُ إِبْرَاهِيمُ (60)
Iwo adati, “Ife tinamva mnyamata wotchedwa Abrahamu akunena za milunguyo.”
قَالُوا فَأْتُوا بِهِ عَلَىٰ أَعْيُنِ النَّاسِ لَعَلَّهُمْ يَشْهَدُونَ (61)
Iwo adati, “Mubweretseni pamaso pa anthu onse kuti achitire umboni.”
قَالُوا أَأَنتَ فَعَلْتَ هَٰذَا بِآلِهَتِنَا يَا إِبْرَاهِيمُ (62)
Iwo adati, “Kodi iwe ndi amene wachita izi ku milungu yathu? Oh Abrahamu!”
قَالَ بَلْ فَعَلَهُ كَبِيرُهُمْ هَٰذَا فَاسْأَلُوهُمْ إِن كَانُوا يَنطِقُونَ (63)
Iye adati, “Iyayi. Ndi uyu, wamkulu kuposa zonse amene waziphwanya. Afunseni, ngati angayankhule”
فَرَجَعُوا إِلَىٰ أَنفُسِهِمْ فَقَالُوا إِنَّكُمْ أَنتُمُ الظَّالِمُونَ (64)
Pamenepo iwo adayang’anizana okha nati, “Ndithudi inu ndinu anthu ochimwa kwambiri.”
ثُمَّ نُكِسُوا عَلَىٰ رُءُوسِهِمْ لَقَدْ عَلِمْتَ مَا هَٰؤُلَاءِ يَنطِقُونَ (65)
Ndipo adayang’anizananso nati, “Ndithudi iwe uli kudziwa kuti milungu iyi siiyankhula.”
قَالَ أَفَتَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ مَا لَا يَنفَعُكُمْ شَيْئًا وَلَا يَضُرُّكُمْ (66)
Abrahamu adati, “Kodi inu mumapembedza mowonjezera pa Mulungu zinthu zimene sizingathe kukuthandizani chilichonse kapena kukuonongani?”
أُفٍّ لَّكُمْ وَلِمَا تَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ ۖ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (67)
“Tsoka likhale pa inu ndi pa mafano anu amene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu! Kodi mulibe nzeru?”
قَالُوا حَرِّقُوهُ وَانصُرُوا آلِهَتَكُمْ إِن كُنتُمْ فَاعِلِينَ (68)
Onse adati, “Mutentheni kuti muteteze milungu yanu ngati mufuna kuchita china chilichonse.”
قُلْنَا يَا نَارُ كُونِي بَرْدًا وَسَلَامًا عَلَىٰ إِبْرَاهِيمَ (69)
Ife tidati, “Iwe moto khala wozizira ndi wamtendere kwa Abrahamu.”
وَأَرَادُوا بِهِ كَيْدًا فَجَعَلْنَاهُمُ الْأَخْسَرِينَ (70)
Ndipo iwo adafuna kumuononga Iye koma Ife tidawapanga iwo kukhala olephera
وَنَجَّيْنَاهُ وَلُوطًا إِلَى الْأَرْضِ الَّتِي بَارَكْنَا فِيهَا لِلْعَالَمِينَ (71)
Koma Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi Loti ndipo tidawaika ku dziko limene tidalidalitsa kuti zolengedwa zonse zikhalemo
وَوَهَبْنَا لَهُ إِسْحَاقَ وَيَعْقُوبَ نَافِلَةً ۖ وَكُلًّا جَعَلْنَا صَالِحِينَ (72)
Ndipo Ife tidamupatsa Isake ndi Yakobo ngati chidzukulu chake ndipo tidawapanga onse kukhala anthu angwiro
وَجَعَلْنَاهُمْ أَئِمَّةً يَهْدُونَ بِأَمْرِنَا وَأَوْحَيْنَا إِلَيْهِمْ فِعْلَ الْخَيْرَاتِ وَإِقَامَ الصَّلَاةِ وَإِيتَاءَ الزَّكَاةِ ۖ وَكَانُوا لَنَا عَابِدِينَ (73)
Ndipo Ife tidawasankha iwo kukhala atsogoleri olangiza anthu ku ulamuliro wathu ndipo tidawalamulira kuti azigwira ntchito zabwino ndipo, azipitiriza kupemphera ndi kupereka zothandizira osauka. Ndipo iwo anali kutitumikira Ife nthawi zonse
وَلُوطًا آتَيْنَاهُ حُكْمًا وَعِلْمًا وَنَجَّيْنَاهُ مِنَ الْقَرْيَةِ الَّتِي كَانَت تَّعْمَلُ الْخَبَائِثَ ۗ إِنَّهُمْ كَانُوا قَوْمَ سَوْءٍ فَاسِقِينَ (74)
Ndi Loti tidamupatsa luntha, utumiki ndi nzeru za chipembedzo ndipo tidamupulumutsa ku mzinda umene anthu ake anali kuchita zoipa. Ndithudi, iwo anali anthu ochita zoipa ndipo anali osamvera Mulungu
وَأَدْخَلْنَاهُ فِي رَحْمَتِنَا ۖ إِنَّهُ مِنَ الصَّالِحِينَ (75)
Ndipo Ife tidamulowetsa m’chisomo chathu, ndithudi, iye adali mmodzi wa anthu olungama
وَنُوحًا إِذْ نَادَىٰ مِن قَبْلُ فَاسْتَجَبْنَا لَهُ فَنَجَّيْنَاهُ وَأَهْلَهُ مِنَ الْكَرْبِ الْعَظِيمِ (76)
Ndi pamene Nowa adatipempha poyamba, Ife tidamva pempho lake ndipo tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake ku chilango choopsa
وَنَصَرْنَاهُ مِنَ الْقَوْمِ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا ۚ إِنَّهُمْ كَانُوا قَوْمَ سَوْءٍ فَأَغْرَقْنَاهُمْ أَجْمَعِينَ (77)
Ndiponso Ife tidamupulumutsa ku gulu la anthu amene adakana chivumbulutso chathu. Ndithudi iwo anali anthu oipa ndipo onse tidawamiza m’madzi
وَدَاوُودَ وَسُلَيْمَانَ إِذْ يَحْكُمَانِ فِي الْحَرْثِ إِذْ نَفَشَتْ فِيهِ غَنَمُ الْقَوْمِ وَكُنَّا لِحُكْمِهِمْ شَاهِدِينَ (78)
Pamene Davide ndi Solomoni adaweruza mulandu wa munda umene nkhosa zosochera za anthu ena zidadya nthawiyausiku. Ndipo Ifetidalimbonipachiweruzochawo
فَفَهَّمْنَاهَا سُلَيْمَانَ ۚ وَكُلًّا آتَيْنَا حُكْمًا وَعِلْمًا ۚ وَسَخَّرْنَا مَعَ دَاوُودَ الْجِبَالَ يُسَبِّحْنَ وَالطَّيْرَ ۚ وَكُنَّا فَاعِلِينَ (79)
Ife tidapatsa Solomoni nzeru zoweruzira nkhaniyi ndipo aliyense wa iwo tidamupatsa luntha, utumwi ndi nzeru. Tinalamula mapiri ndi mbalame kuti zikhale pamodzi ndi Davide pomutamanda Mulungu. Ndife amene tidachita zonsezi
وَعَلَّمْنَاهُ صَنْعَةَ لَبُوسٍ لَّكُمْ لِتُحْصِنَكُم مِّن بَأْسِكُمْ ۖ فَهَلْ أَنتُمْ شَاكِرُونَ (80)
Ndipo tidamuphunzitsa luso lopanga zovala za nkhondo kuti zizikutetezani pa nthawi ya nkhondo, Kodi ndinu othokoza
وَلِسُلَيْمَانَ الرِّيحَ عَاصِفَةً تَجْرِي بِأَمْرِهِ إِلَى الْأَرْضِ الَّتِي بَارَكْنَا فِيهَا ۚ وَكُنَّا بِكُلِّ شَيْءٍ عَالِمِينَ (81)
Ndi Solomoni, Ife tidampeputsira mphamvu ya mphepo. Iyo inali kuomba potsatira malamulo ake kupita kudziko limene Ife tidalidalitsa. Ndipo Ife timadziwa zinthu zonse
وَمِنَ الشَّيَاطِينِ مَن يَغُوصُونَ لَهُ وَيَعْمَلُونَ عَمَلًا دُونَ ذَٰلِكَ ۖ وَكُنَّا لَهُمْ حَافِظِينَ (82)
Ndipo pakati pa a Satana padali ena omwe amaimira m’malo mwa iye ndipo amachitanso ntchito zina. Kuonjezera apa ndipo ndife amene timawayang’anira iwo
۞ وَأَيُّوبَ إِذْ نَادَىٰ رَبَّهُ أَنِّي مَسَّنِيَ الضُّرُّ وَأَنتَ أَرْحَمُ الرَّاحِمِينَ (83)
Ndi Yobu pamene adaitana Ambuye wake nati, “Ine, ndithudi, mavuto andikuta ndipo Inu ndinu wachisoni kuposa achisoni onse.”
فَاسْتَجَبْنَا لَهُ فَكَشَفْنَا مَا بِهِ مِن ضُرٍّ ۖ وَآتَيْنَاهُ أَهْلَهُ وَمِثْلَهُم مَّعَهُمْ رَحْمَةً مِّنْ عِندِنَا وَذِكْرَىٰ لِلْعَابِدِينَ (84)
Motero Ife timamuyankha pempho lake ndipo tidamuchotsera mavuto ake ndipo tidamubwezeranso banja lake ndi zinthu zambiri zimene tidamupatsa ngati chisomo chochokera kwa Ife ndi chikumbutso kwa onse amene amatipembedza Ife
وَإِسْمَاعِيلَ وَإِدْرِيسَ وَذَا الْكِفْلِ ۖ كُلٌّ مِّنَ الصَّابِرِينَ (85)
Ndipo Ishimayeli, Idris ndi dhulkifl, onse adali anthu opirira
وَأَدْخَلْنَاهُمْ فِي رَحْمَتِنَا ۖ إِنَّهُم مِّنَ الصَّالِحِينَ (86)
Ndipo Ife tidawalowetsa m’chisomo chathu. Ndithudi iwo adali anthu olungama
وَذَا النُّونِ إِذ ذَّهَبَ مُغَاضِبًا فَظَنَّ أَن لَّن نَّقْدِرَ عَلَيْهِ فَنَادَىٰ فِي الظُّلُمَاتِ أَن لَّا إِلَٰهَ إِلَّا أَنتَ سُبْحَانَكَ إِنِّي كُنتُ مِنَ الظَّالِمِينَ (87)
Ndi dhan-Nun pamene adachoka mokwiya kwambiri chifukwa iye adali kuganiza kuti Ife sitingamulenge iye. Koma mu mdima iye adaitana, “Kulibe Mulungu wina koma Inu nokha. Ulemerero ukhale kwa Inu! Ndithudi ine ndidali mmodzi mwa anthu olakwa!”
فَاسْتَجَبْنَا لَهُ وَنَجَّيْنَاهُ مِنَ الْغَمِّ ۚ وَكَذَٰلِكَ نُنجِي الْمُؤْمِنِينَ (88)
Motero Ife tidayankha pempho lake ndipo tidamupulumutsa ku mavuto ake. Motero ndimo mmene timapulumutsira anthu okhulupirira
وَزَكَرِيَّا إِذْ نَادَىٰ رَبَّهُ رَبِّ لَا تَذَرْنِي فَرْدًا وَأَنتَ خَيْرُ الْوَارِثِينَ (89)
Ndi Zakariya pamene anaitana Ambuye wake nati, “Ambuye wanga! Musandileke ndekha. Ndipo Inu ndinu wabwinomwaokhalitsaonse.”
فَاسْتَجَبْنَا لَهُ وَوَهَبْنَا لَهُ يَحْيَىٰ وَأَصْلَحْنَا لَهُ زَوْجَهُ ۚ إِنَّهُمْ كَانُوا يُسَارِعُونَ فِي الْخَيْرَاتِ وَيَدْعُونَنَا رَغَبًا وَرَهَبًا ۖ وَكَانُوا لَنَا خَاشِعِينَ (90)
Motero Ifetidamuyankha pempho lake ndipo tidamupatsa Yohane ndipo tidathetsa uchumba wa mkazi wake. Ndithudi iwo adali ofulumira pochita ntchito zabwino ndipo amatipempha Ife ndi chikhulupiriro ndi mantha ndiponso amadzichepetsa kwa Ife
وَالَّتِي أَحْصَنَتْ فَرْجَهَا فَنَفَخْنَا فِيهَا مِن رُّوحِنَا وَجَعَلْنَاهَا وَابْنَهَا آيَةً لِّلْعَالَمِينَ (91)
Adali mkazi amene adasunga unamwali wake. Ife tidauzira mwa iye ndipo tidamupanga iye pamodzi ndi mwana wake wa mwamuna kukhala chizindikiro kwa zolengedwa zonse
إِنَّ هَٰذِهِ أُمَّتُكُمْ أُمَّةً وَاحِدَةً وَأَنَا رَبُّكُمْ فَاعْبُدُونِ (92)
Ndithudi! Ichi ndi chipembedzo chanu ndipo ndi chipembedzo chimodzi, ndipo Ine ndine Ambuye wanu motero ndipembedzeni Ine ndekha
وَتَقَطَّعُوا أَمْرَهُم بَيْنَهُمْ ۖ كُلٌّ إِلَيْنَا رَاجِعُونَ (93)
Ndipo iwo adapatukana ndi kugawa chipembedzo chawo pakati pawo ndipo ndi kwa Ife kumene adzabwerera
فَمَن يَعْمَلْ مِنَ الصَّالِحَاتِ وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَلَا كُفْرَانَ لِسَعْيِهِ وَإِنَّا لَهُ كَاتِبُونَ (94)
Motero aliyense amene achita ntchito zabwino ndipo ndi wokhulupirira moona ntchito zake sizidzakanidwa ayi. Ndithudi Ife timazilemba zonse m’Buku la chiwerengero
وَحَرَامٌ عَلَىٰ قَرْيَةٍ أَهْلَكْنَاهَا أَنَّهُمْ لَا يَرْجِعُونَ (95)
Ndipo ndi koletsedwa kuti mudzi umene tidawuwononga kuti ubwererenso
حَتَّىٰ إِذَا فُتِحَتْ يَأْجُوجُ وَمَأْجُوجُ وَهُم مِّن كُلِّ حَدَبٍ يَنسِلُونَ (96)
Mpaka pamene anthu a Ya-juj ndi Majuj adzamasulidwa ndipo iwo adzakhala akutsika kuchokera kumalo aliwonse wokwera
وَاقْتَرَبَ الْوَعْدُ الْحَقُّ فَإِذَا هِيَ شَاخِصَةٌ أَبْصَارُ الَّذِينَ كَفَرُوا يَا وَيْلَنَا قَدْ كُنَّا فِي غَفْلَةٍ مِّنْ هَٰذَا بَلْ كُنَّا ظَالِمِينَ (97)
Ndipo pamene lonjezo loona lidzafika, maso a anthu onse osakhulupirira adzapenyetsetsa mwamantha nati “Tsoka kwa ife! Ndithudi ife tidali osalabadira zimenezi. Zoonadi ife tidali ochita zoipa.”
إِنَّكُمْ وَمَا تَعْبُدُونَ مِن دُونِ اللَّهِ حَصَبُ جَهَنَّمَ أَنتُمْ لَهَا وَارِدُونَ (98)
Ndithudi! Inu pamodzi ndi zimene mukupembedza kuonjezera pa Mulungu, mudzakhala nkhuni za ku Gahena! Kumeneko nonse mudzalowako
لَوْ كَانَ هَٰؤُلَاءِ آلِهَةً مَّا وَرَدُوهَا ۖ وَكُلٌّ فِيهَا خَالِدُونَ (99)
Iyo ikadakhala milungu, siikadalowa kumeneko ndipo onse adzakhala kumeneko
لَهُمْ فِيهَا زَفِيرٌ وَهُمْ فِيهَا لَا يَسْمَعُونَ (100)
Kumeneko iwo adzalira ndipo adzakhala osamva
إِنَّ الَّذِينَ سَبَقَتْ لَهُم مِّنَّا الْحُسْنَىٰ أُولَٰئِكَ عَنْهَا مُبْعَدُونَ (101)
Ndithudi iwo amene tawaonetsera chifundo chathu, iwo adzakhala kutali ndi moto
لَا يَسْمَعُونَ حَسِيسَهَا ۖ وَهُمْ فِي مَا اشْتَهَتْ أَنفُسُهُمْ خَالِدُونَ (102)
Iwo sadzamva mkokomo wake pamene iwo ali kumene mitima yawo imafuna mpaka kalekale
لَا يَحْزُنُهُمُ الْفَزَعُ الْأَكْبَرُ وَتَتَلَقَّاهُمُ الْمَلَائِكَةُ هَٰذَا يَوْمُكُمُ الَّذِي كُنتُمْ تُوعَدُونَ (103)
Zoopsa sizidzawadandaulitsa ayi ndipo Angelo adzawalandira iwo nati,“Ili ndi tsiku lanu limene inu mudalonjezedwa.”
يَوْمَ نَطْوِي السَّمَاءَ كَطَيِّ السِّجِلِّ لِلْكُتُبِ ۚ كَمَا بَدَأْنَا أَوَّلَ خَلْقٍ نُّعِيدُهُ ۚ وَعْدًا عَلَيْنَا ۚ إِنَّا كُنَّا فَاعِلِينَ (104)
Tsiku limene tidzapinde thambo monga momwe timapindira tsamba la Buku. Monga momwe tidayamba chilengedwe choyamba momwemonso tidzachibwezeranso. Ili, ndithudi, ndi lonjezo kwa Ife. Ndithudi, Ife, tidzachita motero
وَلَقَدْ كَتَبْنَا فِي الزَّبُورِ مِن بَعْدِ الذِّكْرِ أَنَّ الْأَرْضَ يَرِثُهَا عِبَادِيَ الصَّالِحُونَ (105)
Ndipo, ndithudi, Ife tidalemba m’Buku la Masalimo, motsatira chikumbutso kuti akapolo anga angwiro adzakhala ku dziko lapansi
إِنَّ فِي هَٰذَا لَبَلَاغًا لِّقَوْمٍ عَابِدِينَ (106)
Ndithudi mu ili muli Uthenga womveka kwa anthu amene amapembedza Mulungu
وَمَا أَرْسَلْنَاكَ إِلَّا رَحْمَةً لِّلْعَالَمِينَ (107)
Ndipo sitidakutumize iwe pa chifukwa china koma ngati madalitso kwa zolengedwa zonse
قُلْ إِنَّمَا يُوحَىٰ إِلَيَّ أَنَّمَا إِلَٰهُكُمْ إِلَٰهٌ وَاحِدٌ ۖ فَهَلْ أَنتُم مُّسْلِمُونَ (108)
Nena, “Zavumbulutsidwa kwa ine kuti Mulungu wanu ndi mmodzi yekha. Kodi inu mudzadzipereka kwa Iye?”
فَإِن تَوَلَّوْا فَقُلْ آذَنتُكُمْ عَلَىٰ سَوَاءٍ ۖ وَإِنْ أَدْرِي أَقَرِيبٌ أَم بَعِيدٌ مَّا تُوعَدُونَ (109)
Koma ngati iwo safuna kumvera nena, “Ine ndili kukuchenjezani kuti tonse tidziwe. Ine sindidziwa kuti chimene mwalonjezedwa chidza msanga kapena chikadali patali.”
إِنَّهُ يَعْلَمُ الْجَهْرَ مِنَ الْقَوْلِ وَيَعْلَمُ مَا تَكْتُمُونَ (110)
Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mumayankhula mokweza ndipo amadziwanso zimene mubisa
وَإِنْ أَدْرِي لَعَلَّهُ فِتْنَةٌ لَّكُمْ وَمَتَاعٌ إِلَىٰ حِينٍ (111)
Ndipo ine sindidziwa ngati awa ndi mayeso kwa inu ndi chisangalalo cha kanthawi kochepa
قَالَ رَبِّ احْكُم بِالْحَقِّ ۗ وَرَبُّنَا الرَّحْمَٰنُ الْمُسْتَعَانُ عَلَىٰ مَا تَصِفُونَ (112)
Iye anati, “Ambuye wanga! Weruzani mwachilungamo! Ambuye wathu ndi Mwini chisoni chosatha amene chithandizo chake chimafunika pa zimene inu muonjezera.”
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس