طسم (1) Ta Sin Mim |
تِلْكَ آيَاتُ الْكِتَابِ الْمُبِينِ (2) Awa ndi mawu a m’Buku lofotokoza bwino |
نَتْلُو عَلَيْكَ مِن نَّبَإِ مُوسَىٰ وَفِرْعَوْنَ بِالْحَقِّ لِقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (3) Tidzakuuza zina za mbiri ya Mose ndi Farawo mwachoonadi kuti uuze anthu okhulupirira |
إِنَّ فِرْعَوْنَ عَلَا فِي الْأَرْضِ وَجَعَلَ أَهْلَهَا شِيَعًا يَسْتَضْعِفُ طَائِفَةً مِّنْهُمْ يُذَبِّحُ أَبْنَاءَهُمْ وَيَسْتَحْيِي نِسَاءَهُمْ ۚ إِنَّهُ كَانَ مِنَ الْمُفْسِدِينَ (4) Ndithudi Farawo adadzikweza pa dziko lapansi ndipo adagawa anthu ake m’magulumagulu ndipo gulu lina iye anali kulizunza pomapha ana awo aamuna ndi kusiya ana aakazi. Ndithudi iye adali wochita zoipa |
وَنُرِيدُ أَن نَّمُنَّ عَلَى الَّذِينَ اسْتُضْعِفُوا فِي الْأَرْضِ وَنَجْعَلَهُمْ أَئِمَّةً وَنَجْعَلَهُمُ الْوَارِثِينَ (5) Koma chidali chifuniro chathu kuti tiwapatse zabwino anthu amene adali oponderezedwa pa dziko ndi kuwasandutsa iwo kukhala atsogoleri a anthu ndi kuwapanga iwo kulowa m’malo mwa ufumu wa Farawo |
وَنُمَكِّنَ لَهُمْ فِي الْأَرْضِ وَنُرِيَ فِرْعَوْنَ وَهَامَانَ وَجُنُودَهُمَا مِنْهُم مَّا كَانُوا يَحْذَرُونَ (6) Ndikuwakhazikitsa m’dziko ndipo tinamupatsa Farawo, Hamani ndi gulu lawo la nkhondo zimene iwo anali kuopa |
وَأَوْحَيْنَا إِلَىٰ أُمِّ مُوسَىٰ أَنْ أَرْضِعِيهِ ۖ فَإِذَا خِفْتِ عَلَيْهِ فَأَلْقِيهِ فِي الْيَمِّ وَلَا تَخَافِي وَلَا تَحْزَنِي ۖ إِنَّا رَادُّوهُ إِلَيْكِ وَجَاعِلُوهُ مِنَ الْمُرْسَلِينَ (7) Ife tidauza amayi ake a Mose ponena kuti, “Muyamwitse iye koma ngati ukuda nkhawa za kukhala kwake mwamtendere, mponye mu mtsinje. Usaope ndipo usade nkhawa ayi chifukwa Ife tidzamubweretsa iye kwa iwe ndi kumupanga iye kukhala mmodzi wa Atumwi.” |
فَالْتَقَطَهُ آلُ فِرْعَوْنَ لِيَكُونَ لَهُمْ عَدُوًّا وَحَزَنًا ۗ إِنَّ فِرْعَوْنَ وَهَامَانَ وَجُنُودَهُمَا كَانُوا خَاطِئِينَ (8) Ndipo adamutola iye a banja la Farawo kuti akhoza kukhala mdani ndiponso madandaulo kwa iwo. Ndithudi Farawo, Hamani ndi Asirikali awo, onse adali ochimwa |
وَقَالَتِ امْرَأَتُ فِرْعَوْنَ قُرَّتُ عَيْنٍ لِّي وَلَكَ ۖ لَا تَقْتُلُوهُ عَسَىٰ أَن يَنفَعَنَا أَوْ نَتَّخِذَهُ وَلَدًا وَهُمْ لَا يَشْعُرُونَ (9) Mkazi wake wa Farawo adati kwa iye, “Mwana uyu akhoza kubweretsa chisangalalo kwa ine ndi iwe. Musamuphe ayi. Mwina akhoza kutithandiza kapena tikhoza kumutenga kuti akhale mwana wathu.” Koma iwo sadadziwe chimene anali kuchita |
وَأَصْبَحَ فُؤَادُ أُمِّ مُوسَىٰ فَارِغًا ۖ إِن كَادَتْ لَتُبْدِي بِهِ لَوْلَا أَن رَّبَطْنَا عَلَىٰ قَلْبِهَا لِتَكُونَ مِنَ الْمُؤْمِنِينَ (10) Mtima wa amayi ake a Mose siumaganiza zina ayi koma za Mose yekha. Iye akadaulula za iye kukadapanda kuti Ife tidamupatsamphamvukutiapitirizekukhalawokhulupirira weniweni |
وَقَالَتْ لِأُخْتِهِ قُصِّيهِ ۖ فَبَصُرَتْ بِهِ عَن جُنُبٍ وَهُمْ لَا يَشْعُرُونَ (11) Iye adati kwa mlongo wake wa Mose, “Pita umutsatire.” Iye anali kumuona kuchokera patali pamene iwo sadadziwe ayi |
۞ وَحَرَّمْنَا عَلَيْهِ الْمَرَاضِعَ مِن قَبْلُ فَقَالَتْ هَلْ أَدُلُّكُمْ عَلَىٰ أَهْلِ بَيْتٍ يَكْفُلُونَهُ لَكُمْ وَهُمْ لَهُ نَاصِحُونَ (12) Tsopano Ife tidamupanga kuti azikana kuyamwa mawere a amayi ena. Mlongo wake adati kwa iwo, “Kodi ndingakulondorereni banja limene likhoza kumulera m’malo mwanu ndi kumusamala bwino?” |
فَرَدَدْنَاهُ إِلَىٰ أُمِّهِ كَيْ تَقَرَّ عَيْنُهَا وَلَا تَحْزَنَ وَلِتَعْلَمَ أَنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (13) Ndipo tidamubweretsa iye kwa Amayi ake kuti asangalale, asiye kudandaula ndiponso kuti adziwe kuti lonjezo la Mulungu ndi loona. Koma anthu ambiri sachidziwa chimenechi |
وَلَمَّا بَلَغَ أَشُدَّهُ وَاسْتَوَىٰ آتَيْنَاهُ حُكْمًا وَعِلْمًا ۚ وَكَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (14) Ndipo pamene iye adakula msinkhu ndi kukhala munthu wokwana, tidamupatsa iye luntha ndi nzeru. Mmenemu ndi mmene timalipirira anthu ochita zabwino |
وَدَخَلَ الْمَدِينَةَ عَلَىٰ حِينِ غَفْلَةٍ مِّنْ أَهْلِهَا فَوَجَدَ فِيهَا رَجُلَيْنِ يَقْتَتِلَانِ هَٰذَا مِن شِيعَتِهِ وَهَٰذَا مِنْ عَدُوِّهِ ۖ فَاسْتَغَاثَهُ الَّذِي مِن شِيعَتِهِ عَلَى الَّذِي مِنْ عَدُوِّهِ فَوَكَزَهُ مُوسَىٰ فَقَضَىٰ عَلَيْهِ ۖ قَالَ هَٰذَا مِنْ عَمَلِ الشَّيْطَانِ ۖ إِنَّهُ عَدُوٌّ مُّضِلٌّ مُّبِينٌ (15) Ndipo Iye adalowa mu mzinda, osaonedwa ndi anthu ndipo adapeza anthu awiri ali kumenyana, wina adali wa mtundu wake ndi wina wa mtundu wa adani ake. Munthu wa mtundu wake adamupempha iye chithandizo kuti agonjetse mdani wake. Ndipo Mose adamumenya mdani wake ndi dzanja lake ndipo adamupha. Mose adati, “Iyi ndi ntchito ya Satana. Ndithudi Iye ndi mdani wa munthu wosokoneza kwenikweni.” |
قَالَ رَبِّ إِنِّي ظَلَمْتُ نَفْسِي فَاغْفِرْ لِي فَغَفَرَ لَهُ ۚ إِنَّهُ هُوَ الْغَفُورُ الرَّحِيمُ (16) Iye adati, “Ambuye! Ine ndidalakwira mzimu wanga kotero ndikhululukireni.” Ndipo Mulungu anamukhululukira iye chifukwa Iye ndi Mwini kukhululukira ndi Mwini chisoni chosatha |
قَالَ رَبِّ بِمَا أَنْعَمْتَ عَلَيَّ فَلَنْ أَكُونَ ظَهِيرًا لِّلْمُجْرِمِينَ (17) Iye adati, “Chifukwa cha chifundo chimene mwandionetsa Ambuye, ine ndili kulumbira kuti sindidzathandiza wina aliyense wochita zoipa.” |
فَأَصْبَحَ فِي الْمَدِينَةِ خَائِفًا يَتَرَقَّبُ فَإِذَا الَّذِي اسْتَنصَرَهُ بِالْأَمْسِ يَسْتَصْرِخُهُ ۚ قَالَ لَهُ مُوسَىٰ إِنَّكَ لَغَوِيٌّ مُّبِينٌ (18) M’mawa mwake iye anali kuyenda mu mzinda ndi mantha poyembekezera mavuto. Munthu uja, amene amamuthandiza cha dzulo, adamuitananso kuti amuthandize. Mose adati, “Ndi choonekeratu kuti iwe ndiwe munthu wosokoneza.” |
فَلَمَّا أَنْ أَرَادَ أَن يَبْطِشَ بِالَّذِي هُوَ عَدُوٌّ لَّهُمَا قَالَ يَا مُوسَىٰ أَتُرِيدُ أَن تَقْتُلَنِي كَمَا قَتَلْتَ نَفْسًا بِالْأَمْسِ ۖ إِن تُرِيدُ إِلَّا أَن تَكُونَ جَبَّارًا فِي الْأَرْضِ وَمَا تُرِيدُ أَن تَكُونَ مِنَ الْمُصْلِحِينَ (19) Ndipo pamene Mose ankati azim’menya mdani uja, munthuyo adati, “Iwe Mose! Kodi ufuna kundipha monga momwe unaphera munthu uja dzulo? Ndithudi iwe ufuna kukhala munthu wankhanza m’dziko lino ndiponso iwe siufuna kukhala mmodzi mwa anthu angwiro.” |
وَجَاءَ رَجُلٌ مِّنْ أَقْصَى الْمَدِينَةِ يَسْعَىٰ قَالَ يَا مُوسَىٰ إِنَّ الْمَلَأَ يَأْتَمِرُونَ بِكَ لِيَقْتُلُوكَ فَاخْرُجْ إِنِّي لَكَ مِنَ النَّاصِحِينَ (20) Ndipo munthu wina adadza kuchokera ku malire a mzinda ali kuthamanga. Iye adati, “Mose! Anthu ndi mafumu ali kuchita upo woti akuphe iwe. Tuluka mu mzindawu. Ine ndili kukulangiza iwe mwachoonadi.” |
فَخَرَجَ مِنْهَا خَائِفًا يَتَرَقَّبُ ۖ قَالَ رَبِّ نَجِّنِي مِنَ الْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (21) Iye adachoka ku Aiguputo mwamantha, ali kuyembekeza kuti zoipa zim’peza. Anali akunena kuti, “Ambuye, ndipulumutseni ku anthu oipa.” |
وَلَمَّا تَوَجَّهَ تِلْقَاءَ مَدْيَنَ قَالَ عَسَىٰ رَبِّي أَن يَهْدِيَنِي سَوَاءَ السَّبِيلِ (22) Ndipo pamene anali kuyandikira ku Midiyani Iye adati, “Ambuye anditsogolera ku njira yoyenera.” |
وَلَمَّا وَرَدَ مَاءَ مَدْيَنَ وَجَدَ عَلَيْهِ أُمَّةً مِّنَ النَّاسِ يَسْقُونَ وَوَجَدَ مِن دُونِهِمُ امْرَأَتَيْنِ تَذُودَانِ ۖ قَالَ مَا خَطْبُكُمَا ۖ قَالَتَا لَا نَسْقِي حَتَّىٰ يُصْدِرَ الرِّعَاءُ ۖ وَأَبُونَا شَيْخٌ كَبِيرٌ (23) Ndipo pamene adafika pa chitsime cha ku Midiyani, iye adapeza gulu la anthu aamuna amene adali kumwetsa ziweto zawo. Ndipo kuonjezera paiwo, padali akazi awiri amene anali kungosunga nkhosa zawo. Mose adati, “Kodi vuto lanu ndi chiyani?” Iwo adati, “Sitingathe kumwetsa nkhosa zathu pokhapokha abusa awa atachotsa ziweto zawo. Ndipo bambo wathu ndi munthu wokalamba.” |
فَسَقَىٰ لَهُمَا ثُمَّ تَوَلَّىٰ إِلَى الظِّلِّ فَقَالَ رَبِّ إِنِّي لِمَا أَنزَلْتَ إِلَيَّ مِنْ خَيْرٍ فَقِيرٌ (24) Mose adawamwetsera nkhosa zawo ndipo adachoka ndi kukakhala pa m’thunzi nati, “Ambuye, ine ndili kusowa zabwino zimene munganditumize.” |
فَجَاءَتْهُ إِحْدَاهُمَا تَمْشِي عَلَى اسْتِحْيَاءٍ قَالَتْ إِنَّ أَبِي يَدْعُوكَ لِيَجْزِيَكَ أَجْرَ مَا سَقَيْتَ لَنَا ۚ فَلَمَّا جَاءَهُ وَقَصَّ عَلَيْهِ الْقَصَصَ قَالَ لَا تَخَفْ ۖ نَجَوْتَ مِنَ الْقَوْمِ الظَّالِمِينَ (25) Mmodzi mwa akazi aja adadza kwa iye akuyenda mwamanyazi nati, “Abambo anga ali kukuitanani kuti akakulipireni chifukwa chomwetsera ziweto zathu.” Ndipo pamene Mose adadza kwa iwo, adafotokoza nkhani yake kwa iye. Bambo uja adati, “Usaope. Tsopano wapulumuka m’manja mwa anthu oipa.” |
قَالَتْ إِحْدَاهُمَا يَا أَبَتِ اسْتَأْجِرْهُ ۖ إِنَّ خَيْرَ مَنِ اسْتَأْجَرْتَ الْقَوِيُّ الْأَمِينُ (26) Mmodzi mwa akazi aja adati, “Atate, mulembeni ntchito munthu uyu. Munthu wabwino kumulemba ntchito ndi amene ali ndi mphamvu ndiponso wokhulupirika.” |
قَالَ إِنِّي أُرِيدُ أَنْ أُنكِحَكَ إِحْدَى ابْنَتَيَّ هَاتَيْنِ عَلَىٰ أَن تَأْجُرَنِي ثَمَانِيَ حِجَجٍ ۖ فَإِنْ أَتْمَمْتَ عَشْرًا فَمِنْ عِندِكَ ۖ وَمَا أُرِيدُ أَنْ أَشُقَّ عَلَيْكَ ۚ سَتَجِدُنِي إِن شَاءَ اللَّهُ مِنَ الصَّالِحِينَ (27) Atate adati, “Ine ndidzakupatsa mmodzi wa ana anga aakazi kuti umukwatire ngati ungakhale zaka zisanu ndi zitatu uli kundigwirira ntchito. Koma ngati ufuna ukhoza kugwira ntchito zaka khumi. Ine sindifuna kukuzunza ayi. Ngati Mulungu afuna, udzaona kuti ine ndine munthu wangwiro.” |
قَالَ ذَٰلِكَ بَيْنِي وَبَيْنَكَ ۖ أَيَّمَا الْأَجَلَيْنِ قَضَيْتُ فَلَا عُدْوَانَ عَلَيَّ ۖ وَاللَّهُ عَلَىٰ مَا نَقُولُ وَكِيلٌ (28) Mose adati, “Zimenezi zikhale pakati pa inu ndi ine. Mwa nthawi ziwirizi ine ndidzakwaniritsa ndipo pasadzakhale cholakwa kwa ine. Ndipo Mulungu ndi mboni pa zimene tili kukambiranazi.” |
۞ فَلَمَّا قَضَىٰ مُوسَى الْأَجَلَ وَسَارَ بِأَهْلِهِ آنَسَ مِن جَانِبِ الطُّورِ نَارًا قَالَ لِأَهْلِهِ امْكُثُوا إِنِّي آنَسْتُ نَارًا لَّعَلِّي آتِيكُم مِّنْهَا بِخَبَرٍ أَوْ جَذْوَةٍ مِّنَ النَّارِ لَعَلَّكُمْ تَصْطَلُونَ (29) Ndipo pamene adamaliza nthawi yake, iye anali kupita ndi mkazi wake. Mose adaona moto kuonjezera pa phiri la Sinai. Iye adati kwa mkazi wake, “Khala pano chifukwa ndili kuona moto. Mwina mwake ndikhoza kubweretsa kuchokera kumeneko nkhani kapena mwatso woyaka umene ukhoza kuotha.” |
فَلَمَّا أَتَاهَا نُودِيَ مِن شَاطِئِ الْوَادِ الْأَيْمَنِ فِي الْبُقْعَةِ الْمُبَارَكَةِ مِنَ الشَّجَرَةِ أَن يَا مُوسَىٰ إِنِّي أَنَا اللَّهُ رَبُّ الْعَالَمِينَ (30) Ndipo pamene adafika pamalo paja, iye adaitanidwa kuchokera kumbali ya manja ya chigwa pa malo odalitsika kuchokera mumtengo. “oh iwe Mose! Ndithudi, Ine ndine Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse.” |
وَأَنْ أَلْقِ عَصَاكَ ۖ فَلَمَّا رَآهَا تَهْتَزُّ كَأَنَّهَا جَانٌّ وَلَّىٰ مُدْبِرًا وَلَمْ يُعَقِّبْ ۚ يَا مُوسَىٰ أَقْبِلْ وَلَا تَخَفْ ۖ إِنَّكَ مِنَ الْآمِنِينَ (31) “Ndipo ponya pansi ndodo yako.” Ndipo pamene adaona ndodo yake ili kuyenda ngati njoka, adatembenuka nathawa osabwevukanso. “Iwe Mose! Bwerera ndipo usaope. Iwe ndiwe mmodzi wa anthu otetezedwa.” |
اسْلُكْ يَدَكَ فِي جَيْبِكَ تَخْرُجْ بَيْضَاءَ مِنْ غَيْرِ سُوءٍ وَاضْمُمْ إِلَيْكَ جَنَاحَكَ مِنَ الرَّهْبِ ۖ فَذَانِكَ بُرْهَانَانِ مِن رَّبِّكَ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ وَمَلَئِهِ ۚ إِنَّهُمْ كَانُوا قَوْمًا فَاسِقِينَ (32) “Ika dzanja lako m’thumba, ndipo ilo lidzakhala loyera kwambiri lopanda chilema ndipo ika dzanja lako pamtima pako kuti uchoke mantha. Kotero zimenezi ndi zizindikiro ziwiri za Ambuye wako kwa Farao ndi mafumu ake. Mosakaika iwo ndi anthu osakhulupirira.” |
قَالَ رَبِّ إِنِّي قَتَلْتُ مِنْهُمْ نَفْسًا فَأَخَافُ أَن يَقْتُلُونِ (33) Mose adati, “Ambuye wanga! Ine ndidapha mmodzi mwa anthu awo ndipo ndili ndi mantha kuti mwina akhoza kukandipha.” |
وَأَخِي هَارُونُ هُوَ أَفْصَحُ مِنِّي لِسَانًا فَأَرْسِلْهُ مَعِيَ رِدْءًا يُصَدِّقُنِي ۖ إِنِّي أَخَافُ أَن يُكَذِّبُونِ (34) “Ndipo Aroni, m’bale wanga, amayankhula bwino kuposa ine. Mutumizeni iye pamodzi ndi ine kuti akhoza kukandithandiza kuti akandiyankhulire. Ndithudi ine ndiopa kuti akandikana.” |
قَالَ سَنَشُدُّ عَضُدَكَ بِأَخِيكَ وَنَجْعَلُ لَكُمَا سُلْطَانًا فَلَا يَصِلُونَ إِلَيْكُمَا ۚ بِآيَاتِنَا أَنتُمَا وَمَنِ اتَّبَعَكُمَا الْغَالِبُونَ (35) Iye adati, “Ife tidzakuonjezera mphamvu pokhala ndi m’bale wako ndipo ndiika pa inu awiri umboni ndipo iwo sadzatha kukupwetekani inu chifukwa cha zizindikiro zathu. Inu pamodzi ndi onse amene amakutsatirani mudzapambana.” |
فَلَمَّا جَاءَهُم مُّوسَىٰ بِآيَاتِنَا بَيِّنَاتٍ قَالُوا مَا هَٰذَا إِلَّا سِحْرٌ مُّفْتَرًى وَمَا سَمِعْنَا بِهَٰذَا فِي آبَائِنَا الْأَوَّلِينَ (36) Ndipo pamene Mose adadza kwa iwo ndi zizindikiro zathu zooneka, iwo adati, “Izi si zina ayi koma matsenga ongopeka ndiponso ife sitidamvepo kuti za mtundu uwu zinachitikapo kuchokera kwa makolo athu akale.” |
وَقَالَ مُوسَىٰ رَبِّي أَعْلَمُ بِمَن جَاءَ بِالْهُدَىٰ مِنْ عِندِهِ وَمَن تَكُونُ لَهُ عَاقِبَةُ الدَّارِ ۖ إِنَّهُ لَا يُفْلِحُ الظَّالِمُونَ (37) Ndipo Mose adati, “Ambuye wanga amadziwa bwinobwino munthu amene amabweretsa chilangizo chochokera kwa Iye, ndiponso kwa amene tsogolo lake ndi labwino. Ndithudi anthu onse ochimwa sadzapambana ayi.” |
وَقَالَ فِرْعَوْنُ يَا أَيُّهَا الْمَلَأُ مَا عَلِمْتُ لَكُم مِّنْ إِلَٰهٍ غَيْرِي فَأَوْقِدْ لِي يَا هَامَانُ عَلَى الطِّينِ فَاجْعَل لِّي صَرْحًا لَّعَلِّي أَطَّلِعُ إِلَىٰ إِلَٰهِ مُوسَىٰ وَإِنِّي لَأَظُنُّهُ مِنَ الْكَاذِبِينَ (38) Farawo adati, “oh inu mafumu! Inu mulibe mulungu wina amene ine ndimudziwa kupatula ine ndekha. Haman, ndipangireni ine njerwa zadothi ndipo mundimangire nyumba yaitali, yonga nsanja, kuti ndikwerepo kupita kwa Mulungu wa Mose. Ndithudi ine ndili kumuganizira kuti Mose ndi mmodzi mwa anthu abodza.” |
وَاسْتَكْبَرَ هُوَ وَجُنُودُهُ فِي الْأَرْضِ بِغَيْرِ الْحَقِّ وَظَنُّوا أَنَّهُمْ إِلَيْنَا لَا يُرْجَعُونَ (39) Farawo ndi Asirikali ake adadzikweza kwambiri mu dziko la Aiguputo popanda chifukwa ndipo iwo anali kuganiza kuti sadzabwereranso kwa Ife |
فَأَخَذْنَاهُ وَجُنُودَهُ فَنَبَذْنَاهُمْ فِي الْيَمِّ ۖ فَانظُرْ كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الظَّالِمِينَ (40) Ndipo tidamutenga iye pamodzi ndi asirikali ake ndipo tidawamiza m’nyanja. Ganiza chimene amaona anthu ochita zoipa |
وَجَعَلْنَاهُمْ أَئِمَّةً يَدْعُونَ إِلَى النَّارِ ۖ وَيَوْمَ الْقِيَامَةِ لَا يُنصَرُونَ (41) Ife tidawapanga iwo kukhala atsogoleri oitana anthu kuti apite kumoto koma pa tsiku la kuuka kwa akufa, palibe mmodzi amene adzawathandiza iwo |
وَأَتْبَعْنَاهُمْ فِي هَٰذِهِ الدُّنْيَا لَعْنَةً ۖ وَيَوْمَ الْقِيَامَةِ هُم مِّنَ الْمَقْبُوحِينَ (42) Ife tidawatsatira ndi matemberero m’dziko lino ndipo pa tsiku la kuuka kwa akufa iwo adzakhala anthu onyozeka |
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ مِن بَعْدِ مَا أَهْلَكْنَا الْقُرُونَ الْأُولَىٰ بَصَائِرَ لِلنَّاسِ وَهُدًى وَرَحْمَةً لَّعَلَّهُمْ يَتَذَكَّرُونَ (43) Ndipo ife tidaononga mibadwo yoyamba yakale ndipo tidamupatsa Mose Buku la Chipangano Chakale monga nyali, langizo ndi chifundo kwa anthu kuti mwina akhoza kuchenjezedwa |
وَمَا كُنتَ بِجَانِبِ الْغَرْبِيِّ إِذْ قَضَيْنَا إِلَىٰ مُوسَى الْأَمْرَ وَمَا كُنتَ مِنَ الشَّاهِدِينَ (44) Iwe kudalibe, ku mbali ya kumadzulo kwa phiri, pamene Ife tinali kumupatsa Mose udindo wake ndiponso iwe kunalibe pa mwambowu |
وَلَٰكِنَّا أَنشَأْنَا قُرُونًا فَتَطَاوَلَ عَلَيْهِمُ الْعُمُرُ ۚ وَمَا كُنتَ ثَاوِيًا فِي أَهْلِ مَدْيَنَ تَتْلُو عَلَيْهِمْ آيَاتِنَا وَلَٰكِنَّا كُنَّا مُرْسِلِينَ (45) Koma Ife tidalenga mibadwo yambiri Mose atafa kale imene inali ndi moyo wautali. Iwe siunakhale pakati pa anthu a ku Midiyani ndi kumawalakatulira chivumbulutso chathu. Koma Ife ndi amene timatumiza Atumwi |
وَمَا كُنتَ بِجَانِبِ الطُّورِ إِذْ نَادَيْنَا وَلَٰكِن رَّحْمَةً مِّن رَّبِّكَ لِتُنذِرَ قَوْمًا مَّا أَتَاهُم مِّن نَّذِيرٍ مِّن قَبْلِكَ لَعَلَّهُمْ يَتَذَكَّرُونَ (46) Ndipo iwe kudalibe m’mbali mwa phiri la Sinai pamene tidamuitana Mose. Koma adali madalitso ochokera kwa Ambuye wako kuti ukachenjeze mtundu wa anthu umene unalipo iwe usanadze kotero kuti akhoza kuchenjezedwa |
وَلَوْلَا أَن تُصِيبَهُم مُّصِيبَةٌ بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيهِمْ فَيَقُولُوا رَبَّنَا لَوْلَا أَرْسَلْتَ إِلَيْنَا رَسُولًا فَنَتَّبِعَ آيَاتِكَ وَنَكُونَ مِنَ الْمُؤْمِنِينَ (47) Tikanapanda kukutumiza iwe ndipo mazunzo akadawagwera chifukwa cha ntchito zawo zoipa, iwo akadati, “Ambuye, chifukwa chiyani simudatitumizire Mtumwi kotero kuti tikadatsatira mawu anu ndiponso tikadakhala okhulupirira.” |
فَلَمَّا جَاءَهُمُ الْحَقُّ مِنْ عِندِنَا قَالُوا لَوْلَا أُوتِيَ مِثْلَ مَا أُوتِيَ مُوسَىٰ ۚ أَوَلَمْ يَكْفُرُوا بِمَا أُوتِيَ مُوسَىٰ مِن قَبْلُ ۖ قَالُوا سِحْرَانِ تَظَاهَرَا وَقَالُوا إِنَّا بِكُلٍّ كَافِرُونَ (48) Ndipo pamene choonadi chadza kwa iwo kuchokera kwa Ife, iwo ali kufunsa kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani iye sadapatsidwe monga zomwe zidapatsidwa kwa Mose?” Kodi iwo sadakane zimene zidapatsidwa kwa Mose kale? Iwo amati, “Zizindikiro ziwiri za matsenga zili zothandizana.” Ndiponso amanena, “Ife sitidzakhulupirira mu china chilichonse cha zimenezi.” |
قُلْ فَأْتُوا بِكِتَابٍ مِّنْ عِندِ اللَّهِ هُوَ أَهْدَىٰ مِنْهُمَا أَتَّبِعْهُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (49) Nena, “Bweretsani Buku lochokera kwa Mulungu limene lili ndi langizo labwino kuposa malangizo awa ndipo ine ndidzatsatira ngati zimene muli kunena ndi zoona.” |
فَإِن لَّمْ يَسْتَجِيبُوا لَكَ فَاعْلَمْ أَنَّمَا يَتَّبِعُونَ أَهْوَاءَهُمْ ۚ وَمَنْ أَضَلُّ مِمَّنِ اتَّبَعَ هَوَاهُ بِغَيْرِ هُدًى مِّنَ اللَّهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الظَّالِمِينَ (50) Ngati iwo akanika kukuyankha, dziwa kuti iwo ali kutsatira zilakolako zawo. Kodi ndani amene ali wolakwa kwambiri kuposa munthu amene amatsatira zilakolako zake opanda langizo la Mulungu? Ndithudi Mulungu satsogolera anthu olakwa |
۞ وَلَقَدْ وَصَّلْنَا لَهُمُ الْقَوْلَ لَعَلَّهُمْ يَتَذَكَّرُونَ (51) Ndithudi tatumiza mawu athu motsatana kwa iwo kuti akhoze kuchenjezedwa |
الَّذِينَ آتَيْنَاهُمُ الْكِتَابَ مِن قَبْلِهِ هُم بِهِ يُؤْمِنُونَ (52) Iwo amene kale tidawapatsa Buku lino lisadadze, amakhulupirira mwa ilo |
وَإِذَا يُتْلَىٰ عَلَيْهِمْ قَالُوا آمَنَّا بِهِ إِنَّهُ الْحَقُّ مِن رَّبِّنَا إِنَّا كُنَّا مِن قَبْلِهِ مُسْلِمِينَ (53) Pamene limalakatulidwa kwa iwo, amati iwowo “Ife tili kulikhulupirira Bukuli chifukwa ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wathu. Ife tidadzipereka kwathunthu kalekale mawu awa asadadze.” |
أُولَٰئِكَ يُؤْتَوْنَ أَجْرَهُم مَّرَّتَيْنِ بِمَا صَبَرُوا وَيَدْرَءُونَ بِالْحَسَنَةِ السَّيِّئَةَ وَمِمَّا رَزَقْنَاهُمْ يُنفِقُونَ (54) Anthu awa mphotho yawo idzaperekedwa kwa iwo kawiri chifukwa iwo adapirira ndipo amagonjetsa choipa pochita chabwino ndi kumapereka gawo la chaulere pa katundu amene tidawapatsa |
وَإِذَا سَمِعُوا اللَّغْوَ أَعْرَضُوا عَنْهُ وَقَالُوا لَنَا أَعْمَالُنَا وَلَكُمْ أَعْمَالُكُمْ سَلَامٌ عَلَيْكُمْ لَا نَبْتَغِي الْجَاهِلِينَ (55) Ndipo iwo akamva mawu oipa, salabadira zonenazo koma amati, “Ife tili ndi ntchito zathu ndipo nanunso muli ndi ntchito zanu. Mtendere ukhale kwa inu. Ife sitifuna kugwirizana ndi anthu osadziwa.” |
إِنَّكَ لَا تَهْدِي مَنْ أَحْبَبْتَ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ يَهْدِي مَن يَشَاءُ ۚ وَهُوَ أَعْلَمُ بِالْمُهْتَدِينَ (56) Iwe siungamutsogolere aliyense amene umufuna. Ndi Mulungu yekha amene amatsogolera aliyense amene Iye wamufuna. Iye amadziwa bwino anthu amene ali oyenera |
وَقَالُوا إِن نَّتَّبِعِ الْهُدَىٰ مَعَكَ نُتَخَطَّفْ مِنْ أَرْضِنَا ۚ أَوَلَمْ نُمَكِّن لَّهُمْ حَرَمًا آمِنًا يُجْبَىٰ إِلَيْهِ ثَمَرَاتُ كُلِّ شَيْءٍ رِّزْقًا مِّن لَّدُنَّا وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (57) Iwo amati, “Ngati ife titsatira chilangizo chako, ife tikuopakulandidwadzikolathu.”KodiIfesitidawakhazikire malo otetezedwa kumene zipatso za mtundu uliwonse zimaperekedwa ngati chakudya kuchokera kwa Ife? Ndithudi ambiri a iwo ndi anthu osadziwa |
وَكَمْ أَهْلَكْنَا مِن قَرْيَةٍ بَطِرَتْ مَعِيشَتَهَا ۖ فَتِلْكَ مَسَاكِنُهُمْ لَمْ تُسْكَن مِّن بَعْدِهِمْ إِلَّا قَلِيلًا ۖ وَكُنَّا نَحْنُ الْوَارِثِينَ (58) Kodi ndi mizinda ingati imene tidaononga imene idali kunyada chifukwa cha chuma chake? Kotero zimenezi ndizo nyumba zawo zimene sadakhalitsemo ndipo tsopano eni ake ndife |
وَمَا كَانَ رَبُّكَ مُهْلِكَ الْقُرَىٰ حَتَّىٰ يَبْعَثَ فِي أُمِّهَا رَسُولًا يَتْلُو عَلَيْهِمْ آيَاتِنَا ۚ وَمَا كُنَّا مُهْلِكِي الْقُرَىٰ إِلَّا وَأَهْلُهَا ظَالِمُونَ (59) Ndipo Ambuye wako sadaononge mizinda mpaka pamene Iye adadzutsa kuchokera mu iyo, Mtumwi amene amalalikira za chivumbulutso chathu ndipo Ife sitidzaononga mzinda pokhapokha anthu okhala mmenemo ali olakwa |
وَمَا أُوتِيتُم مِّن شَيْءٍ فَمَتَاعُ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَزِينَتُهَا ۚ وَمَا عِندَ اللَّهِ خَيْرٌ وَأَبْقَىٰ ۚ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (60) Zinthu zimene mwapatsidwa si zina koma chakudya ndiponso chionetsero chopanda pake cha m’moyo uno. Koma chimene chili ndi Mulungu ndicho chabwino ndiponso chokhalitsa. Kodi simungathe kuzindikira |
أَفَمَن وَعَدْنَاهُ وَعْدًا حَسَنًا فَهُوَ لَاقِيهِ كَمَن مَّتَّعْنَاهُ مَتَاعَ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ثُمَّ هُوَ يَوْمَ الْقِيَامَةِ مِنَ الْمُحْضَرِينَ (61) Kodi anthu awiriwa ndi ofanana? Iye amene tamulonjeza lonjezo labwino ndipo adzalikwaniritsa ndi iye amene tamupatsa zokoma zambiri za m’moyo uno koma pa tsiku lachiweruzo adzakhala m’gulu la iwo olangidwa |
وَيَوْمَ يُنَادِيهِمْ فَيَقُولُ أَيْنَ شُرَكَائِيَ الَّذِينَ كُنتُمْ تَزْعُمُونَ (62) Pa tsiku limeneli Mulungu adzawaitana ndipo adzati, “Kodi aja munkati ndi anzanga ali kuti?” |
قَالَ الَّذِينَ حَقَّ عَلَيْهِمُ الْقَوْلُ رَبَّنَا هَٰؤُلَاءِ الَّذِينَ أَغْوَيْنَا أَغْوَيْنَاهُمْ كَمَا غَوَيْنَا ۖ تَبَرَّأْنَا إِلَيْكَ ۖ مَا كَانُوا إِيَّانَا يَعْبُدُونَ (63) Iwo amene adzapezeka ndi mlandu wotere adzati, “Awa ndiwo anthu amene ife tidawasocheretsa. Ife tidawasocheretsa chifukwa nafenso tidali osochera. Ife tsopano tadzipatula (kuchoka mwa iwo) ndi kudza kwa inu. Si ndife amene iwo anali kupembedza.” |
وَقِيلَ ادْعُوا شُرَكَاءَكُمْ فَدَعَوْهُمْ فَلَمْ يَسْتَجِيبُوا لَهُمْ وَرَأَوُا الْعَذَابَ ۚ لَوْ أَنَّهُمْ كَانُوا يَهْتَدُونَ (64) Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti, “Itanani anzanu kuti akuthandizeni.” Iwo adzawaitana koma iwo sadzawamva ayi. Ndipo iwo adzalawa chilango chowawa. Iwo adzafunitsitsa akadatsogozedwa bwino |
وَيَوْمَ يُنَادِيهِمْ فَيَقُولُ مَاذَا أَجَبْتُمُ الْمُرْسَلِينَ (65) Tsiku limene Mulungu adzawaitana nati, “Kodi inu mudanena zotani kwa Mtumwi?” |
فَعَمِيَتْ عَلَيْهِمُ الْأَنبَاءُ يَوْمَئِذٍ فَهُمْ لَا يَتَسَاءَلُونَ (66) Zodandaula zawo sizidzamveka ayi, kotero sadzatha kufunsana wina ndi mnzake |
فَأَمَّا مَن تَابَ وَآمَنَ وَعَمِلَ صَالِحًا فَعَسَىٰ أَن يَكُونَ مِنَ الْمُفْلِحِينَ (67) Akakhala iye amene alapa zoipa zake nakhulupirira ndipo achita ntchito zabwino, mwina akhoza kudzakhala pakati pa anthu opambana |
وَرَبُّكَ يَخْلُقُ مَا يَشَاءُ وَيَخْتَارُ ۗ مَا كَانَ لَهُمُ الْخِيَرَةُ ۚ سُبْحَانَ اللَّهِ وَتَعَالَىٰ عَمَّا يُشْرِكُونَ (68) Ndipo Ambuye wako amalenga ndi kusankha aliyense amene Iye wamufuna. Kusankha si kwawo ayi. Ulemerero ukhale kwa Mulungu ndipo Iye atalikirane ndi zimene amamufanizira nazo |
وَرَبُّكَ يَعْلَمُ مَا تُكِنُّ صُدُورُهُمْ وَمَا يُعْلِنُونَ (69) Ambuye wako amadziwa zonse zimene amazibisa m’mitima mwawo ndiponso zimene amaziulula |
وَهُوَ اللَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ لَهُ الْحَمْدُ فِي الْأُولَىٰ وَالْآخِرَةِ ۖ وَلَهُ الْحُكْمُ وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (70) Iye ndi Mulungu ndipo palibenso mulungu wina koma Iye yekha. Kuyamikidwa konse ndi kwake m’moyo uno ndiponso m’moyo umene uli nkudza. Ndipo chake ndi chiweruzo ndipo kwa Iye mudzabwerera |
قُلْ أَرَأَيْتُمْ إِن جَعَلَ اللَّهُ عَلَيْكُمُ اللَّيْلَ سَرْمَدًا إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ مَنْ إِلَٰهٌ غَيْرُ اللَّهِ يَأْتِيكُم بِضِيَاءٍ ۖ أَفَلَا تَسْمَعُونَ (71) Nena, “Ndiuzeni! Ngati Mulungu atapanga usiku kuti usache mpaka pa tsiku louka kwa akufa, kodi ndi mulungu uti kupatula Mulungu weniweni amene akhoza kukupatsani usana? Kodi simukumva?” |
قُلْ أَرَأَيْتُمْ إِن جَعَلَ اللَّهُ عَلَيْكُمُ النَّهَارَ سَرْمَدًا إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ مَنْ إِلَٰهٌ غَيْرُ اللَّهِ يَأْتِيكُم بِلَيْلٍ تَسْكُنُونَ فِيهِ ۖ أَفَلَا تُبْصِرُونَ (72) Nena, “Ndiuzeni! Ngati Mulungu atapanga usana kuti kusade mpaka pa tsiku louka kwa akufa, kodi ndi mulungu uti kupatula Mulungu weniweni amene akhoza kukupatsani usiku umene inu mumapumulamo? Kodi inu simukuona?” |
وَمِن رَّحْمَتِهِ جَعَلَ لَكُمُ اللَّيْلَ وَالنَّهَارَ لِتَسْكُنُوا فِيهِ وَلِتَبْتَغُوا مِن فَضْلِهِ وَلَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (73) Mwachifundo chake wakupatsani usiku ndi usana kuti muzipezamo mpumulo ndi kufunafuna chisomo chake ndi kuti muzithokoza |
وَيَوْمَ يُنَادِيهِمْ فَيَقُولُ أَيْنَ شُرَكَائِيَ الَّذِينَ كُنتُمْ تَزْعُمُونَ (74) Ndipo pa tsiku limene adzawaitana iwo nati, “Kodi ali kuti iwo amene mumaganiza kuti ndi anzanga?” |
وَنَزَعْنَا مِن كُلِّ أُمَّةٍ شَهِيدًا فَقُلْنَا هَاتُوا بُرْهَانَكُمْ فَعَلِمُوا أَنَّ الْحَقَّ لِلَّهِ وَضَلَّ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَفْتَرُونَ (75) Ndipo nthawi yomweyo tidzaitana mboni kuchokera ku mtundu uliwonse ndipo tidzati, “Bweretsani umboni wanu.” Nthawi imeneyo adzadziwa kuti mwini wake choonadi ndi Mulungu ndipo zonse zimene amapeka zidzawathawira |
۞ إِنَّ قَارُونَ كَانَ مِن قَوْمِ مُوسَىٰ فَبَغَىٰ عَلَيْهِمْ ۖ وَآتَيْنَاهُ مِنَ الْكُنُوزِ مَا إِنَّ مَفَاتِحَهُ لَتَنُوءُ بِالْعُصْبَةِ أُولِي الْقُوَّةِ إِذْ قَالَ لَهُ قَوْمُهُ لَا تَفْرَحْ ۖ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ الْفَرِحِينَ (76) Ndithudi Karuni, mosakayika, adali wa ku mtundu wa Mose. Koma iye amawanyoza iwo chifukwa Ife tidamupatsa nkhokwe za chuma zimene ndithudi makiyi ake samatheka kunyamulidwa ndi anthu angapo a mphamvu. Anthu ake adati kwa iye, “Usadzikundikire chifukwa Mulungu sakonda anthu odzikundikira chifukwa cha chuma.” |
وَابْتَغِ فِيمَا آتَاكَ اللَّهُ الدَّارَ الْآخِرَةَ ۖ وَلَا تَنسَ نَصِيبَكَ مِنَ الدُّنْيَا ۖ وَأَحْسِن كَمَا أَحْسَنَ اللَّهُ إِلَيْكَ ۖ وَلَا تَبْغِ الْفَسَادَ فِي الْأَرْضِ ۖ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ الْمُفْسِدِينَ (77) “Koma ufunefune, kudzera m’zimene Mulungu wakupatsa iwe, kuti upeze moyo umene uli nkudza, ndiponso usaiwale udindo wako m’dziko lino. Khala wabwino monga Mulungu wakuonetsera ubwino wake. Ndipo usalimbike pochita zoipa padziko lapansi chifukwa Mulungu sakonda anthu ochita zoipa.” |
قَالَ إِنَّمَا أُوتِيتُهُ عَلَىٰ عِلْمٍ عِندِي ۚ أَوَلَمْ يَعْلَمْ أَنَّ اللَّهَ قَدْ أَهْلَكَ مِن قَبْلِهِ مِنَ الْقُرُونِ مَنْ هُوَ أَشَدُّ مِنْهُ قُوَّةً وَأَكْثَرُ جَمْعًا ۚ وَلَا يُسْأَلُ عَن ذُنُوبِهِمُ الْمُجْرِمُونَ (78) Iye adati, “Chuma ichi chidapatsidwa kwa ine chifukwa cha nzeru zanga.” Kodi iye sadadziwe kuti Mulungu adaononga m’badwo wonse wa anthu amene adali ndi mphamvu zambiri ndiponso olemera kwambiri iye asanabadwe? Anthu ochita zoipa sadzafunsidwa za machimo awo |
فَخَرَجَ عَلَىٰ قَوْمِهِ فِي زِينَتِهِ ۖ قَالَ الَّذِينَ يُرِيدُونَ الْحَيَاةَ الدُّنْيَا يَا لَيْتَ لَنَا مِثْلَ مَا أُوتِيَ قَارُونُ إِنَّهُ لَذُو حَظٍّ عَظِيمٍ (79) Kotero iye adapita kwa anthu ake monyadira atavala bwino. Anthu amene adali kukonda moyo wa pa dziko lapansi adati, “Tikadakhala kuti tidali nazo ngati zinthu zimene zili ndi Karuni! Ndithudi iye ndi wolemera kwambiri.” |
وَقَالَ الَّذِينَ أُوتُوا الْعِلْمَ وَيْلَكُمْ ثَوَابُ اللَّهِ خَيْرٌ لِّمَنْ آمَنَ وَعَمِلَ صَالِحًا وَلَا يُلَقَّاهَا إِلَّا الصَّابِرُونَ (80) Koma iye amene adapatsidwa nzeru adati: “Tsoka kwa inu! Mphotho ya Mulungu m’moyo umene uli nkudza ndi yabwino kwa iwo amene amakhulupirira ndipo amachita zabwino.” Koma mphothoyo palibe amene adzailandira kupatula okhawo amene amapirira |
فَخَسَفْنَا بِهِ وَبِدَارِهِ الْأَرْضَ فَمَا كَانَ لَهُ مِن فِئَةٍ يَنصُرُونَهُ مِن دُونِ اللَّهِ وَمَا كَانَ مِنَ الْمُنتَصِرِينَ (81) Kotero Ife tidalamulira nthaka kuti imumeze Karuni pamodzi ndi chuma chake ndipo sadapeze wina womuthandiza kwa Mulungu ndipo iye sadathe kudziteteza |
وَأَصْبَحَ الَّذِينَ تَمَنَّوْا مَكَانَهُ بِالْأَمْسِ يَقُولُونَ وَيْكَأَنَّ اللَّهَ يَبْسُطُ الرِّزْقَ لِمَن يَشَاءُ مِنْ عِبَادِهِ وَيَقْدِرُ ۖ لَوْلَا أَن مَّنَّ اللَّهُ عَلَيْنَا لَخَسَفَ بِنَا ۖ وَيْكَأَنَّهُ لَا يُفْلِحُ الْكَافِرُونَ (82) Ndipo iwo amene anali kukhumbira chuma chake chadzulo adayamba kunena kuti, “Taonani! Mulungu amapereka moolowa manja kwa aliyense amene wamufuna ndi monyalapsa kwa aliyense amene Iye wamufuna. Akadakhala kuti sadatilangize ife chisoni chake, Iye akadalamulira nthaka kuti itimeze. Taonani! anthu okana Mulungu sadzakhala opambana ngakhale pang’ono.” |
تِلْكَ الدَّارُ الْآخِرَةُ نَجْعَلُهَا لِلَّذِينَ لَا يُرِيدُونَ عُلُوًّا فِي الْأَرْضِ وَلَا فَسَادًا ۚ وَالْعَاقِبَةُ لِلْمُتَّقِينَ (83) Kunena za m’moyo umene uli nkudza, udzakhala wa iwo amene sadzikweza pa dziko lapansi kapena kuchita zoipa. Ndipo mapeto abwino ndi a iwo amene ali angwiro |
مَن جَاءَ بِالْحَسَنَةِ فَلَهُ خَيْرٌ مِّنْهَا ۖ وَمَن جَاءَ بِالسَّيِّئَةِ فَلَا يُجْزَى الَّذِينَ عَمِلُوا السَّيِّئَاتِ إِلَّا مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (84) Aliyense amene achita zabwino adzalipidwa zochuluka. Koma iye amene achita zoipa ndiponso iwo amene achita ntchito zoipa adzangolipidwa molingana ndi zimene anali kuchita |
إِنَّ الَّذِي فَرَضَ عَلَيْكَ الْقُرْآنَ لَرَادُّكَ إِلَىٰ مَعَادٍ ۚ قُل رَّبِّي أَعْلَمُ مَن جَاءَ بِالْهُدَىٰ وَمَنْ هُوَ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (85) Ndithudi Iye amene adalamulira Buku la Korani kuti livumbulutsidwe kwa iwe adzakubwezera kumalo komwe udzapite. Nena, “Ambuye wanga adziwa bwino iye amene amabweretsa langizo loonadi ndiponso iye amene ndi wosochera.” |
وَمَا كُنتَ تَرْجُو أَن يُلْقَىٰ إِلَيْكَ الْكِتَابُ إِلَّا رَحْمَةً مِّن رَّبِّكَ ۖ فَلَا تَكُونَنَّ ظَهِيرًا لِّلْكَافِرِينَ (86) Ndipo iwe siumayembekezera kuti Buku lolemekezeka lidzavumbulitsidwa kwa iwe koma ndi chifundo chochokera kwa Ambuye wako. Kotero usavomereze zochita za anthu omwe ali osakhulupirira |
وَلَا يَصُدُّنَّكَ عَنْ آيَاتِ اللَّهِ بَعْدَ إِذْ أُنزِلَتْ إِلَيْكَ ۖ وَادْعُ إِلَىٰ رَبِّكَ ۖ وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ الْمُشْرِكِينَ (87) Usalole wina aliyense kuti akubweze ku chivumbulutso cha Mulungu pamene chavumbulutsidwa kwa iwe ndipo aitane anthu kuti adze kwa Ambuye wako ndipo usakhale m’gulu la anthu amene amaphatikiza milungu ina ndi Mulungu weniweni |
وَلَا تَدْعُ مَعَ اللَّهِ إِلَٰهًا آخَرَ ۘ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۚ كُلُّ شَيْءٍ هَالِكٌ إِلَّا وَجْهَهُ ۚ لَهُ الْحُكْمُ وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (88) Ndipo usamphatikize mulungu wina ndi Mulungu weniweni. Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Zinthu zonse ndi zakutha kupatula Iye yekha. Chake ndi chiweruzo ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera |