حم (1) Ha Mim |
تَنزِيلُ الْكِتَابِ مِنَ اللَّهِ الْعَزِيزِ الْحَكِيمِ (2) Chivumbulutso cha Buku ndi chochokera kwa Mulungu, Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru |
إِنَّ فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ لَآيَاتٍ لِّلْمُؤْمِنِينَ (3) Ndithudi kumwamba ndi dziko lapansi kuli zizindikiro kwa anthu okhulupirira |
وَفِي خَلْقِكُمْ وَمَا يَبُثُّ مِن دَابَّةٍ آيَاتٌ لِّقَوْمٍ يُوقِنُونَ (4) M’chilengedwe chanu nyama zimapezeka paliponse pa dziko lapansi ndipo ndi zizindikiro kwa iwo amene ali okhulupirira kwenikweni |
وَاخْتِلَافِ اللَّيْلِ وَالنَّهَارِ وَمَا أَنزَلَ اللَّهُ مِنَ السَّمَاءِ مِن رِّزْقٍ فَأَحْيَا بِهِ الْأَرْضَ بَعْدَ مَوْتِهَا وَتَصْرِيفِ الرِّيَاحِ آيَاتٌ لِّقَوْمٍ يَعْقِلُونَ (5) Ndi m’kasinthidwe ka usiku ndi usana ndi m’chakudya chimene amatumiza kuchokera ku mitambo ndipo amapereka moyo ku nthaka imene idali yakufa ndipo m’kasinthidwe ka mphepo, muli zizindikiro kwa anthu ozindikira |
تِلْكَ آيَاتُ اللَّهِ نَتْلُوهَا عَلَيْكَ بِالْحَقِّ ۖ فَبِأَيِّ حَدِيثٍ بَعْدَ اللَّهِ وَآيَاتِهِ يُؤْمِنُونَ (6) Ichi ndi chivumbulutso chochokera kwa Mulungu chimene tili kulakatula kwa iwe mwachoonadi. Nanga ndi uthenga uti wa Mulungu ndi chivumbulutso chake chiti chomwe iwo akhoza kukhulupirira |
وَيْلٌ لِّكُلِّ أَفَّاكٍ أَثِيمٍ (7) Tsoka kwa wochimwa aliyense wabodza |
يَسْمَعُ آيَاتِ اللَّهِ تُتْلَىٰ عَلَيْهِ ثُمَّ يُصِرُّ مُسْتَكْبِرًا كَأَن لَّمْ يَسْمَعْهَا ۖ فَبَشِّرْهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٍ (8) Amene amamva mawu a Mulungu amene ali kunenedwa kwa iye ndipo amapitirizabe kunyada ngati iye sanamve. Motero muuze iye za chilango chowawa |
وَإِذَا عَلِمَ مِنْ آيَاتِنَا شَيْئًا اتَّخَذَهَا هُزُوًا ۚ أُولَٰئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ مُّهِينٌ (9) Ndipo pamene iye akamva mawu a Mulungu, amawasandutsa kukhala masewera. Ndipo kwa otere kudzakhala chilango chochititsa manyazi |
مِّن وَرَائِهِمْ جَهَنَّمُ ۖ وَلَا يُغْنِي عَنْهُم مَّا كَسَبُوا شَيْئًا وَلَا مَا اتَّخَذُوا مِن دُونِ اللَّهِ أَوْلِيَاءَ ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌ (10) Kutsogolo kwawo kuli Gahena, ndipo sadzapeza phindu lina lililonse pa ntchito zawo kapenakwaiwoameneadawasandutsakukhalawowasamala poonjezera pa Mulungu. Ndipo iwo adzalandira chilango chowawa |
هَٰذَا هُدًى ۖ وَالَّذِينَ كَفَرُوا بِآيَاتِ رَبِّهِمْ لَهُمْ عَذَابٌ مِّن رِّجْزٍ أَلِيمٌ (11) Ichi ndi chilangizo choona. Ndipo iwo amene amakana zizindikiro za Ambuye wawo, adzalandira chilango chapadera chowawa |
۞ اللَّهُ الَّذِي سَخَّرَ لَكُمُ الْبَحْرَ لِتَجْرِيَ الْفُلْكُ فِيهِ بِأَمْرِهِ وَلِتَبْتَغُوا مِن فَضْلِهِ وَلَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (12) Ndi Mulungu amene adachepetsa mphamvu ya nyanja kuti masitima aziyenda mwaulamuliro wake ndipo kuti inu mukhoza kufuna chisomo chake kuti muzimuthokoza |
وَسَخَّرَ لَكُم مَّا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ جَمِيعًا مِّنْهُ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يَتَفَكَّرُونَ (13) Ndipo Iye adachepetsa mphamvu ya chinthu chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu amene amaganiza mofatsa |
قُل لِّلَّذِينَ آمَنُوا يَغْفِرُوا لِلَّذِينَ لَا يَرْجُونَ أَيَّامَ اللَّهِ لِيَجْزِيَ قَوْمًا بِمَا كَانُوا يَكْسِبُونَ (14) Auze iwo amene amakhulupirira kuti akhululukire iwo amene sakhulupirira m’masiku a Mulungu kuti Iye akhoza kulipira anthu chimene amachita |
مَنْ عَمِلَ صَالِحًا فَلِنَفْسِهِ ۖ وَمَنْ أَسَاءَ فَعَلَيْهَا ۖ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُمْ تُرْجَعُونَ (15) Aliyense amene amachita zabwino amachitira mzimu wake ndipo aliyense amene amachita zoipa adzilakwira yekha. Pomaliza nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu |
وَلَقَدْ آتَيْنَا بَنِي إِسْرَائِيلَ الْكِتَابَ وَالْحُكْمَ وَالنُّبُوَّةَ وَرَزَقْنَاهُم مِّنَ الطَّيِّبَاتِ وَفَضَّلْنَاهُمْ عَلَى الْعَالَمِينَ (16) Ndithudi Ife tidawapatsa ana a Israyeli Buku ndi luntha lozindikira mawu a Mulungu ndi Utumwi ndipo tidawapatsa zinthu zokoma ndipo tidawakonda iwo kuposa mitundu ina yonse |
وَآتَيْنَاهُم بَيِّنَاتٍ مِّنَ الْأَمْرِ ۖ فَمَا اخْتَلَفُوا إِلَّا مِن بَعْدِ مَا جَاءَهُمُ الْعِلْمُ بَغْيًا بَيْنَهُمْ ۚ إِنَّ رَبَّكَ يَقْضِي بَيْنَهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ فِيمَا كَانُوا فِيهِ يَخْتَلِفُونَ (17) Ndipo Ife tidawapatsa zizindikiro zooneka za chipembedzo. Ndipo iwo adayamba mipatuko pamene nzeru zidaperekedwa kwa iwo chifukwa cha njiru pakati pawo. Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa tsiku lachiweruzo pa nkhani zimene anali kutsutsana |
ثُمَّ جَعَلْنَاكَ عَلَىٰ شَرِيعَةٍ مِّنَ الْأَمْرِ فَاتَّبِعْهَا وَلَا تَتَّبِعْ أَهْوَاءَ الَّذِينَ لَا يَعْلَمُونَ (18) Ndipo iwe takuika pa njira yoyenera. Motero tsatira yoyenerayo ndipo usatsatire zilakolako za iwo amene sadziwa chilichonse |
إِنَّهُمْ لَن يُغْنُوا عَنكَ مِنَ اللَّهِ شَيْئًا ۚ وَإِنَّ الظَّالِمِينَ بَعْضُهُمْ أَوْلِيَاءُ بَعْضٍ ۖ وَاللَّهُ وَلِيُّ الْمُتَّقِينَ (19) Ndithudi iwo sangakuthandize chilichonse ku mkwiyo wa Mulungu. Ndi anthu oipa okha okha omwe amakhala ngati atetezi a wina ndi mnzake koma Mulungu ndi Mtetezi wa iwo amene amalewa zoipa |
هَٰذَا بَصَائِرُ لِلنَّاسِ وَهُدًى وَرَحْمَةٌ لِّقَوْمٍ يُوقِنُونَ (20) Uwu ndi umboni womveka kwa anthu ndi langizo ndi chisomo kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro chokhazikika |
أَمْ حَسِبَ الَّذِينَ اجْتَرَحُوا السَّيِّئَاتِ أَن نَّجْعَلَهُمْ كَالَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ سَوَاءً مَّحْيَاهُمْ وَمَمَاتُهُمْ ۚ سَاءَ مَا يَحْكُمُونَ (21) Kodi anthu amene amachita zoipa amaganiza kuti Ife tidzawasamala monga mmene tidzasamalire anthu amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino zofanana ndi moyo wawo ndiponso imfa yawo? Iwo amaweruza molakwa |
وَخَلَقَ اللَّهُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ بِالْحَقِّ وَلِتُجْزَىٰ كُلُّ نَفْسٍ بِمَا كَسَبَتْ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (22) Ndipo Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi kuti mzimu uliwonse ukhoza kupeza dipo lake molingana ndi zimene udachita ndipo palibe amene adzaponderezedwa |
أَفَرَأَيْتَ مَنِ اتَّخَذَ إِلَٰهَهُ هَوَاهُ وَأَضَلَّهُ اللَّهُ عَلَىٰ عِلْمٍ وَخَتَمَ عَلَىٰ سَمْعِهِ وَقَلْبِهِ وَجَعَلَ عَلَىٰ بَصَرِهِ غِشَاوَةً فَمَن يَهْدِيهِ مِن بَعْدِ اللَّهِ ۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ (23) Kodi wamuona iye amene amasandutsa zilakolako zake kukhala mulungu wake? Mulungu wamusocheretsa iye ndipo wakhazikitsa chophimba m’makutu mwake ndi mu mtima mwake. Ndipo waika chophimba m’maso mwake? Kodi ndani amene akhoza kumutsogolera iye kupatula Mulungu? Kodi tsopano simudzakumbukira |
وَقَالُوا مَا هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا الدُّنْيَا نَمُوتُ وَنَحْيَا وَمَا يُهْلِكُنَا إِلَّا الدَّهْرُ ۚ وَمَا لَهُم بِذَٰلِكَ مِنْ عِلْمٍ ۖ إِنْ هُمْ إِلَّا يَظُنُّونَ (24) Ndipo iwo amati, “Kulibe china chilichonse kupatula moyo wathu wa pa dziko lapansi. Ife timakhala ndi moyo ndipo timafa ndipo palibe chimene chimationonga ife koma nthawi yokha ndiyo.” Ndipo iwo sadziwa chilichonse cha izo koma amangonena zongoganiza |
وَإِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِمْ آيَاتُنَا بَيِّنَاتٍ مَّا كَانَ حُجَّتَهُمْ إِلَّا أَن قَالُوا ائْتُوا بِآبَائِنَا إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (25) Ndipo pamene chivumbulutso chathu chomveka chimanenedwa kwa iwo, mtsutso wawo siukhala wina koma kuti, “Bweretsa makolo athu akale ngati zimene ukunena ndi zoonadi.” |
قُلِ اللَّهُ يُحْيِيكُمْ ثُمَّ يُمِيتُكُمْ ثُمَّ يَجْمَعُكُمْ إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ لَا رَيْبَ فِيهِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (26) Nena: “Mulungu amakupatsani inu moyo, amakuphani ndipo Iye adzakusonkhanitsani pa tsiku la kuuka kwa akufa limene lilibe chikayiko. Koma ambiri sadziwa zimenezi.” |
وَلِلَّهِ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَيَوْمَ تَقُومُ السَّاعَةُ يَوْمَئِذٍ يَخْسَرُ الْمُبْطِلُونَ (27) Mulungu! Wake ndi ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo patsiku limene ola lidzadza, onse amene amanenazinthuzabodzaadzatayachilichonse |
وَتَرَىٰ كُلَّ أُمَّةٍ جَاثِيَةً ۚ كُلُّ أُمَّةٍ تُدْعَىٰ إِلَىٰ كِتَابِهَا الْيَوْمَ تُجْزَوْنَ مَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (28) Ndipoiwe udzaona mtundu uliwonse utagwada pansi ndipo mtundu uliwonse udzaitanidwa monga mmene zidalembedwera. Lero mudzalipidwa molingana ndi zimene mudachita |
هَٰذَا كِتَابُنَا يَنطِقُ عَلَيْكُم بِالْحَقِّ ۚ إِنَّا كُنَّا نَسْتَنسِخُ مَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (29) Buku lathuli lili kunena za inu mwachilungamo. Ndithudi timalemba zonse zimene mumachita |
فَأَمَّا الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ فَيُدْخِلُهُمْ رَبُّهُمْ فِي رَحْمَتِهِ ۚ ذَٰلِكَ هُوَ الْفَوْزُ الْمُبِينُ (30) Ndipo iwo amene adakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Ambuye wawo adzawalowetsa m’chisomo chake. Kumeneku ndiko kupambana kwenikweni |
وَأَمَّا الَّذِينَ كَفَرُوا أَفَلَمْ تَكُنْ آيَاتِي تُتْلَىٰ عَلَيْكُمْ فَاسْتَكْبَرْتُمْ وَكُنتُمْ قَوْمًا مُّجْرِمِينَ (31) Koma iwo amene sadakhulupirire adzauzidwa kuti, “Kodi chivumbulutso changa sichidalakatulidwe kwa inu? Koma inu munali onyada ndipo munali anthu ochita zoipa.” |
وَإِذَا قِيلَ إِنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ وَالسَّاعَةُ لَا رَيْبَ فِيهَا قُلْتُم مَّا نَدْرِي مَا السَّاعَةُ إِن نَّظُنُّ إِلَّا ظَنًّا وَمَا نَحْنُ بِمُسْتَيْقِنِينَ (32) Ndipo pamene zidanenedwa kuti, “Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona ndipo palibe zokayikitsa za kudza kwa Ola”, inu mudati, “Ife sitidziwa kuti Ola ndi chiyani ndipo ife sitiliganiza kupatula kuti ndi maganizo opanda pake ndipo ife sitilikhulupirira ayi.” |
وَبَدَا لَهُمْ سَيِّئَاتُ مَا عَمِلُوا وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (33) Ndipozoipazonsezimeneadachitazidaonekerapoyera kwa iwo ndipo zonse zimene anali kunyoza zidzawapeza |
وَقِيلَ الْيَوْمَ نَنسَاكُمْ كَمَا نَسِيتُمْ لِقَاءَ يَوْمِكُمْ هَٰذَا وَمَأْوَاكُمُ النَّارُ وَمَا لَكُم مِّن نَّاصِرِينَ (34) Ndipo kudzanenedwa kuti, “Lero takuiwalani inu monga momwe inu mudaiwalira za tsiku lanuli. Ndipo malo anu okhala ndi ku Moto ndipo kumeneko sikudzakhala wina wokuthandizani.” |
ذَٰلِكُم بِأَنَّكُمُ اتَّخَذْتُمْ آيَاتِ اللَّهِ هُزُوًا وَغَرَّتْكُمُ الْحَيَاةُ الدُّنْيَا ۚ فَالْيَوْمَ لَا يُخْرَجُونَ مِنْهَا وَلَا هُمْ يُسْتَعْتَبُونَ (35) “Ichi ndi chifukwa chakuti mudatenga chivumbulutso cha Mulungu ngati chinthu choseweretsa ndipo moyo wa padziko lino lapansi udakunyengani inu.” Motero patsiku limeneli, iwo sadzachotsedwa ndipo sadzaloledwa kukonza zolakwa zawo |
فَلِلَّهِ الْحَمْدُ رَبِّ السَّمَاوَاتِ وَرَبِّ الْأَرْضِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (36) Motero kuyamikidwa konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa Kumwamba ndi Ambuye wa padziko lapansi ndi Ambuye wa zolengedwa zonse |
وَلَهُ الْكِبْرِيَاءُ فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (37) Ndipo wake ndi Ufumu wakumwamba ndi padziko lapansi ndipo Iye ndi Wopambana ndi Wanzeru zonse |